13.07.2015 Views

KUKONDWERERA CHIYERO

KUKONDWERERA CHIYERO

KUKONDWERERA CHIYERO

SHOW MORE
SHOW LESS

Create successful ePaper yourself

Turn your PDF publications into a flip-book with our unique Google optimized e-Paper software.

Lokonzedwa ndi Mpingo Wa NazareneChigawo Cha AfricaMwezi wa November 2011DONGOSOLO LOKONDWERERA <strong>CHIYERO</strong>Chaka cha 2012kuchokera ku Chigawo cha EurasiaDONGOSOLO LA UTUMIKI WA MPINGO,Kuthandiza Kukula Pa Moyo Wa Uzimu3


ZAMKATIMUGawo 1:Mungakhale Bwanji ndi Nthawi yachete Nthawi……………………………….6Gawo 2: Mphamvu ya KuukaKuchoka ku Pasala Mpaka ku PentecosteDevotions…………………………………………………………………………….. 7MAU OYAMBA………………………………………………………………………… 8Mphamvu ya Kuuka …………………………………........................................... 9WIKI YOYAMBA………………………………………………………………………… 12Mafunso oonjezeraMafunso……………………………………………………………………………….. 15WIKI 2…………………………………………………………………………………… 16Mafunso oonjezera …………………………………………………………………… 19WIKI 3…………………………………………………………………………………… 20Mafunso oonjezera………………………………………..………………………………………………… 22WIKI 4…………………………………………………………………………………… 23Mafunso oojezera……………………………………………………………………… 26WIKI 5…………………………………………………………………………………... 27Mafunso oonjezera…………………………………………………………………… 29WIKI 6 ………………………………………………………………………………….. 30Mafunso oonjezra……………………………………………………………………… 32WIKI 7……………………………………………….…………………………………… 33Mafunso oonjezera…………………………………………………………………….. 364


MUNGAKHALE BWANJI NDI NTHAWI YA CHETE PAPEMPHEROMlembi Dr Richard J KrejcirInto Thy Word Ministries6


7www.churchleadership.org


MUNGAKHALE BWANJI NDI NTHAWI YA CHETE PAPEMPHEROKUYAMBA: Mmene mungayandikire kwa Mulungu polimbikitsa ubale wanu ndi Mulungu!Petro woyamba akunena za kudzichepetsa kolola kuti munthu akule mwauzimu pophunzira mwapadera.Mwanjirazi pali kudzipereka pawekha komanso kukhala gawo la maphunziro a Mau a Mulungu. Petroakutiuza kuti tilolerane wina ndi mzake kuti tikadziwe chisomo cha Mulungu osati kupandukira Mulungu.Kachiwiri Iye akuti kuti sitiyenera kukhala odzichepetsa kwa wina ndi mzake komanso kwa Mulungu. Izindizodziwikiratu. Izi nzofunika kukula muuzimu osati chiwerengero chokha ayi. Tiyenera kukhalaophunzira a Yesu ndikukula muuzimu pakhalidwe lakupembedza Mulungu wamoyo!Kodi ndingalimbikitse Bwanji Ubale Wanga Ndi Mulungu kuti ndikhale wozama pamoyo wangawauzimu?Pano Pali Mfundo Zisanu ndi Zinayi (9) Zokuthandizani kulunjika kunjira yoyeneraA. CHOLINGA: Onani pamene muli mmoyo wanu wauzimu (Macitidwe 22:8-10; Afilipi 2:13) ndipomulunjike kumene mukufuna kupita. Kenaka khalani ndi cholinga ndikuchimvetsa bwino. Cholinga chanundikukhala odzala mwa Khristu Yesu (Akolose 1: 28), kapena munjira ina kunena kuti moyo wamunthuamene afanana ndi Yesu (Aefeso 4: 13). Kodi muli pati muuzimu komanso mukupita kuti? Osati kumenemukufuna kupita komanso kumene Mulungu akufuna kuti mupite?B. DONGOSOLO KAPENA ULENDO. Dziwani kuti pali Ndondomeko (Masalimo 16:11; 73:28;Miyambo 16:9; Ahebri 11:1-6) ikugwira ntchito. Sizimachitika tsiku limodzi kapena kukagula kusitolo ayi.Dongosololi ndinjira imodzi yothandiza kukula. Iyi ndi njira komanso ulendo. Iyi ndi sitepe yokuthandizanikukhala ndi nthawi yapadera ndi Mulungu tsiku ndi tsiku.Mwa ichi, ulendowu ngofunika zedi kutitiphunizre ndikukula! Ngati titafika paulendowu opanda kuvutika ndiye kuti sitingakule mmoyo wathuwauzimu! Onetsetsani kuti zolinga zanu zifanane ndi za Mulungu!C. Mukonze Pulani: Nthawi Isadafike (Yesaya 26:3; Marko 1:35). Izi sizimangochitika zokha.Muyenera kukhala ndi ndondomeko yabwino kuti nthawi yanu yapadera ikhala yabwino. Mungathekukhala ndi mabuku auzimu abwino ndikusankha amene mukhale mukuwerenga masiku 7 otsatirawo.Izi zidzathandizan kukhala ndi mabuku okwanira amene mungathe kuwalingalira. Mungathe kupezamlozo okuthandizani izi.D. Zoyenera Kuwerenga: Mukhale olunjika pazazimene Mukufuna kuwerenga panthawi yake(Masalimo 16:8-11) mmaphunziro anu. Mwezi umodzi mungathe kuphunzira buku limodzi lolembedwandi Paulo. Kenaka mungathe kuwerenga mabuku osimba zankhani zina monga la 1 Samuel. Kenakamungathe kupita ku Buku la chipangano chatsopano ndikukawerenga Buku lachiphunzitso chapaderamonga la Aroma. Kenaka nkupita kubuku la aneneri aang’ono monga Yoweli. Yesetsani kuwerengaBuku Lopatulika lonse pachaka chimodzi kapena ziwiri. Muyenera kuwerenga ndikudziwa mabuku onseosati kungowerenga ochepa okha. Muchite izi powerenga mabuku apadera auzimu. Muyenerakusakaniza mabukuwa!E. Kulunjika: Mukhale ndi nthawi patsiku yolunjika kukula kwanu kwauzimu tsiku ndi tsiku(Masalimo 119:130; Yesaya 42:16; Yohane 4: 23-24; 15), ndikuonetsetsa kuti izi zikuchitika. Lolani Yesukuti akusintheni maganizo anu ndi mau a Mulungu. Maganizo anu ndi ofunika zedi! Mukakhala pamasopa Mulungu mmau Ake, muyenera kuwerenga mavesi mosamalitsa osati mothamanga. Izizidzakuthandizani kulunjika. Anthu ambiri amakonda kulemba zimene akuwerenga ndikukafunsa anthuena kuti awathandize bwinobwino.F. ZIPANGIZO: Mukhale ndi zipangizo komanso Buku Lopatulika labwino (Aefeso 4:1-3) mukhalendi mtundu wa Buku Lopatulika umene mungathe kuumvetsa bwino. Mukhalenso ndi kopelokuthandizani kulemba zinthu zimene mwaphunzira komanso zimene simukuzimvetsa bwino.G. MALO OYENERA: Sankhani Malo a Chete (Luka 5:16) mukhale ndi malo opanda phokoso lambiri.Mutseke chitseko, wailesi, TV ndi zina zokusokonezani. Ngakhale foni muizimitse. Nthawiyi ndiyokumana ndi Mulungu!H. NTHAWI YOYENERA: Khalani ndi Nthawi yabwino (Aefeso 2:18). Sankhani nthawi yanuyowerenga mau mwapadera. Kawirikawiri mmawa ndi wabwino kukadali bata. Ngati simumathakulawira sankhani nthawi imene mumakhala ochangamuka patsiku lanu kuti mukumane ndi Mulunguwanu. Mukhale ndi nthawi yowerenga mau a Mulungu komanso kupemphera. Kumbukirani nthawi ndiyopatulika chomwecho muyenera kupatula nthawi yokumana ndi Mulungu wanu. Musangotaya nthawipa inu nokha koma kufuna Mulungu kuti mukule mmoyo wanu wauzimu.8


HOW TO HAVE A DEVOTIONAL TIMEI. KUGAWANA NDI ANZANU: Zimene mwaphunzira (Masalimo 55:14; Mateyu 18:20; Aroma 12; 2Akorinto 12:18). Timaphunziranso pakuchita ndi kugawana ndi Ena. Zimene taphunzira siza Ife tokhakomanso tiphunzitse Ena! Mzimu wofuna ndi wophunzitsika ndi umene umapanga ophunzira wabwinowa Yesu!Kuchokera kumfundo 9 zimene taphunzira zidzathandiza Ife kukhala okula mmoyo wathu wauzimu.Tiyenera kuchita zimene ophunzira ayenera kuchita osati kungophunzira kapena kulalikira. Ife tiyenerakukhala zitsanzo zabwino kwa Ena. Tiyenera kulipira dipo lake kuti tikhale ophunzira oyenera AkhristuYesu. Zikatere tidzazama mumoyo wathu wauzimu!KUCHITAPO KANTHU: Nazi mfundo zina zothandizira kuchitapo kanthu panthawi yachete ndiMulungu:A. Simudzakhala okondwa ndi nthawi yachete pokhapokha mutakhala ndi nthawi yakuchita zimenemukuphunzira panthawi yacheteyo kwa Mulungu. Muphunzire modzipereka kuti Mulungu akuuzenichochita panthawi yachete. Keneka muzichita zimene Mulungu akukuuzani mosaopa. Dalirani pa Yesundi mau Ake!B. Muchite momveka bwino. Mukhale ndi ntchito yoyenera kuchita kwa banja lanu, anzanu, makolo ndiEna mukatha kuphunzira ku mau a Mulungu.”C. Nthawi zina mungathe kupeza njra zingapo zimene Mulungu angathe kukuyankhulani pamenemukuwerenga mau a Mulungu. Muyenera kusankha ndime ina imene mwaiona ndikuchita zomweMulungu akufuna mmoyo mwanu. Musankhe njira imene mungakwanitse kuichita panokha.D. Mukhale ndi zochita zanu nthawi yapafupi monga tsiku, sabata mwezi ndi moteromo. Mukhalenso ndichimene mungachite mutawerenga mau pachaka kapena zaka zingapo. Zikachitika, muyamikeniMulungu. Mulungu ayenera kugwira ntchito yatsopano mwa Inu ndipo muyenera kumthokoza tsiku nditsiku.KUTSILIZA:Pali njira zambiri tingathe kuwerengera mau a Mulungu komanso kupemphera patokha. Akhristu ambiriamaganiza kuti akule mmoyo wao wauzimu ndikumvera kanema kapena ulaliki pawailesi pokha. Komaiyi sinjira yakuti mukakule muuzimu. Tiyenera kuulula mmoyo wathu wauzimu powerenga mau aMulungu patokha. Tiyenera kuwerenga mau a Mulungu, kupemphera komanso kudzipereka ku utumikipochita zimene mau a Mulungu akunena: Yesu sadafunse anthu kutumikira popanda mphamvu yake. Izizikulimbikitseni inu (Mateyu 28:20)!Kumbukirani kuti Yesu amakukondani Inu. Njira zake zimationesa Ife ndipo timukhulupirire mpakamuyaya osati pazofuna zathu!Onani 1 Akorinto 2:14-15Mavesi Ena oyenera kuwalingalira pakukula mwa Ambuye ndi awa; Miyambo 18:24; Mateyu 7:18-24;10:1- 42; 19:28-30; 28:16-20; Marko1:1-5; 1:35 – 2:12; Luka 9:23-25; 48; Luka 14:26-27; Yohane 8:31;12:20-26; Yohane 14; 15; 1 Yohane 5:3; Aroma 12; 1 Akorinto 3:5-11; 12; Agalatiya 6:1-10; 2 Timoteyo2:7; 1 Petro 3:159


MPHAMVU YAKUUKAKuchoka ku Pasaka kunka ku PentekosteMlembi Gary MooreMavesi Atengedwa ku Buku Lopatulika , NEW INTERNATIONAL VERSION®. Copyright © 1973, 1978,1984 by Biblica, Inc. All rights Reserved Worldwide. Used by Permission.10


ZOONJEZERAMPHAMVU YAKUUKAChigwawo cha Africa mumpingo wathu chikulimbikitsa kugwilitsa ntchito maphunziro auzimuwakuyambira mmabanja. Zonse zimayambira pabanja ndipo banja liyenera kupindula izi.Makolo akulimbikitsidwa kuphunzira ndi ana komanso achinyamata pamaphunziro apaderawapazokambiranazi. Pachifukwachi, taika mafunso olimbikitsa kukambirana pakutha pasabata iliyonse.Izi zilimbikitsa kukambirana mmabanja ndikugonjetsa mayesero. Atsogoleri ayenera kuwerenga bukuliasanaphunzitse kuti alimvetse bwino.Pophunzitsa Ana mavesi akhale aafupi kuti azindikire bwino). Ndibwinonso kuti mulembe mapempheroapadera kwa Ana kuti atsatire bwino.Dr Gary Moore ndi mlembi wamaphunziro 6 oyambirira. Maphunziro apadera a wiki 7 adalembedwa ndianthu otsatirawa pokhudzana ndikukondwerera chiyero:Dr Stan A Toler (SAT), General Superintendent wa Chigawo cha Africa , Dr Filimao Chambo (FMC),Mkulu woyendetsa ntchito zampingo muno mu Africa, Rev P Collin Elliott (PCE), mkulu woyendetsantchito zampingo wathu kummwera kwa Africa, ndi Dr Louis E Bustle (LEB), mkulu woyendetsa ntchitozamishoni muno mu Africa. Maina onse a Alembi akupezekanso pakutha pamaphunziro amene Iwoadalemba.Ndi pemphero lathu kuti pakutha pamaphunzirowa msabata zingapo zikudzazo, muona chigonjetsondikuuka kwa Yesu ndipo limodzi ndi mpingo wa Nazarene muno mu Africa mukondwerera chiyero!11


MPHAMVU YAKUUKAKodi mukaganiza zakuuka ndi chiyani chimene chimabwera mmaganizo Anu? Kwa Ena ndi zimenezidachitika zaka zoposa 2,000 zapitazo. Timakambirana pa pasaka koma ndi nthawi iti imenetimanenanso za izi? Mwina sinthawi zonse. Timatha kunena za katswiri wampira, wandale komansowothamanga kwambiri pamene sitikonda kukamba zakuuka kwa Yesu pamoyo wathu watsiku ndi tsiku.Paulendo wathu wasabata 7 zikudzazi tikamba kwambiri zakuuka kwa Yesu kwa Akufa. Komabesitikufuna kunena za izi ngati mbiri chabe koma kudalira kwa Yesu kuti atiphunzitse Ife tonse.Mphamvu yakuuka imene akunena pa Afilipi 3: 10-11 ndiyosintha moyo. Ambiri mwa Inu mungathekuchitira umboni koma mumatha kungofika kwa Yesu pokhulukilidwa machimo ndikufuna moyo wosathachabe. Uku ndiye kusinthika kwa moyo. Pamene mphamvu yakuuka imene Paulo akunena ingathekusintha miyoyo yathu tsiku ndi tsiku. Uku ndikuyankhula molimba mtima. Mwina Ena simungathekugwilizana nazo.Ulendowu ndiwozindikira mphamvu yakuuka yosintha dera lililonse lamoyo wathu. Ndikupemphani kutimutsekule mitima yanu ndikulola Mulungu kuti akuonetseni mphamvu yakuuka kuti mukhale ogonjetsammiyoyo yanu.Nthawi iyi ingathe kukhala yoyenera kupemphera limodzi pemphero ili:“Ambuye tikudziwa kuti munatidalitsa, kutikhululukira machimo, komanso kutisankha Ife. Tikufunakukhala miyoyo yathu mokusangalatsani inu. Ife tikufuna kuti tikudziweni Inu komanso mphamvu yanuyakuuka Inu Yesu. Amen.”12


WIKI 1MPHAMVU YAKUUKA“Ndikufuna kudziwa khristu ndi mphamvu ya kuuka kwake komanso kugawana naye masautsoAke komanso kupeza kuuka kwa Akufa Afilipi 3:10-11.TSIKU LOYAMBAKodi mumaganiza chiyani mukamva mau akuti mphamvu? Izi zimatengera zimene mukuganiza kaya ndipandale kapena mpira. Mukaganizanso za anthu odziwika mwina maina a Mayi Teresa kapena aGandhi ndi amene amabwera msanga mmaganizo.Mukamva mau akuti mphamvu yauzimu kodi mumaganiza chiyani? Ena mwa Ife timaganiza zachikhulupiriro, machiritso, kumasulidwa,zodabwitsa, kapena uneneri. Ifenso sitingalakwitse ponena kutiizi zimalumikizika ndi mphamvu yauzimu. Tiyeni tidzipatse mayeso ophweka kaye Kodi zinthuzanenedwadi zingakhale zitsanzo za mphamvu yauzimu, inuyo moyo wanu uli pati? Kodi mumaonamachitachita otani okhudzana ndi machiritso, zodabwitsa, chikhulupiriro ndi zina mmoyo wanu? Ambirimwa Ife tinena kuti sikwambiri kapenanso kuti palibe chilipo.Tiyeni tione mphamvu ina yokhudzana ndi mphamvu yauzimu macitidwe 1:8, “mudzalandira mphamvuya mzimu woyera ndipo mudzakhala mboni zanga, mzimu woyera atadza pa Inu. Mwina tikanenazakuchitira umboni sitinayambe izi.Timakonda kumva za mphamvu yakuuka koma ambiri mwa Abusa, amishoni ndi alaliki sitifunakuzilumikizitsa kumphamvu yamzimu woyera. Ambiri mwa Ife tikuchita mwa ife tokha koma tikulephera.Timakonda Mulungu ndi chisomo chake koma ndi angati mwa Ife amene tikuyenda mumphamvu yaMulungu?Ndikukhulupirira kuti tingathe kukhala amphamvu muuzimu kulikonse kumene tili. Mulungu watipatsachilichonse kuti tikhale amphamvu muuzimu.Chofunikira ndi kukhala malo oyenera ndikuchita zoyenera. Mzimu Woyera atithandize kukhala malooyenera muuzimu. Tiyeni tivomeleze kulephera kwathu kuti Mulungu atithandize.Pemphero Lalero:“Mulungu wanga, ndikudziwa za chisomo ndikupezeka kwanu. Inu mwandipatsa chilichonse chofunikamwa Yesu Khristu, mwana wanu. Mmasiku akudzawa mundithandize kuti ndikhale mmalo oyenerakulandira mphamvu yamzimu woyera kuchokera kwa inu. Amen.”TSIKU LACHIWIRIKodi, mphamvu yakuuka ndi chiyani? Tiyeni tione mwapadera mavesi a pa Afilipi 3: 10-11. Vesi 10ikuyamba ndikuti, “Ndikufuna kudziwa khristu.” Onani Afilipi 3:8-9, ndikulunjika pa vesi 8,“…Ndaganizira chilichonse kukhala chotayika kusiyanitsa ndi kupambana kwakukulu kodziwa YesuKhristu Ambiye wathu.” Awa ndi mau amphamvu. Tiyeni tikhale oona mtima ndikufunsa mafunso amenetimafunsa, “Kodi Paulo amatanthauzadi zimene amanena?” Kodi Iye amatanthauzanji kuti kudziwa Yesukudali kofunika kuposa zonse?Timakonda kunena kuti Iye adali mtumwi ndipo Ine ndine munthu wamba ndiye sindingathe kufika paPaulo mtumwi. Koma mukalola kuti mphamvu yakuuka ikonzenso moyo wanu ndiye kuti mungathekukhala ngati Paulo mtumwi.Tiyeni tione vesi lapaderali. Mau akuti kudziwa pa vesi 10 ndi ochititsa chidwi. Tikangowatenga mauwamwachizolowezi ndiye kuti sititha kumvetsa chimene Paulo akunena. Kodi munthu akakufunsanizamunthu wina ngati mukumudziwa mumamuyankha bwanji? Nthawi zambiri mumati inde pamenemunthuyo ndi mzanu chabe. Koma akakupanikizani mumati sindimamudziwa Iye kwambiri.”Mau amene Paulo akugwiritsa ntchito sakanatha kugwiritsidwa ntchito pamenepa. Mau ameneadagwilitsidwa ntchito mu chigriki akunena zamunthu amene ali bwenzi lenileni. Mauwa amagwilitsidwantchito pachigriki kwa anthu okhalira malo amaodzi ngati banja. Pogwlitsa ntchito mauwa zikutanthauzaubale weniweni ndi Khrist.Koldi ndi ubale wotani muli nawo ndi anthu Ena pakalipano. Ngati muli pabanja, mwina ndi akazi kapenaamuna anu. Kodi ubalewu udakhala wamphamvu motani? Khalani ndi nthawi yolganiza mmene ubalewu13


ungalimbikitsidwe. Kenaka mudzaona zimene Paulo amatanthauza pomudziwa Yesu.” Kenakadzifunseni mmene ubale wanu ndi Mulungu ukuyendera. Kodi zikufana ndi mmene ukuyendera ndibanja lanu? Taganizani mmene mungachitire kuti ubale wanu ukhale womdziwa Yesu kotheratu”Pemphero Lalero:“Ambuye Mulungu,sindikufuna kunena kuti: ‘sindikumudziwa bwino.’Koma ndikufuna kunena kuti:‘ndikumudziwa’ Ndingathe kukonzanso ubalewu poyesetsa kukhala ngati Inuyo.Ndithandizeni Ambuyekukudziwani nthawi iliyonse koposa kale lomwe. Amen.”TSIKU LACHITATUSitingathe kukhala ndi mphamvu ya kuuka ngati sitimudziwa Yesu.Nchifukwa chake Yohane 15:4ndithandizo kwa Ife. Apa ndi pamene Yesu akukhazikitsa kwa Ophunzira Ake kuti Iye ndi mpesa ndipoIfe ndi nthambi zake.pa vesi 4, “khalani mwa ine ndipo ndidzakhala mwa Inu. Palibe nthambi imeneingabale zipatso osakhala mumpesa. Yesu akuti sitingabale zipatso ngati sitikhala mwa Iye). Izituzikutanthauza kukhala mwa Yesu mmene Paulo adanenera ku Afilipi pomdziwa Yesu. Kubereka zipatsokukufanana ndi mphamvu yakuuka.Kodi Mphamvu yakuukayi ndi chiyani? Kuti tiyankhe tione kuti chimachitika ndi chiyani kukhala opandamphamvu pamene tikuti ndife Akhristu. Ife tingathe kunena kuti mkhristu ndi amene amakhala mwakhristu” (2 Akorinto 5: 17) komanso wotsatira wa Yesu weniweni. Ngati izi sizili chomwechi ndi Inu,muime kaye ndikupempha Yesu kuti alowe mmoyo mwanu kuti muyambe kumdziwa. Muyenera kulapapa 1 Yohane 1:9 akuti“Ngati tivomereza machimo athu, ali wolungama Iye, kutisambitsa ndikutichotseramachimo athu onse).Kodi inu moyo wanu uli pati? Kodi ndi chiyani chimene chikutikaniza kulandira mphamvu yauzimu?Tingathe kulemba zambiri mwa izo zakunja kwa thupi lathu.Izi ndikunena ngati kusadziwa mau aMulungu komanso zokumana nazo tsiku ndi tsiku.Zinthu zina zimene zimatichotsera mphamvu ndi mavuto opezeka mmasiku omaliza.Kodi zimatichotsera mphamvuyi ndi chiyani? Imfa kapena uchimo kodi. Tikadzisanthula mmoyo mwathutingathe kupeza zenizeni zotipombonetsa. Khalani ndi nthawi yapemphero. Kodi mmaganiza chiyanizaimfa ndi uchimo? Muganize mozama.Pemphero Lalero:“Ndikupemphera lero kuti ndikufuneni ndikundisanthula chimene chikundilepheretsa kupeza mphamvuyanu yakuuka imene Paulo adainena. Ndikufuna kukhala mwa Inu ndikubala zipatso. Amen.”TSIKU LACHINAYIPoganiza mozama mungathe kutsutsana nazo kuti Imfa ndi uchimo ndi zimene zikutikaniza kupezamphamvu yakuuka yauzimu. Kodi kumudziwa Yesu ndikuuka kwake kungasinthe miyoyo yathu? Tiyenitione zinthu zakupha mphamvuzi komanso kuti zimatikanikiza pansi bwanji kuti tisaone mphamvuyakuuka.Kodi uchimo ndi chiyani komanso umatikhudza bwanji? Choyamba chokhudzana ndi uchimo ndichakutichimatilekanitsa ndi Mulungu wathu. Mumachaputala atatu oyamba mbuku la geneses tikuona mmeneuchimo unasiyanitsira munthu ndi Mlengi wake. Chifukwa chiyani? Mulungu ndi Oyera ndiposalumikizana ndi uchimo. Kumbukirani Mose pamaso pa Mulungu pamene adaopa kuti afa? Iyeadadziwa kuti munthu ndi ochimwa ndipo munthu akalumikizana ndi Mulungu ali ochimwa angathe kufa.Yesaya adakumananso ndi izi pamene adati pa Yesaya 6:5 “tsoka kwa Ine.” Kodi amalira chiyani? Iyeamaopa kuti afa chifukwa adadziwa kuti ndi ochimwa koma adaona Mulungu oyera. Kuyambira nthawiya Adamu timabadwa ochimwa Aroma 5:12 pamene Aroma 6:23 akuti Pakuti onse adachimwanaperewera pa ulemerero wa Mulungu.Kodi mukadakhala bwanji mukadadziwa kuti uchimo ulibe mphamvu pa Inu? Kodi Yesu atafa pamtandaadatenga chiyani ndi Iye. Werengani Akolose 2: 13-15. Iye adasenza machimo athu onse. 1 Petro akutiYesu ndi chilungamo chathu”Ndili ndi vesi ina yakuti muwerenge mwapadera. 1 Yohane 3:4-10. Kodi mwawerenga? Pa vesi 8pamandikhudza kuti Yesu adadza kudzaononga ntchito za satana.”Yesu asadangobwerera14


kudzatipulumutsa ndikutipatsa moyo wosatha komanso kudzaononga satana. Ngati Yesu adakwaniritsantchito yake ndiye kuti uchimo uli ndi mphamvu yotani pa Ife?Kuuka kwa Yesu kudaononga mapulani onse a Satana. Kuuka kudalungamitsa Imfa ya Yesu komansochilichonse chimene kuphatikizapo mphamvu yathu pa uchimo. Pokhala mphamvu yakuukazikutanthauza kukhala a ufulu ku uchimo.Pemphero Lalero:“Zikomo Yesu pochotsa uchimo wanga onse pamene mudakhomedwa pamtanda chifukwa cha Inechifukwa ndili ndi ufulu mwa Inu. Chonde ndithandizeni kuti ndisaiwalire tanthauzo la mphamvu yakuuka kwanu. Amen.”TSIKULACHISANUNdikudziwa kuti mukuganizabe za nkhani ya uchimo. Mukuganiza za kufunika kwake. Inde mphamvu yakuuka ndi yokoma zedi. Tidzanena za izi sabata lamawa pamene tidzamva mmene tingapezeremphamvu yakuuka. Lero lino, tione zachinthu china chimene chimatilepheretsa mphamvu ya kuukachimene ndi Imfa.Palibe amasangalala ndi Imfa. Mkudziwa kapena kusadziwa takhulupirira mau akuti moyo umabwerakamodzi ndiye tichite zimene tikufuna. Kodi ndi izi timachita chiyani wina akatikumbutsa za imfa? Nthawizambiri timathawa kunena za ichi. Kodi timatani?Kodi tiyenera kufa chifukwa chiyani? Chifukwa cha Imfa. Pa Genesesi 2:17, Mulungu akuti kwa Adamundi Hava asadye chipatso chakudziwitsa zabwino ndi zoipa chifukwa adzafa” panthawiyi Adamu ndiHava adali asadafe chifukwa Iwo adali atalengedwa kuti akhale masiku onse koma uchimoudawasokoneza (Onani Genesesi 1:27). Nkhani yoona ndiyakuti Adamu ndi Hava sadafe nthawiyomweyi. Koma kuyambira tsiku ilo adayamba kuonana ndi imfa. Chifukwa cha uchimo adaona imfa.Uchimo udalowa mdziko mwa Adamu, Aroma 5:12 zotsatira zake ndi Imfa pa (Aroma 6:23).Ganizirani za Yesu pamtanda. Sizinali zabwino. Taonani Yesu wolungama adaweluzidwa. Onani 2Akorinto 5:21. Mulungu adachita izi kukaononga ntchito za satana.Ife amene tili mwa Yesu tikusinthika kuti tifanane ndi Yesu(2 Akorinto 3:18)Kodi mudakadziwa kuti mudzakhala nthawi yonse ndikuti uchimo ulibe mphamvu pamoyo wan u,mukadakhala bwanji mmoyo mwanu? Koma mukuti tidzafabe! Buku Lopatulika likuta Kwaikikakwamunthu kufa kamodzi ndipo pakutha pake chiweruzo,” (Ahebri 9:27)? Koma kwa Ife amenemphamvu ya kuuka ili mwa Ife chiweluzo chilibe mphamvu pa Ife lero lino pamene tifa kumoyo uno.Werengani mau a Mulungu pa Afilipi 3:18-21. Kukhala mumphamvu yakuuka zikutanthauza kutitimaonera zinthu munjira ina. Timaona zinthu mwa ufumu wakumwamba. Imfa siyankho yotsiliza. Kodikukhala mphamvu yakuuka kumatisintha motani mchikhalidwe chathu:“Ndikuthokoza Mulungu chifukwa Imfa siyankho lotsiliza kwa Ine.ndithandizeni kuti ndikhale mmoyo wamphamvu yakuuka. Ndisintheni kuti ndifanane ndi Inu. Amen.”TSIKU LA CHISANU NDI CHIMODZILero ndikufuna kuti tionenso zimene mwaphunzira mmasiku asanu apitawa.talembani kuti moyo wanuukadakhala wotani ngati uchimo ndi imfa ukadachotsedwa ngati zitsa zamoyo wanu. Ngakhalemukudziwa kuti izi sizoona yesetsani kulemba. Kodi moyo wanu ungasinthe kapena ayi?Pemphero Lalero:“Ndikulingalira za Inu Ambuye lero chifukwa cha zimene mwandionetsa masiku apitawa ngati nditasinthandikukhala mmoyo wa mphamvu yakuuka kwanu. Amen.”TSIKU LA CHISANU NDI CHIWIRILero ndikufuna kuti muwerenge Masalimo 103 panokha. Muone Masalimo 103 ndimphamvu yakuukakwa Yesu. Muwerenge, kuloweza komanso kuimba. Mukhale ndi tsiku labwino. Tionane mawa pamenetidzayamba kuyankha mafunso akuti Ndingapeze Bwanji Mphamvu ya Kuuka?”Pemphero Lalero:15MPHAMVU YAKUUKA


“Chikondi chanu pa Ine ndi chodabwitsa, zifundo zanu ndi malonjezo anu mu Masalimo 103 angathekukhala anga pamene ndikhulupirira ndikuona mumphamvu yanu. Amen.”MAFUNSO OONJEZERA MMABANJA:Kuuka kutanthauza kupezanso moyo; mphamvu ndiyakutha kuchita. Mwa ichi mphamvu yakuukandikuthekera kuchita zinthu chifukwa mphamvu yakuuka ili mwa Ife.Kuti Ana anu azolowere za mphamvu yakuuka achite izi pamene amva mphamvu yakuuka:• Kukweza manja awo kuchoka munsi mwa chuuno kupita pamwamba pamutu• Kenaka kutsitsa manja awo kuti minofu itakasukeTSIKU LOYAMBA:1. Kodi mukuganiza kuti kuli amuna ndi akazi a Mulungu amene ali ndi mphamvu yakuuka lero lino?Mungathe kunena za Ena amene mukuwadziwa?2. Tanenani zimene zimawayenereza kutero.3. Kodi mukuganiza kuti kupempha thandizo ndiye kuti mwalephera?TSIKU LACHIWIRIMzanu kwambiri ndi ndani? Mudakhala bwanji abwenzi? Umu ndi mmene Paulo amamudziwira Yesu.Kodi mungatani kuti Yesu akhale mzanu wa ponda apa nane mpondepo?1. Kuti mukhale ndi ubale wabwino ndi Ena mumayenera kudzipereka kwa iwo. Kodi izizikutanthauzanji?2. Kodi munthu angadzipereke motani kwa Mulungu kuti amudziwe kwathunthu?TSIKU LACHITATUKulapa kumatanthauza kukana uchimo ndikupita kwa Mulungu. Timayamba kukhala monga Yesu.Kulapa machimo ndi pamene tavomereza ndikulola Mulungu kuti atikhululukire. Uchimo ndi zimenetimachita pomukwiyitsa Mulungu wathu. Anthu amachimwa chifukwa anabadwa ndi nthenda yotchedwauchimo imene imawachimwitsa.1. Kodi ndi zinthu ziti zimene mumachita zimamukwiyitsa Mulungu?2. Kodi ndi chifukwa chiyani chimene Mulungu adamutumizira Yesu?3. Onani uchimo uli mkati mwanu umene ukuchititsa kuti mphamvu yakuuka isagwire bwino ntchitomwa Inu.4. Kodi kufa muuzimu kukutanthauzanji?TSIKU LACHINAYI1. Kodi ndi zoona kuti Yesu adapachikidwa chifukwa chamachimo athu?2. Kodi uchimo umachita chiyani kwa Inu?3. Kodi ufulu wa ku uchimo umachititsa kuti tipitirire kuchimwa kapena ayi?4. Malingana ndi 1 Yohane 3: 4-10, kodi mungasiyanitse bwanji Ana a Satana ndi Ana a Mulungu?5. Kodi izi zikunenanji zamphamvu yakuuka kumene imachokera?TSIKU LACHISANU1. Kodi mukuganiza chifukwa chiyani anthu safuna kumva kapena kunena za Imfa?2. Kodi Afilipi 3: 18-21 akuti akhristu kwao ndikuti? Izi zikusintha motani za imfa?TSKU LA CHISANU NDI CHIMODZI1. Jambulani chithunzi chosonyeza mphamvu ya Mulungu mmoyo wanu.2. Ganizirani njira zimene Mulungu wakugonjetserani msabatayi.TSIKU LA 71. Kodi mukuona chiyani za Mulungu pa Masalimo 103?2. Nanga mukuona chiyani za inu mu Masalimo 116


WIKI 2“Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, . Monga nthambi siingathe kubala chipatso payokha, ngatisiikhala mwampesa. , motero mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine. Yohane 15:4.TSIKU LOYAMBANdidamva zankhani ya mnyamata wina amene adali paulendo kuchoka ku Amerika kupita ku Ulaya. Iyeadadza ku Amerika kuchoka ku England ali wachichepere ndi makolo Ake ndipo amaganiza zokachezaku England kumudzi kwao. Apa nkuti ndege kudalibe ndipo amaganiza kuti akwera sitima kuchoka kuNew York kupita ku England. Iye adasunga ndalama yogulira tiketi yaulendo wake kwazaka zambiri.Kenaka Iye adakwera sitima nayamba ulendo wakwao ngati kutulo.Panthawi yachakudya chamadzulo, mnymatayo adapita kuchipinda chake natengako cheese ndimabisiketi chifukwa adali ndindalama zochepa. Tichakudyato timakoma ndipo sadadere nkhawa kutiulendo wake onse akudya zakudya zofanana.Ali paulendo Iye amatha kucheza ndi anzake mmbali mwa sitimayo. Tsiku lina mnyamata nzakeadamufunsa kuti nthawi yachakudya chamadzulo Iye sakumaoneka. Iye adati ndikadakonda kuperekachilichonse kuti ndipeze chakudya nchifukwa chake ndimapita kuchipinda kwanga ndikukadyacheese.”Mzake adamufunsa kodi siudagule tikiti yasitimayi?.Mnyamatayo adati ndili nayo nchifukwa ndili muno!Mzakeyo adati kodi Iwe siudziwa kuti tikiti yako ikulola kudya zakudya zabwino musitima ino kumaloodyera?.”Akhristu Ena ali chimodzimodzi, akufuna kuzunzika paulendo wao wakumwamba pokana mphamvu yaYesu ya kuuka. Kodi mphamvuyi tingaipeze bwanji monga Paulo adachitiraMau a Mulungu akuti pokhulupirira Yesu tili ndi moyo wosatha Yohane 3:16.Werengani pa Yakobo 2:14-19.Pemphero Lalero:“Zikomo Ambuye pondiitana kugome lanu lachipulumutso ndi mphamvu.Ndikufuna kuti paulendo wangawauzimu ndiyende mumphamvu yakuuka. Amen.”TSIKU LACHIWIRIMPHAMVU YAKUUKATikaitana anthu kumpingo komanso kugawana nawo uthenga wabwino, timayesetsa kuupanga kukhalawophweka kuumva. Kumbukirani sabata latha tidanena za Aroma 6:23, kuti Pakuti mphoto ya uchimondi Imfa?”koma kutsiliza akuti koma mphotho ya Mulungu ndi moyo wosatha mwa Yesu khristu.”Chipulumutso ndi mphatso ya chisomo (Aefeso 2:8-9).Tiyeni tionenso pa Yohane 3:16 . Kodi ngati ndikufunika kukhulupirira kuti ndipeze moyo wosatha kodimphamvu yakuuka ndi yofunika bwanji? Kodi mphamvu yakuuka ndidzaifuna ndikafa osati pano. Mongamnyamata amene amadya cheese koma tikiti ikumulola kudya nyama ifenso tiyenera kuonazotiyenereza paulendo wauzimu?.Kodi Yesu amaitanira anthu kuchipulumutso motani? Yesu asadaumilize Nikodemo kuti abadwensokoma adamuuza zakubadwa mwamadzi ndi mzimu (Yohane 3:3). Werengani Mateyu 4:18-22. KodiYesu adati chiyani kwa Andreya, Petro, Yakobo ndi Yohane? “Idzani munditsate Ine.” Pa Luka 5:27-31,Yesu akuitana Levi (Mateyu) kuti unditsate ine.”Mungathe kunena kuti Yesu amanena ophunzira Ake osati Inu ndi Ine. Ngati mukufuna kudziwa mmeneYesu amaitanira Anthu Ake ndi mphamvu ya kuuka werengani Mateyu 19:16-26. Tayerekezani mmeneIfe tikugawira uthenga kwa Anthu lero lino. Pamene mnyamata adati wasunga malamulo onse, mwinasitikanangomubatiza koma kumukhazikanso kukhala mkulu wampingo wathu. Koma Yesu adamuuzakuti Idza unditsate Ine.”Nkhani ndiyakuti sitingatsatire Yesu mumphamvu yathu ayi. Nchifukwa chake atafunsidwa kuti ndindaniangathe kupulumuka, Yesu adati mumphamvu yake nzosatheka koma mumphamvu ya Mulungu Mateyu19:25.17


Kodi inu pochitapo kanthu mutalandira uthenga wabwino mudapulumuka kuti muzipita kumwambakapena kumutsatira Yesu?Pemphero lalero:“Ambuye Mulungu sindikufuna kukutsatani mwamphamvu yanga, kuopa kukhala opusa. Mudanena kalekuti zinthu zonse zitheka ndi Inu osati munthu. Amen.”TSIKU LACHITATUImodzi mwa ndime zimene zimandisangalatsa mu Buku Lopatulika ndi Mateyu 16:13-28. Tsekulanipamenepa kuti tiwerenge pamodzi. Apa Yesu adali ataletsa namondwe panyanja, kuchotsa ziwanda,kudzutsa kabuthu kakufa komanso kudyetsa anthu zikwi zisanu. Mitu ya ophunzira idazizwa ndimphamvu ya Mulungu. Yesu adawafunsa funso kuti kodi inu mumati ndine ndani?”Kodi ndifunso lofunika bwanji kwa tonse.Petro adayankha yankho la mphamvu ndi loona: “Inu ndinu Khristu, mwana wa Mulungu wamoyo.” Yesuadayankha kuti mwamphamvu yakuuka adzamanga mpingo wake (18-19). Iye adanena zamasautsondipo Petro adamudzudzula Yesu. Chifukwa chiyani? Petro amafuna za Iye yekha ndipo sadamvetsecholinga cha Yesu.Pa vesi 24, tikufika pamtima pamphamvu yakuuka. Choyamba ndikudzikana wekha. Tikane zokhumbazathu.Kwa Ena kudzikana timaganiza zambiri monga nyengo ya Lenti kupunguza ndikusala kudya izinzofunika koma osati kwambiri.Pokhapokha titakumana ndi Yesu moyo wathu umakhala wamphamvu.Pamene takhala mwa Yesutimalolera kutsogozedwa ndi mphamvu yake. Tiyenera kumudziwa Iye.Tiyenera kusangalatsa Mulungu osati munthu monga Paulo adachitira. Tiyenera kuchita zimene Yesuakufuna.Tiyeni tiwerengenso Afilipi 2:1-11. Pa vesi 7 akuti mwa Iye yekha Paulo ali chabe.Kudzikana tokha ndikuchita zimene Yesu akufuna poombola miyoyo yotaika. Tiyenera kumudziwa Yesundi mphamvu yake.Pemphero Lalero:“Ambuye Mulungu mundithandize lero, kutha kuona mmene ndingadzikanize ndekha, kuzinthuzondilepheretsa kukhala inuyo. Ndikufuna kuti zokhumba zanu zikhalenso zanga, kukhudzika kwanukukhalenso kwanga. Sindikufuna kuti nditaye kudzipereka kwanga kwa Inu chifukwa ndikufunakukufunani Inu koposa kale. Amen.”TSIKU LA CHINAYIDzulo tidaona kuitana kwa Mulungu kumphamvu yakuuka. Lero tiona gawo lachiwiri lokhudzana ndi paMateyu 16:24. Yesu atatha kutiitana kuti tidzikanize tokha akunena kuti titenge mtanda wake.” Koditingachite bwanji izi? Ndimaganiza kuti Yesu adafa pamtanda kale ndipo Ife sitiyeneranso kutero. Koditingasenze bwanji mtanda wake?Tiyeni tipite kuvesi lathu limene lamanga nthenje la pa Afilipi 3:10-11. “Ndikufuna kudziwa Khristu ndimphamvu yakuuka kwake komanso kugawana naye masautso Ake.” Kodi izi zikutanthauza chiyanipadziko pano?Mudziko lino kusenza mtanda kulibe tanthauzo lenileni. Anthu ambiri sangalimbikitsidwe ndi uthengawakuzunzika. Kodi ndi chifukwa chake Yesu akuti tisenze mtanda wake? Yesu akutimema kusenza kutitidzikanize tokha kuti tisenze mtanda wake. Pa ife tokha sitingathe. Cholinga cha Mulungundikupulumutsa komanso kutiombola. Werengani pa Akolose 1:20 pamene akunena za utumikiwachiyanjanitso.Kumbukirani kulira kwa Davide pa Masalimo 51 vesi 10. Davide adadziwa kuti njira yokhayo yabwino ndiyakuti Mulungu alengere Davide mtima watsopano wosangalatsa Mulungu. Iye adadziwa kuti ndi mtimawokhawo wochokera kwa Mulungu umene ungamusangalatse Mulungu (v. 10), chimwemwe (v. 12),18


mtima wolangiza otaika (v. 13),mtima wopembedza Mulungu (vv. 14-15), komanso mtimawodzichepetsa (v. 17).Uwu ndi mtima wapamtanda umene akutipempha kuti tiusenze. Sitiyenera kudzikakamiza kuusenzakoma ngati sititero tisemphana ndi mphamvu yakuuka. Kumbukirani kuti uchimo umaphanso mphamvuyakuuka. Nthenda imene aliyense amatenga pakubadwa ndi uchimo chifukwa cha Adamu (Aroma 5:12)Iyenera kuchotsedwa kuti timukonde Mulungu komanso kusenza mtanda wake. Ife tikamulora Yesundiye kuti tidzatha kusenza mtanda wake. Mphamvu yakuuka imatheka pamene tichita za pa mau aAgalatiya 5:24: “Kuti Iwo amene ali mwa Yesu adapachika zokhumba zawo….)Yesu amatitsuka kumphammvu ya uchimo odzikonda. Moyo watsopano umene akuunena pa Masalimo51, Davide akuuzidwa ndi Mulungu kuti timayenda moyo wamzimu wogonjetsa uchimo” mongaakunenanso pa Agalatiya 5:24-25).Pemphero lalero:“Ndikufuna mtima wamtanda chifukwa Yesu akufuna kuti ndisenze mtanda wake. Ndikufuna mtimawanga kudzazidwa ndi mzimu wake komanso chimwemwe. Koma koposa ndikupempha moyowodzichepetsa. Amen.”TSIKU LACHISANUMPHAMVU YAKUUKAKodi zikutanthauzanji akati kugawana naye mmasautso Ake? Tiyeni tione pa Mateyu 16:24 pagawolachitatu limene Yesu akutiitana ku mphamvu yakuuka. Iye akutiitana monga adachitira ndi Andreya,Petro, Yakobo, Yohane komanso Mateyu: “Unditsate Ine.” Kumbukirani kuti Yesu adamuitana Petrokwanthawi yaitali koma Iye adali asadakonzeke? Iye sadakonzeke pacholinga cha Mulunguchakupulumutsa miyoyo koma zofuna zake. Ngati tiyenda munjira ya Yesu zovuta ziliponso.Ndidali Mbusa kwazaka zosachepera ziwiri pamene ndidayamba kuphunzira izi. Ndimakondwa kulalikirandi kulamulira anthu koma osadziwa kuti izi zidali kukonzekera pamasautso a Yesu. Ndidalandira fonikuchokera kwa membala wina wampingo lamulungu masana. Mayiyu adali akuphunzitsa sande sukulukwa zaka zambiri mumpingo wathu. Adandiuza zamtsikana wina amene adamuphunzitsa ameneadakwatiwanso kachikena.Mwamuna adakwatirana naye kachiwiri adali ndi ananso kotero kuti awiriwo amalera Ana asanu ndimmodzi pamodzi. Tsikulo Iye ndi mwamuna wake adali atakangana. Patapita nthawi adapita pafamuimene Iwo amakhala. Adatenga muvi nakamuyang’ana mwamuna wake. Asadamupeze mwamunawake, mkaziyo adatenga muvi nazipha.Mphunzitsi wa sande sukulu amafuna kudziwa ngati nditapite kukapepesa kubanjalofedwa.Ndivomereze kuti sindimafuna kupita. Maphunziro a ku Ubusa saanandikonzekeretse pamavutongati amenewa ndipo sindidadziwe chochita panthawi ngati iyi.Patapita nthawi ndidazindikira kuti banja lonselo silidali lotsatira Yesu. Kenaka ndidamva Mzimu Woyeraakuyandkhula kwa Ine mwakayaziyazi ndipo ndidafunsa kuonana ndi Mwamunayo mwapadera.Ndidakhala ndi Bamboyo koma ndidadziwa kuti palibe vesi imene ikadamulimbikitsa Iye. Chimenendidachita ndikulira naye limodzi. Izi zidali zovuta koposa kumupatsa mau achilimbiktso ammau aMulungu.Potsata Yesu tiziona mmene Yesu amaonera munthu aliyense. Ndipamene Paulo akunena pa 2Akorinto 5:16.Munthawi ya utumiki wathu, tidadutsa munthawi zovuta ndi banja lina. Kudzera mumatenda oopsamwana wao wamkazi anamwalira mmasiku 15. Iyeyu adali ndi zaka 15. Ubale wathu udali bwino ndibanjali ngakhale pena timasemphana. Pamene timachezerana ndi banjali mchipatala tidayambakugawana masautso a Yesu. Nkhani yabwino ndiyakuti mwana adasinthika pamene timachezerana ndibanjalo. Pakali pano banja lawo ndi lathu limayanjana kwambiri.Pamene titsatira Yesu, timayanjana naye koposa. Mphamvu yakuuka imagonjetsa uchimo ndi Imfapamene tigawana naye masautso.”19


Pemphero Lalero:“Okondeka Yesu, ndikupempha kuti ndifanane nanu ndikuona dziko mmene Inu muonera. Ndikufunamtima wanga ulimbikitse chiyanjano ndi chipulumutso. Ndikufuna kuti chiyanjano changa ndi Inuchikulebe. Amen.”TSIKU LA CHISANU NDI LIMODZITengani cholembera chanu ndi pepala ndipo muunikire ulendo wanu ndi Yesu. Werengani Mateyu16:13-28. Kodi mwamuyankha bwanji Yesu pamene akufunsa kuti Inu mumati Yesuyo ndindani? Kodimwachitapo chiyani pamene akuti mudzikanize nokha ndikusenza mtanda wake?Pemphero Lalero:“ndikuthokozani Ambuye pondidziwitsa chimene Inu muli—mwana wa Mulungu wamoyo. Chifukwa chaichi ndikufuna kudzikana ndekha ndikusenza mtanda wanu ndikukutsatani tsiku lililonse. ZikomoAmbuye. Amen.”TSIKU LA CHISANU NDI CHIWIRILero lino werengani ndikulingalira pa Masalimo 37. Mulungu akutipempha kuti tikondwere mwa Iye. Iyitundi mbali ina yachinsinsi cha mphamvu yakuuka ndikumudziwa Yesu. Tionana mawa pamene tiyambekuona mphamvu yakuuka ndi maitanidwe anu.Pemphero Lalero:“Mulungu okondeka,ndikufuna kukondwera mwa Inu, kudikira pa Inu komanso kusunga malamulo Anu.Ndikufuna kuti Inu mukhale mphamvu yanga munthawi yansautso. Ndikudziwa kuti mundiombola Ine.Amen.”MAFUNSO OKAMBIRANA MMABANJA:TSIKU LOYAMBA:1. Kodi mwamupempha Yesu kuti akukhululukireni machimo Anu?2. Kodi ndi ziti zimene mumachita kwa Ena zosonyeza kuti Yesu ali mkati mwanu?3. Kodi mungachite ntchito zotani kulalikira za Yesu kwa Ena?4. Kodi ulendo wanu wachipulumutso ukufanana ndi Yakobo 2?5. Kodi mumachita zimene mumayankhula"?TSIKU LACHIWIRI1. Kodi ndi chifukwa chiyani mnyamata munkhaniyi sadamutsate Yesu?2. Kodi chidakupangitsani Inu kusankha Yesu ndi chiyani?3. Kodi kusiyana kuli pati kukhululukidwa machimo ndikutsata Yesu?4. Kodi mwazindikira tsopano kuti simungatsate Yesu mumphamvu yanu?TSIKU LACHITATUKukhala ndi cholinga ndikukhala ndi mapulani Athu. Kukana chimene ife tili ndikutaya zotikondweretsa.1. Kodi mumafuna kudzachita chiyani mukadzakula?Kodi ndizokhumba ziti zimene zili zofunika kwa Inu?2. Kodi Yesu ndindani kwa Inu?3. Kodi mwakonzeka kutaya zokhumba zanu kuti mumutsate Yesu?4. Kodi zolinga zanu zingakupatseni Inu chimwemwe?TSIKU LACHINAYI1. Kodi Davide amafuna mtima wotani pa Masalimo 51:10?2. Kodi mtima wotero ungakonde chiyani?3. Kodi inu ngatinso Davide mungapeze bwanji mtima wotero?4. Kodi mtima wanu watsukidwa kuuchimo?TSIKU LACHISANUCholinga cha Mulungu ndikuyanjanitsa, kupulumutsa ndikukhululukira machimo. Izi zidzaphatikizapomachimo.20


MPHAMVU YAKUUKA1. Kodi mudakhalapo ndi munthu wina amene akumva kuwawa kapena wachisoni? Kodi mudamvabwanji. Kodi mukayandikana ndi Yesu mmavuto mumamva bwanji?2. Kodi Mulungu wagwiritsa ntchito nyengo ina yovuta kuti mufike chifupi ndi mzanu kapena Mulungu?3. Kodi pali nyengo ina imene Mulungu waibweretsa kuti mumulemekeze IyeWIKI 3“Pakuti muli opulumutsidwa kuchokera ku chisomo chakucita mwachikuchulupiriro,ncosachokera kuntchito zanu kuti wina asadzitamandire, chili mphatso ya Mulungu kutiasadzitamandire munthu aliyense” Aefeso 2:8-10.TSIKU LOYAMBAKodi mukuganiza kuti mwaitanidwa kuchina chake? Ena mwa Inu mukuganiza kuti ndikumva kutindaitanidwa kukakhala wamishoni ku Amerika, Jamaica kapena ku Zimbabwe. Pali chimpwilikitipokhudzana ndi maitanidwe mmoyo uno. Anthu Ena akhala akusamvetsa maitanidwe a Mulungundikuyamba kusokoneza zinthu.Kodi zimatanthauza chiyani kuitanidwa ndi Mulungu? Pamene tapeza mphamvu yakuuka ndi pamenetimatumikira bwino. Apa ndi pamene timakhala ndikulimbika mtima kuti Mulungu watiitana. Timafana ndiiye mu imfa yake.”Kodi timafana ndi Yesu bwanji mu imfa yake? Kodi tiyenera kufa pamtanda monga adachitira? Iyayi.Koma mau a Mulungu pa Akolose 2:12 akuti tidaikidwa mmanda ndikuukitsidwa ndi Iye koterotidzikanize ku uchimo. Izi zidzatithandiza pa utumiki wake wachiyanjanitso komanso chipulumutsondikugonjetsa uchimo ndi imfa.Malingana ndi Afilipi 2, Yesu adatifera kuti titchedwenso anthu oomboledwa. Iye akutipempha kutitidzichepetse ngati Iyenso vesi 5). Mwa ichi kukhala ngati Yesu ndikufanana ndi Iye pa utumiki wakekwa otaika. Ndi pamene tionanso pa utumiki wamuyaya wamphamvu yakuuka?Pemphero Lalero:“Ndikupemphera lero kuti mundipatse kulimbika mtima kuti pamene mundiitana ku utumiki wanumundipatsanso mphamvu ndi chisomo pokwaniritsa maitanidwewo. Amen.”TSIKU LACHIWIRIKodi timadziwa bwanji maitanidwe a Mulungu kwa Ife? Timaganiza kuti mpingo ndi thupi la Khristu ndipondi zoona. Komabe mpingo mu chipangano chatsopano umatanthauza anthu oitanidwa komansoosankhidwa. Izi zikutanthauza anthu ovuwulidwa mmachimo ndikupulumuka.Werengani Ahebri 5:11-6:3. Kodi ndi chifukwa chiyani timakonda kumwa mkaka ngati Ana mmalomoyamba kudya chakudya cholimba monga nsima? Kodi ndi chifukwa chiyani timangokhazikika paziphunzitso zoyamba monga zaubatizo. Kodi ndi chifukwa chiyani sitifuna kukhwima muuzimu?Pali zifukwa zambiri koma nkhani yaikulu ndi yakuti tiyamba kukhala mumphamvu yakuuka. Izizikufanana ndi phunziro lasabata lathu la pa Yohane 3:16. Ife timangoopa zakutaika koma osafunakukhala muufumu wake.Mwa ichi timalunjika pa chikhristu pomafunsa kuti kodi ndinu obadwanso mwatsopano kapena ayi.Koma Yesu akufunsa kuti kodi mukunditsata Ine. Uwu ndi uthenga wachisomo.Moyo wamphamvu yakuuka ndi kuvomera kwa Mulungu kuchisomo chake mmoyo mwanga komansomumtima mwanga ndi mdziko lino. Khalani ndi nthawi yolingalira zachisomo chake cha Mulungu.Pemphero Lalero:“Ambuye Mulungu wanga, Ndikufuna kulunjika pamoyo wosatha podzikana ndekha ndikusenza mtandawanu. Amen.”21


TSIKU LACHITATUNyimbo ina imene ndimaikonda ndi yachisomo chodabwitsa.”Tikunenabe zamaitanidwe athu a chisomo. Mulungu amatiitana mwa chisomo chimene chimalimbikitsamaitanidwe athu. Izi zimatipangitsa kudalira pa Mulungu. Mphamvu yakuuka ndi ya mwa Mulungu osatipa Ife tokha. Ndichifukwa chake tiyenera kutsukidwa ku machismo athu ndi mphamvu yakuukapotsukidwa ndi mwazi wake (1 Yohane 1:9).Werengani Agalatiya 5:16-26. Onani mmene Paulo akusiyanitsira cholinga cha uchimo ndi cholingachamzimu vesi 16, 25). Izi ndi zimene zikutanthauza pamene Paulo akuti tibatizidwe ndi Mzimu Woyera(Macitidwe 1:5).Mzimu Woyera angathe kutidzaza chifukwa champhamvu yakuuka mmiyoyo yathu. Mauoyamba akubatiza ndikuzama mmadzi ndikusinthika. Mzimu Woyera amatikonzanso kuti titumikire Iye.Monga tidanenera sabata latha, nthawi zina timatenga mphamvu yamzimu woyera ngati yathu. Ifetimatenga mzimu ngati zodabwitsa chabe. Zodabwitsa ndi gawo limodzi la mphamvu yakuuka.Chofunika kwambiri ndikuchita chifuniro cha Mulungu (Aefeso 4:1).Paulo akufaniziranso mphamvu yakuuka ndi chikondi cha Mulungu payakuuka ndi imene imatisintha kuti tifanane ndi Iye.222 Akorinto 5:14. MphamvuTsopano ndife okonzeka kuona maitanidwe a Mulungu kwa Ife. Pokonzekera mawa tiwerenge paAefeso 2:10.Pemphero Lalero:“Cholinga chamtima wanu kuti mundithandize kukwaniritsa cholinga chanu mwa Ine, kukhala moyowamaitanidwe Anu amene ndalan dira mothandizidwa ndi chikobdi chanu. Amen.”TSIKU LACHINAYIAefeso 2:l0 ndi vesi ina yakuti tiloweze pamtima: “For we are God’s workmanship, created in ChristJesus to do good works, which God prepared in advance for us to do.”Mau akuti chipango ndi olimbikitsa zedi. Mulungu ndi amene Adatilenga Ife.Mulungu adatikonzeratgu Ife dziko lapansi lisadalengedwe. Ife sitidalengedwe mwangolzi ayi. Mulunguadadziwiratu kuti mudzakhala padziko pano lero.Mudalengedwa mwa Yesu kukachita ntchito zabwino mothandizidwa ndi Mulungu. Akolose 1:20).Tiyamikire ntchito ya Abusa, Atumwi, Alaliki, Aphunzitsi a Mau ndi anenero koma ntchito ya Mulungu ilipaliponse ngakhale kunja kwampingo. Malinga ndi Aefeso 4 Mulungu watiitana kukalalikira anthu onsemummphamvu yake.2 Akorinto 5:11-21 paulo akuti Mulungu waitana aliyense ku utumiki wachiyanjanitso mwa Yesu Khristu.Ife tili ngati Akazembe amene amaimira Dziko lakwao monga ifenso tikuimira dziko lakumwamba.Izi zikutanthauza kuti Mulungu watidalira mofanana kukhala akazembe a Yesu kuno kudziko lapansi.Pemphero Lalero:“Zikomo Ambuye pokhala chipango chanu, ndikuthokoza chifukwa cha ichi.Mudandidziwiratu dzikolapansi lisadelengedwe ndipo mudandikonda. Ndadzipereka kukhala kazembe wanu. AmenTSIKU LACHISANUDzulo tidaona kuti Ife tasankhidwa kukhala a Kazembe a Yesu pa uthenga woyanjanitsa anthu ndiMulungu pakulapa kwa machismo awo. Tionenso Aefeso 2:10. Mulungu watipangiratu kukachita ntchitozabwino.Maitanodwe anu ndi ofunika ndi china chili chonse chimene muuchita kaya ndi bizinezi kayanso ntchitozamalonda.Kumbukirani za Davide pa Masalimo 51? Tikuona Iye akukhudzika ndi Mulungu. Mumphamvu yakuuukamoyo wamunthu umakhudzika ndi Mulungu koposa china chilichonse. Anthu Ena amatha kukondamasewero ampira kuposa Mulungu. Ena kukonda zimene ali nazo koma Mulungu akhale olyambawazonse. Nthawi zina zinthu zimene timazikonda zimatha kutenga malo a Mulungu ngati tizikondakwambiri. Izitu sizimamusangalatsa Mulungu kumusakaniza ndi zina.


Kodi mumakonda chiani mmoyo wanu. Yesu akufuna kutu Iye akhale woyamba mmoyo wanu. Kodichuma chanu chili kuti? Werengani Mateyu 5:8 ndi 6:19-24.Pemphero Lalero:“Msabata ziwiri zapitazo pamaphunziro apadera a Mau a Mulungu ndaphunzira kukudziwani koposakale koma zimene mukufuna kuti ndichite pamene mukundiitana Ine. Ndikufuna kuti ndikhudzike ndiutumiki wachiyanjanitso ndi chipulumutso. Amen.”TSIKU LA 6Dzulo tidaona kuti kukhudzika ndi njira imene tingakwanilitsire utumiki wa Yesu wachiyanjanitsol umeneIye watipatsa. Tiyenera kuchita izi ngati a Kazembe a Yesu.Tiyenera kupeza mwayi wotumikira mmabanja, kuntchito, kumpingo, kumsika, koyenda komansommabizinezi athu.Mateyu 28:18-20 akuti timuke kudziko lonse lapansi kwa anthu amtundu wonse kukalalikira uthengawabwino kaya ndi andale ndi ena onse tiwauza za Yesu ameneyu Pali ponse pamene inu muli ndinuKazembe wa Yesu.Pemene mukukhala muzolinga zako, kodi mumaganiza chiani? Mwai wonse umene ulipo umathakukhala wanu. Pamene tikukhala mumphamvu yakuuka nkhani yakudzikonda wekha imachoka mkatimwako koma umakhala ndi moyo chifukwa cha khristu Yesu ndipo umakhala ndi moyo watsopano 2Akorinto 5:l5). Ife sitimaona mwadziko lapansi ayi koma mphamvu yakuuka poimira Boma lakumwambapautumiki woyanjanitsa ngati kazembe wa Yesu.Tikamakhala mumphamvu yakuuka sitimaona za ife tokha timadalira mwa Yesu yekha basi n diMulungu mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.Pemphero lalero:“Choonde Ambuye ndithandizeni kuona zinthu mdzikoli monga inu muonera. Ndikufuna kugwiritsantchito mwayi wokhala kazembe wanu polalikira za Inu Khristu. Amen.”TSIKU LACHISANU NDI CHIWIRIMPHAMVU YAKUUKAWerengani mau a Mulungu pa Masalimo 16. Muyenera kulemba nsonga zamaitanidwe anumunkhaniyi. Kenaka muone zinthu zimene mwakhudzidwa nazo panokha lembani mwai umenemwakhala mukuwulekerera mpaka pano. Onani mwai wauzimu umene mwautaya kale kuchokera kwaMulungu. Mawa tiyamba kuona za mphamvu yakuuka komanso kuti zimatikhudza bwanji.Pemphero Lalero:“Lero ndikulandira mau anu pamene ndikuti kwa Inu ‘Mundionetsa njira yamoyo podzala ndichimwemwe chanu pamkono wanu wamanja nthawi zonse.’ Ndiyenera kupeza njira zakutindikutumikireni bwino? Amen.”MAFUNSO OONJEZERA AMABANJA:TSIKU LOYAMBA:1. Kodi mukuganiza kuti Mulungu akukupemphani kanthu kakuti muchite? Perekani mpata kwa Anakuti ayankhe.)2. Pamene Mulungu watiitana kodi amatipatsa chiani kuti tikwaniritse maitanidwe athu?3. Ndi zokhumba zanji zimene Mulungu alinazo pa Inu?TSIKU LACHIWIRI1. Chisomo ndi ukoma waulere kwa Ife. Kodi moyo wanu wasinthika motani chifukwa cha chisomo chaYesu pamtanda kwa Inu?2. Kodi mungakhale bwani moyo wapadera podziwa kuti Mulungu adakusankhani Inu?TSIKU LACHITATU1. Liwu lakale la ubatiozo ndilakuti kuikidwa mumadzi akalala ndipo kumizidwa ndikusintha mtndu.Ndikusintha kwanji kumene kudadza mmoyo mwanu mutabatizidwa?2. Chikondi cha Yesu chimatilimbikitsa Ife.23


TSIKU LACHINAYI1. Kodi ndi mautumiki ati amene tiyenera kuchita mumpingo posamalira Ena?2. Kodi zimatanthauza chiani kukhala kazembe wa Yesu? Kodi Ena amadziwa za Yesu mwa Inu?TSIKU LACHISANU1. Kodi ndi zinthu ziti zimene Mulungu amatipatsa kuti tichite ntchito yake?2. Kodi mumakonda kuchita chiani chimene mungathe kuchita masiku onse?3. Kodi mumakondwera ndi chiani mu utumiki wadziko lino?4. Munjira ziti zimene Mulungu angakugwiritseni ntchito kudziko lapansi?TSIKU LACHISANU NDI CHIMODZI1. Kodi mutakhala ndi mwai omuuza munthu za Yesu mungamuuze zotani?2. Kodi ndi mwai wotani umene Yesu adakupatsani ngati kazembe wake. Kodi mudachita chiani?WIKI 4“Cifukwa cace ngati munthu ali mwa Khristu, ali woelengedwa watsopano, zakale zapita taonanizakhala zatsopano!” 2 Akorinto 5:17TSIKU LOYAMBAMsabata zitatu zapitazo takhala tikunena za mphamvu yakuuka ya Yesu. Ziphona ziwiri zimene ndiadani athu, imfa ndi uchimo zathetsedwa mphamvu pa Kavali. Werengani Akolose 2:15 pokhudzana ndichigonjetso mwa Yesu mwamphamvu ya Mzimu Woyera.Yesu ndi chitsanzi chathu cha moyo wogonjetsa. Ena mutha kunena kuti Iye adagonjetsa chifukwachakuti ndi Mulungu koma Iye adavalanso thupi ngati Inu ndi Ine padziko pano. Pamene tikhulupiriraYesu mphamvu yakuuka imalowanso mwa Ife kuti tikhale agonjetsi.Yesu adali wathuthu ngati Mulungu komanso wathuthu ngati munthu pamene adabadwa kwa namwaliMariya mwa Mzimu Woyera. Ndi chifukwa chake timamutcha Emmanuel, Mulungu nafe. Yesu adalinsondi abale komanso Ena adamuda pokhala.Kodi Inu muli ndi abale? Ndikunena za alongo anu, achimwene anu, amfumu, amuna anu, akazi anu,ana anu, makolo anu, abusa anu anzanu a kusukulu ndi Ena.Ndikufuna kuti muchite izi.Tsopano werengani Mateyu 7:12 . Mufananitse kapena kusiyanitsa maubalewo ndi moyo wanu.Pemphero Lalero:“Palibe adanena kuti kudzakhala kosavuta kukhala ndi maubwenzi onsewo koma Inu mudanena kale.Mudali ndi Adani Inu Yesu koma mudawakondadi. Lero lino ndithandizeni kupeza njira zodalitsira AnthuEna ndikuikiza mphamvu yakuuka mwa Iwo.. Amen.”TSIKU LACHIWIRIAmbiri mumadziwa zalamulo lodziwika. Muwachitire Ena zimene mukufuna kuti Iwo achitire Inu.Mukudziwanso muja akuti muwachitire Ena Iwo asadakuchitireni Inu. Zonsezi zidzatheka ndi mphamvuyakuuka.Kodi mudayamba mwadzifunsapo kuti ndi chifukwa chiyani maubale ali ovuta zedi? Mwina mumachitabwino pamaubale kapena ayi? Kodi ndi chifukwa chiyani ubale wabwino umatsilizika ndi kunyozanamonga zimachitikira mmabanja ambiri. Kodi ndi zovuta bwanji?Tiyeni tionenso ziphona ziwiri zakupha zija-imfa ndi uchimo. Werengani pa Agalatiya 5:16-26. Tionensopa vesi 19-21. Ichi ndi cholinga cha uchimo kumbukirani izi? Mungathe kuona kuti cholinga cha uchimondi chakudzikonda.Akunena zambiri monga, migawano, njiru, mipatuko, kaduka, nsanje ndi zina zotere.Vesi 17 akuti thupi limafuna motsutsana naye mzimu. Munthu amabadwa ochimwa monga pa Aroma5:12. Kodi tikakonda wina amapambana ndi ndani. Munthu payekha.24


MPHAMVU YAKUUKATiyeni tionenso kuti izi zimakhala bwanji mmoyo wamunthu. Tasanthulani Davide pa Masalimo 51.Mulungu adamuitana Davide kukhala mfumu ya Israeli komanso taonani Iye adali msilikali ameneadapha Goliati). Iye ndi mtsogolerinso wabwino wauzimu. Koma Iye ubale wake ndi Saulo siudali bwinokomanso si Iye adali wolakwitsa zonse. Koma chifukwa cha nsanje ndi zilakolako zoipa Iye adagona ndimkazi wa Uriya Muhiti Beteseba. Ubwenzi wake udakhudzana ndi udindo komanso chiwerewere.Zotsatira zake zidali Imfa basi. Chidachitika ndi chiyaniDavide kenaka addziwa uchimo wake nalapa pa Masalimo 51:5. Ambuye alemekezeke kuti mphamvuyakuuka ingathe kutitsuka ku uchimo tikalapa monga adachitira Davide kuti mundilengere mtimawatsopano ndikugonjetsa mphamvu zasatana (l Yohane 3:8), tingathe kuyembekezera maubale abwino.Lamulo lodziwika lachikondi ligwire ntchito mkati mwanu.Pemphero Lalero:“‘Mundilengere mtima watsopano Mulungu.’ Ili lidali pemphero la Davide ndipo likhalenso lanu lero.Mphamvu yanu yakuuka ingathe kundikonzanso. Amen.”TSIKU LACHITATUMulungu watitsuka mmitima mwathu kuchotsa chikhalidwe cha uchimo. Mphamvu ya uchimoyamezedwa ndi Yesu pamtanda paja pamene adaukitsidwanso mwa mphamvu yakuuka ya MzimuWoyera. Mateyu 5:8 Odala ali Oyera mtima chifukwa adzaona Mulungu. Apa sadati odala adzachitazamphamvu koma adzaona Mulungu?Kuona Mulungu ndikuona mmene Yesu amaonera ku miyoyo yotaika.Pamene tiona Mulungu timaona mphamvu komanso chisomo chake. Muyenera kudziwa kuti simaubaleonse amene ali abwino. Maubale Ena ndi oononga ngati akukulimbikitsani kuchita uchimo.Pamene mukhala ndi anthu okonda uchimo mudzadana nawo ngati simukuchita zaozo. Mwa ichimuyenera kupewa maubale amene si abwino.Tsopano moyo wanu watsukidwa ndi mwazi wa Yesu. Simuyenera kukhala muzimenezo . kumbukiranimau a Mulungu pa 2 Akorinto 5:17 akuti zakale zapita taonani zakhala zatsopano. Pemphani MzimuWoyera kuti akuthandizeni okhala oyera mdziko lovutali.Pemphero Lalero:“Ndikhulupirira kuti moyo wanga watsukidwa ndi mwazi wa Yesu. Mzimu Woyera ndithandizeni kuonandi maso oyera. Ndikufuna Inu nokha. Amen.”TSIKU LACHINAYITsekulani Buku Lopatulika pachiphunzitso chapaphiri pa Mateyu 5-7. Yesu adayamba utumiki wake ndimaunso amene adanena Yohane Mbatizi pa Mateyu 4:17 kuti lapani pakuti ufumu wakumwambawayandikira. Mau Ena a Yesu adali kungoonetsera ukulu ndi ufumu wake. Ena amati chiphunzitsochapaphiri si chanthawi ino koma ufumu umene ukudza patsiku lomalizalo. Tikaona mauwa ndimaganizo a uchimo ndiye kuti sitingathe kumvetsa izi. Koma tikaona ndi mphamvu yakuuka tidzathakuyamikira chiphunzitso chapaphiri.Onani pa 5:43-48. Pamene mukuwerenga ndimeyo, kodi mumaganiza chiyani? Ikuoneka ngatiyachikunja sichoncho? Kondani Adani anu? Ndani angachite izi? Pemphererani amene amakuzunzanikomanso kukunenerani monama. Ndani angatsatire izi? Tikamanena ndi maganizo a uchimo sitingathekuzimvetsa izi. Yesu akutilamulira kuwakonda adani athu ndikuwafunira zabwino. Izi tidzachita ndimphamvu yakuuka.Tsopano tiyenera kugwilitsa ntchito mphamvu yakuukayi. Afilipi 2:3 Mkudzichepetsa yense ayesemzake womposa Iye mwini. Onaninso Afilipi 2:6 akuti sitisamala zotiyenera kuti tikaombole Ena.Malo ena ogwilitsa ntchito mphamvu yakuuka ndi 2 Akorinto 5:15-16. Poona zamphamvu yakuukatikuona kuti mdani wathu adamuferanso Yesu kuti apulumuke kotero tiyenera kumukonda. Akunenansopa Aroma 5:8 kuti Mulungu aonetsa chikondi chake mmenemo kuti pokhala Ife ochimwa Khristuadatifera.25


Yesu akadationa mwa umunthu ndiye sakadatifera Ife. Ndi mphamvu yakuuka ya Yesu tingathensokukonda munthu ochimwa. Ngati tingathe kukonda ochimwa koposa kotani abale athu kapena anzathu.Werengani pa Mateyu 5-7 mofatsa mtima. Mulole Mulungu akuonetsereni anthu amene mungathekuwakonda ndi mphamvu yakuuka.Pemphero Lalero:“ndikufuna kutsata moyo wanu wakudzichepetsa nthawi zonse. Ndikufuna kukhala woombola miyoyomonga kazembe wanu. Mwandionetsa kuti munandifera ndikadali ochimwa. Amen.”TSIKU LACHISANUUlendo wanu wapaphiri udali bwanji? Sizapafupi kukwanitsa zonse. Wina adati khalidwe lakale silithatsiku limodzi lokha. Izi zili chomwechi pokhudzana ndi Abale. Moyo wathu umakhudzana ndi abwenziamene Ena atamva kuti amatha kuononga mphamvu yakuuka. Koma tikakhala m’mphamvu yakuukatidzatha kugonjetsa zonse. Mphamvu yakuuka Yesu adagonjetsa satana. Mumphamvu imeneyi tingathekugonjetsa uchimo ndi Imfa.Tiyambe ndi pemphero pa Mateyu 6:9-15. Tilunjike pa vesi 12 ndi 14-15. Yesu akunena kuti ngatisitikhululuka mphamvu yakuuka mmiyoyo yathu idzachoka. Choyamba tidziwe kuti Mulunguanatikhululukira ndi mwazi wake. 1 Yohane 1:9 . Kukhululukidwa motani? Kumbukirani masiku apitawamutawerenga pa Masalimo 103. Vesi ya 3 akuti Mulungu amakhulukira nthenda zonse.Vesi 12 akuti monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo ndi mmene Iye wachotsera machimo athu.Mulungu amakhudzika ndi kukhululukira? Mateyu 6, Yesu akuti simupeza chikhululukiro mpaka Inumutatero.Mau a Mulungu pa Mateyu 7 akutinso tisaweluze kuti tingaweluzidwe.Akhristu ambiri adzala ndikusakhululuka komanso mkwiyo.Ngati Ana a Mulungu tiyenera kukhala okhululukira. Sitimakhulupirira Mulungu kuti asamalire anthuamene amatida Ife. Kumbukirani muyeso umene tiyezera Ena, tidzayesedwa ndi omwewo.Pemphero Lalero:“Izi ndi zabwino kuzimva! Ndatsukidwa ndi mwazi wa Yesu. Palibe chifukwa chokhalira moyo wakale!Ndikufuna kukhululukira iwo amene ndidawaweluza ndikupempherera chisomo pa Iwo; Ndi yekhayoamene angatichitire izi. Ndikufuna kukhala mphamvu yakuuka mmoyo wanga. Amen.TSIKU LACHISANU NDI CHIMODZIMphanvu yakuuka iyeneranso kugwira ntchito mmabanja. Ngati siuli pabanja khala nafe komandikudziwa uli ndi mzako kwambiri.Kwa inu apabanja takhalani phe! Ndikuganiza pang’ono zabanja lanu. Kodi likuyenda bwanji. Tiyenerakukhala ndi mphamvu yakuuka kuti tikondane wina ndi mzake.Pa Aefeso 5 akutiuza zachikondi chambanja, mwamuna, mkazi, ndi ana.Ngati tikhala mu uchimo nkovuta kumukonda mzathu. Koma ndi mphamvu yakuuka zonse nzotheka.(Kumbukirani mau a Yesu pamtanda kuti akhululukireni pakuti sadziwa chimene achita Sitiyenerakuweluza Yeremiya 31:34 akuti Mulungu amakwirira machimo onse. 1 Akorinto 13;5 akuti chikondisichiyang’anira zonama.Mphamvu yakuuka imayenera kugwira ntchito mmbanja. Palibe amene amakondwera kuti ukwati wathuunyikidwe mumphamvu yakuuka. Werengani pa Aefeso 5:26-27 kachikena. Kumbukirani kutimaitanidwe athu ku mphamvu yakuuka komanso utumiki wa chiyanjano.Pemphero Lalero:“Mulungu wanga, ndikufuna kukonda banja langa monga Inu munakonda mpingo wanu powuferapamtanda. Amen.”26


TSIKU LACHISANU NDI CHIWIRIMPHAMVU YAKUUKAKhalani pansi mutatenga cholembera ndi pepala ndikuganiza za maubale anu. Muone maubalewamugalasi yamphamvu yakuuka kwa Yesu. Kodi mungasinthe ziti? Kodi mukuyenera kukhululuka maloati. Unikani zabanja lanu Mateyu 5-7, Aefeso:21-33, ndi 1 Akorinto 13.Mukalola mau a Mulungu kukhala mkati mwanu mphamvu yakuuka idzakhala mwa inu.Pemphero Lalero:“Ndikufuna kupeza chisomo chanu mwa Ine.ndikufuna kupereka chisomo chakukhulukira kwa Ena.Amen.”MAFUNSO OKAMBIRANA MMAB ANJA:TSIKU LOYAMBA:1. Kodi ndi maubale otani mbanja lanu amene ali ofunika? Kusukulu kapena kumpingo? Ndi chifukwachiyani?TSIKU LACHIWIRI1. Powerenga Masalimo 51, kodi mukuganiza kuti chikhalidwe chanu cha uchimo chimakutsogoleraniku uchimo?2. Kodi mungazione nokha mukukhala choonadi cha mphamvu ya kuuka?TSIKU LACHITATU1. Ndi chikhalidwe chiti chimene chimasonyeza umunthu wakale pamene muli ndi anthu ena chimenemungafune kuti Mulungu akuchotsereni?.2. Kodi Mulungu watiitana ku utumiki wotani?TSIKU LACHINAYI1. Kodi mumachita lamulo lalikulu?2. Kodi nzotheka bwanji kukonda adani athu3. Kodi mumalola ndi kuimba zakufunika kwa mphamvu yakuuka ya Yesu mkati mwanu? Fotokozeraniyankho lanu.TSIKU LACHISANU1. Kodi mumamukwiyira mzanu?2. Kodi mumavutika kukhululukira Ena?3. Kodi mungathe kukhululukira wokulakwiraniyo?4. Ganizirani zawanthu ofunikira kuwakhululukira. Kodi ndi zofunika bwanji kukhululukira?5. Kodi Yesu adakhululukira ndani ngati chitsanzo chathu chabwino?TSIKU LACHISANU1. Makolo ayenera kugwiritsa ntchito Aefeso 5:22-6:4 pounukira mmene akuyendera mabanja awo.Ngakhale banja mwamuna ndi mkazi angathe kugwilitsanso ntchito izi polimbikitsa ubale wao.2. Kodi ndi dera liti la ubale limene likubweretsa mavuto kwa Inu?3. Kodi ndinu okonzeka kudalira Mulungu pa izi?4. Kodi mwakonzeka kudzipereka kwa Mulungu pavuto lanu?27


WIKI 5Kodi mau Akuoneka bwanji ndi masomphenya auzimu?“Koma ngati tiyenda mkuunika, monga Iye Ali mkuunika, tiyanjana wina ndi mzake ndipo mwaziWA Yesu mwana wache utisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse 1Yohane 1:7, 9TSIKU LOYAMBAPa Macitidwe 1:8 akuti Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera atadza mwa Inu ndiponmudzakhala mboni zanga mYerusalemu, myudeya lonse ndi msamariya ndikufikira malekezero adzikolonse lapansi. Awa adali mau a Yesu asadanke kukwera kuwamba. Pa vesi 11. Tikuona mau a Angeloomwe adalengeza kuti Yesu amene mwamuona kukwera kunka kumwamba pamaso pa ophunziramudzamuonanso akutsika kumwamba tsiku lina. Ife tikuyembekezera izi padziko pano.Yesu akuikiratu utumiki wathu. Iye akuti ndi mphamvu yakuuka imene idzapezeke patsiku la pentekoste,tidzakhala mboni za Yesu kamba ka Mzimu Woyera pamenenso Paulo akuti ndife akazembe a Yesu.Ifeyo mwamphamvu yakuuka tiyenera kulalikira utumiki wachiyanjanitso mphamvu ya Mulungu mwaYesu amene adatifera pamtanda. Akolose 1:20.Mulungu adaitana mpingo anthu opulumutsidwa kuti akaigwire ntchitoyi kuno kudziko lapansi. Ife tisaonemavuto amdziko koma kudalira Yesu yekha basi pautumiki wathu kuti tigonjetse.Aliyense ayenera kutumikira mosadalira abusa okha kuti akalalikire uthenga wachipulumutsopodaliranso mphamvu yakuuka.Mphamvu yakuuka timagonjetsa imfa ndi uchimo komanso mphamvu za satana 1 Yohane 3:8, Yesuadadza pano padziko kudzaononga mphamvu za satana. Ife tingathe kukhala osachimwa podaliraMzimu Woyera ndi mphamvu yake yakuuka.Werengani 2 Akorinto 5:14-15. Chikondi cha Mulungu chimatilimbikitsa kukalengeza zachikondi chakekudziko lotaikali monga alembera pa Macitidwe 1:8. Nchifukwa chake Paulo akuti monga Yesu adatiferatiyenera kumudalira pazonse pa utumiki wathu.Kodi chimakutherani nthawi yanu ndi chiyani. Mupemphe Mulungu akupatseni chidwi chokonda anthuotaika kuti amudziwe Yesu ngati mpulumutsi wao.Pemphero Lalero“Zikomo Ambuye posawerengera uchimo wanga. Ndikufuna kumakhala mokukondweretsani pa utumikiwachiyanjanitso. Amen.”TSIKU LACHIWIRIMonga tidanenera dzulo ndikovuta kukhala mphamvu yakuuka ngati ife sitikhala mu utumikiwachiyanjanitso wa Mulungu? Izi zikutantahuza kuti onse akhale amishoni kapena mbusa. Chofunikandi kukhudzika ndi utumiki wa Yesu.Anthu Ena timadzidelera kuti Mulungu sangathe kugwira ntchito mwa Ife koma tingodalira mphamvuyakuuka ya Yesu basi pa utumiki wa chiyanjanitso.Paulo akupherezera izi pa 2 Akorinto 5:16 podalira Mzimu Woyera. Ngakhale Masalimo 51 Davideadalapa ndikudalira thandizo la Mulungu. Tidalire Mulungu ndi Mzimu Woyera kuti atithandize ndimphamvu yakuuka pa utumuki wathu.Pemphero Lalero:“Ambuye mundidzaze ndi Mzimu wanu woyera. Ndifuna kukhala ndi mtima watsopano monga Davideadapempherera polapa. Mtima wokhudzidwa ndi ochimwa. Amen.”TSIKU LACHITATU2 Akorinto 5:17 akuti Chifukwa chache ngati Munthu ali mwa Khristu, ali wolengedwa watsopano zakalezapita taonani zakhala zatsopano. Utsopano ndi umene udanenedwa mbuku la Genesesi pamene28


Mulungu adapanga Adamu ndi hava opanda uchimo. Mpamene akunenanso pa 2 Akorinto 3:18 akutitikusinthika muchifanizo cha Yesu. Komanso Paulo akuti umbadwa wathu uli kumwamba pa Afilipi 3:20.Kodi ndi chifukwa chiyani sitimamva kusinthika kwauzimuku. Mau a Mulungu pa Yohane 2:15 akutitisakonde dziko lapansi ngakhale zinthu zili momwemo.Chinthu china chimene chimaletsa kukhala ndi mphamvu yakuuka ndi ndalama. Mulungu atithandizekuti ndalama tiilamulire osati iyo itiuze zochita kuopa kutisokoneza ndi mphamvu ya yakuuka. Pauloadati chikondi chapandalama ndi muzu wa uchimo wonse?Poyambira pathu ndi pa Mateyu 6:19-24. Apa akuti musunge chuma chanu kumwamba kumene njenjetendi dzimbiri sizingaononge ayi. Akutinso simungathe kutumikira Ambuye awiri, chuma ndi Mulungu.Nzosatheka.”Ife sitingathe kukana kuti ndalama yasanduka kamulungu mdzikoli.Ena adati kumene kuli chuma chako mtima wako umakhala komweko. Kodi inu ndalama zanu zimatherapa chiyani?Kafukufuku wina wasonyeza kuti ndi 105 yawanthu amumpingo wokha amene amapereka chakhumichawo kwa Mulungu. Mu buku la Levitiko 27:30 Mulungu akuwapempha anthu kupereka chakhumi chaokwa Mulungu (Malaki 3:10).Ena akhala akunama kuti chakhumi chidali chachipangano chakale ndipo muchipangano chatsopanondi nthawi ya chisomo. Mzosatheka. Pa Mateyu 5:17, Yesu akuti sadadze kudziwa lamulo komakulikwaniritsaKhalani ndi nthawi younikira kuti chuma chanu chili kuti? Kodi mukuyenera kusiya zinthu ziti zimenezikukulepheretsani kupeza chuma chakumwamba. Timaliza phunziroli mawa lino.Pempherolo Lalero:“Lero pamene taphunzira kuti tisunge chuma chathu kumwamba ndithandizeni kutero Ambuye.Ndithandizeni kupereka chakhumi changa ndi zopereka zina mokondwera.Amen.”TSIKU LACHINAYIMPHAMVU YAKUUKATaona pa Mateyu 6 kuti sitingathe kutumikira Ambuye awiri chuma kapena ndalama. Pa 1 Timoteo 6:10,Paulo akuti “Pakuti chikondi cha pandalama ndi uchimo. Ena amati sindimakonda ndalama komazimene ndalama imagula. Koma pa Mlaliki 5:10 Solomo akuti Iye wokonda ndalama sizimakukwanira.Awa ndi mau amphamvu.Ife timapereka chakhumi ndi zina kwa Mulungu chifukwa kupereka ndi gawo lina lakupembedzaMulungu wathu.Nkhani yonseyi yachakhumi tikupeza pa Malaki 3:10. Akuti tiperekle kwa Mulungu munyumbayosungiramo ndipo tidzadalitsidwa.Sindikudziwa ngati mumapereka chachikhumi kapena ayi koma ngati mumapereka pali madalitso ngatisimutero palinso matemberero. Amene simudayambe chonde yambanipo lero lino. Muyeneransokumapereka chakhumi choyenera.Kumbukirani kuti ngati sitimvera ndiye kuti tasokoneza mphamvu yakuuka. Koma tikatsukidwa kuuchimo ndikumvera Mzimu Woyera mphamvu yakuuka imagwira ntchito bwino. Yakobo 4:17 akuti Iyeamene adziwa kuchita bwino koma osachita kwa Iye kuli uchimo.Pemphani kwa Mulungu akuchotsereni kusakhulupirika ngati ndikusapereka chakhumi lapani kwaMulungu ndikuyamba kupereka mokhulupirika.Pemphero Lalero:“Ambuye ndikupemphera kuti mundithandize kuyambanso kupereka chakhumi moyenera kuti ubalewanga ndi Inu ukhalenso wabwino. Amen.”29


TSIKU LACHISANUMPHAMVU YAKUUKATionenso Machitidwe 1:8. Muyeneranso kuliloweza pamtima kuti zikuchitireni ubwino. Mphamvu imeneMulungu amatipatsa mwa Mzimu Woyera ndikukhala mboni zake komanso akazembe ake padzikoli.Muyenera kumva kuitana kwake inu ndi akazembe Aefeso 2:10.?Pa Mateyu 28:18-20 akuti Ife tilalikire uthenga wabwino kudziko lonse. Ngati Yesu adatifera ifensotilalikire Ena utumiki wachiyanjanitso.Ife kuti titumikire bwino tidalire mphamvu yakuuka ndi mphamvu ya Mzimu Woyera. Pa Luka 12:48 akutiIye amene wapatsidwa zambiri kwa Iye kudzafunikanso zambiri kotero tiyenera kudzipereka ku utumikiwachiyanjanitso kuti anthu asiye uchimo”Sitiyenera kukonda ndalama zokha pamene tikutumikira koma kukonda anthu a Mulungu kuti alowe muufumu wakumwamba ndikukhala akazembe abwino a Yesu.Pemphero Lalero:“Chonde Atate ndipangeni kukhala kazembe wabwino komanso mdindo pazimene mwandipatsa ndipomunditsogoze Ine. Amen.”TSIKU LACHISANU NDI CHIMODZI NDI TSIKU LACHISANU NDI CHIWIRIMungathe kukhala ndi nthawi yapemphero lero lino ndikuwerenganso pa Mateyu 5, 6, ndi 7. Mulembezimene Mulungu wakuyankhulani msabatayi ndikupempheranso mwapadera. Kodi ndi chiyanichikusokoneza mphamvu yakuuka mmoyo mwanu?Pemphero Lalero:“Zikomo Ambuye pamene mukundisintha kukhala munthu wabwino zikomo pazimene ndaphunziramsabatayi..”MAFUNSO OONJEZERA:TSIKU LOYAMBA:1. Kodi utumiki wathu ndi otani?2. Kodi chikutisokoneza mphamvu yakuuka ndi chiyani?TSIKU LACHIWIRI1. Kodi mukuyenera kukhala otani kuti Mulungu akugwiritseni ntchito?2. Kodi ndi ndani angakuthandizeni kuchita bwino munthawi zovuta?3. Kodi ndi khalidwe lotani limene Mulungu angakuthandizeni kuchita bwino kuposa kale.4. TSIKU LACHITATU1. Kodi ndi zinthu ziti zapadziko zimene zimakusokonezani kuti musaone Yesu?2. Chakhumi chimakhudzanso nthawi ndi luso. Kodi inu mumagwiritsa izi motani polemekezaMulungu?3. Malinga ndi mayankho, chuma chanu chili kuti pakalipano?4. Kodi mukufuna Mulungu akusinthireni chiyani?TSIKU LACHINAYI1. Kodi chopereka ndi chiyani? Kodi mumapereka liti?2. Kodi chakhumi ndi chiyani?3. Kodi chakhumi ndi chandani?4. Kodi muyenera kukhala ndi zaka zingati kuti mupereke chakhumi?TSIKU LACHISANU1. Kodi tichite chiyani kuti Mulungu atigwiritse ntchito moyenera?2. Kodi Mulungu waikiza chiyani mwa Inu?3. Kodi Mulungu waikiza chiyani mwa Ife chakuti tidalitse nacho Ena?4. Kodi muli ndi zotani zokatumikira nazo Ena?30


WIKI 6Kodi Ndikhala Bwanji Olunjika?“Chifukwa chache ndikupemphani Inu Abale, mwazifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anumonga nsembe yamoyo ndi yopatulika, yokondweretsa Mulungu ndiko kupembedza kwanukoyenera. Koma musafanizidwe ndi maonekedwe adziko lapansi koma mukhale osinthikammaganizo anu. Ndipo mudzatha kudziwa chifuno cha Ambuye mchiyani.”Aroma 12:1-2.TSIKU LOYAMBAKodi chimafika mmaganizo anu ndi chiyani mukaganiza zamtsogolo? Ena timakondwa Ena kuganiza zachivomerezi , ena mafunde. Mulungu akutipempha kuti tidalire Mulungu pazamawa lathu mongaalembera pa Mateyu 6:34.”Mulungu akufuna kuti timudalire Iye panyengo iliyonse yamoyo wathu. Ife tikukhala munthawi yakudaliraMzimu Woyera pamene Yesu akubweranso kachiwiri.Paulo akutipempha kuti timukhulupirire Iye kufikira nthawi yachimaliziro. Afilipi 1;6. Tiyenera kuchitantchito yakutumikira.Takhala tikuphunzira zokhudzana ndi mphamvu yakuuka. Mverani ku mai a Paulo pa Afilipi 1:6,“Pokhulupirira pamenepo kuti Iye amene anayamba ntchito mwa yabwino, adzitsiriza kufikira tsiku laYesu Khristu.”Pa Macitidwe 5:32 akuti Mzimu Woyera watipatsa kuthekera komuopa Mulungu ndikuchita chifunirochake.Pamene sitinamvere timupemphe Mulungu kutikhululukira monga alembera pa 1 Yohane 1:7.Pemphero Lalero:“Pamene mukutsiliza ntchito yanu mwa Ine ndithandizeni kuyenda muchiyero chanu ndikuwala kwanu.Mwazi wanu unditsuke ndikundiyeretsa. Amen.”TSIKU LACHIWIRIWerengani Aroma 12:1-2 (muyesenso kuloweza pamtima).Kodi mavesiwa akutithandiza bwanji kukulamphamvu yakuuka? Paulo akunena za chisomo chotithandizira. Pa Ife tokha sitingathe. Tidalire mwachisomo cha Yesu basi.Paulo akutiuzanso zakupembedza. Ukutu ndikofunika mu mphamvu yakuuka pamene ntchito zathuzilalikira khristu. Akunenanso kuti tapangidwa kukhala oyera mwa Yesu yemweyo ndi mzimu wake.Paulo akuti tipereke nsembe matupi athu ndiko kupembedza kwathu koyenera. Nsembe ya Yesupamtanda ndiyokwanira kuti tikhale ndi fungo labwino pantchito yathu yotumikira Mulungu komansoEna. Pa 2 Akorinto 4:10 akuti timatenga imfa ya Yesu mwa Ife kuti ulemerero wa Mulungu ukaonekere.Kodi mumadziwa kupembedza? Inu mumapembedza motani? Kodi izi ndizofunika bwanji kumphamvuyakuukaPemphero Lalero:“Ndikufuna moyo wanga ukhale oyera kwa Inu. Ndikufuna kukupembedzani Inu mchoonadi ndikulandirachisomo chanu. Amen.”TSIKU LACHITATUTikuona kuti ndikakule bwanji mumphamvu yakuuka ndipo mavesi athu ndi Aroma12: 1-2. Mwinankutheka mwaloweza onse.Dzulo tidaona zakupereka nsembe matupi athu pokondweretsa Mulungu. Tili ndi wansembe wathupamene tachimwa (1 Yohane 2:2), ndipo timasenza imfa ndi moyo wa khristu mwa Ife. Ukundikupembedza kwathu koyenera monga Paulo akunenera. Ife timatsukidwa ndi mwazi wa Yesukomanso kutsogozedwa ndi mzimu wake. Uku ndikupembedza kwathu koyenera.31


MPHAMVU YAKUUKATiyenera kufika kwa Mulungu ndi maganizo akupulumutsa miyoyo yotaika osati kufuna zathu zokha.Tikatere kupembedza kumakhala kopanda ntchito.Tiyenera kusangalatsa Mulungu pakupembedza polapa machimo athu.Tikabwera pamodzi popembedza Mulungu Iye amakondwera ndipo anati timpembedze Iye mumzimundi mchoonadi. ( Yohane 4:24) Kupembedza pawekha kapena pagulu kumayenera kusenza mtanda waYesu.Mukupembedza tilingalire za Mulungu osati mavuto athu. Tsopano khalani ndi nyimbo yakupembedzaimene mumaikonda ndikuwerenganso mau a Mulungu akupembedza.Pemphero Lalero:“Inu mumandidziwa komanso kuti ndimadalitsika ndikupembedza. Apa ndi pamene kupembedzakumakhala kwatanthauzo. Ndikufuna kumva mphamvu yakuuka mmoyo mwanga pamenendikupembedza Inu. Amen.”TSIKU LACHINAYITionebe pa Aroma 12:1-2. Ndikhulupirira kuti taona ndikumva kuitana kukupembedza Mulungu wathuwamoyo. Kenaka tionetse ntchito zabwino mwamphamvu yakuuka. Mulungu anaononga mphamvu yauchimo ndi imfa pakufa pamtanda. Ife sitiyeneranso kulamulidwa ndi uchimo. Ndife nzika zakumwambandipo kumeneko ndiye kwathu.Taonanso kuti monga tinabadwa mu uchimo tiyenera kudalira Yesu kuti tigonjetse mayesero asatana.Masiku apitawa timakamba zakusinthika mmoyo wathu wauzimu potenga chikhalidwe chathu choyambachimene Adamu adali nacho asadachimwe.(l Akorinto 15). Ulendo wathu ukutitengera kwa Yesupamene Iye akukula Ife nkuchepa. Mulungu adatipanga kukhala oyera pamtanda paja Mateyu 5:8),koma tifanane ndi Iyeyo.Kodi kusinthikaku kumadza motani. Pokonzanso maganizo athu?Pamene tilingalira Iye tidzakhala anthu okonza maganizo ake powerenga mau Ake ndikupeza mphamvuyakuuka ya Yesu. Tidzapitiriza mawa.Pemphero Lalero:“Zikomo Ambuye, mundithandize kufana nanu ndikundipanga kukhala watsopano. Mudzina la Yesu.Amen.”TSIKU LACHISANUKodi timadzisiyanitsa bwanji kuchoka kudziko ndikukonzanso miyoyo yathu? Tiyenera kulingalirakwambiri.Akhristu ambiri ali ngati ophunzira sukulu. Mulungu amatiyankhula pokhudzika ndi zinthu za ufumuwakumwamba. Pamene timaona Buku Lopatulika ngati tikuphunzira mkalasi kusukulu. Mwina timathakuwerenga Buku Lopatulika mongodzionetsera. Zimene timawerenga mu Buku Lopatulika ngati palibemphamvu yakuuka ndiye kuti tili chabe. Tiyenera kuwerenga Buku Lopatulika modalira Mzimu Woyerakuti tisanthulike mitima.Timachita chimodzimodzi ndi mapemphero amene timachita mongodziganizira Ife tokha komaosapempherera moyo wauzimu wathu. Tiyenera kugonja pamaso pa Mulungu pamene tikupempherapolapa machimo athuTiyenera kupemphera ngati Davide pa Masalimo 51 pamene anati mundilengere mtima watsopanoMulungu ndikundisanthulanso.Mulungu akanatha kumupatsa Davide mtima watsopano nthawi yomweyo koma adayenera kutsukidwakaye.Paulo akuti muzadziwa kuti chifuno cha Ambuye ndi chiyani? Mungadziwe bwanji chifuno cha Ambuye.Muyenera kufika pa mulingo umene mudzipemphera ndi kuwerenga mau a Mulungu mchoonadi ndithu.32


Tingathe kufanizira ndi izi pamene munthu akuphunzira chiyankhulo. Iye ayenera kupilira zedi. Izisizatsiku limodzi. Palibe zachidule potenga mphamvu yakuuka.Kwa Enafe zingathe kukhala zovuta kupeza mphamvu yakuuka monga mmene timaphunzilirachiyankhulo chatsopano. Koma pamene mwaphunzira mumakhala okondwa kulumikizana ndi Ena.Pokonza maganizo anu ndikudana ndi uchimo ndi pamene mphamvu yakuuka imakhala yamphamvu ndiyamoyo mkati mwathu. Nkhani yabwino ndi yakuti mungathe kukwanitsa. Mulungu akuthandiza ndithumwachisomo chake.Chofunika inu ndikuvomera kumphamvu yake pamene Yesu adatha kale zonse pamtanda uja wa kavari.Pemphero Lalero:‘Pepani Ambuye chifukwa ndakhala ndikupeputsa Buku Lopatulika ngati la ku sukulu chabe, kutindipambane mayeso. Ndikufuna kuphunzira mau anu ndikuyankhula ndi Inu. chonde mukonzensomtima wanga. Amen.”TSIKU LA 6Powunikiranso phunziroli muyenera kuwerenganso mavesi amene alembedwa maphunziro athuam’mbuyomu. Muwawerenge, kuwalingalira komanso kupemphera mwapadera. Kenakamumapemphero anu asabata lamawa musadzipempherere nokha mungomvera kuyankhula kochokakwa Mulungu.Pemphero Lalero:“Ambuye lero lino, ndili okondwa kumva kuchoka kwa Inu mmau anu, chilengedwe chanu, abale,munyimbo ndi zina. Zikomo pondilola kuti ndikuyamikeni motere. Amen.”TSIKU LA CHISANU NDI CHIWIRIYakhala nthawi yabwino masabata apitawo. Mukhale ndi pepala ndikulemba zamphamvu yakuuka.Mukalemba, pangani pangano ndi Mulungu kuti mwathandizo lake mudzakhala mumphamvu yakuuka.Chinthu chimodzi chimene ndichidziwa ndichakuti Mulungu amasunga pangano lake. Iye akufuna inukuti mukhale mumphamvu yakuuka.Pemphero Lalero:“Atate lero lino, ndikufuna ndikuthokozeni kuti mwandiphunzitsa zamphamvu yakuuka msabatazapitazo.Ndikufuna kukhala mphamvu yakuuka komanso osinthika. Ndikukondani komansondikupemphera kuti mundithandiza kuchita chifuniro chanu chokha. Amen.”MAFUNSO OKAMBILANA:TSIKU LOYAMBA:1. Kodi pali Madera Ena amene mukuganiza kuti Mulungu sanayenera kuchita zimene anachita?2. Kodi kuyenda mkuunika ndi chiyani’?3. Kodi ndinu okonzeka kukhala ndi chikhalidwe cha munthu omvera?TSIKU LACHIWIRI1. Kodi mukukumbukira kuti chisomo ndi chiyani?2. Kodi kupembedza ndi chiyani kwa Mulungu?3. Kodi tipereke chiyani kwa Mulungu ngati nsembe yamoyo?4. Kodi kupembedza ndikofunika bwanji mumphamvu yakuuka?TSIKU LACHITATU1. Kodi tiyenera kukhala ndi moyo wotani pamene tikupembedza Mulungu?2. Kodi tipembedzere kuti poona mmene Mulungu aliri ndikudziwa chimene Iye ali?3. Kodi chimachitika ndi chiyani ngati sitilambira?33


TSIKU LACHINAYI1. Kodi ndi Madera ati amene mwaona kukula mmoyo wauzimu pakuyankhula, ubale, ndi zochitapamene mudayamba kutsata khristu.2. Ndimadera ati amene mukufuna kuti Yesu akukonzeni mwa Mzimu wake kuti mukhale oyerandikufanana ndi Iye?TSIKU LACHISANU1. Funsani Yesu kuti akutsogozeni mu ungwiro wake lero.MPHAMVU YAKUUKAWIKI YA 7“Koma mudzalandira mphamvu Mzimu woyera atdza p;a Inu;ndipo mudzakhala mboni zangamyelusalemu, ndi myudaytea lonse, msamariya ndikufikira kumalekezero anthawi yapansi pano”Macitidwe 1:8.TSIKU LOYAMBAA General William Booth amene adayambitsa mpingo wa Salvatgion Army mzaka za mma 1900 anatimpingo wa khristu udzasiya chiyero ngati sipadzakhala chitsitsimutso. A Booth adalosera kuti nthawiikudza pamene padzakhala:• Chikhristu chopanda Khristu• Chikhululukiro chopanda kulapa• Chipulumutso chosapindula miyoyo yina• Chipembedzo chopanda Mzimu Woyera• Kayendetsedwa kazinthu popanda Mulungu• Kumwamba kopanda GehenaMonga Mbusa ndimalira poganiza zamauwa ndipo ndimapempherera chitsitsimutso mumpingo mwathu.Ndinapempherera monga mwa 2 mbiri 7:14 kuti ikhale yamoyo mumpingo mwanga mwapaderadera.Izi nzotheka kudzera mmapemphero ndikulalikira Uthenga Wabwino padziko lonse lapansi!Muli ndi njala ya kutsitsimuka? Kodi mwakonzeka kutsekula mtima wanu kuti Mzimu Woyera ayendemwapadera kuyambira pampingo wanu? Ngati ndi choncho muyenera kulumikizana ndi A Nazareneonse padziko lapansi popempherera chitsitsimutsoPemphero Lalero:“Atate lero lino, tikupemphera ngati ophunzira a Yesu pa Macitidwe 4:31 panthawi zakutsitsimukakogwedeza miyoyo yathu mwamzimu woyera. Tikhulupirira kuti mukufuna kugwedeza dziko lonse mwamzimu wanu woyera. Amen.”TSIKU LACHIWIRIMpingo uyenera kumanga nthenje pakulalikira Uthenga Wabwino. Mpingo ulionse wachiyero uyenerakulalikira za kupulumuka.Ndidatsogozedwa ndi mphunzitsi wina pamene ndidali ndi zaka zinayi. Irma Shook adatseka kalasiponena kuti anyamata ndi atsikana muyenera kudziwa kuti Yesu ndiye mpulumutsi ndipo muyenerakumulandira ngati mbuye ndi mpulumutsi wamoyo wanu. Munthu wina adakhumata nati Ambuyendikulandirani.Aphunzitsi anga adali chitsanzo. Iwo amaonetsetsa kuti ana aang’ono alandire Yesu. Chifukwa cha ichindidaphunzira kulalikira Uthenga Wabwino kwa Ena munjira ya zilembo za ABC. Pochitira umboni zaYesu:A vomerani kuti ndinu ochimwa. Aroma 3:23B vomerani kuti Yesu angakupulumutseni Yohane 1:12C zindikirani kuti Iye ndiye mbuye wamoyo wanu. Aroma 10:9-1034


Mzanga Mbusa Dr Louie Bustle, wakhala akulalikira zokhudzana ndi kuti munthu mmodzi abwere kwaYesu ndi mzake. Ndimakonda kukhudzidwa kwake kumiyoyo yotaika. Uthenga wake ndichikumbutsochapadera chakuti akhristu ayenera kulalikira za Yesu.Mulungu atipatse kukhudzika kumiyoyo yotaika monga dalembera pa Mateyu 28:18-20.Pemphero:“Mulungu wanga okondeka, ndipatseni chikondi kumiyoyo yotaika ndikupanga ophunzira amitunduyonse … kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene adatilamulira kuti tisunge. Tsekulani maso angakuona munthu ofunika kumuuza za Yesu lero lino. Amen.”TSIKU LACHISANU“…Werengani 1 Timoteo 4:7-8.FIFA Soccer World Cup 2010 idali nkumano wa anthu onse padziko lapansi. Padali anthu oonerakomanso ena amene adakonzekera masewerowa. Osewera adakhala ndi nthawi yokonzekera kutiawine ndikutenga chikho cha dziko lonse cha 2012.Ndidaona Abambo Ena akulira ngati Ana akhanda pakutha pamasewerowa pakuti adalephera kutengachikho. Padali kukhumudwa zedi. Iwo amene adachita bwino kuposa Ena ndiwo adapambana.Ndidakhudzika kuti ndi chifukwa chiyani akhristu samakhudzika ndi chiyero komanso mau a Mulungummene amachitira ndi osewera mpirawa.Nzoona kuti timapulumutsidwa ndi Yesu koma tiyenera kuyesetsa kupemphera komanso kukhala mmaua Mulungu mmene mau a Mulungu akunenera kuti tikhale oyera mtima.Akhristu a lero timatanganidwa ndi zina mmalo motanganidwa ndi Mau a Mulungu opatsa moyo.Mulungu angathe kuchita nafe za mphamvu koma tisataye ubale wathu ndi Mulungu.Tikakhazikika mu u Mulungu ndiye kuti chisomo chidzakhala nafe.FMCPemphero Lalero:“Atate ndipatseni njala ndi ludzu lamau Anu kuti ndikule mokudziwani Inu. Mupange moyo wangakukhala modutsamo Mzimu Woyera ndi chisomo kwa Ine komanso Anthu Ena. Amen”TSIKU LACHINAYI“Pachifukwachi, ndikukumbutsani kuti musazime mzimu uli mwa Inu… pakuti Mulungu sanatipatsamzimu wamantha koma wamphamvu ndi chidziwitso” 2 Timoteo 1:6-7. Mwezi wa June ndi July of 2010pamasewero a World Cup, ndidali ndichithunzithunzi chokhudzana ndi chiyero cha m’Buku Lopatulikachilili. Anthu ambiri adafika ku Africa kudzaonera masewerowa ndipo chidwi chidakula zedi pamenemaiko adaonera mpirawo. Kodi titachita choncho ngati akhristu kulalikira Uthenga Wabwinochingachitike nchiyani? Chitsitsimutso. Mipingo yathu itaonetsera chikondi zingayende bwino.Uchimo monga katangale, ziwelewele, kuphana ndi zina zimafooketsa anthu nkumanena kuti kusinthasikungachitike. Chifukwa cha ichi dziko limapenekera kuti dziko lingasinthike. Koma mmabanja,mmipingo ndi malo Ena mungathe kukhala zamphamvu za Mulungu ngati muli chikondi, ndikupempherakuti pakhala chitsitsimutso mu Africa muno pamene tidzaona chiyero. Paulo adati;“Pakuti Uthenga Wabwino siundichititsa manyazi, pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsaaliyense wokhulupirira kuyambira myuda mpaka Helene: ‘Pakuti kwalembedwa okhulupirira adzakhalandi moyo ndi chikhulupiriro’”Aroma 1:16-17.FMCPemphero Lalero:“Chonde Ambuye, yenderani mipingo yathu lero ndi mabanja athu. Tiyitane kukulapa ndi kumvera Inu,tidzozeni kuti tilalikire uthenga wanu wachiyero lero kuti tione kutsitsikumukansol! Amen.”TSIKU LACHISANU“…Pokhulupirira mwa Inu kuti Iye amene anayamba ntchito mwa Inu adzaitsiliza mpaka tsiku la Khristu”35


MPHAMVU YAKUUKAAfilipi1:6.Ngati okhulupirira tilole mphamvu ya Yesu kutitsuka Ife. Mulungu ayenera kutidzoza Ife kuti tichitezimene Iye akufuna. Mulungu ali ndi moto wonyeketsa uchimo wonse mwa Ife.Akhristu amene samvera Mulungu adzataya ungwiro wao. Liwu lakuti Dema lidatchulidwa mu Akolose4:14. Koma tikuona dema adamusiya Paulo napita ku Tesalonika (2 Timoteo 4:10). Izi zidachitika Pauloali kundende. Dema adakonda dziko lapansi.Paulo akunena zabwino za Epafrodito wa ku filipi wodzazidwa ndi Mzimu Woyera. Iye amapatsidwaulemu ndi Paulo komanso Afilipi onse. Iye adali odzipereka ngakhale mmavuto.Kodi mavuto akadza tidzakhala ngati dema kapena Epafrodito?Moyo wauzimu siophweka nthawi zonse, tiyenera kuchirimika.PCEPemphero Lalero:“Atate wathu wakumwamba tikupempha kuti Mzimu Woyera utitsogolere kuti tikhwime mudzina la Yesu.Amen.”TSIKU LA 6Nzotheka kukhala moyo wogonjetsa opanda uchimo kapena kuchimwira Mulungu mwadala Yakobo 4:17akuti ngati tidziwa kuchita bwino koma osachita kwa Ife kuli tchimo.Pali mitundu iwiri ya machimo oyamba ndi lobadwa nalo kuchoka kwa Adamu lina ndi lochim wira dalaMulungu mwakufuna kwathu. (Onani Luka 24:49, Acts 1:8, Aefeso 3:16- 20).Chiyero ndi mtima wa Uthenga Wabwino. Mulungu ndi oyera Ifenso tikhale oyera. Iye waperekachisomo chake kwa Ife. Tiyeneranso kuyeretsedwa mwa mau Ake komanso Mzimu Wake kuti tiyanjanenaye.Pa Ahebri 12:14 akuti londolani mtendere ndi anthu onse ndi chiyeretso chimene akapanda ichi palibemmodzi adzaona Ambuye Yesu.Pemphero Lalero:“Ambuye Yesu nditsukeni ndi mwazi wanu ndikundiyeretsa mudzina la Yesu Amen. Amen.”TSIKU LA 7“Werengani Macitidwe 1:8 1:8.Yesu akulonjeza mphatso yamzimu woyera kwa aliyense wa Ife. Aliyense wakhululukidwa ndi Yesu. .Izi zitithandiza kukhala moyo wachigonjetso komanso kuchitira umboni kwa Ena za YesuPemphero Lalero:“Atate ndikuthokozani chifukwa cha mphamvu yathu mwa Yesu komanso kulalikira Ena mudzina laYesu. Amen.”MAFUNSO OKAMBIRANA AMMABANJATSIKU LOYAMBA1. Chitsitsimutso ndi chiyani?2. Chitsitsmutso cha chiyero ndi chiyani?3. Chidzachitika ndi chiyani tikatsata malamulo a Yesu 2 mbiri 7:14? Macitidcwe 1:8?TSIKU LACHIWIRI1. Kodi ntchito yofunikira pampingio paokha ndi yotani?2. Kodi tichite chiyani kuti tipulumutsidwe?3. Kodi tichite chiyani titatha kupulumutsidwa?TSIKU LACHITATU36


1. Kodi osewera mpira a World Cup 2010 adatenga nthawi yotani kukonzekera kukamenyamasewerowo?2. Kodi Akhristu tikhale ndi nthawi yotani kukonzekera kuti tikhale a umulungu komanso auzimu?3. Kodi tichite chiyani kuti tikhale auzimu?4. Kodi chidzachitike ndi chani tikadziphunzitsa tokha kukhala auzimu?5. Kodi chiyero cha mmau a Mulungu ndi chiyani?TSIKU LACHINAYI1. Kodi ndi chiyani chimene chidathandizira dziko la South Africa kutakasa masewero ampira wadzikolonse mchaka cha 2010?2. Kodi tichite chiyani kuti titakase mpingo paokha?3. Ndindani angayatse moto wauzimu mumpingo?4. Kodi mpingo umene wayaka moto wauzimu ungakhale wotani?TSIKU LACHISANU1. Kodi Dema adasiya utumiki chifukwa chiyani?2. Kodi chidamuthandiza ndi chiyani kuti Efradito kuti akhale okhulupirika mu utumiki wake komansowa Khristu?3. Kodi Mzimu Woyera angatithandize bwanji Ife titamulora kutero?TSIKU LA 61. Kodi Mulungu amatipanga Ife motani kukhala Oyera?TSIKU LA 71. Kodi lonjezano lalikulu ndi liti limene Mulungu adapereka kwa okhulupirira Yesu aliyense?2. Kodi Mzimu Woyera amachita chiyani kuti Ife tiyanjane ndi Mulungu?3. Kodi Mzimu Woyera amachita chiyani kuti tikhale othekera pa dziko lapansi pano?37

Hooray! Your file is uploaded and ready to be published.

Saved successfully!

Ooh no, something went wrong!