10.03.2017 Views

Miyambi ya Patsokwe by Bonwell Rodgers

You also want an ePaper? Increase the reach of your titles

YUMPU automatically turns print PDFs into web optimized ePapers that Google loves.

MIYAMBI YA PATSOKWE

By Bonwell Rodgers

Miyambi ya Patsokwe

Miyambi, kapena kuti mikuluwiko, ndi mawu okhala ndi

tanthauzo lobisika kapena lophiphiritsa. Nthawi zambiri imakhala

chiganizo, ndipo kawirikawiri imakhala mutu wa nkhani kapena

nthano inayake. Munthu akaponya mwambi, anthu amakumbukira

nkhani yake yonse komanso phunziro lake. Miyambi ndi chida

chabwino kwambiri pothandiza ena. Ukhoza kupereka malangizo

amphamvu, kudzudzula kapena kuchenjeza munthu popanda

kumukhumudwitsa. Ena amanena miyambi pofuna kubisa

tanthauzo la zomwe akunena kuti ana a makutu akuthwa kapena

anthu ena asadziwe zimene akutanthauza. Timaponyanso miyambi

pofuna kukometsera nkhani kuti isakhale yozizira, koma kuti ikhale

ndi chikoka. Kungoti pamafunika ukadaulo kuti tiluke nkhani

n’kuponya mikuluwikoyo pamalo oyenera. N’chifukwa chake

kudziwa tanthauzo la mwambi ulionse n’kofunika kwambiri.

Miyambi ya Patsokwe

1

The Series Of Rodgers Bounty Books [RBB]

Copyright © January 2016 by Bonwell Rodgers.

All rights reserved. No part of this publication may be reproduced or transmitted in any form or by any means, electronical or

mechanical, including photocopy, recording or any imformation storage and retrieval system, without permission in writing from the

owner.

Requests for permission should be mailed to: Bonwellrodgers91@gmail.com

Phone: 0881813953, 0881831435

Miyambi ya Patsokwe

2

A

Abwino sakhalitsa.

-Anthu abwino sakhala moyo nthawi yaitali.

Achimseka pachimera.

-Mwambiwu umanena za anthu amene

amakonda munthu akakhala ndi chinachake

choti awapatse monga zakudya, zakumwa

kapena zinthu zina zomwe akudziwa kuti

akhoza kupindulapo. Zinthuzo

zikangomuthera amamutaya.

Achimseka pamaso, mumtima muli zina.

-Pali anthu ena omwe pamaso amaoneka

ngati anzako, koma kumbali amakudya

miseche kapena kukukonzera zoipa. Ena

amakhala oti mumtima mwawo anakupha

kalekale.

Miyambi ya Patsokwe

3

Achoke malizagudu, tiyanike inswa ziume.

-Mwambiwu umanenedwa ndi anthu omwe

sakufuna kuti anzawo akhalepo akamachita

zinazake. Mwachitsanzo, akhoza kukhala

kuti akufuna aphike nsima koma sakufuna

kuti anzawowo adye nawo. Zikatero

amadikira kaye enawo achoke ndipo pouzana

ndi amene amagwirizana nawo amati,

“Dikirani kaye, achoke malizagudu, tiyanike

inswa ziume.” Mwambiwu ukhoza

kunenedwanso ngati wina akungofuna kuti

achite zinazake anthu ena akachoka.

Adadya Kalikongwe wa nzeru zayekha.

-Mwambiwu umanena za munthu amene

samvera malangizo. Nthawi zambiri munthu

wotereyu amadzakumana ndi mavuto

kapenanso kufa kumene. Nkhani yake

imanena za mbewa yotchedwa Kalikongwe.

Tsiku lina anzake ankaiuza kuti, “Usakhale

Miyambi ya Patsokwe

4

apa anthu angakuphe,” koma Kalikongwe

sanamvere. Anzakewo atachoka,

kunabweradi anthu ndipo atamupeza

anamupha n’kukamudyera nsima.

Adatha mphika ndi “n’talawa.”

-Kukomedwa ndi chinthu kumapangitsa kuti

uzolowere kenako umatha kupalamula.

Adera amakoma podya nawo.

-Anthu adera amakonda munthu akakhala

pabwino koma zikamuvuta kapena

akasauka, amamuthawa. Achibale ake okha

ndi amene amamusamalabe.

Adye zabwino anadya zowawa.

-Mwambiwu umachenjeza munthu amene

amafuna atapeza zabwino zonse nthawi

imodzi. Akapanda kusamala amatha

kukumana ndi mavuto. Choncho, zabwino

zimabwera pang’onopang’ono, munthu

amangofunika kudikira kuti nthawi yake

Miyambi ya Patsokwe

5

ifike.

Adzidyera pamutu pa mfumu.

-Nthawi zina munthu amapeza mwayi

chifukwa cha munthu wina osati chifukwa

cha khama lake lokha ayi.

Agona chimwini nsomba.

-Nsomba imakhala ngati yagona koma

ikuona zonse zomwe zikuchitika. Mwambiwu

umanenedwa munthu wina akamakhala

mosamala kapena akamagona makutu ali

kunja poopa kuti ena akhoza kumuchita

chipongwe.

Akafuna kuchita, Kalulu azembera Galu.

-Pali anthu ena omwe amati akachita choipa

amayamba kunamizira osalakwa kapena

omwe nkhaniyo sikuwakhudza. Nthawi

zambiri anthu ngati amenewa amaoneka

ofatsa. Zimene anthu oterewa amachita

zikuyerekezedwa ndi zimene zingachitike

Miyambi ya Patsokwe

6

ngati Kalulu wachita chinachake choipa

koma mlandu n’kugwera Galu wosalakwa.

Akakhala mfulu ndi matenda, koma kapolo

ndi ulesi.

-Chinthu chimodzi chomwecho

chimatchulidwa mosiyasiyana malinga ndi

anthu ake. Munthu wolemera akhoza

kutenga chinthu cha mwini n’kumati

anangolakwitsa. Koma akakhala wosauka

amati waba.

Akam’meta n’kumva wapinama.

-Anamwali amaoneka ngati omvera komanso

ofatsa akamapatsidwa malangizo. Koma

akangomaliza kuwapatsa malangizowo,

amakayambiranso makhalidwe awo oipa.

Amaiwalilatu zimene analangizidwa zija.

Mwambiwu umanena za anthu amene

samvera malangizo. Akalangizidwa amakhala

ngati amva, koma pakangopita nthawi

Miyambi ya Patsokwe

7

amayamba kuchitanso zomwe zija.

Akapsala sagulitsana nkhwangwa yoduka.

-Akamberembere sangapusitsane okhaokha.

Mwachitsanzo, si kawirikawiri akuba

kuberana okhaokha.

Akapsala sapisana m’thumba.

-Nthawi zambiri, anthu a makhalidwe

ofanana sangapusitsane. Mwachitsanzo, si

kawirikawiri akuba kuberana okhaokha.

Akayanjana aleke.

-Anthu amene amagwirizana nthawi zina

amatha kuyambana kapena kudana kumene.

Zikatere chimene chimafunika ndi kuyesetsa

kuchita zinthu zoti agwirizanenso.

Akoma akadadza.

-Anthu amene poyamba amasonyeza

makhalidwe abwino kenako n’kuonetsa

khalidwe lawo lenileni.

Miyambi ya Patsokwe

8

Akugwira ziputu.

-Mawuwa amanenedwa mophiphiritsa za

munthu amene akukana kuchoka pamalo

kapena amene akukana kupita kumlandu

chifukwa akudziwa kale kuti zikamuvuta.

Akamanena za munthu wotereyu amati

“akugwira chiputu kapena ziputu.”

Akukana kali kutsaya.

-Pali anthu ena amakana mlandu kapena

zinthu zina m’maso muli gwa ngakhale kuti

pali umboni wonse wosonyeza kuti achita ndi

iwowo. Munthu akamakana zitafika

pamenepa timati akukana kali kutsaya.

Akula pusi wokhala patsekera.

-Pusi sangayende patsekera chifukwa ndi

wamkulu kwambiri. Chimodzimodzinso

munthu wamkulu, sayenera kumachita

zachibwana kapena kumasewera ndi ana.

Miyambi ya Patsokwe

9

Akula vumbwe wotantha patsekera.

-Vumbwe sangayende patsekera chifukwa ndi

wamkulu kwambiri. Chimodzimodzinso

munthu wamkulu, sayenera kumachita

zachibwana kapena kumasewera ndi ana.

Akulu n’kudzala.

-Munthu wamkulu pamudzi kapena

pantchito amakhala ngati kudzala chifukwa

nkhani zonse zimakathera kwa iye.

Akuluakulu amapempha ndi maso.

-Nthawi zambiri akuluakulu sachita kukuuza

kuti uwathandize. Amangokuyang’ana kuti

wekha udziwe zochita. Mwambiwu

umanenedwa munthu wina wamkulu

akachita zimenezi. Anthu amati,

“Tangowapatsani, akuluakulutu amapempha

ndi maso!”

Akuluakulu ndi m’dambo mozimira moto.

-Moto wolusa umazima ukafika m’dambo

Miyambi ya Patsokwe

10

chifukwa cha madzi kapena chinyezi.

Akuluakulunso amatha kuyanjanitsa anthu

akadana kapenanso kukhazikitsa mitima ya

anthu pansi ngati pali zina zovuta komanso

kupereka malangizo abwino. Komanso,

nthawi zambiri ana akapalamula vuto lonse

limafikira kwa makolo ndipo makolowo ndi

amene amavutika nalo.

Akuluakulu saika mtima pa imfa yako,

nawenso umwalira posachedwa.

-Osamafunira mnzako zoipa chifukwa

nawenso zikhoza kukuchitikira.

Akunja n’kunkhokwe.

-Anthu ochokera kwina amakhala ngati

nkhokwe chifukwa amabwera ndi zachilendo.

Si chinthu chanzeru kumanyoza anthu adera

chifukwa nthawi zina ndi amene

angatithandize kuthetsa mavuto athu.

Miyambi ya Patsokwe

11

Akupempha, kali kutsaya.

-Mawuwa amanenedwa pamene munthu

akupempha chikhululukiro kusonyeza

kulapa koma n’kumapitirizabe kuchita zoipa.

Akupempha, lumo lili kumutu.

-Mawuwa amanenedwa wina akamalapa

kapena kupepesa zinthu zitavuta kale.

Akuthawa mfuu yake yomwe.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

akukana ntchito kapena cholakwa chomwe

wachita. Mwachitsanzo mnyamata angakane

mtsikana amene wamuchimwitsa (popeza

onse amakhala achimwa mwina tinene kuti

wachimwa naye).

Alendo akaipitsa m’nyumba, m’mawa

agona kuti?

-Si bwino kuwononga zinthu pamalo amene

tikukhala tikumaganiza kuti sitikhalitsapo,

chifukwa mawa tidzafunanso kugona

Miyambi ya Patsokwe

12

pomwepo.

Ali dere n’kulinga utayenda naye.

-Munthu umadziwa bwino makhalidwe a

mnzako ngati utakhala naye limodzi kapena

kuyenda naye.

Ali dere n’kulinga utayenda naye.

-Umboni weniweni umafunika kuchoka pa

zimene waziona.

Ali ndi amayi anadala, amayenda

monyada.

-Kukhala wamasiye n’kopweteka kwambiri.

Makolo ndi ofunika kuti mwana azisangalala

komanso kuti akule bwino.

Ali ndi mwana agwiritse.

-Mawuwa amanenedwa pamene pabuka vuto

lalikulu ndiye wina akuchenjeza anzake kuti

pakufunika kulimba nazo. Mwambiwu

unabwera chifukwa nthawi zambiri anthu

Miyambi ya Patsokwe

13

akakhala pamavuto, amayambirira

kusamalira ana awo.

Ali patsogolo ali pambuyo pomwe.

-Munthu amene waima pamzere kutsogolo

akhoza kukhala kumbuyo ngati atauza

anthuwo kuti atembenuke. Si bwino

kumathamangira zamtsogolo chifukwa

chilichonse chili ndi nthawi yake.

Ali patsogolo ndi amene ali pambuyo.

-Nthawi zina amene ali patsogolo amatha

kukhala pambuyo ngati anthuwo atauzidwa

kuti atembunuke. Chimodzimodzi ndi mwayi

umene ena ali nawo, mawa zikhoza

kutembenuka n’kupezeka kuti ndi wathu.

Alibe pokomera, chili m’pokomera

n’chirombo.

-Pali anthu ena omwe amati akathandizidwa

amayambanso kunyoza amene

awathandizawo. Anthu oterewa ndi oipa

Miyambi ya Patsokwe

14

kuposa chilombo chifukwa nthawi zina

chilombo ukachichitira zabwino

chimayamika.

Aliona potuluka, polowa salipenya.

-Mawuwa amanenedwa poopseza munthu

amene walakwira mnzake kuti saliona dzuwa

likamalowa chifukwa afa atalodzedwa.

Mawuwa anabwera chifukwa cha

zikhulupiriro za ku Africa kuno zoti anthu

amalodza anzawo kapena kuwachesula kuti

akumane ndi zoopsa.

Aliyense adzadya thukuta lake.

-Munthu amafunika kulimbikira ntchito kuti

apeze zimene akufuna.

Aliyense akondwa potsiriza.

-Munthu amasangalala akamaliza kugwira

ntchito mwakhama n’kulandira malipiro ake.

Miyambi ya Patsokwe

15

Amadziombera ng’oma yekha.

-Mawuwa amanena za munthu amene

amakonda kuuza ena zokhudza zimene

amachita komanso luso lake.

Amalume khalani pansi, ana akudziweni.

-Si bwino kumangokhalira kuyendayenda.

Ndi bwino kumakhalako pakhomo nthawi

zina.

Amapatsa mosiyana.

-Si bwino kusirira kapena kuchitira nsanje

anzathu opeza bwino kapena amene

zikuwayendera.

Amene akufuna kuswa fupa amapita

kuuzimba.

-Ukafuna chinthu umafunika kugwira

ntchito. Kuti uswe fupa la nyama umafunika

kukasaka nyama kuthengo m’malo

mongolongedza miyendo n’kumadikira kuti

ikupeze pamene wakhalapo.

Miyambi ya Patsokwe

16

Amene amagona kunsi kwa mwala, ndi

amene amaona mwala ukupuma.

-Ngati munthu ukufuna kumva zoona za

zinthu ungachite bwino kufunsa amene

analipo pamene chinthucho chinkachitika.

Amene umadya naye mbale imodzi ndi

amene amakupereka.

-Mnzako amene umamukhulupirira ndi

amene amakupereka kwa adani ako monga

mmene zinachitikira ndi Yesu. Anaperekedwa

ndi wophunzira wake.

Ana a ngoma opanda makutu.

-Mawuwa amanenedwa kwa ana osamvera.

Amawayerekezera ndi ana a ngoma omwe

alibe makutu.

Anadya matako a galu.

-Si kawirikawiri kuona galu atakhala pansi

ndi matako ake. Nthawi zonse amangokhalira

kuyendayenda. Ndiye munthu akakhalanso

Miyambi ya Patsokwe

17

kuti samakhala pansi, amangokhalira

kuyendayenda amati, “anadya matako a

galu.”

Anadya mtedza wa ching’onga.

-Mwambiwu umanena za munthu amene

sachedwa kuiwala zinthu. Ching’onga

chimati chikabisa kanthu chimaiwala

msanga, ndipo anthu amadzatola.

Anadya mtima wa Kalulu, nkona ali ndi

mtima wokaluluka.

-Mwambiwu umanena za munthu amene ali

ndi mtima wapachala, wosachedwa kupsa

mtima.

Anadya mtima wa Sontho.

-Mwambiwu umanena za munthu amene

amachita zinthu mopupuluma kapena

mofulumira kwambiri. Sontho ndi mbewa

imene imakonda kukhala m’makoko a

chimanga chikakhala kuti sichinakololedwe.

Miyambi ya Patsokwe

18

Ndiyeno mbewayi imasonthoka ikamva

phokoso la anthu okolola. N’chifukwa chake

amaitchula kuti Sontho. Choncho, chifukwa

chakuti munthu wopupuluma amachita

zofanana ndi zimene mbewazi zimachita

zikamathawa m’makoko a chimanga,

amangoti anadya mtima wa Sontho.

Anafa ndi nsanjikizo.

-Anthu akamanena za munthu amene

wadzigwiritsa chifukwa choti ananena zinthu

zambirimbiri kapena ananena zinthu zomwe

zamuika m’mavuto, amanena mwambiwu

kuti, “Anafa ndi nsanjikozo.” Mwambiwu

umanenanso za munthu amene samamva

kamodzi akalangizidwa.

Anafa wolongosola, aliko ndi kanthu

umachita.

-Mwambiwu umanenedwa ngati mfumu

yabwino kapena munthu wina yemwe

Miyambi ya Patsokwe

19

amachita bwino zinthu zinazake wamwalira.

Amaunena mfumu ina yosalongosoka

ikakhala pampando kapena wina

akamagwira ntchito imene munthu

anamwalira uja ankagwira.

Anagula mbereko mwana asanabadwe.

-Mbereko ndi nsalu yoberekera kapena

kufunditsa mwana wakhanda. Mwambiwu

umanena za munthu amene akuchita zinthu

mopupuluma nthawi yochitira zinthuzo

isanakwane.

Anagulula nkhwangwa n’chambuyo.

-Mawuwa amanena za munthu wosabereka.

Anagwirizana malo okumana, koma

anagona m’mitengo yosiyana.

-Mwambiwu umanenedwa ngati anthu ena

omwe amayendera limodzi asemphana

chichewa n’kusiya kuyendera limodzi kapena

kusiya kugwirizana.

Miyambi ya Patsokwe

20

Anakhoma mutu wa Kalulu.

-Mutu wa Kalulu ndi wofewa moti kuukhoma

suchedwa kusweka. Mwambiwu

umatanthauza kupalamula mlandu.

Analawira m’mawa ndiye anapita.

-Anthu ena atanyanyalitsana, wina

anangolawira kuchokapo. Kukangana

kumabalalitsa anthu.

Anamva ili m’mutu

-Mawuwa amanena za munthu amene

amamva akakumana ndi mavuto. Munthu

wotero amakhala ngati wamva nkhwangwa ili

m’mutu.

Anamwa tiyi adzamwanso, bola kusunga

masupuni.

-Pamoyo wa munthu pamakhala mavuto,

tikakhala pamavuto tisamaganize kuti zinthu

sizidzayendanso.

Miyambi ya Patsokwe

21

Anandimangira njoka m’masamba kuti

andipweteke.

-Mwambiwu umanenedwa pamene anzako

akuchitira zoipa mwakabisira kuti ukumane

ndi mavuto kapena akupweteke.

Ananditseka mawu kuti ndisayankhule.

-Mawu omwe amatanthauza kuti munthu ali

ndi mawu, koma kuti ayankhule,

akumuletsa.

Anaotha chichiri cha tsimba.

-Tsimba ndi nyumba imene amasungirako

mafumu olandira udindo kapena anamwali.

Chichiri ndi mtengo ndipo monga mwa

mwambo wa Achewa, mtengo umenewo

kuuotcha amakhala malawulo. Mwambiwu

umanenedwa munthu akapalamula

pokwiyitsa anthu amene ankamuthandiza.

Tsimba likhoza kukhalanso nyumba

yamasiye. Chifukwa cha zikhulupiriro, anthu

Miyambi ya Patsokwe

22

amaopa kuphikira kapena kuotha nkhuni

zake. Ndiye ngati munthu wina watenga

nkhuni zake n’kuotha amamuona kuti

wapalamula. N’chifukwa chake munthu

akapalamula anthu amanena kuti, “Waotha

chichiri cha tsimba.”

Anataya udzu womwetamweta.

-Mwambiwu umanena za munthu amene

wataya mwawi chifukwa chosakhazikika

kapena kuyendayenda.

Anatsogoza mawu nyama isanafe.

-Mwambiwu umachenjeza anthu kuti

azidikira kaye n’kuona kuti zinthu zikhala

bwanji m’malo mofulumira kuyankhula.

Anayamwira kubere.

-Nthawi zambiri munthu amatengera

khalidwe kuchokera kwa makolo ake.

Miyambi ya Patsokwe

23

Andiitana pakalowa njoka, pakalowa

mbewa akumba okha.

-Mawuwa amanena za anthu omwe amafuna

anzawo akakhala pamavuto, koma akakhala

pabwino sagwirika.

Anditame anasupula mtembo wa eni ake.

-Si bwino kumachita zinthu mojijirika

kapena kumadzitama pa zinthu zomwe

sukuzidziwa bwino.

Angakulande, gwiritsa.

-Mawuwa amachenjeza munthu kuti asamale

zimene ali nazo. Pali anthu ena omwe

amafuna kuti zinthu za anzawo zikhale zawo,

choncho m’pofunika kumateteza zinthu zako.

Angatero ndi maliro ndithu.

-Ngakhale munthu utanyada bwanji, tsiku

lina udzakhalabe maliro. Choncho, kunyada

kulibe phindu, chachikulu ndi kukondana

ndi anzathu chifukwa ngakhale tiyerekedwe,

Miyambi ya Patsokwe

24

tidzamwalirabe.

Angoni satha onse.

-Mawuwa amatanthauza kuti ngakhale

zinthu zitavuta bwanji, pamakhalabe ena

opulumuka. Mwambiwu unayamba pa

nthawi imene Angoni ankamenyana ndi

Alomwe. Alomwewo anaphika kalongonda,

ndiye Angoni ena ataona kalongondayo ndi

njala ndi njala, anangoyamba kudya

osadziwa kuti ndi zosasuluka. Ambiri anafa

ndipo Angoni anayamba kutchula Alomwe

kuti angurudi (kutanthauza akuluakulu

pankhondo). Masiku ano pamalo amene

zimenezi zinachitikira pamatchedwa pa

Ngurudi. Ngakhale anafa ambiri, Angoni ena

anapulumuka.

Anthu aluso sadyera mwabwino.

-Nthawi zambiri anthu amene amalangiza

anzawo sakhala ndi makhalidwe abwino.

Miyambi ya Patsokwe

25

Zimenezi n’zofanana ndi zimene anthu aluso

amachita. Amakonzera ena zinthu zabwino

kwambiri n’kumalephera kupanga zoti

azigwiritsa ntchito iwowo.

Anthu muziwaopa, sali ndi miyendo inayi

ngati Mkango.

-Tiyenera kulemekezana ngati anthu,

chifukwa tsiku lina tidzafuna anzathu kuti

atithandize. Anthu sali ngati nyama

zakutchire zoti ungathe kuthawa mkwiyo

wawo.

Anthu ndi mchenga sawundika.

-Anthu ena amakhala osadalirika.

Ukapangana nawo zinthu amachita zina.

Anthu ndi miyala sakukutika.

-Mwambiwu umasonyeza kuti nthawi zina,

ngakhale anthu uwachitire zabwino

sathokoza. Nthawi zina amayambanso

kukunyoza kapena kukuchitira chipongwe

Miyambi ya Patsokwe

26

ngati kuti ndi udindo wako kuti

uziwathandiza. Pomwe ena amakhala

osadalirika. Ukapangana nawo zinthu

amachita zina.

Anthu ndi miyala sawundika.

-Anthu ena amakhala osadalirika.

Ukapangana nawo zinthu amachita zina.

Anthu oyanjana sagona manda amodzi.

-Mpofunika kumakondananso ndi anthu ena

m’malo mongokonda munthu m’modzi.

Anyang’wa a insa, aona ukonde waguluka.

-Anthu ochita zoipa monga ankhanza

komanso akuba amatengerapo mwayi akaona

kuti mfumu kapena wolamulira ndi wofatsa

ndiponso woleza mtima, moti amayamba

kuzunza anzawo ndi kuchita zoipa zina

zomwe sakanachita zikanakhala kuti mfumu

yake ndi yankhanza kapena yolamulira

pomenya matebulo.

Miyambi ya Patsokwe

27

Anyani amaonana zikang’a.

-Osamasekana wina akalakwitsa chifukwa

nafenso nthawi zina timalakwitsa ngati iyeyo.

Mmalo mwake tizikhululukirana ndi

kulemekezana. Komanso si bwino

kumanyoza kapena kuseka ena pa zinthu

zomwe nawenso umachita.

Anyani kuseweretsa magwafa.

-Mawuwa amanenedwa munthu akamachita

chibwana ndi zinthu zofunika kapena

akamaseweretsa zinthu zofunika.

Anyani sasekana zikundu.

-Osamasekana wina akalakwitsa chifukwa

nafenso nthawi zina timalakwitsa ngati iyeyo.

Mmalo mwake tizikhululukirana ndi

kulemekezana. Komanso si bwino

kumanyoza kapena kuseka ena pa zinthu

zomwe nawenso umachita.

Miyambi ya Patsokwe

28

Aonenji adagwira kanthu mumdima.

-Anthu onyozeka amatha kuchita zinthu

zomwe anthu odziwika sangakwanitse monga

kukhala olemera komanso kukhala ndi banja

labwino.

Aonenji anapha mvuu m’mono.

-Anthu ena amaoneka ngati onyozeka mwina

chifukwa cha kusauka ndipo ena

sawathandiza poganizira kuti palibe chomwe

angadzawabwezere. Tsiku lina anthu otere

amadzachita chinthu chodabwitsa kapenanso

kukhala ndi china chofunika. Kuyeserera

n’kofunika kusiyana ndi kungoyang’ana

zinthu poganiza kuti sizingatheke.

Tisamapeputse nzeru za ena mpaka titaona

zotsatira zake.

Aonenji anapha njovu ndi mwala.

-Anthu ena amaoneka ngati onyozeka mwina

chifukwa cha kusauka ndipo ena

Miyambi ya Patsokwe

29

sawathandiza poganizira kuti palibe chomwe

angadzawabwezere. Tsiku lina anthu otere

amadzachita chinthu chodabwitsa kapenanso

kukhala ndi china chofunika.

Apawo ndi mchenga, madzi apita pansi.

-Munthu ukakhala mlendo sudziwa zomwe

eni mudzi akupangana, umangoona

zikuchitika. Ali ngati mchenga omwe

sudziwika kuti pansi pake pali madzi.

Choncho, ukakhala pamudzi umayenera

kusamala chifukwa nthawi zina amaoneka

ngati sagwirizana pomwe amagwirizana

ndithu.

Apawo ndi mizu ya kachere, amakumana

pansi.

-Munthu ukakhala mlendo sudziwa zomwe

eni mudzi akupangana, umangoona

zikuchitika. Ali ngati mizu ya kachere yomwe

sudziwika kuti yakumana pansi. Choncho,

Miyambi ya Patsokwe

30

ukakhala pamudzi umayenera kusamala

chifukwa nthawi zina amaoneka ngati

sagwirizana pomwe amagwirizana ndithu.

Atadya anamwera.

-Chilichonse chimakhala ndi nthawi yake.

Atambala awiri salira m’khola limodzi.

-N’zovuta kuti anthu awiri azilamulira

chinthu chimodzi.

Atambwali sametana, amaopa kuchekana.

-Nthawi zambiri anthu amene amachita

zofanana zimakhala zovuta kuti apusitsane.

Atambwali sangapitane pansi.

Atambwali sametana, amawopa

kuchekana.

-Ochenjera okhaokha sangapusitsane.

Aulesi sangapate kanthu.

-Palibe chinthu cholongosoka chimene

munthu waulesi angapeze. Nthawi zambiri

Miyambi ya Patsokwe

31

usiwa umamugwira munthu wotereyu ngati

kapolo.

Awonenji adapha mvuwu m’mono.

-Munthu aliyense ali ndi mwayi wake.

Choncho, si bwino kuganiza kuti anthu ena

ooneka onyozeka sangapeze mwayi.

Awonenji adapha njovu ndi mbuna.

-Munthu aliyense ali ndi mwayi wake.

Choncho, si bwino kuganiza kuti anthu ena

ooneka onyozeka sangapeze mwayi.

Miyambi ya Patsokwe

32

B

Bango likauma, limabwera linzake.

-Anthu sasangalala ndi munthu wovuta

kapena woipa. Mwachitsanzo, mwana

akakhala wamwano kapena wosamvera,

makolo ake anganene kuti, “Olo atamwalira,

tidzabereka wina.”

Banja lili ngati mzinda wozunguliridwa ndi

adani, ena amafuna atalowamo, pomwe

ena amafuna atatulukamo.

-Munthu amene sali pabanja amafuna

atalowa m’banja, koma amene ali pabanja,

akaona zokhoma za m’banjamo amafuna

atalithawa. Ndi bwino kumayamba taganiza

mwakuya komanso kusankha bwino

tikamafuna kulowa m’banja.

Miyambi ya Patsokwe

33

Banja ndi anthu awiri, wachitatu ndi

wosokoneza.

-Pabanja sakhala anthu atatu. Ndi bwino

kukhala ndi wachikondi m’modzi.

Banja ndi gombe, silichedwa kugumuka.

-Mawuwa amanena za banja kapena ubwenzi

umene umayamba chifukwa cha katundu

kapena chuma. Nthawi zambiri zinthuzo

zikatha, ubwenzinso umathera pomwepo, si

nanga munthuyo amakhala anakwatira

kapena anali pa ubwenzi ndi chumacho!

Batani lapansana amakumanga ndi

mnzako.

-Pali zinthu zina zomwe zimafuna mnzako

kuti akuthandize.

Bemberezi adziwa nyumba yake.

-N’zosatheka kuti munthu aiwale kwawo.

Miyambi ya Patsokwe

34

Bisani matenda, maliro tidzamva.

-Munthu utha kubisa mavuto ako aang’ono,

koma akafika poipa kwambiri, umafuna

anzako kuti akuthandize.

Bodza likhoza kuyenda n’kuzungulira

theka la dziko lonse lapansi, choonadi

chikuvalabe nsapato zake kuti chilitsatire.

-Bodza limafala mofulumira kusiyana ndi

choonadi.

Bodza lilibe mwini.

-Anthu amene sitimayembekezera kuti

anganame nthawi zina amanena bodza

m’maso muli gwa.

Bodza limabwerera mwini wake.

-Munthu ukanena bodza, bodzalo

limakusakasaka mpaka kukupeza. Ndi bwino

kumasamala ndi zimene timanena, ngati

tilibe nkhani ndi bwino kungokhala chete

m’malo momapeka mabodza.

Miyambi ya Patsokwe

35

Bololo sakonda madzi.

-Pamene munthu watsimikiza kuchita

kanthu kena, amakumana ndi mavuto

komanso mayesero. Komabe, sayenera kulola

kuti zimenezi zimulepheretse cholinga chake

kapena kumugwetsa mphwayi.

Bongololo anali ndiwo, timadya ndi a uje.

-Si bwino kumadzitama pa zinthu zomwe

sunapange chifukwa nthawi zina

umangonama kuti unapanga.

Bongololo sadzolera mafuta pagulu.

-Si bwino kuulula zinsinsi zathu zonse, pali

zinthu zina zomwe sitiyenera kuuza ena

monga zam’banja. Nthawi zambiri munthu

akaulula zimenezi amayalutsa banja lakelo.

Bonongwe mkoma akadadza.

-Nthawi zina mlendo amaonetsa makhalidwe

abwino, koma akakhalitsa amaonetsa

khalidwe lake lenileni.

Miyambi ya Patsokwe

36

Buluzi kuthandiza mbewa kuthawa.

-Nthawi zina anthu amene sitigwirizana nawo

kapena amene sitiwadziwa ndi amene

amatithandiza.

Buluzi wa ize (mnyengo) anapanidwa ndi

chitseko.

-Kuchita zinthu zachinyengo monga

chiwerewere kapena kuba kukhoza kutiika

m’mavuto osaneneka.

Bwato silidya.

-Nsengwa, dengu kapena bwato

zimangosunga zinthu zimene mwaikamo,

sizimachepa kapena kuwonjezereka.

Tizikhutira ndi zimene tili nazo pamoyo

wathu.

Bwenzi lako ndi la wina.

-Tizichenjera ndi anzathu amene timacheza

nawo chifukwa tikawauza kathu, iwonso

amakauza anzawo.

Miyambi ya Patsokwe

37

Bwenzi mkoma uli moyo.

-Pali anthu ena amene amakonda anzawo

zinthu zikamayenda, koma zikavuta

amawathawa.

Bwenzi ndi mthanthira, mlamba udaolotsa

khoswe.

-Bwenzi lenileni liyenera kukhala lokonzeka

kuthandiza mnzake akakumana ndi mavuto,

osangoti pa zabwino zokha.

Bwerera ali konse.

-Mnzako akakuchitira chabwino umafunika

kumuthokoza. Koma iwenso umayenera

kudzamuchitira zabwino, asamangochita

yekha.

Bza sapita kawiri.

-Bza ndi mvekero wa kuthawa mwamwayi.

Ngati munthu wapulumuka pa vuto

mwamwayi, si bwino kubwereza kuchitanso

zomwezo.

Miyambi ya Patsokwe

38

C

Chabadwa chafa, chili kumpani chauma.

-Ngati munthu uli ndi moyo, dziwa kuti

udzafa ndithu ndiponso mavuto udzakumana

nawo.

Chadodometsa mleme chili ndi khambi.

-Munthu akasiya chizolowezi chake ndiye

kuti chilipo chimene chamudabwitsa kapena

chamuchititsa mantha. Ukaona chomwe wina

chamupezetsa tsoka, umayesetsa kupewa

kuchita zomwezo.

Chadza ndi yani chokwera ndi mwana

kunkhokwe?

-Tisamachite zomwe zingabweretsere ena

mavuto. Kale anthu ankapewa kukwera ndi

mwana munkhokwe kuopa kugwa ndi

mwanayo n’kumuvulaza.

Miyambi ya Patsokwe

39

Chadza ndi yani chopha nkhuku anzanu

akudwala dzino?

-Mawuwa amanenedwa munthu akachita

zinazake zomwe akudziwiratu kuti nzake

sachita nawo chifukwa akudwala kapena

wapanikizika ndi zina.

Chafa chaola, phwiti wasekera nthenga.

-Munthu akamwalira, si anthu onse omwe

amaliradi chifukwa cha chisoni. Ena amalira

kwinaku akusangalala kuti adzatenge chuma

chamasiye kapena adzalowe udindo wa

womwalirayo.

Chafuna mwini chili kwa Bongololo (kwa

Mandala).

-Munthu ukafunitsitsa chinthu, ndi bwino

kulimbikira kugwira ntchito ndipo ukhoza

kuchipeza.

Chagwa pamtutu sichidyeka.

-Mwambiwu umanena za munthu amene

Miyambi ya Patsokwe

40

akulephera kugamula mlandu chifukwa

mlanduwo ndi wa m’bale wake.

Chagwera pamfuno sichidyeka.

-Mwambiwu umanena za munthu amene

akulephera kugamula mlandu chifukwa

mlanduwo ndi wa m’bale wake.

Chaipira Galu kuluma Mbuzi.

-Munthu anganene mawuwa akamadandaula

ndi mavuto omwe amulepheretsa kuchita

zinthu zimene amafuna. Munthu

anganenenso mawuwa podandaula zinthu

zopanda chilungamo zimene ena amuchitira.

Chakanachakana, dazi lilibe mankhwala.

-Pali zinthu zina zomwe ndi umunthu wathu

sitingazithe. Zoterezi tiyenera kuvomereza

kuti zikhale mmene zilili ndi kukhutira ndi

zimene tili nazo.

Miyambi ya Patsokwe

41

Chakanachakana, Kalulu sasenda nguwo.

-Tizivomereza ngati zinthu zavuta,

osamachita ukamberembere.

Chako n’chako sichilingana, n’chamwini.

-Chinthu chako umachigwiritsa ntchito

mwanjira iliyonse, koma chamwini

umachiopa.

Chakomera nzako umasimba.

-Ndi bwino kumayamikirako zabwino zimene

ena achita.

Chakomera Mbuzi kugunda Galu, Galu

akati agundeko akuti wapenga.

-Osamachita zinthu mokondera kapena

kumachitira ena nkhanza tikudziwa kuti ena

atiikira kumbuyo.

Chakomera Mbuzi kugunda Galu, Galu

akati alumeko akuti waboola nguwo.

-Osamachita zinthu mokondera kapena

Miyambi ya Patsokwe

42

kumachitira ena nkhanza tikudziwa kuti ena

atiikira kumbuyo.

Chakometsa Ntchentche, inachilimika

kuuluka.

-Kuti munthu upeze bwino umafunika

kukhala ndi podalira komanso kuchita

khama.

Chakonda mnzako mlekere, mawa

chidzakonda iwe.

-Mnzathu akachita mwayi si bwino

kumuchitira nsanje n’kuyamba kumuchitira

zoipa. Ndi bwino kumangoyamikira chifukwa

sudziwa chidzachitike mawa. Mwina mwayi

udzakhala wako.

Chalowa m’khutu, chalowa.

-Zimene munthu wamva, zimakhala kuti

wazimva basi. Sungachitenso chilichonse

kuti zibwerere. Tizisamala tisanayankhule.

Miyambi ya Patsokwe

43

Chakubala chimasanzitsa, obereka

amanyansidwa.

-Makolo ayenera kukhutira ndi mphatso za

ana omwe Mulungu wawapatsa.

Chakudya chawekha sichikoma, koma

cholimbirana.

-Pali zinthu zina zomwe sizikoma kupanga

wekha monga mapwando, ntchito komanso

zina. Ndi bwino kumagawanako ndi ena

zimene tili nazo.

Chakudya chimodzimodzi sichinona.

-Ndi bwino kumasinthasinthako pochita

zinthu.

Chakudya chimodzimodzi sichinonetsa.

-Si nzeru munthu kukhulupirira nzeru zake

zokha. Ndi bwino kumafunsako ena kuti

tikhale ndi chinthunzithunzi chokwanira cha

moyo kapena ntchito.

Miyambi ya Patsokwe

44

Chakudya sichichepa, chimachepa ndi

chovala.

-Chovala chimodzi simungathe kuvala anthu

awiri nthawi imodzi. Koma chakudya

ngakhale chitachepa bwanji mukhoza

kugawana. Mawuwa amanenedwa poitanira

ena kuti adzadye nawo chakudya.

Kumayamikira zimene timapeza.

Chakudza sichiimba ng’oma.

-Kumakonzekera zam’tsogolo, chifukwa

zamawa sizidziwika.

Chakufa sichiopa kutulutsa fungo.

-Chilichonse chimakhala ndi zotsatira zake

ndipo sitingaziletse. Munthu amene walakwa

walakwa basi. Mbiri yake imaipa ndipo

amapatsidwa chilango.

Chakufa sichiyankhula.

-Munthu amene kunalibe sangaikire umboni

pa nkhani imene yangogwa. Komanso

Miyambi ya Patsokwe

45

munthu amene wamwalira sangachite

chilichonse, ngati akuyankhula ndiye kuti

adakali moyo.

Chakumbakumba chalema, chatenga

mchira chayesa mala.

-Nthawi zina munthu amasiya kuyesayesa

kuthetsa mavuto n’kuyamba kumangokhala

poganiza kuti atha okha.

Chakuti “tswo” chakuyambira, chakuti

“tseche” chakupha.

-Tisamadandaule ndi zovuta zomwe

zimabwera pang’onopang’ono koma zomwe

zimabwera kamodzim’kamodzi.

Chakwathu n’chakwathu adamangira

nkhokwe m’nyumba.

-Ndi bwino kumamvera zimene ena akunena.

Osamangoumirira njira zakale popanda

chifukwa chomveka bwino, chifukwa mapeto

ake timapezeka kuti talakwitsa.

Miyambi ya Patsokwe

46

Chala chimodzi sichiswa nsabwe.

-Palibe munthu amene angathe kuchita

zonse payekha. Choncho, ndi bwino

kumadalirana. Pogwira ntchito kapena

pothetsa vuto, thandizo la anthu ena ndi

lofunika.

Chala sicholoza mwini.

-Munthu sakonda kuona kulakwa kwake

koma kwa ena.

Chalaka (chakanika) Bakha, Nkhuku

singatole.

-Chimene chakanika katswiri munthu

wamba sangachithe.

Chalaka Galu, fupa la matongwe.

-Mawu amenewa amanena za munthu yemwe

ndi wosamva ngakhale mutamulangiza

motani. Amakhala ngati fupa louma lomwe

agalu alephera kuliswa.

Miyambi ya Patsokwe

47

Chalaka Nyani chili ndi khambi.

-Munthu akasiya chizolowezi chake ndiye

kuti chilipo chimene chamudabwitsa kapena

chamuchititsa mantha.

Chalimba chalimba, shati sikhala yopanda

kolala.

-Ngakhale chinthu chikhale champhamvu,

chimasowabe china chochichirikiza. Aliyense

ndi wofunika.

Chalowa m’khutu chayanza malo.

-Chimene munthu wamva

sangachitulutsenso. Choncho, mpofunika

kuchenjera polankhula kuopa kulakwitsa.

Chambo chimaona konse.

-Munthu ukakhala pabanja, si bwino

kumathandiza abale ako okha. Umayenera

kumathandizanso abale a mkazi kapena

mwamuna wako.

Miyambi ya Patsokwe

48

Chamkuka nkhali yagaga.

-Mawu amenewa amanena za munthu

waulesi, wongokonda kukhala m’nyumba.

Chomwe amadziwa ndi kudya basi.

Chamuna sayanika.

-Munthu ukakhala ndi mphamvu

usamadzionetsere, chifukwa tsiku lina

umadzakumana ndi anzako omwe

amadzakuphuvumula n’kukuchititsa

manyazi.

Chamwini m’chamwini, ungalimbe maka.

-Anthu ena maso amangokhala pa zinthu za

anzawo, osakhutitsidwa ndi zomwe ali nazo.

Tifunika kumachenjera ndi anthu amenewa.

Osamadalira kwambiri zinthu za ena.

Changodza m’chironda, mankhwala palibe.

-Mawuwa amanenedwa munthu

akamadandaula kuti, ngakhale mavuto

monga matenda komanso milandu abwera,

Miyambi ya Patsokwe

49

palibe njira yowathetsera.

Chaomba guta.

-Tsoka likagwera mlendo, anthu sadandaula

kwenikweni. Koma chisoni chimakula

pamene wapamudzi pomwepo wakumana ndi

mavuto.

Chaona maso, mtima suiwala.

-Ndi bwino kumasamala ndi zimene timaona

chifukwa zikhoza kutigwetsera m’mavuto

aakulu monga chigololo. Zimene munthu

waona amazikumbukira ngakhale patadutsa

nthawi yaitali.

Chaona mchira gondwa ali m’mphako.

-Kusaonetsetsa kapena kusamvetsa zinthu

kumapangitsa kuti munthu azinena nkhani

popanda umboni weniweni.

Miyambi ya Patsokwe

50

Chaona mnzako chapita, mawa chili pa

iwe.

-Osamasangalala ena akamakumana ndi

mavuto chifukwa nawenso akhoza kukupeza.

Chaona munda wakuthungo, mawa

chidzaona munda wapakati.

-Munthu ukakhala pabwino umaona ngati

sungadzavutike. Nthawi zina munthu

umatha kukumana ndi chinthu chimene

sumayembekezera kuti chingachitike.

Chaona mwana tola, ukulu n’kuona kako.

-Chaona mwana chitole chifukwa udzadya

naye. Tisanyozere chimene munthu amene ali

pansi pathu wapeza, chifukwa chikhoza

kutithandiza.

Chaphulika chapsa, mkamwini konza

nguwo.

-Chinthu chikachitika, monga imfa,

pamafunika kulimba mtima chifukwa

Miyambi ya Patsokwe

51

chachitika chatha. Palibenso njira ina

yochithetsera.

Chapita apa wachiona ndi munthu.

-Pa moyo wa munthu anthu ena ndi ofunika

chifukwa amakuchenjeza.

Chapitamo wosenda luzi pamwala.

-Mawuwa amanena za munthu wodziwa

kwambiri mankhwala a zitsamba kuposa

onse.

Chati chubwi, sichinaoloke, koma chati

kapakapa.

-Mawuwa amatanthauza kuti mawu oyamba

ndi malonje chabe, nkhani yeniyeni

sinayambe.

Chati chubwi! chisati kapa! sichinaoloke.

-Mawuwa amatanthauza kuti mawu oyamba

ndi malonje chabe, nkhani yeniyeni

sinayambe.

Miyambi ya Patsokwe

52

Chati deru chadabwitsa mlenje.

-Kanthu sikachitika popanda chifukwa

kapena choyambitsa chake. Ndiye

kachizindikiro kangachepe bwanji, tizikhala

nako tcheru.

Chati deru chawopsa mlenje.

-Munthu akasiya chizolowezi chake ndiye

kuti chilipo chimene chamudabwitsa kapena

chamuchititsa mantha.

Chati khocho (tswa) sichinapite.

-China chake chikakudabwitsa, khala tcheru.

Chatuluka m’dzira n’chiyani?

-Mwamuna akamakana kuti si amene

anachimwitsa mkazi, anthu amanena mawu

amenewa pofuna kudziwa ngati mwana

wobadwayo akufanana ndi mwamunayo. Pa

mlandu uliwonse payenera kukhala umboni.

Miyambi ya Patsokwe

53

Chauluka chidzatera.

-Tingatchuke kapena kulemera bwanji, tsiku

limadzafika loti timadzasauka kapena

kudzamwalira n’kusiyana nazo zonse. Moyo

umanyenga.

Chenjerechenjere pa m’meto, pa maliro

panalibe.

-Mawuwa amanena za munthu amene

amajijirika kapena kuchenjera pakakhala

palibe mavuto, koma mavuto akagwa

amafuna kuti anthu ena amuthandize.

Chenjerechenjere sadzimeta, amakumeta

ndi mnzako.

-Ngakhale munthu aoneke wochenjera

motani, monga kuthawa ntchito za gulu ngati

pamaliro, tsiku lina zimadzamugwera ndipo

amadzafuna chithandizo cha ena.

Miyambi ya Patsokwe

54

Chenjerechenjere samapha nsomba,

amapha nsomba n’kombe.

-Kuyankhula kwambiri pantchito

sikusonyeza kuchenjera. Sikutanthauza kuti

ntchito ikugwiridwa, koma kugwira ntchito

n’kumene kumayendetsa ndime.

Chenjerechenjere, anapsa ndi phala

logona.

-Kusamva kapena kuchenjeretsa

kumabweretsa mavuto aakulu.

Chete n’kunena (kukhala chete n’kunena).

-Pa mlandu munthu akafunsidwa koma

osayankha, ndiye kuti akuvomera kulakwa

kwake.

Chetechete ndi upumbwa, akoma ndi

suyosuyo.

-Tisamazengereze pogwira ntchito, koma

kungogwiriratu popeza zamawa sizidziwika.

Miyambi ya Patsokwe

55

Chetechete sautsa nyama, autsa nyama

n’kuwani.

-Ngati munthu wakasuma kukhoti,

uyeneranso kulongosola tsatanetsatane wa

nkhani. Ngati sutero, mlanduwo ukhoza

kukuvuta.

Chetechete sautsa nyama, autsa nyama

ndi suyo suyo.

-Kungokhala chete sikuthandiza ngati

munthu ukufuna kukwaniritsa chinachake.

Chetechete sautsa nyama, koma suyosuyo.

-Kungokhala pamene mukuona zinthu

zikulakwika sikuthandiza, koma kuyankhula

kuti zinthu zikonzedwe.

Chibale cha nkhondo, amawo akafa

n’kumva ndiika nawo.

-Mawuwa amanena za munthu amene si

m’bale wako weniweni, koma chifukwa choti

makolo anakhalira limodzi nthawi yaitali,

Miyambi ya Patsokwe

56

amakhala ngati m’bale wako weniweni.

Chibale n’chipsela.

-Chibale sichitha.

Chibale n’chipsera, sichitha.

-Sitingathe kuthetsa ubale, zivute zitani.

Chibale n’kuyenderana.

-Kuti chibale chilimbe pamafunika

kuyenderana komanso kuthandizana.

Chibale ndi fupa, sichiwola.

-Pangakhalitse abale osaonana, sikuti chibale

chimatha.

Chibale ndi fupa.

-Chibale sichitha.

Chibale ndi litsiro, sichisansika.

-Chibale sichitha, abale amatha kuoneka

ngati adana koma amadzagwirizana.

Miyambi ya Patsokwe

57

Chibale pamowa.

-Anthu amene amakhala mabwenzi

zikamayenda, koma pamavuto amakuthawa.

Chibangiri chimapita ndi mwini dzanja.

-Sungakakamize munthu kuchita zimene

sakufuna.

Chibwana chidatayitsa nguwo ya njuzi.

-Chifukwa cha chibwana, anthu amataya

mwayi mwina wa banja kapena ntchito.

Chibwana ndi chironda.

-Mwana sachedwa kuvulala chifukwa alibe

mantha. Ndiye munthu wachibwana, kapena

wosalemekeza akuluakulu amapeza mavuto.

Chibwenzi cha bulangete chopitira limodzi

kumanda.

-Umenewu ndi ubwenzi weniweni, wopanda

chinyengo.

Miyambi ya Patsokwe

58

Chibwenzi cha mphaka chobisa zala

m’thumba.

-Pali anthu ena omwe amaoneka ngati

abwenzi pamaso koma kumbali

amakuganizira zoipa.

Chibwenzi cha nkhwangwa chikoma

pokwera.

-Pali anthu ena omwe amakonda anzawo

akaona kuti akhoza kuwathandiza,

akangopeza zimene amafuna ubwenzi

umathera pomwepo.

Chibwenzi cha nkhwangwa chokoma

pokwera, potsika achita kuponya.

-Munthu akamakwera mumtengo

amanyamula bwinobwino nkhwangwa koma

akamatsika amangoiponya. Mawuwa

amanenedwa munthu akamanyoza anzake

chifukwa choti zimene umafuna zatheka.

Munthu ameneyo amamuti wachita,

Miyambi ya Patsokwe

59

“chibwenzi cha nkhwangwa chokoma

pokwera.”

Chibwenzi n’kuwonjezera.

-Kupatsana mphatso n’kumene

kumalimbitsa ubwenzi.

Chibwenzi sichipherana makoswe.

-Ubwenzi weniweni ulibe chinyengo. Chomwe

wamuuza kapena wam’lonjeza mnzako

chimakhala chomwecho.

Chibwereza chidaphetsa kunda.

-Munthu ukamachita chinthu choipa

n’kupulumuka, tsiku lina ukamadzati

uchitenso anthu amadzakugwira. Ngati

munthu wapulumuka pa vuto mwamwayi, si

bwino kubwereza kuchitanso zomwezo.

Chidakwa chinakana kulipira ngongole ya

thobwa.

-Si bwino kumangonamizira anthu amene

Miyambi ya Patsokwe

60

tikuwaona kuti ndi zitsiru kapena opepera.

Chidamlendo mbombo.

-Munthu woti akakhala ndi chakudya

sakonda kugawira anthu ena.

Chidede kukanika chitayang’anana.

-Ndi bwino kumayesetsa kuchita khama

pochita zinthu. Zichite kukanika zokha.

Chidule chimapondetsa matope.

-Zinthu zochitika mofulumira kapena

mwachidule sizichitika bwino.

Chidule chinagwetsa njati m’mbuna.

-Si bwino kuthamangira kapena kuchita

zinthu usakudziwa ndondomeko kapena

dongosolo lake chifukwa zimenezo zikhoza

kukubweretsera mavuto.

Chidwi chinapha mkonzi.

-Ukakhala munthu wachidwi ndi wofuna

kudziwa chilichonse, tsiku lina umadzakhala

Miyambi ya Patsokwe

61

mboni pa mlandu woopsa, mwina ukhozanso

kupeza nazo mavuto.

Chidziwa mwini m’khuto wa fulu.

-N’kovuta kudziwa zomwe munthu akuganiza

mumtima. Ena akhoza kuoneka ngati

sakuganiza chilichonse koma akuganiza

zambiri. Munthu aliyense amadziwa yekha

zinthu zimene angakhutire nazo.

Chidziwe n’chipande powomola.

-Aliyense amakolola malinga ndi khama lake.

Munthu akadyeratu kapena akamachita

ulesi, amalandira zochepa.

Chifuko sakumbira.

-Chibale chenicheni sichisowa.

Chifulumizo chokoma ukalasa.

-Tiziganiza mofatsa tisanayankhe chifukwa

tikhoza kuyankhula zopanda pake. Komanso

munthu umakamba mosangalala ukamachita

Miyambi ya Patsokwe

62

zinthu zabwino.

Chifundo chidaphetsa msemamitondo.

-Chifundo nthawi zina chimapweteketsa.

Nkhani yake imati, nthawi ina alenje

anavumbulutsa gondwa ndipo anayamba

kumuthamangitsa. Alenjewo

anamupezeketsa gondwayo moti anangotsala

pang’ono kumugwira. Gondwayo anayesetsa

kukoka phazi koma sizinam’thandize moti

anaganiza zopempha thandizo kwa munthu

wina yemwe ankasema mitondo

m’nkhalangomo. Atatoperatu, gondwayo

anapempha wosema mitondoyo kuti,

“Ndithandizeni chonde ndagwira mwendo

wanu. Alenjewa akufuna moyo wanga,

chonde ndipulumutseni!” Wosema mitondoyo

anamva chisoni kwambiri ndipo anauza

Gondwayo kuti amubisa. Koma popeza

panalibe malo pafupi pomwe

Miyambi ya Patsokwe

63

akanamubisapo, wosema mitondoyo

anangoganiza zomubisa m’kamwa. Alenjewo

atafika anafunsa wosema mitondoyo kuti,

“Mwaona Gondwa atadutsa apa?” Koma

wosema mitondoyo anapukusa mutu

posonyeza kuti sanamuone. Ndiyeno alenjewo

atachoka, munthuyo anauza Gondwa uja

kuti, “Alenje ajatu apita, ukhoza kutuluka

tsopano!” Koma gondwayo anayankha kuti,

“Tadikirani kaye pang’ono, muli kenakake

kokoma muno!”

Chifundo chidaumitsa mvunguti.

-Tiyenera kuona muyeso woyenera pochitira

ena chifundo. Ukachitira ena chifundo

mopitirira muyeso, ukhoza kuwononga

ntchito ngakhalenso moyo wako umene.

Chifundo chili m’manja.

-Mawuwa amanenedwa pofuna kuonetsa kuti

umafunitsitsa utakumana ndi mnzako

Miyambi ya Patsokwe

64

n’kumupatsa moni.

Chifundo chimaitana chifundo.

-Munthu ukamachitira ena chifundo, tsiku

lina nawonso amadzakuchitira chifundo.

Chiimba chili m’mimba.

-Kudya n’kumene kumathandiza munthu

kuti agwire ntchito.

Chikachita mang’a chileke, mawa

chituluka.

-Munthu akamakana kuti sanalakwe,

kungomusiya, tsiku lina choipa chake

chidzamutsata ndipo zoipa zake zidzaululika.

Chikadzakula, sichidzasowa.

-Mawuwa amanenedwa potanthauza kuti

khalidwe loipa likadzafika poipa,

sipadzakhala wodabwa.

Chikaipa usataye.

-Ngati chinthu chikuoneka chopanda ntchito,

Miyambi ya Patsokwe

65

usachitaye chifukwa tsiku lina chikhoza

kudzakhala chofunika.

Chikakhala pamuvi sichipheka.

-Mawuwa amanena za munthu amene

akulephera kugamula mlandu chifukwa choti

ndi wa m’bale wake.

Chikakuluma chakuda umaopa ndi khala

lomwe.

-Munthu wina akakupusitsa, sukhulupirira

aliyense.

Chikaona mnzako osamaseka.

-Mnzako akaona tsoka usamamuseke

chifukwa mwina mawa udzaonanso zomwezo.

Chikaonda chimakoma ndi mchere.

-Chinthu chingakhale choipa maka, koma

powonjezera tina n’tina tokometsera,

chinthucho chimakhalanso chokongola.

Chimodzimodzi mkazi amaoneka bwino ndi

Miyambi ya Patsokwe

66

kuvala.

Chikaonekera ng’amba, mawa chituluka.

-Mbewu ikamamera imayamba yatukula

dothi kenako n’kuonekera. Zinthu zina

zikamaoneka pamakhala pataoneka kale

zizindikiro zake.

Chidebe chopanda kanthu n’chimene

chimasokosa kwambiri.

-Anthu opanda nzeru ndi amene amakhala

olongolola kwambiri.

Chikomekome cha mkuyu, m’kati muli

nyerere.

-Osamatengeka ndi maonekedwe a munthu

chifukwa nthawi zina mumtima mumakhala

moipa. Nthawi zambiri anthu okongola ndi

amene amakhala a makhalidwe oipa.

Chikondi cha “chotsa phazi mpondepo.”

-Chimenechi ndi chikondi chenicheni

Miyambi ya Patsokwe

67

chochitira zinthu limodzi.

Chikondi cha bulangete chopitira limodzi

kumanda.

-Chikondi chopanda chinyengo komanso

dyera, chokhalira limodzi pamavuto ndi

pamtendere pomwe.

Chikondi cha chotsa phazi m’pondepo.

-Chikondi chodalirika kapena chokondana

kuchokera pansi pa mtima.

Chikondi cha mphaka, chobisa zala

m’thumba.

-Chikondi chobisilana cholinga chako

chenicheni. Chikondi chachinyengo.

Chikondi chili m’manja.

-Mawuwa amanenedwa pofuna kuonetsa kuti

umafunitsitsa utakumana ndi mnzako

n’kumupatsa moni.

Miyambi ya Patsokwe

68

Chikondi ndi kutherana zakukhosi.

-Chizindikiro cha chikondi chenicheni ndi

kuululirana zakukhosi, osati kusungirana

chakukhosi.

Chikumbumtima chinapha njovu.

-Tikachita choipa chikumbumtima, chomwe

ndi munthu wam’kati, chimatiimba mlandu

ndipo timasowa mtendere. Chikumbumtima

chikhoza kumakupwetekabe ngakhale

utafunda mabulangete ambirimbiri. Ndi

bwino kumavomereza tikalakwitsa ndi

kupempha kuti atikhululukire. Nkhani yake

imati, tsiku lina njovu inatenga katundu wa

mwini wake. Ndiye kalulu ataifunsa inakana

kuti sinatenge. Kenako kalulu anauza

njovuyo kuti, “Ngati mwatengadi ndi inuyo

n’kumakana, chikumbumtima chikuphani.”

Njovu inayamba kuchita mantha kwambiri

chifukwa inkaganiza kuti chikumbumtima

Miyambi ya Patsokwe

69

ndi nyama ina yaikulu kwambiri kuposa

iyoyo. Njovuyo inasiya kutuluka panja kuti

ikasake zakudya mpaka inaonda kwambiri.

Inkaopa kuti ikumana ndi chikumbumtima.

Kenako njovuyo inafa ndi njala. Phunziro

lake ndi lakuti ndi bwino kumavomera

ukalakwitsa, chifukwa ukapanda kutero

umavutika ndi chikumbumtima.

Chikumbutsa nkhwangwa n’chikuni.

-Ngakhale tiiwale kanthu kena kapena

kuchita mphwayi kugwira ntchito inayake,

tsiku lina pamadzakhala china

chotikumbutsa chomwe tinaiwala. Nthawi

zina mavuto amatichititsa kugwira ntchito

molimbika komanso kugwira ntchito zomwe

tinkaziona ngati zopanda pake.

Chikumbutsa nkhwangwa n’chisanu.

-Ngakhale tiiwale kanthu kena kapena

kuchita mphwayi kugwira ntchito inayake,

Miyambi ya Patsokwe

70

tsiku lina pamadzakhala china

chotikumbutsa chomwe tinaiwala. Nthawi

zina mavuto amatichititsa kugwira ntchito

molimbika komanso kugwira ntchito zomwe

tinkaziona ngati zopanda pake.

Chikuni cha m’bwalo chikoma

n’kugwirizana.

-Kuthandizana n’kofunika kwambiri m’malo

momadzipatula.

Chikuni cha utsi timafumula.

-Pakakhala munthu wosokoneza pamudzi

kapena pantchito pamafunika kumulangiratu

kuopa kuti angasocheretse ena.

Chikuni chimodzi sichipsetsa mphika.

-Kuti ntchito iyende pamafunika

kuthandizana.

Chikuni pakutha, chimataya therere.

-Nthawi zambiri ntchito imaonongeka

Miyambi ya Patsokwe

71

kumapeto. Ndi bwino kumasamala pogwira

ntchito mpaka kumapeto.

Chilekwa (wamasiye) n’chosakhala

kupatira chabwino.

-Nthawi zina mwana wamasiye amatha

kupeza msanga chithandizo. Zinthu

zonyozeka zingathe kutipatsa zabwino.

Chilendo ndi kulumpha chiunda.

-Munthu ukangotuluka m’nyumba mwako

kwina konse umakhala mlendo.

Chili kumunda n’chambewu, chakumudzi

n’chakudya.

-Tizisunga zina kuti tidzagwiritse ntchito

m’tsogolo.

Chili kumwamba ndi chamwini.

-Si bwino kukhumbira zinthu za eni kapena

zinthu zomwe tikudziwa kuti sitingathe

kuzipeza.

Miyambi ya Patsokwe

72

Chili kwa mnzako n’kumati, “chigwire

nyanga.”

-Sizivuta kupeza zolakwa za mnzako n’kusiya

zako kapena kuuza ena zoti achite koma zoti

iweyo sungakwanitse. Osamaderera mavuto a

mnzako.

Chili kwa mnzako ndiye “psinyitsa,” chili

kwa iwe ndiye, “psinya bwino.”

-Mnzathu akalakwa ndiye timafuna kuti

alandire chilango chowawa, koma zikakhala

kwa ife, timafuna kuti atimvere chisoni

potipatsa chilango chofewa.

Chili kwa mnzako umati “chigwire

nyanga!”

-Munthu amaona vuto la mnzake ngati si

vuto ayi, koma vuto ngati lomwelo

likamuonekera m’pamene amaliwona kuti ndi

phiri.

Miyambi ya Patsokwe

73

Chili kwa mnzako, utenga madzi numwera.

-Mavuto akakhala kwa ena kumakhala

kosavuta kuwalangiza zomwe anachita kuti

apeze mavutowo, koma zikatigwera sititha

kumvetsa chomwe chachititsa mavutowo.

Chili kwa nyani, pusi sachitengera

malonda.

-Nthawi zambiri pakati pa abale sipakhala

kugulitsana zinthu koma kungopatsana basi.

Chili n’kudza chisonkha moto paphale,

chipala (phulusa) chitaya kuthengo.

-Mawuwa amanenedwa munthu akamanena

kuti alipo wina womuposa amene akubwera.

Chilichonse chili ndi nthawi yake.

-Ndi bwino kumachita zinthu pa nthawi yake.

Kumadziwa nthawi yabwino yochita

chilichonse monga kuyankhula kapena

kukhala chete.

Miyambi ya Patsokwe

74

Chilichonse chotentha, pamapeto pake

chimazizira.

-Munthu wina atatopa kulumidwa ndi

Nsikidzi, anaganiza zotereka madzi kuti

azikhaulitse. Kenako anatenga bulangete

lakelo n’kuliika munkhali n’kutenga madzi

obwadamuka n’kuwakhuthulira momwe

munali bulangetelo kuti nsikidzizo zikhaule.

Ndiye zimenezi zitangochitika, Nsikidzi

yomwe inali m’bulangetemo inauza ana ake

kuti, “Ana anga, muyenera kukhala opirira,

chifukwa chilichonse chotentha, pamapeto

pake chimazizira. Vuto lingatenthe bwanji,

limakhala ndi mapeto ake.” Mavuto angakule

bwanji, amakhala ndi polekezera.

Chilimwe chinaphetsa munda.

-Munthu wofuna zabwino asamathawe

zopinga monga kuuma komanso kulimba

kwa dothi, amafunika kupirira.

Miyambi ya Patsokwe

75

Chilimwe, ndipatse munda.

-Munthu akafuna kuti adzapeze zabwino

m’tsogolo amafunika kukonzekera.

Chiloli chinapha ngondo.

-Ukakhala munthu wachidwi ndi wofuna

kudziwa chilichonse, tsiku lina umadzakhala

mboni pa mlandu woopsa, mwina n’kupeza

mavuto.

Chilosi chidabwerera lunguzi.

-Mukanyoza munthu osam’patsa moni

chifukwa choti ndi mlendo, tsiku lina

mumadzakam’peza kwawo n’kuchita

manyazi.

Chilungamo chiziyenda ngati madzi.

-Chilungamo chimafunika chioneke.

Tikamachita zinthu zonse, tiyenera

kumaonetsetsa kuti tikuchita zinthu

mwachilungamo kwa aliyense mosatengera

maonekedwe.

Miyambi ya Patsokwe

76

Chilungamo n’chipongwe.

-Nthawi zina anthu amadana ndi kumva

chilungamo chifukwa chimamveka ngati

chipongwe.

Chim’mawa chidalambalalitsa fulu bowa.

-Tizichita zinthu mofatsira ndi mwaluso osati

mongofulumira, chifukwa tikamatero tikhoza

kuiwala zinthu zofunika.

Chimanga cha palikodza amakolola ndi

Sakhwi.

-Ndi bwino kumadziwa zinthu zomwe

sungakwanitse. Pali zinthu zina zomwe ngati

utazikakamira kwambiri zikhoza

kungokubweretsera mavuto ngati chimanga

chomwe chili palikodza, lomwe ndi tchire

loyabwa kwambiri. Ndi bwino kusiyira

Asakhwi zinthu zimenezo.

Chimanga chimalola opanda mano.

-Nthawi zina munthu umapeza chinthu choti

Miyambi ya Patsokwe

77

ulibe nacho ntchito pamene munthu wina

akuchifunitsitsa.

Chimasomaso chinakwatitsa mkazi

wosam’funa.

-Mnyamata wosakhala ndi mkazi m’modzi

koma kumangoti apa wagwira apa wagwira,

mapeto ake amadzakwatira mkazi wosakhala

wakumtima kwake, mwinanso kupeza

mavuto.

Chimene chakupundula chitsate,

chikupatsa khongozo.

-Munthu uyenera kudyerera chomwe

wavutikira.

Chimene ukufuna kuti ena akuchitire,

iwenso uziwachitira chomwecho.

-Kuti tizichitira ena zabwino, ndi bwino

kumayamba taganiza kaye kuti, “Kodi wina

atandichitira zimenezi ndingasangalale?”

Ngati tikuona kuti sitingasangalale,

Miyambi ya Patsokwe

78

tingachite bwino osazichita.

Chimkonda cha nsikidzi chidanka ndi

maliro kumanda.

-Osamakonda zinthu zoipa monga

chiwerewere, mowa kapena chamba chifukwa

mapeto ake ndi imfa.

Chimkwangukwangu chisititsa makadabo.

-Kulimbirana zinthu kukhoza kuyambitsa

ndewu kapenanso mkangano

n’kuwonongetsa zinthu zambiri.

Chimuyesoyeso cha Khwangwala

chinathetsa ana.

-Si bwino kuyesa kuchita zinthu zoipa monga

kusuta chamba chifukwa mapeto ake

chimadzakhala chizolowezi n’kudziwononga

tokha.

Chimvano cha mavu choning’a pakati.

-Ndi bwino kumachita zinthu mogwirizana.

Miyambi ya Patsokwe

79

Ngakhale kuti pangano limavuta kusunga

nthawi zina, komabe tiziyesetsa kusunga

zomwe tagwirizana popewa kukhumudwitsa

ena.

China n’china Fisi alibe bwenzi, bwenzi

lake ndi mdima.

-Anthu ochita zoipa sakhala mabwenzi

abwino, mabwenzi awonso amakhala ochita

zoipa.

Chinansi cha kholowa chinadyetsa

mbatata yapansi.

-Zinthu zina zimaululika chifukwa cha

zinanso zimene zachitika. Makhalidwe oipa

monga chiwerewere ndi kuba amayamba

pang’onopang’ono. Pamafunika kudziletsa

kuchita zinthu zomwe mapeto ake akhoza

kukhala kuchimwa kwakukulu.

Chinasala chinakanika Fisi.

-Chinasala ndi chisilamu. Anthu achisilamu

Miyambi ya Patsokwe

80

amasala nyama zina. Koma Fisi ndi

wankhwiru kwambiri moti sangakwanitse

kusiya kudya nyama ngakhale itakhala

kapado. Pali zinthu zina zimene

sitingakwanitse kuzisintha chifukwa cha

chibadwa chathu. Choncho, munthu ayenera

kumadziwa zomwe angathe kuchita komanso

zomwe sangathe.

Chinenepetsa Nkhumba sichidziwika.

-Ndi bwino kumangoyesa kuchita

zosiyanasiyana, chifukwa chimene

chingakupulumutse sichidziwika.

Osamangodalira chimodzi.

Chingaipe sunga, mkucha udzayesa

ankhoswe.

-Chinthu chingaipe, tsiku lina umadzaona

pokomera pake.

Chingavuwe n’chako.

-Ngakhale anzathu kapena makolo athu

Miyambi ya Patsokwe

81

akhale osaoneka bwino, ndi anthu basi.

Choncho, tifunika kumawasamalira komanso

kuwapirira.

Chingwe ndicho chithera msampha

mphamvu.

-Tikamangomvera nkhani zabodza za anthu

ena tingadziputire mlandu. Zikhoza

kutitsatira n’kupeza nazo mavuto.

Chingwinjiri maliralira, chinalira m’msolo

wa mbala.

-Munthu ukakhala wapakamwa,

umadzanena zinthu zina kwa ena omwe

amafuna kudziwa zimenezo ndipo umapeza

mavuto.

Chinsanjesanje chinaoletsa mazira a

mpheta.

-Munthu wansanje amachedwa ndi kufufuza

mkazi kapena mwamuna wake, potero

amadziwitsa ena za khalidwe la mwamuna

Miyambi ya Patsokwe

82

kapena mkazi wakeyo n’kudziwonongera

banja.

Chinsisi sichikhala pa anthu awiri.

-Ukauza mnzako nkhani yachinsisi

n’kumukhulupirira, umakhala ukudzinamiza

chifukwa nayenso amakhala ndi anzake ena

apamtima.

Chinthu chikataika chimalira mwini wake,

monganso mwini wake ali kuchilira.

-Ngati tatola chinthu chamwini tiyenera

kuchibweza kuopera kuti chingatisowetse

mtendere mumtima popeza timaoneka ngati

tachiba.

Chinthu ndi mtima, kanthu ndi khama.

-Pamene waikapo mtima wako, uyenera

kuchita khama kuti chinthucho chitheke.

Chinziri chimanyang’wa ndi tsala lake

(lakwawo).

Miyambi ya Patsokwe

83

-Munthu aliyense amanyadira zinthu zake

monga zovala, ntchito ndiponso banja lake.

Chipande cha therere chimakoma

n’kuyenderana.

-Kuti mnzako akuchitire zabwino pafunika

kumubwezera zabwino. Choncho, kuti anthu

muthandizane pamafunika pakhale ubale

weniweni pakati panu.

Chipande chomwe umawomorera mnzako,

nawe adzakuwomorera chomwecho.

-Ngati ukufuna kuti anzako azikuchitira

chifundo, yamba ndi iweyo kuwachitira.

Chipititsira m’ngunda.

-Mwambiwu umagwiritsidwa ntchito pamene

munthu wanena dala zosagwirizana ndi

nkhani kuti asokoneze anthu, makamaka pa

mlandu.

Miyambi ya Patsokwe

84

Chipungu sataya nthenga.

-Mawuwa amanena za munthu waumbombo

yemwe safuna kugawira anzake zinthu.

Chipwete mpamtsitsi.

-Chipwete chimakhala chaminga kuchokera

ku mbewu. Chimodzimodzinso khalidwe la

munthu limachokera kwa makolo.

Chirombo chinafera m’dambo la kamundi.

-Chifukwa cha nsanje anthu ena amafuna

kutchuka pantchito za eni mwina chifukwa

choti anamwalira, komabe anthu

amawadziwa ndipo mapeto ake amaputa

nazo mlandu.

Chisakomere Mbuzi kugunda Galu, Galu

akaluma ati ndi woipa!

-Pali anthu ena omwe amakonda kuchitira

anzawo zinazake, anzawowo akawachitira

zangati zomwezo amaona kuti awalakwira

kwabasi.

Miyambi ya Patsokwe

85

Chisanakondwe chilonda njira,

chikakondwa chachenjera.

-Zotigwera zina zimatikumbutsa nsanga

kumudzi koma pa zosangalatsa timachita

ngati taiwalako.

Chisoni chinapha Nkhwali.

-Nthawi zina chisoni chikhoza

kukubweretsera mavuto. Nkhani yake imati,

kalekalelo Njoka inkafuna kuwoloka mtsinje

wina. Ndiye popeza palibe chimene

ikanachita kuti iwoloke yokha, inapempha

Nkhwali kuti aithandize. Nkhwaliyo inamva

chisoni zedi ndi mmene Njokayo inkaonekera

ndipo inavomera kuti ichitadi zimene Njokayo

inkafuna. Inauza Njokayo kuti, “Zizengereze

m’khosi mwangamu!” Kenako inanyamuka

n’kuuluka. Itafika kutsidya, Nkhwaliyo

inauza Njokayo kuti, “Bwanawe, tafikatu.

Tsopano ukhoza kutsika kuti uzipita.” Koma

Miyambi ya Patsokwe

86

Njokayo inakana kwamtuwagalu kuti

sichoka. Pamapeto pake, chisoni chinachitsa

kuti Nkhwali ione tsoka la nkhuku.

Chisoni chinapha nsemamitondo.

-Munthu amene umamuthandiza poganizira

kuti akusowa thandizo ndi amene

amadzakuukira, mwinanso ngakhale

kukupha kumene.

Chisoni n’kumatenda, kumaliro

kumakhala nkhani.

-Pamene munthu akudwala anthu amakhala

ndi chisoni, koma akamwalira, chisoni

chonse chimatha popeza amadziwa kuti

palibenso chimene angachite. Mwina ena

amayamba kukamba mbiri ya womwalirayo,

zabwino kapena zoipa.

Chiswe chikaboola chikwa, chayambira

patali.

-Munthu ukakhala ndi cholinga n’kuchita

Miyambi ya Patsokwe

87

khama, umapeza zimene ukufuna.

Ungatanthauzenso kuti vuto likamaonekera

ndiye kuti layambira patali.

Chiswe chimalowa m’mphasa yongoimika.

-Munthu waulesi amakumana ndi zovuta

zambiri.

Chiswe chimodzi sichiumba chulu.

-Ngati titamathandizana tikhoza kugwira

bwino ntchito zathu mpaka kumapeto.

Chithupsa chosatumbula sichigonetsa

tulo.

-Munthu ukapalamula kapena ukakhala ndi

mlandu, mtima sukhala pansi, umada

nkhawa mpaka mlandu utakambidwa.

Chitoletole chidaphetsa manja.

-Munthu wakuba tsiku lina amadzapezana

ndi tsoka monga kudulidwa manja.

Miyambi ya Patsokwe

88

Chitosi cha nkhuku yachilendo

chimatalika.

-Mlendo akafika pamudzi n’kulakwa,

kulakwa kwake kumaonekera kwambiri

ngakhale kuti nawonso eni mudzi amalakwa

mwina kuposa mlendoyo.

Chitsa chagwede chinagwetsa nkhalamba.

-Kulakwa kwa ana kukhoza kusowetsa

mtendere munthu wamkulu. Zochita za ana

zimavutitsa akulu.

Chitsime chakele chimaphetsa ndi ludzu.

-Osamanyoza zinthu kapena anzathu akale

chifukwa tsiku lina tidzawafunanso. Choncho

ngati timawanyoza sadzatilandira.

Mwambiwu ungatanthauzenso kuti tikasiya

kuchita zoipa tifunika kuchita khama kuti

tisabwererenso ku zochita zoipazo.

Miyambi ya Patsokwe

89

Chitsime chimadziwika kuti ndi chakuya

chikauma.

-Munthu wabwino amadziwika akapita.

Mwachitsanzo, ena amazindikira kuti mkazi

kapena mwamuna wawo anali wabwino banja

likatha. Nthawi zambiri amazindikira

zimenezi akakwatirana ndi chilombo.

Chitsiru chimafa ndi ludzu mwendo uli

m’madzi.

-Pali anthu ena omwe amavutika zinthu zoti

zikhoza kuwathandiza zili m’nkhonde.

Mwachitsanzo, kumavutika ndi njala dimba

ali nalo.

Chitsiru chinaomba ng’oma, ochenjera

navina.

-Nthawi zina anthu ooneka ngati opusa ndi

ofooka amatha kuchita zodabwitsa motero

kuti anthu odziyesa ochenjera n’kutengerapo

phunziro.

Miyambi ya Patsokwe

90

Chitsiru chinaona nkhondo.

-Si bwino kunyoza munthu chifukwa santha

kuchita zinthu zina. Nayenso akhoza kukhala

ndi mbali ina yomwe amachita bwino.

Chitsiru nachonso chili ndi amake.

-Ana kapena ziweto zimadziwa makolo

komanso mbuye wawo. Munthu sulephera

kuzindikira chinthu chako.

Chitsulo chimanola chitsulo chinzake.

-Anthu ochita zofanana amathandizana. Kuti

munthu akhale ndi luso amayenera

kumatengera anzake.

Chitukuko ndi kupirira.

-Kuti atsikana kapena azimayi atchene, kaya

ndi m’mutu, amafunika kupirira ululu.

Mwachitsanzo, ena amapsa ndi livuloni koma

samasiya.

Miyambi ya Patsokwe

91

Chiwindi cha Nkhandwe chalaka mwini

msampha.

-Chomwe chakanika munthu wakale kapena

wanzeru, mwana sangachithe.

Chiyipira achaje, amake amati mwana.

-Ngakhale anthu ena atamanyoza munthu

chifukwa cha maonekedwe kapena khalidwe

lake, makolo ake ndi abale ake

amamukonda, sangamutaye kapena

kumunyoza.

Chizolowezi cha namkholowa chidaululitsa

mbatata.

-Si bwino kuchita khalidwe loipa chifukwa

likhoza kukubweretsera mavuto.

Chizolowezi cha namkholowa chidazulitsa

mbatata yapansi.

-Zinthu zina zimaululika chifukwa cha

zinanso zimene zachitika. Makhalidwe oipa

monga chiwerewere ndi kuba amayamba

Miyambi ya Patsokwe

92

pang’onopang’ono. Pamafunika kudziletsa

kuti usachite zinthu zomwe mapeto ake

akhoza kukhala kuchimwa kwakukulu.

Chizolowezi chidadya mzuzya.

-Zotsatira za zizolowezi zoipa ndi mavuto

monga matenda, milandu komanso imfa.

Chizolowezi chinalowetsa nsabwe kumutu.

-Ukamacheza ndi anthu ochita zoipa

nawenso umayamba kuchita zoipa.

Choipa chitani mbiri siigonera.

-Mbiri imamveka msanga. Ngakhale

utayesetsa kuimphimba anthu amamva.

Koma sipapita nthawi amayamba kuiwala.

Choipa chitsata mwini.

-Palibe munthu amene angachite choipa

n’kuthawa, tsiku lina ndithu amadzakumana

ndi zotsatira za zoipa zimene anachitazo.

Miyambi ya Patsokwe

93

Choipa ndi mnyanga ya njovu.

-Munthu ukhoza kumachita zoipa

n’kumaganiza kuti sichidzaululuka. Koma

monga mnyanga ya njovu sitheka kuibisa,

choipacho tsiku lina chimadzaululika ndipo

munthu umadzalangidwa.

Choka m’mbuyo Khwangwala atole

mphutsi.

-Umafunika kupereka mpata kwa anzako

kuti akhale omasuka pang’ono.

Osamatsekereza mwayi wa ena.

Cholira Njovu chidalira minyanga.

-Aliyense ali ndi ufulu wogwira ntchito imene

akufuna popanda kukakamizidwa.

Chonona chifumira ku dzira.

-Maonekedwe ndi makhalidwe a munthu

amakhala ochokera kwa makolo ake.

Miyambi ya Patsokwe

94

Choopera patali, nyani anadzipha yekha.

-Si bwino kumangoopera chinthu patali.

Chosadziwa anausa mvula m’dziwe.

-Nthawi zina tikhoza kumaganiza kuti

tikuthawa mavuto n’kudzilowetsa m’mavuto

aakulu mmalo mongopirira n’kuyesa

kuthetsa vutolo. Mwachitsanzo, munthu

amene wadzimangirira amati akuthawa

mavuto.

Chosadziwa ndi nkhondo, adausa nkhondo

padziwe.

-Nthawi zina tikhoza kumaganiza kuti

tikuthawa mavuto n’kudzilowetsa m’mavuto

aakulu mmalo mongopirira n’kuyesa

kuthetsa vutolo. Mwachitsanzo, munthu

amene wadzimangirira amati akuthawa

mavuto.

Chosamva adachiphikira m’masamba.

-Anthu amene samvera malangizo

Miyambi ya Patsokwe

95

amakumana ndi zokhoma kapena kufa

kumene. Wina akakulangiza pamafunika

kumvera.

Chosatha n’chiyani?

-Chilichonse chimatha pakapita nthawi.

Chotola salanda.

-Kutola kanthu si kuba, koma ukatenga

pakhomo pa munthu osapempha.

Chozemba chinakumana ndi chokwawa.

-N’kovuta kuthawa mavuto kapena milandu

chifukwa nthawi zina pothawapo

umakumana ndi vuto lina lalikulu. Nthawi

zina munthu amazemba, koma tsiku lina

amadzagwidwa.

Chozemba chinalinda kwawukwawu.

-N’kovuta kuthawa mavuto kapena milandu

pamoyo wamunthu chifukwa nthawi zina

pathawapo umakumana ndi vuto lina

Miyambi ya Patsokwe

96

lalikulu.

Chozingwa sichilira nkhata.

-Tikakhala pamavuto pafunika kuyamba

kudzithandiza tokha osamangoyembekezera

kuthandizidwa ndi ena. Tikadzithandiza

tokha enanso adzatha kutithandiza.

Chule anadabwa m’madzi muli mwake.

-Pali zinthu zina zomwe zimachita

kuonekeratu kuti sizimakhala choncho.

Chule anadabwa madzi atafika m’khosi.

-Mawuwa amanenedwa munthu

akamadabwa ndi zinthu zomwe zimayenera

kuchitika pamoyo wathu.

Chule wodzikuza adaphulika.

-Sibwino kumadzikuza chifukwa umatha

kudzichititsa manyazi pagulu.

Miyambi ya Patsokwe

97

Chulu sichiyendera chiswe, chiswe

chimayendera chulu.

-Chithu ukachifuna umafunika uchite

chinthucho.

Chulukechuluke n’ngwa njuchi, umanena

za iyo yakuluma.

-Pokamba nkhani pafunika kunena zenizeni

m’malo momangozungulirazungulira.

Mwambiwu umanenedwanso pakakhala

anthu ambiri amene akuganiziridwa kuti

alakwa, koma pamapeto pake amapezeka

m’modzi. Ungatanthauzenso kuti chinthu

chimene chimakuchititsa chidwi ndi chimene

ukuchidziwa bwino. Ngakhale patakhala

zinthu zochuluka, umanena za chimene

chakuchititsa chidwi.

Chulukechuluke ngwa chambo, doko n’la

ntchira (kambuzi).

-Ngakhale ogwira ntchito akhale ambiri,

Miyambi ya Patsokwe

98

komabe, eni ntchito kapenanso amene

akugwira molimbika amadziwika.

Chulukechuluke ngwa njuchi, umaloza

yomwe yakuluma.

-Pokamba nkhani pafunika kunena zenizeni

m’malo momangozungulirazungulira.

Mwambiwu umanenedwanso pakakhala

anthu ambiri amene akuganiziridwa kuti

alakwa, koma pamapeto pake amapezeka

m’modzi. Ungatanthauzenso kuti chimene

chakudolola n’chimene umachitchula

Ungatanthauzenso kuti chinthu chimene

chimakuchititsa chidwi ndi chimene

ukuchidziwa bwino. Ngakhale patakhala

zinthu zochuluka, umanena za chimene

chakuchititsa chidwi.

Chulutsa masamba, ungagwire nsete.

-Mwambiwu umanenedwa pouza munthu

kuti achulutse zonena kuti asagwidwe.

Miyambi ya Patsokwe

99

Chuma chili m’nthaka.

-Ukalimbikira kulima, udzapeza zofuna zako.

Chuma chimuka pa chuma chinzake.

-Anthu amene ali ndi chuma ndi amene

amapeza chuma china.

Chuma chothamangira chimapatsa

matsoka.

-Kususukira kulemera kungatipalasire moto.

Chuma ndi mchira wa khoswe, suchedwa

kupululuka.

-Chuma sichichedwa kutha ngati mmene

umachitira mchira wa khoswe. Ukaugwira,

umangopululuka. Ngati sukuchisamalira

bwino, chimatha chonse phu! Ukakhala

pabwino usamanyoze anzako chifukwa ndi

amene angadzakuthandize ukadzavutika.

Miyambi ya Patsokwe

100

D

Dala la mwana wankhuku lolira make ali

pomwepo.

-Anthu ena amangodandaulabe ngakhale

kuti ali nawo anthu owathandiza. Aliponso

ena amene amavutika koma njira yothetsera

mavuto awo akuidziwa.

Dala lidagoneka munda.

-Kulekerera kumawonongetsa zinthu. Ulesi si

wabwino mpang’ono pomwe.

Dama n’kumeta, mphini ndi chironda.

-Pofuna kuwonjezera kukongola kwa

chibadwa, nthawi zina timadziwononga

potsata njira zosayenera.

Dengu lidawombola mbiya.

-Ndi bwino kumathandizana. Aliyense ndi

wofunika pantchito yake.

Miyambi ya Patsokwe

101

Dengu silidya.

-Nsengwa, dengu kapena bwato

zimangosunga zinthu zimene mwaikamo,

sizimachepa kapena kuwonjezereka.

Tizikhutira ndi zimene tili nazo pamoyo

wathu.

Dikira madzi apite, kenako uziti ndadala.

-Munthu ukakhala pabwino usamati

ndadala, chifukwa ukhoza kukumana ndi

mavuto nthawi iliyonse.

Dingudingu amanena za mnzake, zake

wapsindira.

-Pali anthu ena omwe amakonda kunena

zoipa za anzawo n’kusiya zawo. Munthu

aliyense amayenera kumayamba waona kaye

zimene amachita asanayambe kunena za

anzake.

Diso la Nkhwazi.

-Maso a Nkhwazi ndi akuthwa kwambiri

Miyambi ya Patsokwe

102

omaona chinthu chili patali. Mawuwa

amanena za munthu amene amaona patali.

Diso likatuluka, ndi maliro.

-Maso a munthu akatuluka, ndiye kuti

munthu wamalizika.

Dombolo n’kuwombolana, nthengu

anaombola namfuko.

-Kuti anzako akuthandize pamafunika kuti

nawenso uziwathandiza,

osamangoyembekezera kuti anthu

akuthandize.

Dombolo n’kuwombolana.

-Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi

bwino kumuchitira zabwino. Zimakhala

bwino kumathandizana.

Dothi sinkadakudya, ndakudyera ku uchi.

-Nthawi zina umathandiza munthu osati

chifukwa choti umamukonda, koma chifukwa

Miyambi ya Patsokwe

103

choti umakondana ndi mnzake.

Dulani kachere pumbwa anyale.

-Anthu ena amanyada mwinanso kuzunza

anzawo chifukwa cha udindo, ndalama

kapenanso makolo awo. Zinthu zotere

zikatha, kuzunza ndi kunyada kumathera

pomwepo.

Dyera linapititsa Ntchentche kumanda.

-Kuchita zinthu mwadyera pa chilichonse,

ngakhale chabwino, kumatsekereza zabwino,

monga kukwezedwa pantchito.

Dyeratu, chakudza sichinena.

-Munthu ngati uli ndi chuma uyenera

kusangalala nacho chifukwa zamawa

sizidziwika.

Dzandioneni n’kukhala ndi zako.

-Osamadzitamira katundu wa eni ake koma

wako.

Miyambi ya Patsokwe

104

Dzanja limodzi silikumba mankhwala.

-Kuthandizana n’kofunika popeza pawekha

sungachite zinthu zambiri.

Dzedzeredzedzere (dzandidzandi) salingana

n’kugweratu.

-Kulephera sikutanthauza kuti

sungakwanitse kuchita chinthu. Kuti

munthu achite bwino amafunika kukumana

kaye ndi mavuto.

Dzenje la pida (pinji) limadziwika

n’kuunjika.

-Anthu akamapanda kukuyankhula kapena

kumangokhala ndi msunamo umadziwa kuti

pali nkhani.

Dzera uko sikuyenda, koma tiye kuno.

-Pophunzitsa ena ntchito kapena zinazake, si

bwino kungofotokoza chabe, tizionetsa

chitsanzo chabwino kuti malangizo athu

akhale aphindu.

Miyambi ya Patsokwe

105

Dziko la eni ndi mowa, ukaponda

waledzera.

-Munthu ukayenda umayenera kukumbukira

kuti ndiwe mlendo. Ukalakwitsa zabwino

zako zonse zimaiwalika.

Dziko lingagwe.

-Ukasiya ntchito yomwe munthu umagwira

n’kuyamba ina ndiye munthu

n’kumakufunsa: “Bwanji mutsirize kaye

ntchito yomwe munayamba kaleyi?”

Kuyankha kwake mokana umati: “Dziko

lingagwe.”

Dziko ndi mafuwa, achita kuchilikizana.

-Munthu aliyense ali ndi mbali yake kuti

zinthu ziyende bwino m’dziko kapena

m’mudzi.

Dziko ndi anthu, nyama ndi mambala.

-Anthu ndi amene amakometsa dziko.

Choncho, pafunika kuti anthu azigwirizana

Miyambi ya Patsokwe

106

kuti zinthu ziziyenda bwino pamudzi pawo.

Asamangokhala ngati nyama zomwe

zimadyana zokhazokha.

Dziko ndi mafuwa achita kuchinjiriza.

-Kuti dziko liyende bwino pamafunika anthu

ena oliteteza, ena odziwa zamalamulo

ndiponso ena olamulira. Osangoti mfumu

imodzi yokha ayi. Ngati zitakhala choncho

mtendere sungakhalepo.

Dziko ndi wanu, ndalama ndi wathu.

-Mawuwa amatanthauza kuti tinabwera kuno

kudzapanga ndalama. Amakonda

kugwiritsidwa ntchito ndi amwenye omwe

amapanga bizinezi.

Dziko silimaipa, amaipa ndi anthu.

-Tisamaganize kuti tikachoka pamudzi wina

n’kupita kwina chifukwa cha kukangana

ndiye kuti kukangana kwatha ayi, chifukwa

amene amayambitsa kukangana si malo,

Miyambi ya Patsokwe

107

koma anthu.

Dzimvere mtolo.

-Mawuwa amanenedwa pouza munthu kuti

wamva zimene zanenedwa, kwatsala n’kuti

azigwiritse ntchito.

Dzina silifa.

-Ana akabadwa amatsala ndi dzina la

munthu amene anawabereka.

Dzinena kuti mafano, udzafa maono

adakayera.

-Mwambiwu umatanthauza kuti kunyoza

malangizo a akuluakulu kapenanso

zikhulupiriro zamtundu wako

kungakubweretsere tsoka. Mpofunika

kumanyadzira chikhalidwe chathu komanso

kumamvera malangizo.

Miyambi ya Patsokwe

108

Dzino siliononga nyumba ya msonkhano,

koma lirime.

-Chimene chimachititsa kuti anthu asiye

kugwirizana kawirikawiri silikhala dzino,

koma pakamwa.

Dzira siliola tsiku limodzi.

-Khalidwe la munthu siliyamaipa tsiku

limodzi. Ngati munthu walakwa ndiye kuti

anayamba kale kuchita zinthu zoipa, kungoti

sankagwidwa.

Dzungu limakula kunsonga.

-Nthawi zina munthu wobadwa pambuyo ndi

amene amakhala wamphamvu, wokula bwino

ndiponso wanzeru kuposa woyamba

kubadwa.

Dzungu m’gonera kumodzi.

-Mawuwa amanena za anthu omwe

amangochita zawo. Safuna kumva za ena

kapena kugwirizana ndi anzawo.

Miyambi ya Patsokwe

109

Dzuwa likawomba, wotheratu.

-Mwayi ukapezeka, kapenanso ukakhala ndi

nthawi, mpofunika kuchitiratu zowe ukufuna

kuchita, chifukwa mwina tsiku lotsatira

kudzakhala mitambo.

Dzuwa likung’amba mtengo.

-Mawuwa amanenedwa zinazake zikachitika

poyera anthu akuona.

Dzuwa likuwomba mtengo.

-Mawuwa amanenedwa zinazake zikachitika

poyera anthu akuona.

Dzuwa limanyenga, mdima umasaka.

-Pamene walakwira makolo masana, umatha

kuthawa. Koma kukada umapitanso kwa

makolo ako n’kukalangidwa. Cholakwa

sichithawika, nthawi imafika ndipo munthu

amalandira chilango cha zimene wachita.

Miyambi ya Patsokwe

110

Dzuwa salozerana, aliyense amaliona

yekha.

-Pali zinthu zina zomwe sitimafunika kuchita

kufotokozera anzathu.

Miyambi ya Patsokwe

111

F

Fisi adakana nsatsi.

-Si zonse zimene anthu amanenera munthu

zimakhala zoona. Ngakhale munthu atakhala

wamakhalidwe oipa, pamafunika umboni

weniweni tisanamunene kuti wachita

cholakwa.

Fisi adalira msampha utaning’a.

-Nthawi zina timataya mtima kapena kugwa

mphwayi mavuto athu atatsala pang’ono

kutha. Tiyenera kupirira mpaka pamapeto.

Fisi akagwa m’mbuna sayankhula kanthu.

-Munthu akapalamula mlandu amafunika

kungovomereza ndi kupepesa m’malo

momakula mtima. Mawuwa anganenedwenso

ngati munthu akusowa choyankhula

akagwidwa ndi mlandu.

Miyambi ya Patsokwe

112

Fisi akagwa m’mbuna, mawa adzalandira

nkhwangwa.

-Munthu akachita choipa, zivute zitani

amakumana ndi mavuto a zimene wachitazo.

Choncho ndi bwino kungovomereza ndi

kupepesa m’malo momakula mtima. Mawuwa

anganenedwenso ngati munthu akusowa

choyankhula akagwidwa ndi mlandu.

Fisi akagwira sataya.

-Munthu suyenera kutaya chinthu chimene

umachidalira komanso chimakuthandiza

monga ntchito, chipembedzo ndi zina.

Fisi akakhuta salilira pomwepo.

-Pamene munthu wapeza mwayi wina,

usamawanyang’wire amene akupatsa

mwayiwo monga makolo, aphunzitsi ndi

akuluakulu a pantchito, chifukwa

angakulande zomwe wapezacho.

Miyambi ya Patsokwe

113

Fisi akatola fupa sadyera pomwepo.

-Sibwino kumangouza aliyense za mwayi

umene tapeza monga udindo chifukwa

angayambe kuona kuti ndife onyada.

Fisi akazingwa amadya udzu.

-Munthu ayenera kumakhutira ndi

kangachepe kamene wapeza akakhala

pamavuto.

Fisi amakhalabe fisi, ngakhale atasintha

tchire.

-Munthu woipa ndi woipa, sangasinthe

chifukwa choti wasintha malo.

Chimodzimodzinso chinthu choipa,

sichingasanduke chabwino ngakhale

utachichita pa zolinga zabwino.

Fisi atolapo tsoka.

-Munthu ukakhala wakhalidwe loipa monga

kuba ndiye chinthu n’kusowa pakhomo,

anthu amangoti ndiwe, ngakhale palibe

Miyambi ya Patsokwe

114

umboni wokwanira wachitadi zinthuzo ndiwe.

Fisi ayamika ake maluwa.

-Munthu amakonda kuyamikira zinthu zake

n’kumaona kuti n’zabwino kuposa zonse.

Fisi ndi Mbuzi sizigonera limodzi.

-Mawuwa amanena za zinthu zomwe ndi

zosayenera kukhalira limodzi kapena

kugwirizana. Mwachitsanzo, anthu odana,

sayenera kumakhalira limodzi chifukwa

mapeto ake akhoza kuphana.

Fisi saopa mdima.

-Munthu amene amakonda zoipa saopa

anthu kapena zinthu zoopsa ndi zonyansa.

Amayendanso ndi anzake omwe ndi oipa.

Fodya amakoma ngokoketsana.

-Mawuwa amatanthauza kuti moyo wa

munthu umakoma ndi kugawana zinthu

monga nzeru, zakudya, zovala ndi zina.

Miyambi ya Patsokwe

115

Fodya amakoma ngwamnzako.

-Mawuwa amatanthauza kuti chinthu

chanzako n’chimene chimaoneka chokoma

kuposa chako.

Fodya m’panazale.

-Ana amatengera zimene makolo awo

amachita.

Fodya n’kukhomo.

-Munthu wina akapeza mnzake ali mnyumba

mwake ndi mkazi wa mnyumbamo.

Pomufunsa kuti “Ukutani m’nyumba

mwangamo?” amati, “Ndikupempha fodya.”

Mwini wakeyo amati: “Nanga kupempha

fodya amachita kulowera m’nyumba.”

Mwambiwu umatanthauza kuti tizichita

zinthu modzilemekeza kuti tisasokoneza

maganizo a anthu ena.

Miyambi ya Patsokwe

116

Fodya wako ndi uyo ali pamphuno,

wapachala ngwa mphepo.

-Munthu ayenera kumakhutitsidwa ndi

zomwe ali nazo, chifukwa zimene amafuna

kapena amamva akhoza osadzazipeza

pamoyo wake.

Fodya wako ndi uyo ali pamphuno.

-Tizidalira zinthu zomwe tili nazo kusiyana

ndi zomwe tikungoganizira.

Fulukutufulukutu kuti anzake kumudzi

aziti akulima.

-Sibwino kumangodzitama kapenanso

kumachita zinthu modzionetsera. Ndi bwino

kumagwira ntchito zooneka ndi maso m’malo

momangodzitama. Ndi bwino kumachita

zimene umanena.

Fupa lokakamiza limagulula dzino.

-Zinthu zokakamiza sizichedwa kutha ndipo

nthawi zina zimaononga zinthu zina.

Miyambi ya Patsokwe

117

Fupa lokakamiza limaswetsa mphika.

-Osakakamiza munthu kuchita zomwe

sakufuna monga kukwatira, chifukwa

akapeza mavuto akhoza kudzatiririra.

Fupa lokakamiza silichedwa kuswa

mphika.

-Osakakamiza munthu kuchita zomwe

sakufuna monga kukwatira, chifukwa

akapeza mavuto akhoza kudzatiririra.

Fwinyiririfwinyiriri adachedwa kudzuka,

chinthu chidam’mbwandira.

-Kukhala fwinyiriri n’kudzipindabe pogona

m’malo modzuka n’kumakagwira ntchito.

Nthawi zina kukonda kwambiri chinthu

china kukhoza kutibweretsera mavuto,

monga kungachitire kumangokonda kugona.

Miyambi ya Patsokwe

118

G

Galu adaipitsa yekha alendo.

-Mwambiwu umanena za munthu amene

wadziwonongera tsogolo pochita zinthu

zosayenera.

Galu akati phethi, wataya nyama.

-Pogwira ntchito kapena pochita chinthu

chilichonse, monga maphunziro,

sipamafunika kuyang’ana m’mbuyo kapena

kugwa mphwayi koma kudzipereka ndi

mtima wonse. Ukapusa umapezeka kuti

wataya mwayi.

Galu ndi galu basi.

-Munthu amene ali ndi khalidwe kapena

chizolowezi chinachake zimavuta kuti

asinthe.

Miyambi ya Patsokwe

119

Galu sasowa mbuyake.

-N’zofunika kuti nthawi zonse tizikumbukira

amene amatithandiza, monga makolo ndi ena

makamaka tikakhala pabwino.

Galu sauwa fupa lili m’kamwa.

-Anthu ena akakhala pabwino amaiwala za

umphawi wawo ndipo sasamala za anzawo.

Galu ukam’ponyera mafupa, sachoka

pakhomo.

-Munthu ukakhala woolowa manja kapena

wamsangala, anthu satha phazi pakhomo

pako.

Galu umamudzuma asananye.

-Munthu akayamba kuchimwa kapenanso

zinthu zikamalakwika, timafunika

kumuthandiziratu zinthu zisanafike poipa.

Galu wa mfumu ndi mfumu ya Agalu.

-Amene ali m’maudindo ena monga nduna,

Miyambi ya Patsokwe

120

amaimira mtsogoleri wamkulu, choncho

ngakhale atakhala kuti samatsuka m’kamwa,

timafunikabe kumawalemekeza.

Galu wadyera (wolusa) anapita ndi goli

lake.

-Tisamachite chinthu ndi mtima wongofuna

kusangalatsa ena ngati mmene amachitira

Galu amene anasochera ndi goli lake.

Galu wamiliri anaba nyama n’kuoloka nayo

mtsinje.

-Munthu wopirira ndi amene amapindura

nthawi zambiri. Khama limathandiza kuti

munthu apeze chomwe akufuna.

Galu wamiliri anaoloka mtsinje.

-Munthu wopirira ndi amene amapindura

nthawi zambiri. Khama limathandiza kuti

munthu apeze chomwe akufuna.

Miyambi ya Patsokwe

121

Galu wamkota sakandira pachabe.

-Akuluakulu akamatichenjeza ndiye kuti

alinga ataona kuopsa kwa zimene

tikuchitazo. Choncho, ndi bwino

kumawamvera kuti tipewe mavuto.

Mwachitsanzo, galu wamkota,

sangangokanda popanda kanthu. Mutafufuza

mukhoza kupeza kuti pali nyama.

Galu wandifera m’khwapa.

-Mawuwa amaneneda potanthauza kuti

zangovuta koma tinayesetsa.

Galu wofewerera anapita ndi khongozi

(goli).

-Munthu akakhala wotengeka ndi zonena za

ena komanso madandaulo a ena amasochera.

Galu wouwa saluma.

-Munthu woyankhulayankhula nthawi

zambiri amakhala wopanda mnzeru kapena

wopanda mphamvu.

Miyambi ya Patsokwe

122

Gola akasowa Nkhuku, amatola udzu.

-Gola kapena kuti mphamba, imakonda

kugwira Nkhuku. Koma zikavuta, imatha

kudya udzu. Tisamangoyembekeza zabwino

nthawi zonse. Nthawi zina munthu

amakumana ndi mavuto.

Golo! kumtondo, kumunda kulibe ndime.

-Mawuwa amanena za munthu waulesi,

yemwe amakonda kudya koma n’kumakana

kugwira ntchito.

Gomo likagumuka, zako umadyeratu.

-Pamavuto munthu amayenera kuchita

chilichonse kuti adzipulumutse.

Gona n’kuphe sali kutali.

-Mawa si kalekale, ngati mmene zimakhalira

ndi munthu amene wauzidwa kuti aphedwa

mawa. Nthawi imadutsa mofulumira

kwambiri.

Miyambi ya Patsokwe

123

Gona n’kuphe sikutali.

-Mawa si kalekale, ngati mmene zimakhalira

ndi munthu amene wauzidwa kuti aphedwa

mawa. Nthawi imadutsa mofulumira

kwambiri.

Gonu, kwacha; masiku adyana.

-Munthu aliyense ayenera kukhala

wokonzekera kugwira ntchito chifukwa

zamawa sizidziwika.

Gule aliyense amakoma potsiriza.

-Chinthu chilichonse chimakhala chovuta

komanso chosasangalalatsa

ukamachiyamba. Koma ukachizolowera

chimayamba kukusangalatsa.

Gule n’guleje, umakumbuka podya

nkhwani.

-Osamakomedwa ndi zosangalatsa za

m’dzikoli n’kufika poiwala Mulungu kapena

kuiwala zoti ukhoza kukumana ndi mavuto

Miyambi ya Patsokwe

124

kapena kufa kumene.

Gule ndi wa aliyense, kulakwa n’kuthyola

mwendo.

-Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala,

kuchita komanso kuyankhula chimene

akufuna. Vuto limakhalapo ngati atachita

zinthu zophwanya malamulo.

Gulo akasowa mtengo, amazungulira

chitsa.

-Pamlandu munthu ayenera kugwiritsa

ntchito umboni uliwonse umene uli nawo.

Chimodzimodzinso pamoyo wathu, ngati

tasowa chinthu tiyenera kupeza china choti

chilowe m’malo mwake.

Gumula zikulake.

-N’zosavuta kupeza zolakwa za wina,

kuwononga zinthu, komanso kugwiritsa

ntchito zomwe wina wapanga. Koma kuti

upange zako pamakhala matatalazi.

Miyambi ya Patsokwe

125

Gunda umvetse.

-Pofuna kudziwa zoona zenizeni, munthu

umayenera kufunsa kapena kuchita

zinthuzo.

Gunya sasenda, amene wasenda wakhuta.

-Mukamadya mbatata, anthu anjala sasenda,

akayamba kusenda ndiye kuti ayamba

kukhuta. Choncho, tikamagwira ntchito,

zomwe tingathe kusiya osazigwiritsa ntchito

tisataye nazo nthawi.

Gwada utame, ndikuuze chinapha mako.

-Mawuwa amanenedwa munthu

akamalimbikitsa mnzake kuti asabise

chomwe wabwerera, kuti akatero nayenso

amuuze zinthu zina zachinsisi.

Gwada, umvetse.

-Pofuna kumvetsa kanthu kenake pafunika

kudekha, kudzichepetsa ndi kupempha kuti

wina akuthandize.

Miyambi ya Patsokwe

126

Gwadugwadu ndiko chikulu, chilili ndiko

kupusa.

-Kugwada pamene munthu wamkulu

akuyankhula ndi ulemu komanso

kumasonyeza kukhwima maganizo.

Kungoima ukamayankhula ndi akuluakulu

ndi mwano komanso kuperewera nzeru.

Gwira mpini, kwacha!

-Mawuwa amanenedwa akamachenjeza

munthu waulesi kuti ayambe kugwira

ntchito.

Gwira pali moyo.

-Munthu amayenera kuteteza moyo wake

posamalira zinthu zimene zimamuthandiza,

monga ntchito kapena katundu.

Gwirize n’kodze.

-Munthu woyang’anira katundu wa ena ndi

gwirize n’kodze moti sakhala ndi ulamuliro

pa katunduyo.

Miyambi ya Patsokwe

127

I

Idakula nyanga poopa malunje.

-Kuti munthu akule ndi moyo ndiponso

makhalidwe abwino, ayenera kumalemekeza

akuluakulu ndiponso kumadzisamalira

monga nyama imene imakula nyanga poopa

kuyenda m’nkhalango.

Ikachuluka pakamwa, siipenya pathumba.

-Pantchito pakachuluka anthu, ntchito

siyenda, mmalo mwake zimachuluka ndi

nkhani.

Ikadza njala, umadya kontho.

-Munthu ukakhala pamavuto umachita

zinthu zomwe sungachite uli pamtendere.

Ikadza njala, usamataye gaga.

-Munthu aliyense amafunika kusamalira

chuma chake, chifukwa akachiwononga,

Miyambi ya Patsokwe

128

tsiku lina amadzachifuna akadzakhala

pamavuto.

Ikadza njala, usamataye mtondo.

-Munthu aliyense amafunika kusamalira

chuma chake, chifukwa akachiwononga,

tsiku lina amadzachifuna akadzakhala

pamavuto.

Ikakuthawa imawawa nsuzi.

-Munthu wina anagwira Njiwa ndipo

anasangalala kwambiri chifukwa ankadziwa

kuti nsima ya tsiku limenelo ikayenda. Koma

ali mkati moganiza zimenezi, Njiwayo

inamupulumuka n’kuthawa. Munthuyo

anapsa mtima n’kuyamba kuikuwira Njiwayo

n’kumaiuza kuti, “Iweeeeeeeee, umawawa

msuzi!” Phunziro ndi lakuti osamanyoza

chinthu chikapita.

Ikaola imodzi, zawola zonse.

-Pamudzi munthu akakhala wamakhalidwe

Miyambi ya Patsokwe

129

oipa monga wakuba, anthu amangoti mudzi

wonse ndi wa anthu akuba ngakhale wakuba

ali m’modzi yekha. Kulakwa kwa munthu

wina kukhoza kukhudza anthu ena.

Ili ndi amake simagwa m’mbuna.

-Anthu amene amalangiza ana awo ndipo

anawo namvera malangizo awo, kawirikawiri

amakula bwino popanda mavuto ambiri.

Iliko nja usiku, mkamwini anajiwa dzanja.

-Si bwino kuyembekezera zinthu chifukwa

zikapanda kubwera timadzagwira njakata.

Imfa ilibe odi.

-Imfa siipanganika, imabwera nthawi

yosayembekezereka. Choncho, timafunika

kukonza moyo wathu wauzimu kuti tikhale

ndi tsogolo labwino.

Miyambi ya Patsokwe

130

Imfa siisankha, imatenga mkulu ndi

mwana yemwe.

-Aliyense azikhala wokonzeka kuti tsiku lina

adzamwalira.

Imfa siona nkhope.

-Imfa potenga munthu siyang’ana kuti uyu

ndi ndani.

Imfa sithawika.

-Ngakhale munthu atachita zotani kuti

asamwalire, mapeto ake amafabe.

Ine-ine sin’theka pofula uchi.

-Si bwino kumangomva zathu zokha

komanso kumamva malangizo a ena ndinso

kugawana nawo zomwe tili nazo. Umbombo

suthandiza.

Ine-ine, sindim’tenga.

-Si bwino kumachita zinthu modzikonda

pamalo, mapeto ake umataya mwayi wopeza

Miyambi ya Patsokwe

131

zabwino. Anthu sagwirizana ndi munthu

amene amachita zinthu modzikuza.

Inswa ikaola imodzi, zaola zonse.

-Pamudzi munthu akakhala wamakhalidwe

oipa monga wakuba, anthu amangoti mudzi

wonse ndi wa anthu akuba ngakhale wakuba

ali m’modzi yekha. Kulakwa kwa munthu

wina kukhoza kukhudza anthu ena.

Miyambi ya Patsokwe

132

J

Jekete sapisira.

-Mawuwa anganenedwe ngati wina wachita

zinthu zabwino kwambiri moti

sitingachitirenso mwina koma

kumuyamikira. Anganenedwenso ngati wina

akuyesa kuchita zosatheka. Tisamachite

zinthu zosagwirizana ndi chizolowezi chathu,

monga kupisira jekete.

Jelasi siipindula.

-Njiru kwake n’kuwongonga zinthu komanso

kubwezera zinthu m’mbuyo. Palibe chimene

munthu angapindule ngati atamachita jelasi.

Miyambi ya Patsokwe

133

K

Kachaje sikachepa, kachepa n’kamalonda.

-Tiyenera kuthokoza tikapatsidwa zinthu

mwaulere ngakhale zitakhala zochepa. Koma

ngati tagula ndipo zinthuzo sizinakwane pa

mlingo wake, tiyenera kudandaula.

Kachepa alibe bwalo, ali ndi bwalo ndi

kangachepe.

-Si bwino kumaderera zimene

wangopatsidwa, kumangothokoza.

Kachepa kayenda, kakafa n’kophika.

-Pochita cholakwa munthu umaona ngati

chaching’ono. Koma chikaululika

chimasanduka chachikulu komanso

chochititsa manyazi.

Kachepa n’kovala, kakudya sikachepa.

-Chovala chimodzi simungathe kuvala anthu

Miyambi ya Patsokwe

134

awiri nthawi imodzi. Koma chakudya

ngakhale chitachepa bwanji mukhoza

kugawana. Mawuwa amanenedwa poitanira

ena kuti adzadye nawo chakudya.

Kachepa, n’kuona msandulizo.

-Vuto limachepa ngati tili ndi ena omwe

angatithandize.

Kachepera maso, kamwa lilanda.

-Pali zinthu zina monga chakudya, milandu,

zomwe poziona zimakhala ngati zochepa

koma kuti tizidye kapena kuzikamba

zimakhala zazikulu. Tisamaderere zakudya

kapena kunyozetsa nkhani.

Kachinyiza anang’amba thumba.

-Si bwino kukakamiza wina kuchita chinthu

chomwe sakufuna, chifukwa mapeto ake

timapezeka tawononga, m’malo mokonza.

Miyambi ya Patsokwe

135

Kachinziri kamatupa patsala lake.

-Munthu amamasuka akakhala kwawo.

Akhoza kudya kapena kuchita zinthu zomwe

kukanakhala kuchilendo sakanachita.

Kachipande katherere kamakoma

n’kuyenderana.

-Anthu amene amakhala bwino amafunika

kumayenderana komanso kupatsana zinthu.

Amafunikanso kuthandizana zikavuta,

m’malo momangoyembekezera kuti munthu

m’modzimodzi azitichitira zabwino. Mnzako

akukuchitira zabwino nawenso ndi bwino

kumuchitira zabwino.

Kachirombo kofula m’njira katama mano.

-Munthu aliyense pamene akuyamba kuchita

chinthu, monga banja kapena kulima

munda, amafunika kuona kaye ngati

angakwanitse. Amafunikanso kuona ngati ali

ndi zonse zofunika kuti akwaniritse

Miyambi ya Patsokwe

136

chinthucho. Mwachitsanzo, si bwino kulilowa

banja ukumadalira ena kuti adzakuthandiza

kapena kumabereka ana ukuwerengera kuti

amalume adzawaphunzitsa.

Kadapota nyanga kamadya ndi mvumbi.

-Tiziganizira za tsogolo lathu. Kanyama kena

kankaopa mvula ndipo sikankatuluka kupita

kukadya moti kanaonda. Ndiye mvula itatha

kanapita kukaba chakudya ndipo

kanaphedwa. Kakanadya bwino nthawi ya

mvula bwenzi kali ndi moyo nthawi yosowa

chakudya.

Kaduka ka chinangwa.

-Mawuwa amatanthauza nsanje. Chifukwa

cha nsanje, chinangwa chikazulidwa

sichiphukanso kuopa kuti anthu

angabwerenso ndi kudzathyola masamba ake

kuti akapange ndiwo (chigwada) kapena

kudzachizulanso.

Miyambi ya Patsokwe

137

Kaduwa kokongola kamakopa Njuchi.

-Anthu amatengeka ndi zimene akuona.

Mwachitsanzo, amuna amakopeka ndi

kukongola n’chifukwa chake akazi

amadziphoda kuti akope njuchi.

Kadya n’kena mbiri n’nja Khoswe.

-Pali anthu ena chifukwa cha maonekedwe

awo anthu amaganiza kuti ndi amene achita

zoipa. Tisamaweruze munthu potengera

maonekedwe kapena potengera zimene

anachita m’mbuyomu. Komanso munthu

akakhala woipa kapena wochenjeretsa

amasowa mtendere, chifukwa chilichonse

choipa amangoti wachita ndiwe.

Kadyole pamzinda adathetsa anzake.

-Kusyasyalika kapena kuti kuuza munthu

zinthu zonama n’cholinga choti

umusangalatse kungangoonongetsa zinthu.

Ndi bwino kumauza anthu chilungamo koma

Miyambi ya Patsokwe

138

mwachikondi.

Kadzidzi amalemekeza nkhalango yake.

-Aliyense ali ndi zinthu zimene

zimamuthandiza komanso kuchititsa kuti

azilemekezeka.

Kadziwa mwini mpeni wa m’chiuno.

-Sitingathe kudziwa zambiri za anthu ena

monga maganizo, mavuto kapena

madandaulo awo.

Kadziwa mwini msampha wa m’chipeta.

-Ndi munthu amene watchera msampha mu

udzu kapena kuti m’chipeta amene amadziwa

pamene uli. Choncho, sitingathe kudziwa

zambiri za anthu ena monga maganizo,

mavuto kapena madandaulo awo.

Kadziwa mwini nkhuto wa Fulu.

-Sitingathe kudziwa zambiri za anthu ena

monga maganizo, mavuto kapena

Miyambi ya Patsokwe

139

madandaulo awo.

Kadzola fumbi kalekeni, kali ndi nyimbo.

-Munthu akayamba kuchita zinazake ndiye

kuti pali chimene chikumulimbitsa mtima.

Kagwa m’khutu satong’ola, atong’ola

n’kam’maso.

-N’zosatheka kubweza mawu atayankhulidwa

kale. N’chifukwa chake m’pofunika

kumasamala ndi zimene timayankhula kuopa

kuyambitsa chipwirikiti.

Kagwa m’maso ndi kako.

-Osamawerengera zinthu zimene

sunazilandire, mwina sizibwera. Chomwe uli

nacho ndiye chako.

Kagwa m’maso tola.

-Mwambiwu ukunena za wakuba amene

amatenga chilichonse chomwe waona.

Miyambi ya Patsokwe

140

Kaitana kavula, ukachedwa upeza

katavala.

-Ukaitanidwa umafunika kupita mofulumira,

chifukwa ukachedwa umakapeza zimene

amakuitanirazo zitatha. Kuchita zinthu

panthawi yake komanso mosazengereza

pamene waitanidwa n’kofunika kwambiri.

Ukachedwa umakapeza zatha kale.

Kaitana kavula, ukachedwa ukakapeza

katabopha.

-Ukaitanidwa umafunika kupita mofulumira,

chifukwa ukachedwa umakapeza zimene

amakuitanirazo zitatha. Kuchita zinthu

panthawi yake komanso mosazengereza

pamene waitanidwa n’kofunika kwambiri.

Ukachedwa umakapeza zatha kale.

Kakachenjeretsa sikanona.

-Nthawi zambiri amene amakonda

kuyankhulayankhula kapena ochenjeretsa

Miyambi ya Patsokwe

141

amakhala opanda nzeru. Chimodzimodzinso

okongola, amangokongola nkhope koma

n’kukhala opanda nzeru kapena opanda

khalidwe.

Kalongoda sapsera madzi amodzi.

-Zinthu zina zimafunika khama kuti zitheke.

Komanso kuti munthu achite bwino

amafunika kuthandizidwa kangapo.

Kako n’kako, kamwini katukwanitsa.

-Kanthu kako ukhoza kukagwiritsa ntchito

m’mene ukufunira koma kamwini ayi.

Kako n’kako, kamwini sakandira.

-Ukabwereka chinthu, sukhala ndi ufulu

wochigwiritsa ntchito mmene ukufunira.

Ngati ukufuna kumagwiritsa ntchito chinthu

momasuka, ndiye ungachite bwino

kungopeza chako.

Miyambi ya Patsokwe

142

Kako ndi ako wadya.

-Si bwino kutenga zinthu zimene si zako.

Chomwe munthu wadya ndiye chako

chenicheni chifukwa palibe angakulande.

Kako ndi ako kali m’mimba, kali padera si

kako.

-Munthu uziwerengera chimene uli nacho,

osati chomwe ukuganiza kuti ungadzakhale

nacho.

Kako sikanunkha.

-Umateteza abale ako komanso anzako.

Anthu akamawanenera zoipa,

umawakometsera ngakhale zitakhala kuti

amachitadi zinthuzo.

Kakonda mnzako mlekere, mawa kakonda

iwe.

-Osachita nsanje ndi zinthu kapena mwayi

wa ena, mawa ukhoza kudzakhala mwayi

wako.

Miyambi ya Patsokwe

143

Kakudza kokha kamalaula.

-Kuti upeze chinthu chabwino umayenera

kuchivutikira. Chinthu chongobwera chokha

n’chosadalirika. Choncho, si bwino kukhala

munthu waulesi.

Kale silibwerera.

-N’kupanda mnzeru kumalilira zakale. Ndi

nzeru kumaganizira za mawa mmalo

momataya nthawi kuganizira zinthu zomwe

zinachitika kale ndipo sungazisinthe

ngakhale pang’ono.

Kali kokha n’kanyama, tili awiri n’tianthu.

-Kukhala awiri si mantha, mumathandizana

nzeru. Koma munthu wokonda kuyenda

yekha kapena kuchita zinthu payekha

amavutika kwambiri. Palibe munthu amene

angathe kuchita zonse payekha, choncho ndi

bwino kumadalirana.

Miyambi ya Patsokwe

144

Kalikonse kamakhala ndi chiyambi.

-Palibe chimene sichikhala ndi poyambira.

Kalikonse kouluka kamatera.

-Tingatchuke kapena kulemera bwanji, tsiku

limadzafika loti timadzasauka kapena

kudzamwalira n’kusiyana nazo zonse. Moyo

umanyenga.

Kalindelinde adalinda chiswe.

-Mlesi amataya mwayi wogwira ngumbi

pamene zituluka. Popeza wachedwa kudzuka,

amapeza zatha ndipo amangopeza chiswe.

Kalionera adaphika ntchentche kuyesa

ana a Njuchi.

-Munthu ukamatengera makhalidwe oipa a

anthu, amene umakumana ndi mavuto ndi

iweyo. Osamatengera zoipa zomwe ena

amachita.

Miyambi ya Patsokwe

145

Kalira-ulendo salira, ndi mtu uchepa.

-Munthu akamapita kwinakwake kukafuna

zinthu monga zovala kapena zakudya,

amayenera kutenga zimene angapeze. Akhoza

kubwerera opanda kalikonse ngati

atamaderera n’kumasiya zinthu.

Kalowa m’bwalo kali ndi nyimbo.

-Munthu akayamba kuchita zinazake ndiye

kuti pali chimene chikumulimbitsa mtima.

Kalowa m’bwalo kayanza malo.

-Zimakhala zovuta kuimitsa chinthu chimene

chayamba kale. Zinthu zina zimachitika

mwadzidzidzi chifukwa cha zinazake, ndipo

pambuyo pake zimadziwika.

Kalowa m’bwalo, sikatuluka.

-Zinthu zosangalatsa zimavuta kuzisiya.

Kalowa m’khutu kayala mphasa.

-Chomwe munthu wamva chimakhazikika.

Miyambi ya Patsokwe

146

Kalulu anamva mawu oyamba.

-Mawu oyamba ndi amene amakhala

aphindu komanso ndi amene anthu

amagwira. Tizichenjera tikamanena zinthu

chifukwa anthu amagwira mawu anthu

oyamba.

Kalulu anatuma njovu.

-Mwambiwu utanthauza pamene munthu

wolemekezeka akuchita zinthu zina

atatumidwa kapena m’malo mwa anthu ena

onyozeka.

Kamakuwa ndi kakumsampha, kam’diwa

sikayankhula.

-Wina akagwidwa ndi ndalama yobedwa,

sayankhula. N’zachidziwikire kuti ndi amene

anatenga ndipo amugwira basi.

Kamanenepetsa sikadziwika.

-Ndi bwino kumayesa njira zosiyanasiyana

monga kulima komanso kugwira ntchito.

Miyambi ya Patsokwe

147

Osamangodalira chimodzi.

Kamanga zula.

-Ndi bwino kumathetsa zimene zikuyambitsa

mavuto ako, vutolo lisanakule.

Kamapikula nkhali ndi katsekera.

-Mwambiwu umanena za munthu amene

amakonda kuchepetsa zinthu, pomwe

zotsatitira zake ndi zazikulu.

Kamata m’kati, ng’oma ya chimbulimbuli.

-Mawuwa amanena mokokomeza za munthu

amene amaoneka ngati wabwino pamaso

koma mumtima mwake muli chiwembu.

Kamba amanyerera amene wamtola.

-Pali anthu ena omwe umati ukawathandiza

amabweza chipongwe kapenanso

kukubweretsera mavuto.

Kambalame kam’kamwa sikanona.

-Anthu ambiri sakonda kucheza ndi munthu

Miyambi ya Patsokwe

148

wolongolola ndipo nthawi zambiri munthu

wotereyu amakhala wopanda khalidwe ndipo

anthu amamuthawa.

Kambalame kolawira kadakhuta

nyongolotsi.

-Tikamayesetsa kuchita zinthu moyambirira,

monga kulimba munda, timapeza mphindu

lalikulu. Koma ngati tayamba mochedwa,

timakumana ndi mavuto ambiri n’kupeza

phindu lochepa.

Kambaleme kochenjera sikachedwa

kukoledwa paulimbo.

-Kuchenjeretsa komsamva nako malangizo

kumaika munthu pamavuto aakulu ngati

mmene zimakhalalira ndi mbalame yomwe

imangoti zungulizunguli. Pamapeto pake

imapezeka yakatera paulimbo.

Kambuku sangasinthe manga ake.

-Zimakhala zovuta kuti munthu asiye zinthu

Miyambi ya Patsokwe

149

zimene anazolowera.

Kambuzi kapambuyo kadalinda mkwapulo.

-Kuchita zinthu mochedwa kumapezetsa

mavuto. Zimakhala ngati mbuzi imene ili

m’mbuyo, munthu akamafuna kukwapula

amakwapula imeneyoyo. Ndi bwino

kumakhala patsogolo pochita zinthu.

Kamodzikamodzi ndi mtolo.

-Zinthu zikuluzikulu zimayamba ndi zinthu

zing’onozing’ono. Mwambiwu

umatiphunzitsanso kuti kuchita zinthu

mwachifatse n’kothandiza kusiyana n’kuchita

zinthu mopupuluma.

Kampango woyera kumimba.

-Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene

akukana mlandu ponena kuti, “Ndilibe

mlandu ndi munthu chifukwa palibe umboni

wokwanira.”

Miyambi ya Patsokwe

150

Kamtande alemba pali khola.

-Munthu akakhalitsa kapena kuima

penapake kwa nthawi yaitali, ndiye kuti

akudikira chinachake.

Kamtengo kamwana n’kamene amaphera

njoka.

-Anthu anzeru amatha kulephera kuchita

zinthu zing’onozing’ono, amawathandiza ndi

anthu amene amaoneka ngati opanda nzeru.

Kamtsitsi kadagwetsa abambo.

-Osachepetsa tchimo kapena cholakwa.

Tiyenera kulapa chifukwa lingadzatipezetse

mavuto m’tsogolo.

Kamwana m’chokere, ukulu n’kuona kako.

-Mawuwa amanenedwa pakakhala chakudya

chochepa. Amasonyeza kuti ngakhale

chakudya cha mwana, munthu ukhoza

kukhuta. Ndi bwino kumavomereza zinthu

zikavuta.

Miyambi ya Patsokwe

151

Kamwini kalibe nkhoko m’nkhali.

-Munthu ukapita kwa eni, sumajijirika

mpaka kufika pomauza anthu kuti, “Tisunge

chakudya chinachi kuti tidzadye

m’mamawa.” Kapena kumakanganirana

nawo zakudya zomwe zinatsala dzulo. Ndi

bwino kumakhala munthu woupeza mtima

tikakhala kuchilendo.

Kandimverere adakanena za m’maluwa.

-Zongomva chabe sizikhutiritsa. Pamafunika

pakhale umboni womveka bwino, apo ayi

ndiye umafunika kupita komweko kuti

ukadzionere ndi maso ako.

kandimverere adamva zam’maluwa.

-Ngati tikukayika kapena sitikudziwa

zoyenera kuchita ndi bwino kufunsa kuti

tichite zinthu moyenera.

Kangachepe n’kachipongwe.

-Tisamaikire kumbuyo munthu wolakwa

Miyambi ya Patsokwe

152

chifukwa cha msinkhu wake. Si onse amene

amachita chilungamo komanso chipongwe

sichichepa.

Kangachepe n’kang’oma, mkulu saomba

chitsa.

-Tizikhutitsidwa ndi zomwe tili nazo kapena

tapatsidwa. Mwachitsanzo, munthu

wopemphetsa samafuna kuti amupatse

zodzadza thumba.

Kangachepe, fungo n’lamake.

-Anthufe timatengera makhalidwe ena

kuchokera kwa makolo. Komabe, tiyenera

kayesetsa kuchita zomwe tingathe kuti

tisinthe makhalidwe oipa.

Kangachepe, kako n’kako ndithu, kamwini

sakandira.

-Kanthu kako ukhoza kukagwiritsa ntchito

m’mene ukufunira koma kamwini ayi.

Miyambi ya Patsokwe

153

Kangakanga adathyola nyani mchira.

-Si bwino kumaganiza kuti ukhoza

kukwanitsa kuchita chilichonse wekha

chifukwa ukadzapeza mavuto udzasowa

wokuthandiza.

Kangakanga anathyola nyau.

-Si bwino kumaganiza kuti ukhoza

kukwanitsa kuchita chilichonse wekha

chifukwa ukadzapeza mavuto udzasowa

wokuthandiza.

Kangakanga kanakanga.

-Si bwino kuti munthu udzikhala wodzikonda

kapena woumira chifukwa tsiku lina

zikadzakuvuta umadzasowa wokuthandiza.

Kangaonde kalira mtembo.

-Munthu aliyense ayenera

kumalemekezedwa, osayang’ana mmene alili.

Miyambi ya Patsokwe

154

Kangaonde kamakoma ndi mchere.

-Zinthu zooneka monyozeka zimatha kukhala

zosililika chifukwa chowonjezera tina n’tina.

Kankhuku kachilendo sikachedwa

kugwidwa.

-Chinthu kapena munthu wachilendo pamalo

nthawi zambiri amadedwa. Chilichonse

chikalakwika amati wachititsa kapena

wachita ndi iyeyo.

Kansalu kakafupi, malamulo tho!

-Mwambiwu unayamba chifukwa cha

khalidwe la amuna ena omwe amagulira

akazi awo nsalu yosakwanira

n’kumalongolola kapena kukhazikitsa

malamulo ambirimbiri. Osamavuta kwambiri

tikhala ndi zinthu kapena tikachita

chinachake.

Kanthu kakakhala kako, sikaneneka.

-Ngati nkhani ikukukhudza, si chapafupi

Miyambi ya Patsokwe

155

kuinena. Ambiri zikatero amangokhala du!

Kanthu kali kuchala.

-Kuti udziwe za chinthu, uyenera kuuzidwa

ndi amene akuchidziwa bwino.

Kanthu kali m’makonda Buluzi akhumbira

khonde.

-Zokonda zimasiyanasiyana, choncho

mnzathu akamakonda zinazake, tisamuseke

chifukwa zokonda zathunso zikhoza kukhala

zoseketsa kwa anthu ena.

Kanthu kali m’malira, Kalulu adalilira

makutu.

-Pofunsira ntchito kapena mbeta munthu

azisankha yekha m’malo momusankhira

chifukwa makonda amasiyanasiyana.

Kanthu kali m’mwayi, m’kamwini

mnzanga wadya phiko.

-Anthu ena amakhala ndi mwayi pagulu

Miyambi ya Patsokwe

156

kapena pamudzi.

Kanthu kali munye.

-Munthu umadziwa zinthu kuchokera kwa

ena. Mwachitsanzo, kuti udziwe nkhani

inayake zimadalira kuti ena akuuze.

Kanthu kalikonse m’chifuniro, Buluzi

anakana bweya.

-Munthu aliyense ayenera kumakhala ndi

ufulu wochita zimene akufuna.

Kanthu kandikhalira pamphuno.

-Mawuwa amanenedwa munthu akakumana

ndi mavuto omwe palibe chimene angachite

kuti awathetse. Zimakhala ngati vutolo

lamuyandikira kwambiri moti palibe chimene

angachite kuti alimbane nalo.

Kanthu kavumbu ndi m’manja, m’magona

mosambasamba.

-Pamoyo wathu tizikhala okonzeka

Miyambi ya Patsokwe

157

kukumana ndi zilizonse zotigwera, monga

matenda komanso zina zosayembekezereka.

Kanthu koyambira sikachedwa kuoneka.

-Anzathu akatilangiza pa nkhani inayake

tiyenera kuchita kapena kusintha,

tisamazengereze chifukwa zimadzaonekadi.

Kanthu n’kako uvundukura nupenya.

-Zinthu zako suziopa. Ukhoza kuchita nazo

chilichonse chimene ukufuna.

Kanthu n’kako, kamwini kadalira madzi.

-Zinthu zako suziopa. Ukhoza kuchita nazo

chilichonse chimene ukufuna popanda kuopa

aliyense.

Kanthu n’kako, kamwini n’kamwini.

-Zinthu zako suziopa. Ukhoza kuchita nazo

chilichonse chimene ukufuna popanda kuopa

aliyense.

Miyambi ya Patsokwe

158

Kanthu n’kako, kobwereka sikalimba

m’chiuno.

-Zinthu zobwereka zimakhala zosadalirika,

choncho ndi bwino kumasamala chimene

wabwereka kuti ukachibweze chili bwino.

Kanthu n’kako, waona adakhuta thope.

-Tisamafulumire kusiya kuchita chinthu

chimene chingatithandize kukhala ndi

tsogolo labwino monga sukulu.

Kanthu n’kavumbu, kadavumbula mende

pachisa.

-Chinthu china chimatha kuululitsa chinthu

china chomwe chinali chobisika.

Kanthu n’kugwirizana, fisi adam’landa

mbuzi.

-Kuthandizana n’kofunika. Ukamachita

zinthu limodzi ndi anthu ena mogwirizana

mumatha kupanga zambiri.

Miyambi ya Patsokwe

159

Kanthu ndi khama, phwiti anakwatira

njiwa.

-Ngati titakhala ndi khama tikhoza kuchita

zinthu zazikulu.

Kanthu umaona, chilungulira ndi nthenda.

-Tikangomva m’thupi kupweteka timangoti

ndi malungo. Tiziyamba tadziwadi chimene

tikudwala tisanamwe mankhwala.

Kanyambitira sikanafe.

-Mawuwa amanena za munthu amene

akukakamira khalidwe lopanda pake, monga

kuledzera, kuba komanso kutukwana.

Pamapeto pake munthu wotereyu

amadzakumana ndi mavuto aakulu

mwinanso kufa kumene.

Kaomba nkhadze n’kena, ithobwa otsata

kuusa m’mthunzi.

-Nkhadze ukaithyoka imatulutsa mkaka

umene ungachititse kuti munthu achite

Miyambi ya Patsokwe

160

khungu. Zochita za ana monga kuika mwala

panjira zingabweretse mavuto komanso

zingachititse ngozi.

Kaphovu walowa m’dzombe.

-Anthu oipa akamakhala pamodzi ndi anthu

abwino, amapangitsa kuti abwinowo azioneka

oipa.

Kapinji mayendayenda kasiya anzake

asewera.

-Kuchenjeretsa kapena kuyendayenda

popanda zifukwa zomveka kumabweretsa

mavuto.

Kaponda mvichili.

-Mawuwa akutanthauza mawu abodza

ochokera kwa munthu amene zokamba zake

sizimakhala zoona.

Kapota nyanga, n’kulinga katachenjera.

-Ngati nyama yafika poyamba kupota nyanga

Miyambi ya Patsokwe

161

ndiye kuti inali yochenjera pothawa alenje

ndipo imakhala ndi moyo wautali. Munthu

amene wafika pokalamba ndiye kuti anapewa

zinthu zambiri zomwe zikanatha kuwononga

moyo wake.

Kapusa n’kamake, kopanda amake

kachenjera.

-Anthu ambiri amene amakhala ndi makolo

awo amapusa. Amachenjera makolo awo

akamwalira. Umasiye umaphunzitsa zambiri.

Kasiyagoli.

-Mawuwa amanena za munthu yemwe

amanena bodza lotsekemera n’cholinga choti

zinthu zimuyendere bwino. Anganenedwenso

ponena za munthu amene wapulumuka

pamlandu chifukwa chodziwa kuyankhula.

Kasule wa m’chikho cholimba kuwawa.

-Munthu amene amachita zoipa amakumana

ndi mavuto oopsa ngati mmene chikho

Miyambi ya Patsokwe

162

cholimba chimatulutsira madzi kapena mowa

wowawa.

Kathabwalika thumba lamwala lokanika

kusoka.

-Awa ndi mawu okokomeza onena za munthu

waukamberembere, tambwali.

Kati deru kaopsa mlenje.

-Kanthu sikachitika popanda chifukwa

kapena choyambitsa chake. Ndiye

kachizindikiro kangachepe bwanji tizikhala

nako tcheru.

Kaulamchokero adaika phale padzuwa.

-Tikamafuna kuchoka pamalo kapena

pamudzi, tisamachoke titawonongapo

chifukwa mawa tidzafuna kubwererakonso.

Kaulere sikachepa.

-Tiyenera kumathokoza tikapatsidwa zinthu

ngakhale zitakhala zochepa.

Miyambi ya Patsokwe

163

Kawalewale adapweteka m’dayeretsa.

-Tizichenjera ndi zosangalatsa zomwe

pamapeto pake zimabweretsa mavuto.

Kawerewere kadautsa njovu.

-Ngati sitisamala, chinthu chaching’ono

chitha kubutsa mavuto aakulu monga

mmene kamoto kakang’ono kamayatsira

nkhalango.

Kayenda m’sana kapenya malowo.

-Ngati pamlandu munthu akuyankhula

m’maso muli gwa, ndiye kuti ali ndi podalira.

Kayenda m’sana katamanda maoloko.

-Tizidalira abale ndi alongo athu chifukwa

ndi amene amadzatigwira dzanja

tikadzakumana ndi mavuto.

Khalidwe silifanana ndi kudziwika.

-Munthu akhoza kukhala wodziwika koma

wopanda khalidwe.

Miyambi ya Patsokwe

164

Khama lidaphetsa mbewa zapachulu.

-Tikafuna kupeza chinthu tiyenera kuchita

khama kwambiri. Koma tikachita khamalo,

tizidyerera thukuta lathu.

Khasu la apongozi lopanda chimbetete.

-Munthu sungagwiritse ntchito chinthu

chobwereka m’mene umachitira ndi chako.

N’zofanana ndi kubwereka khasu la apongozi

n’kumaona kuti silingakuthandize chifukwa

lilibe chimbetete kapena kuti kachibonga

koswera zigulumwa.

Khasu limaposa amako ndi atate wako.

-Munthu umayenera kumadzidalira pamoyo

wako pogwira ntchito m’malo mokhala mlesi.

Khasu lobwereka silichedwa kuthyoka.

-Chobwereka suchedwa kuchita nacho ngozi.

Khola ndi mathole.

-Khola lodalilika silikhala ndi ng’ombe

Miyambi ya Patsokwe

165

zikuluzikulu zokhazokha. Limafunika

kukhala ndi ng’ombe zazing’ono zomwe

zimatchedwa mathole. Ana ndi tsogolo la

dziko.

Khoswe akakhala pamkhate sapheka.

-Kumakhala kovuta kuti uweruze mlandu wa

m’bale wako makamaka akapezeka kuti iyeyo

ndi amene ali wolakwa.

Khoswe amaluma n’kuuzira.

-Khoswe amati akaluma amauzira kuti

munthu asamve kupweteka kwambiri.

Tikamanena zinthu ndi bwino kumachita

zinthu mozindikira kuti tisakhumudwitse

ena. Mwachitsanzo, tikamapatsa ena

malangizo, ndi bwino kumawapereka

mwachikondi. Kumakhala ngati taluma

n’kuuzira.

Khoswe sagona ndi nyungu.

-Nyungu ndi nthangala za mawungu zomwe

Miyambi ya Patsokwe

166

ena amazigwiritsa ntchito ngati mtedza.

Mwambiwu umatanthauza kuti zinthu

zodana sizikhalira pamodzi. Komanso

sungaike munthu wakuba pamalo omwe pali

zinthu zomwe angabe.

Khoswe wapatsindwi anaululitsa

wapadzala.

-Chinthu china chimatha kuululitsa chinthu

china chomwe chinali chobisika.

Khotekhote ngwa njoka, umatsata kwaloza

mutu.

-Pofuna kumvetsa nkhani ndi bwino kupeza

mutu wa nkhaniyo.

Khotekhote ngwanjira, palinga mtima

mpomwepo.

-Ngakhale njira yopezera chinthu itakhala

yaitali, ngati munthu waikapo mtima

umachipeza.

Miyambi ya Patsokwe

167

Khoza limapita ndi mwini dzanja.

-Sungakakamize munthu kuchita zimene

sakufuna.

Khwangwala wamantha adafa ndi

ukalamba.

-Munthu akasamalira moyo wake amakhala

ndi moyo wautali. Koma tambwali amafa

nthawi yake isanakwane. Munthu wamantha

amakhala zaka zambiri ndi moyo chifukwa

manthawo amamuthandiza kuti asamachite

mphulupulu zomwe zingachititse kuti afe

msanga.

Kodi kuimirira kwakupindulitsa chiyani,

anzako akupindula ndi werawera?

-Tizigwira ntchito molimbika kuti tipeze

zosowa zathu. Polima timawerama osati

kuimirira.

Kodi mtengo wopanda tsinde mudauona?

-Chilichonse chimakhala ndi poyambira

Miyambi ya Patsokwe

168

pake.

Komekome ngwa m’kamwa, kampeni kali

pafunkha.

-Pali anthu ena omwe amasangalala ndi

anzawo pakamwa pokha, koma mumtima

mwawo muli chiwembu.

Komwe wachoka osamatsekako ndi mwala,

koma mayani.

-Ndi bwino kumasiyana bwino ndi anthu

ukamachoka pamudzi, chifukwa tsiku lina

udzabwererako.

Kondwerekondwere samatha, kumbuka zili

kudza.

-Posangalala pamafunika kumaganizira

zam’tsogolo.

Konsekonse mpeni wansengwa.

-Tiyenera kumachitirana zabwino kapena

kumathandizana. Tisamangodikira kuti ena

Miyambi ya Patsokwe

169

azitithandiza ifeyo n’kumangokhala phwi

osawathandiza. Zikatero nawoso amatopa

n’kusiya kutithandiza.

Konza kapansi kuti kam’mwamba katsike.

-Ngati ukufuna kulandira zabwino kuchokera

kwa anthu enaake umayenera kuonetsa

khalidwe labwino kuti anthuwo akopeke.

Munthu ukafuna kuti anthu akuchitire

chabwino, umafunika kuyamba ndiweyo

kuwachitira zabwino.

Kopanda ntchito umataya.

-Chilichonse ndi chaphindu panthawi yake.

Koyenda sawononga pakumwa.

-Munthu ukakhala kwanu si bwino

kumachitira alendo mwano.

Kubala kwa chule ndi kwa thesi

n’kumodzi.

-Mawuwa amatanthauza kuti onse ndi anthu

Miyambi ya Patsokwe

170

ngakhale atakhala kuti ndi osiyana khungu,

chikhalidwe, msinkhu, kukongola ndi zina

zotero.

Kuchedwa kumphero mseche uchuluke.

-Mawuwa amanenedwa akaona kuti azimayi

akuchedwa kubwera kuchokera kumadzi

kapena kuntchini. Amaona kuti kumeneko

amachedwa ndi kunena miseche.

Kuchenjera kwa Kalulu kunaphetsa

Ankhwere.

-Pali anthu ena odziwa kuzunguza lirime

kwambiri, omwe amatha kuika anzawo

m’mavuto ndi zonena zawo. Tiyenera

kuchenjera ndi anthu oterewa.

Kuchenjera kwa Nkhandwe, kolangiza ena

kuti adule michira chifukwa wake waduka.

-Osamapusitsa ena n’cholinga choti nawonso

agwere m’mavuto, kapena kuti mufanane.

Miyambi ya Patsokwe

171

Kuchenjera n’kosadya nako zabwino.

-Munthu wochenjeretsa anzake amadzakhala

pamavuto aakulu anzakewo akasiya kuchita

naye zinthu.

Kucheza sikudzala mtanga (dengu).

-Kucheza kuyenera kukhala ndi malire

n’cholinga choti tigwire ntchito.

Kuchilendo, tema mbamu zofanana ndi eni

nyumba.

-Ukakhala kuchilendo umafunika kumachita

zimene eni ake akuchita.

Kuchiza nthenda n’kuyambiza.

-Kuyambiza n’kuchita zinthu moyambirira.

Kuti munthu athane ndi matenda,

amafunika kuwatulukira akangoyamba

kumene. Akakula amavuta kutuluka

m’thupi. Komanso angathanthauze kuti, kuti

mwana akhale ndi khalidwe labwino

umayenera kumugwira dzanja

Miyambi ya Patsokwe

172

n’kumamutsogolera, akalakwa osalephera

kumupatsa chilango kuti awongoke.

Kuchoka m’chiwaya n’kugwera pamoto.

-Mawuwa amatanthauza kuchoka pa vuto

lina n’kulowa m’mavuto ena aakulu

kwambiri.

Kuchoka muukonda n’kuleza.

-Ukakhala pamavuto si bwino kumakokanso

mavuto ena poyamba kuyankhula

zambirimbiri. Ndi bwino kumadekha kuti

uchoke muukonde wa mavuto

akupanikizawo.

Kuchotsa mbola n’kuzula.

-Kuti munthu achoke m’mavuto, ayenera

kusiya chinthu kapena khalidwe limene

lamuika m’mavutolo.

Miyambi ya Patsokwe

173

Kuchulukana n’kwabwino, kumaipira

kutha msuzi m’mbale.

-Kuchulukana n’kwabwino, kumangoipira

kuti zinthu sizichedwa kutha. Koma

pakakhala ntchito imayenda ndithu.

Kudandaula sikuthetsa m’landu koma

kuyankhulapo.

-M’malo momangodandaula ndi bwino

kuchita khama kuti vuto lathulo lithe.

Kudandaula sikuthetsa njala koma

kusunja.

-M’malo momangodandaula ndi bwino

kuchita khama kuti vuto lathulo lithe.

Kusunja ndi kupempha kwa ena kuti

akuthandize.

Kudumpha dzenje n’kulionera patali.

-Ukadziwa vuto ukhoza kupeza njira

yolipewera.

Miyambi ya Patsokwe

174

Kudya kudamanitsa vimvi mapiko.

-Tisamachedwe kuchita zinthu zimene

zingadzatithandize m’tsogolo. Vimvi

inachedwa kupita kokalandira mapito

chifukwa cha kudya. Pamene imapitako

inapeza mapiko atatha.

Kudya kwa mnzako sungamwere madzi.

-Munthu azidzidalira yekha pogwira ntchito

m’malo modalira ena. Sungamawerengere

kuti chifukwa choti wina wadya ndiye kuti

iwe umwera madzi, madziwo akapeza chiyani

m’mimbamo popeza amadya ndi mnzako!

Nafenso tisamadalire kuti ena agwire ntchito

kuti atithandize, tizichita khama.

Kudya lapi, kulima kwete.

-Pali anthu ena omwe amasangalala

pakudya, koma akauzidwa kuti agwire

ntchito amakana kapena amanamizira

kudwala. Munthu amayenera kudya thukuta

Miyambi ya Patsokwe

175

lake. Kuti munthu apeze chinthu amayenera

kuchivutikira. Ena kuwauza kuti, “Iwe tiye

kumunda,” amayankha kuti, “Ndikudwala

ineeeeee!” Koma kuwauza kuti, “Tiye

kumowa,” uwamva akuyankha kuti, “Bola

ndikhoza kudzikoka.”

Kudya n’kudya, umakumbuka polowa.

-Tikakhala pabwino tisamaiwale kumane

tachokera kapena mavuto omwe takhala

tikukumana nawo.

Kudya n’kudyabe, kumbuka uko

unachokera.

-Tikakhala pabwino tisamaiwale kumbuyo,

tizikumbukira makolo, achibale komanso

aphunzitsi omwe anatithadiza.

Kudya n’kuika.

-Aliyense ayenera kudya zimene wapeza.

Miyambi ya Patsokwe

176

Kudya n’kunyambitira komanso

kunyong’olera.

-Si kulakwa kusonyeza poyera kuti

wakhutitsidwa ndi zimene wachita kapena

wapatsidwa.

Kuti ndidye ndiponda muno, otsala

ngam’kamwa.

-Mwambiwu m’Chichewa chamakono

umanena za munthu amene akunena kuti,

“Kuti ndipeze chakudya ndiponda muno,

sindikusamala zomwe anthu atanene

chifukwa angokhala am’kamwa.” Tisaleke

kuchita zinthu zofunikira poopa

manong’onon’go. Anthu sadzaleka

kunong’ona akaona wina akuchita zinazake.

Kudya pawiri kunang’ambitsa fisi

miyendo.

-Tizichita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi.

Miyambi ya Patsokwe

177

Kudya za m’gomo yankhwangwa, za

m’khasu osadzidya.

-Tiyenera kukhala anthu okhulupirika,

osunga chinsinsi. Pali zinthu zina zomwe

sitingaime pachulu n’kumanena.

Kudyerana masuku pamutu.

-Mawuwa amanena za kuchenjeretsana.

Anganenedwenso ngati wina akuchitira zake

zopanda chilungamo pomuchenjeretsa.

Timanena kuti, “Akumudyera mnzake

masuku pamutu.”

Kudza kwa mafinya ndi minga

pomweponso.

-Mawuwa amanenedwa anthu akagwira

wakuba limodzi ndi katundu amene waba.

Kudzikuza kwa Udzudzu kouza Njovu kuti

ukupanga mdidi.

Kudzikuza si kwabwino. Udzudzu wina unali

pakhutu pa njovu. Njovu imaoloka mulatho,

Miyambi ya Patsokwe

178

ndiye imati ikamayenda, mulathowo

unkangoti teketeke. ndiye kaudzudzu kaja

kananena kuti, ‘Koma ndiye tikutekesa

mulathotu!’

Kudzinga ngati Mtiri, tionera Mende

kutha.

-Mtiri ndi mtundu wina wa mbewa ndipo

mbewayi imakhala yofatsa. Kufatsa

kumawombola. Osamapupuluma ngati

mende wothawa moto, yemwe amaonedwa

ndi osaka mbewa n’kuphedwa. Tizikhazikika

kuti tione m’mene zithu zithere.

Kudziwa kukoma kwa nyama n’kulinga

utaidya.

-Kuti munthu anene kuti chinthu ichi

n’chabwino, amayenera kuyamba wakhala

nacho.

Kudziwa mphafa ya Buluzi n’kung’amba.

-Ngati ukufuna kudziwa bwino nkhani

Miyambi ya Patsokwe

179

inayake, umayenera kufunsa komanso

kukhala wodekha.

Kudziwana n’kutherana thumba lamchere.

-Kuti udziwane ndi munthu umayenera

kukhala naye kwa nthawi yaitali komanso

kuchita naye zinthu zambiri.

Kudziwika sikufanana ndi kukongola.

-Si nthawi zonse pamene munthu angapeze

mwayi chifukwa cha maonekedwe abwino

koma makamaka chifukwa cha khalidwe

labwino.

Kudzudzulana kumamanga mudzi.

-Kulankhulana momasuka kumathandiza

kuti zinthu ziyende bwino pamalo.

Kufa n’komwe, Tambala alira.

-Ngakhale titamwalira sikuti tambala

angasiye kulira. Mwambiwu umatanthauza

kuti tikalakwa, ngakhale tidzikometse kwa

Miyambi ya Patsokwe

180

anthu, chilango chimakhalapobe. Komanso

sikuti zinthu zingaime padzikoli ifeyo

titamwalira.

Kufula sundwe (khwimbi) ndi nzeru.

-Sundwe ndi chakudya chakalekale. Kuti

munthu atulutse chakudya chakele ndiye

kuti anasunga penapake. Choncho, popeza

zamawa sizidziwika, ndi nzeru kumasunga

zoti zidzatithandize pamavuto.

Kufuna Lumbe chifukwa cha mthenga,

koma osadya nyama yake.

-Anthu ena amakukonda chifukwa cha

zabwino zimene uli nazo, zikatha

amakuthawa.

Kufunsa ndi kudziwa njira.

-Ngati sukudziwa zinazake, m’malo

mongozichita, ndi bwino kufunsa kaye kuti

uzichite bwino.

Miyambi ya Patsokwe

181

Kugona m’kuka n’chitatu.

-Mwambiwu umanena kuti kugona m’kuka,

kapena kuti nyumba ya mayi ako, ndi

uchitsiru wotheratu. Munthu akakula

amafunika kudziimira payekha. Choncho, si

bwino kumadalira makolo nthawi zonse kuti

atithandize.

Kugona pakati n’kuyambirira.

-Kuti munthu upeze malo abwino pagulu,

kaya ukukagona kumaliro, umayenera

kufulumira kwambiri. Ndi bwino kumachita

zinthu moyambirira ngati ukufuna

zikuyendere bwino. Pofuna kuchita zinthu

ndi bwino kuzichita mosachedwa.

Kugonagona kumapangitsa tsitsi kufula.

-Mawuwa amatanthauza kuti kukhala ndi

moyo, kapena kuti kugona masiku ambiri,

kumachititsa tsitsi liyere kapena kuti

ukalambe. Akuluakulu ndi amene amadziwa

Miyambi ya Patsokwe

182

wino zapadzikoli. Choncho, ndi bwino

kumawafunsa malangizo pa nkhani

zosiyanasiyana.

Kuika mkute n’kupangana.

-Munthu akamachita zinthu ndi ena, ndi

bwino kumayamba mwapangana,

osamangochita zokomera munthu mmodzi.

Kuipa khope kumaombola.

-Kusakhala wokongola kumapangitsa kuti

upewe mavuto ena. Mwachitsanzo, mtsikana

akhoza kumaliza sukulu chifukwa choti

anthu sankakufunsirafunsira.

Kuipa satsanzirana.

-Si bwino kumatsanzira anzako akamachita

zoipa.

Kuipira mduliro mutu uli wako.

-Pali ena omwe amadulira tsitsi lawo

n’kupezeka kuti sakuoneka bwino.

Miyambi ya Patsokwe

183

Mwambiwu umatanthauza kuti nthawi

zambiri anthufe timaipitsa zinthu zathu

zomwe zinali zokongola poganiza kuti

zikongola kwambiri.

Kuiwala kulibe mankhwala.

-Kuiwala n’kosapeweka.

Kukana chimbudzi n’kuvomera mikodzo.

-Mwambiwu umanenedwa munthu

akamakana chinthu chomwe chili ndi

umboni wodziwikiratu.

Kukana kali kutsaya.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

akukana zinthu zomwe akudziwa kuti

wachita. Nthawi zinanso ena amakana pali

umboni wooneka bwino woti achita

chinthucho ndi iwowo.

Kukana nsalu ya akulu nkuviika.

-Mawuwa amanena za mwana wamwano,

Miyambi ya Patsokwe

184

yemwe wangolandira nsalu ya munthu

wamkulu kuti aichapa koma iyeyo

n’kungoiviika. Atamufunsa ngati wachapa

anawalozera nsalu yomwe wangoviikayo kuti

wachapa. Mawuwa angagwirenso ntchito kwa

munthu wodzichepetsa, anthu

akamamuyamikira kuti wachita bwino. Iye

angayankhe modzichepetsa kuti, “Kukana

nsalu ya akulu n’kuviika.” Akuluakulu

akatituma, si bwino kukana koma

kungochita zomwe tingathe.

Kukankha konjuta.

-Mawuwa amanena za munthu amene

akupereka chifukwa chosamveka bwino

chomwe walepherera kuchita zinazake.

Kukhala awiri si mantha.

-Anthu akakhala awiri amatha kuchita

zinthu modalirana ndipo amatha

kuthandizana wina akapeza mavuto.

Miyambi ya Patsokwe

185

Kuyenda awiri si mantha.

-Anthu akakhala awiri amatha kuchita

zinthu modalirana ndipo amatha

kuthandizana wina akapeza mavuto.

Kukhala kumunda n’kuona ndime.

-Osamangodzichemerera ndi pakamwa

pokha, koma anthu aziona ntchito za manja

athu.

Kukhala kwa eni n’kuomba m’manja.

-Munthu ukakhala kwa eni umayenera

kumalemekeza anthu amene wawapeza.

Kukhala kwa eni ndi kuweteka.

-Munthu ukakhala kwa eni umayenera

kufatsa. Ukamachita matukutuku

amakuthamangitsa.

Kukhala m’chiluli n’kuyambirira.

-Mawu akuti kukhala m’chiluli akutanthauza

kukhala ndi zochuluka. Tisamazengereze

Miyambi ya Patsokwe

186

tikafuna kuchita kanthu. Tisamachedwe

pochita zinthu.

Kukhala owolowa manja n’kulinga uli ndi

kanthu.

-Munthu yemwe alibe kalikonse sangagawire

ena zinthu, nanga azitenga kuti?

Kukhululukira mamina a fodya.

-Anthu amene amafwenkha fodya, amatha

kufwenkhera limodzi ndi mamina

n’kuwakhululukira chifukwa cha fodyayo.

Pamene munthu waitana munthu m’modzi

yekha, ambiri amene sanaitanidwe

angatsatire, choncho woitanayo amanena

kuti, “Ndakhululukira mamina a fodya.”

Mwambiwu ungatanthauzenso kuti kanthu

kakang’ono kakhoza kubweretsa mavuto

aakulu.

Kukoma kwa dziko n’kulinga utakhalako.

-Kukhala ndi umboni weniweni wa chinthu

Miyambi ya Patsokwe

187

n’kulinga utachiona komanso kukhala

nacho.

Kukoma kwa mnzako ndi kamba wako.

-Kuti munthu udziwe khalidwe la munthu,

umafunika kungoyang’ana amene amacheza

nawo. Munthu ukhoza kuweruzidwa

chifukwa cha khalidwe la anzako. Mbiri yako

ikhoza kuipa kapena kukoma chifukwa cha

amene umayenda nawo.

Kukoma ndi kuwonjezera.

-Zinthu zimakongola kapena kukhala bwino

kwambiri ukamazikongoletsa kapena

kuziwonjezera.

Kukondwa ndi kuonetsa mano.

-Kusangalala kwenikweni kumaoneka. Pali

ena omwe amasekerera n’kumaoneka ngati

adya tsabola.

Miyambi ya Patsokwe

188

Kukula mphuno sikudziwa kumina.

-Kuchenjeretsa sikusonyeza kuti munthu

amadziwa zonse.

Kukula mutu si nzeru.

-Nzeru zenizeni zimaoneka ndi zosankha za

munthu, osati chifukwa choti anabadwa kale

kapena ndi wamkulu mutu.

Kukula saimbira maseche.

-Munthu asamadikire kuti ena achite

kumuuza kuti wakula. Ayenera kusintha

yekha n’kumachita zinthu ngati wamkulu.

Kukwatira chiwiri kudakoma.

-Chinthu chilichonse chili ndi poipira ndi

pabwino pake. Mwachitsanzo, munthu

amene wakwatira chiwiri, amati

akamuthamangitsa uku amapita kwinako.

Koma banja loteroro limakhalanso ndi

mavuto osaneneke monga nsanje komanso

kusasonyezedwa chikondi chokwanira.

Miyambi ya Patsokwe

189

Kukwatira mkazi wokongoka

n’chimodzimodzi kudzala mtengo

wamango m’mbali mwa njira.

-Mavuto amene wakwatira mkazi wokongola

ndi munthu amene wadzala mtengo

wamango m’mbali mwa njira, amafanana

chinthu chimodzi: Onse amavutika ndi anthu

akuba!

Kukweza bankha patsekera.

-Munthu sungakweze bankha patsekera,

likhoza kuthyoka. Munthu wamkulu

asamachite zibwana kapena kumasewera ndi

ana.

Kulamula Vumbwe n’kulinga uli ndi

Nkhukhu.

-Munthu usamapalamule kapena kuputa

dala mavuto ulibe pothawira. Kuti ulamulire

anthu umayenera kukhala ndi ndalama

kapena mphamvu.

Miyambi ya Patsokwe

190

Kulanda mwana n’kudyetsa.

-Munthu ungathe kutenga ndi kulera mwana

ngati ungakwanitse kumudyetsa bwino.

Kulanga nyani n’kuphwanya mutu.

-Poweruza mlandu, si bwino kumawiringula.

Umafunika kunena cholakwa chenicheni

chimene munthu wachita. Ukatero

zimakuyendera.

Kulasa mtengo n’chamuna chomwe.

-Mlenje wina anaphonya Njati n’kukhapa

mtengo. Ngakhale anaphonya, komabe

anachita chamuna ndithu. Ndi bwino kuti

nafenso tiziyesetsa kuchita khama pochita

zinthu, zizichita kukanika zokha.

Kulaula n’kuzula m’mera.

-Mawuwa amanenedwa munthu

akayankhula mosabisa mawu kapena kuti

mwatchutchutchu.

Miyambi ya Patsokwe

191

Kulawa kumatha mphika.

-Osamakhala munthu wokomedwa ndi

zinthu chifukwa ukhoza kukumana ndi

mavuto.

Kulemera ndi kudya, ukavala malaya

akubera.

-Palibe amene angakulande chimene wadya,

choncho kulemera ndi mmene umadyera

osati zinthu zimene anthu ena akhoza

kukubera n’kukhala zawo.

Kulemera ndi kudya.

-Kudya bwino n’kumene kungasonyezedi kuti

munthu ndi wolemera. Palibe amene

adzalowe m’manda ndi katundu. Akuba

akhoza kukubera katundu wako koma

sangakubere chimene chalowa m’mimba.

Kuli zii, azimu adutsa.

-Anthu akangoti zii amati azimu adutsa

chifukwa safuna phokoso. Mawuwa

Miyambi ya Patsokwe

192

anayamba chifukwa cha zikhulupiriro zoti

kunja kuno kuli mizimu.

Kulibe manda a mbeta.

-Aliyense amakaikidwa kumanda

akamwalira. Choncho, tisamade nkhawa ena

akamatinena kuti timwalira tisanakwatiwe

kapena kukwatira.

Kulimana pamsana.

-Mawuwa amatanthauza kuchenjeretsana.

Akakhala kuti amene wachenjeretsedwa ndi

mmodzi, amati amulima pamsana.

Kulimbikira mtunda wopanda madzi.

-Mawuwa amatanthauza kulimbikira kuchita

zinthu zomwe sungaphulepo kanthu.

Angatanthauzenso kuwerengera zinthu

zosakhala zenizeni.

Kulinda mdima ndi nthanthi zako.

-Nthanthi ndi nkhani kapena nthano.

Miyambi ya Patsokwe

193

Mawuwa amanena za munthu amene

akungonena nkhani mozungulira mpaka

mdima kugwa. Tikamanena zinthu ndi bwino

tizipewa kunena nkhani mozungulira. Ndi

bwino kumangotumbula.

Kulinji akudza ndi njira.

-Tikamakhala tizikonzekera chilichonse.

Zinthu zimatha kusintha mwadzidzidzi.

Kulirira kuutsi.

-Mawuwa amanenedwa ngati wina

wakumana ndi mavuto chifukwa chosamva

ndiye akuyesa kuphumba anthu m’maso kuti

asadziwe kuti akuvutika chifukwa cha

kusamvako. Amakhala ngati wakhala

pamene pali utsi kuti anthu aziti akulira ndi

utsiwo, chonsecho akulira chifukwa cha

ululu.

Kuliza ng’oma yowambawamba.

-Mawuwa amanenedwa ngati wina wachita

Miyambi ya Patsokwe

194

zimene ena amayembekezera. Kapena ngati

wachita zinthu zimene enanso amafuna.

Mwachitsanzo, mkazi amene wafunsiridwa

zili zoti nayenso amamufuna angavomere

poyankha mwamanyazi kuti, “Mwayimba

ng’oma yowambawamba.”

Kuloza ndi chala.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wina

anachita zinthu zomwe zamubweretsera

mavuto monga kuba kapena kuchita mwano.

Kulumpha dzenje n’kulionera patali.

-Vuto silivuta kuthana nalo ngati walionera

patali. Ndi bwino kumakonzekera

tisanakumane ndi mavuto.

Kumana anzako n’kudzimana wekha.

-Ukathandiza mnzako umakhala ngati

wadzala, mawa adzakuthandiza iweyo.

Miyambi ya Patsokwe

195

Kumana n’kubisa.

-Si bwino kumanamiza ena.

Kumana n’kudzipha.

-Ukathandiza mnzako umakhala ngati

wadzala, mawa adzakuthandiza iweyo.

Kumanda kulibe chisoni.

-Kumanda kumatenga aliyense, kaya ndi

mphawi, wamkulu kapena amene

sanalidyerere dzikoli.

Kumanda kumapita anthuanthu, n’kusiya

zitsiru.

-Anthu abwino sakhalitsa padzikoli.

Kumanda sankira dumbo.

-Mawuwa amatanthauza kuti tikakhala

pamavuto tisamaloze ena chala kuti ndi

amene akuchititsa.

Miyambi ya Patsokwe

196

Kumanda sikupita mtolo wa udzu,

kumapita mtembo wa munthu.

-Kaya munthu amachita zabwino chotani,

tsiku lina adzamwalira n’kupita

kunsabwerera.

Kumanga khobwe ndi m’mawa.

-Pofuna kuchita zinthu ndi bwino kuzichita

mopanda chidodo kapena mosachedwa.

Kumanga mlaza m’maso.

-Pofuna kukwatira pamafunika kulimba

mtima. Umafunika kukhala ngati wamanga

nsalu m’maso kuti usachita manyazi.

Kumanga mwamanga, koma anyamkalere.

-Anyamkalere ndi timaulusi tomwe timangoti

balalabalala munthu akamanga zinazake.

Tiyenera kuonetsetsa kuti chilichonse

chathadi tisananena kuti tamaliza.

Miyambi ya Patsokwe

197

Kumanga nyumba panjira n’kumangira

alendo.

-Apaulendo samatha pakhomo pako

ukamanga m’mbali mwa msewu, amabwera

kudzapempha malo ogona.

Kumanga sumanga kawiri.

-Pali zinthu zina zomwe zimafunika kuzichita

kapena kugwirizana kamodzi kokha monga

kumanga banja.

Kumangitsa madzi m’masamba.

-Nthawi zambiri anthu sasunga malonjezo.

Akachita zimenezi amakhala ngati

akumangitsa mnzawoyo madzi m’masamba

kapena kuti amupusitsa.

Kumangitsa madzi m’mayani.

-Nthawi zambiri anthu sasunga malonjezo.

Akachita zimenezi amakhala ngati

akumangitsa mnzawoyo madzi m’masamba

kapena kuti amupusitsa.

Miyambi ya Patsokwe

198

Kumawerengera mtengo wake.

-Mawuwa anachokera ku zimene Yesu

ananena zoti, “Ndani amene amene akafuna

kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi

kuwerengera mtengo wake?” Ndi bwino

kumakonzekera tikafuna kuchita chinthu

kuti tisachilephere anthu n’kutiseka.

Kumayenda kuti uwone agalu amichombo.

-Ukayenda m’madera ena a dziko umaona

zinthu zachilendo. Si bwino kungokhala

pamodzimodzi. Kumayenda kuti uphunzire

zinthu.

Kumbire adamka nawo kumanda.

-Si bwino kuzolowera kuchitiridwa chinthu

chifukwa udzavutika amene amakuchitirawo

akadzachoka kapena kumwalira.

Kumbire adanka nawo.

-Tisamadalire munthu m’modzi yekha. Ndi

bwino kugawanako mnzeru kuti ena

Miyambi ya Patsokwe

199

akadzamwalira zinthu zisadzaime.

Mwambiwu unachokera pa mawu omwe

anthu ena ankanena akamafuna kuti wina

awafunire mankhwala. Ankangoti,

“Mukatikumbire mankhwala.” Anapitiriza

kupemphabe mpaka munthuyo anamwalira.

Akanakhala anzeru akanafunsa munthuyo

kuti awauze mitengo yake kuti azikakumba

okha.

Kumbuyo kulibe maso.

-Zimene zinachitika kale sitingazisinthe.

Tiyenera kumaganizira zam’tsogolo zomwe

tingazisinthe.

Kumene kutalire n’kunsonga.

-Mawuwa amatanthauza kuti amene atagonje

ndi wamng’ono. Anthu akamamenyana,

amene amayamba kulira ndi ana ndiye

anawo akuyerekezedwa ndi kunsonga.

Mawuwa amanenedwa pamasewera poderera

Miyambi ya Patsokwe

200

ena kuti ndi ana.

Kumeneku n’kukonza chitseko chimera

chitatha.

-Mawuwa amanenedwa poseka munthu

wozengereza. Ena amazengereza kupalira

m’munda. Mbewu zawo zikayamba

kuwonongeka mpamene amayamba kupalira.

Ena angamaone kuti chimera chawo

chikubeda, koma n’kumangonyalanyaza.

Akamaganiza zoti akonze chitseko chawo,

amapeza kuti chimera chija chatha.

Kumira pachipande.

-Mawu okokomeza omwe amatanthauza kuti

munthuyo akunama mopanda manyazi.

Kumva mawu a akulu n’kuchezera.

-Mawuwa amatanthauza kuti, kuti munthu

amve zimene akuluakulu akukambirana

amafunika kukhala maso osagona. Amene

akufuna zinthu zimuyendere ayenera

Miyambi ya Patsokwe

201

kumvera zimene akuluakulu akumuuza

chifukwa aona zambiri pamoyo wawo.

Kumwamba ndi kumwamba, pansi ndi

pansi.

-Tiyenera kumanena zimene tikudziwa osati

zongopeka.

Kunama n’kudzipha.

-Anthu samathandiza munthu wabodza

akakhala pamavuto.

Kunda adafa ndi diwa.

-Kunda ndi mbewa yaikulu. Mbewayi imatha

kufa ndi diwa ngakhale kuti ndi yaikulu.

Kanthu konyozeka kangathe kupweteka

ngakhale munthu wamkulu.

Kunena kuti manda akufewa, n’kuika

munthu ali m’maso.

-Malangizo othandiza amachokera kwa

munthu amene waona zambiri pamoyo wake.

Miyambi ya Patsokwe

202

Kunena kwa ndithendithe Nanthambwe

adadzitengera tsoka.

-Munthu uyenera kumanena utaganiza

bwinobwino, m’malo mongonena kuti nkhani

ithe chifukwa zikhoza kukubweretsera

mavuto.

Kunena kwa ndithendithe Nanthambwe

adazitengera.

-Si bwino munthu kudzitama kapena

kulonjezeratu chinthu zotsatira zake

zisanadziwike kwenikweni chifukwa mwina

zotsatira zake zitha kukuika m’mavuto

kapena kukutsutsa. Si bwino kumafulumira

kuyankhula kapena kuulura zinsinsi za ena

chifukwa ukhoza kupalamula.

Kunena ndi mtima umodzi.

-Mawuwa amatanthauza kunena

mosatsimikiza.

Miyambi ya Patsokwe

203

Kungapande tambala kudzacha.

-Ndi mawu amene anthu amadzilimbitsa

nawo mtima akakhala paulendo. Amadziwa

kuti ngakhale pangapite masiku, koma

adzafika kawo.

Kunja kuli kutali.

-Munthu asamaderere dziko chifukwa dziko

silitha, amatha ndi anthu.

Kunkira nsale n’kumodzi.

-Nsale ukamakula umakulira kofanana.

Nafenso tizichita zinthu mogwirizana

komanso mofanana kwambiri ngati amodzi.

Kuno n’kunja kudayanja lichero.

-Ukalemera usamanyoze anzako, zamawa

sizidziwika.

Kunong’oneza bondo.

-Mawuwa amatanthauza kudandaula

utakumana ndi mavuto chifukwa cha

Miyambi ya Patsokwe

204

kusamva kapena kunyalanyaza machenjezo.

Kunyaza Katumbu n’kuvuula mono.

-Katumbu amakonda kuba msomba m’mono.

Kuthana naye n’kungovuula monowo.

Chimodzimodzinso ndi ena omwe amachita

zinthu zosokoneza monga kuba, kuti uthane

nawo umafunika kumatseka chitseko chako

ndi loko.

Kuolokera pakangaude.

-Kukhala ndi mwayi wopulumuka m’mavuto

mosadziwika bwino.

Kuombera mapira pamutu.

-Kuchenjerera mnzako pomubisira zoyenera

kuchita kapena kusamuuza zoona zenizeni.

Kuona chidameta Nkhanga mpala.

-Kukumana ndi mavuto kapena kukhaula.

Kuona Fisi si kubadwa kale.

-Mawuwa amatanthauza kuti ngakhale

Miyambi ya Patsokwe

205

mwana akhoza kudziwa zambiri kuposa

munthu wamkulu.

Kuona maso a nkhono n’kudekha.

-Kudekha komanso kuugwira mtima

kumathandiza kuti upeze zabwino. Munthu

wofatsa amadziwa komanso kuona zambiri

kuposa munthu wopupuluma.

Kuonda saombezera.

-Ngati takumana ndi mavuto,

tisamathamangire kuloza ena zala.

Kuonerana m’kodi.

-Mawuwa amatanthauza kunyozana,

kudererana kapena kuchitirana mwano.

Kuonerana m’madzi.

-Mawuwa amatanthauza kunyozana,

kudererana kapena kuchitirana mwano.

Kuopa n’kukhala pambuyo ngati mchira.

-Munthu amene akufuna kuchita bwino

Miyambi ya Patsokwe

206

ayenera kuona mmene ena akuchitira.

Kupata kumasiyana.

-Anthu amapeza zinthu mosiyana, ena

amapeza zambiri kuposa anzawo.

Kupata n’kosiyana.

-Anthu amapeza zinthu mosiyana, ena

amapeza zambiri kuposa anzawo.

Kupatsa n’kudzala, kunama n’kukazinga.

-Ukathandiza mnzako umakhala ngati

wadzala, mawa adzakuthandiza iweyo.

Kupatsa n’kuika, kunama n’kukazinga.

-Ukathandiza mnzako umakhala ngati

wadzala, mawa adzakuthandiza iweyo.

Kupatsa n’kuyikiza.

-Ukamathandiza anzako, nthawi ina nawonso

amadzakuthandiza.

Kupempha si kuba.

-Kuuza munthu kuti akuthandize si

Miyambi ya Patsokwe

207

kulakwa.

Kupenya kumwamba n’kukhala ndi

Nkhuku.

-Munthu ukakhala ndi chinthu umayesetsa

kuchiteteza monga munthu akakhala ndi

Nkhuku amayesetsa kuziteteza kwa

Mphamba.

Kupenya pawiripawiri kudathyola khosi.

-Ndi bwino kusankha kuchita chinthu

chimodzi m’malo mochita zambirimbiri

nthawi imodzi.

Kupepera kulibe mankhwala.

-N’zovuta kusintha kapena kuthandiza

munthu wopepera.

Kupha Galu wachiwewe n’kulelemeza

mpini.

-Pofuna kugwira munthu wochenjera

kwambiri pamafunika kumufatsira komanso

Miyambi ya Patsokwe

208

kumutenga bwino.

Kupha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi.

-Kupeza mwayi waukulu kwambiri

mosayembekezereka.

Kupha Mkango ndi kuweteka.

-Pofuna kuchita zinthu pamafunika kufatsa

ndi kupeza nzeru yeniyeni.

Kupha n’kupha umakumbuka poguza.

-Tisanayambe kuchita chinthu tiziyamba

tadzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi zitha bwanji?’

Kupha Njoka n’kudula mutu.

-Kupha njoka kumafuna kuimenya mutu.

Kuthetsa nkhani n’kulinga utadziwa chimene

chayambitsa. Kuti uthane ndi vuto

umafunika kuthana ndi chimene

chikuyambitsa vutolo.

Kupha Njoka n’kumutu.

-Kupha njoka kumafuna kuimenya mutu.

Miyambi ya Patsokwe

209

Kuthetsa nkhani n’kulinga utadziwa chimene

chayambitsa.

Kuphera Nkhumba pamsikiti.

-Kuchitira ena zinthu zosayenera komanso

zolakwika malinga ndi chikhalidwe kapena

mwambo wawo.

Kuphunzira kumakathera kumanda.

-Pa moyo wa munthu pamakhala zambiri zoti

uphunzire ndipo umaphunzirabe mpaka

kudzamwalira. Ena amati kumwalirako ndi

phunzironso palokha. Nanga umakhala kuti

unamwalirapo ngati? Umaphunzirira

pomwepo kumwalira.

Kuphunzira sikutha.

- Pa moyo wa munthu pamakhala zambiri

zoti uphunzire ndipo umaphunzirabe mpaka

kudzamwalira. Ena amati kumwalirako ndi

phunzironso palokha. Nanga umakhala kuti

unamwalirapo ngati? Umaphunzirira

Miyambi ya Patsokwe

210

pomwepo kumwalira. Kungoti kumatha

ukakhala kuti wamwalira.

Kupsa n’kupsa thuza.

-Kawirikawiri zolakwa zazing’ono tikaziikira

mang’ombe zimaoneka zazikulu.

Kupulumukira m’kamwa mwa mbuzi.

-Kupulumuka pa mlandu chifukwa chonena

bodza. Nkhani yake imati, tsiku lina

anyamata awiri anapeza mbuzi itamangidwa

pamtengo wina ndipo anaganiza zoti aibe.

Atangoyamba kumasula chingwe cha

mbuziyo, mwini wake anabwera ndipo

anawafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani

mukumasula mbuzi yanga?” Anthuwo

anayamba kuchita mantha. Koma m’modzi

anati, “Tinaona kuti pano palibe msipu

wabwino, ndiye tinaganiza zoti tikaimangirire

pamtengo uwo. Taonani msipu wake

ukungoti biriwiribiriwiri, kukongola. Zoona

Miyambi ya Patsokwe

211

mbuziyi ife ndi njala msipu uli m’khonde?”

Mwini mbuziyo atamva zimenezi

anawakhulupiriradi. Koma mbuziyo

inkadziwa kuti anthuwo akunama. Ndiye

chifukwa choti sitha kuyankhula, akubawo

anapulumukira m’kamwa mwa mbuzi.

Kuputa ndewu n’kuimirira.

-Munthu amene akufuna kumenyana ndi

mnzake amati akayamba mnzake amaimirira

kuti amenyane naye. Ukamayamba kuchita

chinthu umafunika kukhala ndi zonse

zokwanira kuti izimalizitse. Ukamawaputa

mavuto umafunika kulimba nazo.

Kuputa Vumbwe n’kulinga uli ndi Nkhuku.

-Kuti anthu azikonda kubwera pakhomo

umafunika kumawadyetsa bwino.

Ukamaputa chinthu umafunika kumakhala

ndi podalira.

Miyambi ya Patsokwe

212

Kusadziwa n’kufa komwe.

-Munthu ukakhala mbuli palibe

chingakuyendere.

Kusafunsa kudadyetsa njuchi.

-Kufunsa kumathandiza kuti tisakumane ndi

mavuto.

Kusafunsa kudamwetsa posamba.

-Kufunsa kumathandiza kuti tisakumane ndi

mavuto.

Kusafunsa kudaphikitsa tsabola.

-Kufunsa kumathandiza kuti tisakumane ndi

mavuto.

Kusafunsa kudapsetsa Tambala.

-Kufunsa kumathandiza kuti tisakumane ndi

mavuto.

Kusalowa m’nyumba salumbira.

-Munthu sunganyanyale kuti sudzachitanso

chinthu chomwe chili chofunika kwambiri

Miyambi ya Patsokwe

213

pamoyo wako, monga kulowa m’nyumba

mwako.

Kuseri kulinji?

-Ngakhale mafumu amanyozedwa kumbali.

Munthu sungadziwe zomwe ena amanena

kuseri.

Kuseri kumvenji?

-Munthu ukakhala pawekha zambiri

zimakupita.

Kuseri kutukwanitsa a Chiwere.

-Ngakhale mafumu amanyozedwa kumbali.

Munthu sungadziwe zomwe ena amanena

kuseri.

Kuseri kwecheche, adagwidwa msanasana.

-Pakhalekhale choipa chilichonse chimene

chimachitidwa mseri, chimadzaonekera

poyera.

Miyambi ya Patsokwe

214

Kusiya fumbi.

-Limeneli ndi bodza lonenedwa ndi munthu

nthawi yamavuto. Nthawi zinanso

angatanthauze kupulumuka pamlandu

chifukwa chodziwa kuyankhula mochenjera.

Angatanthauzenso kuthawa ndi liwiro

lalikulu.

Kusiya n’kute n’kulinga utatolatola

masana.

-Mwambiwu umatanthauza kuti munthu

amene amapeza zochepa, sakhala ndi zambiri

zosunga.

Kusochera ndiko kuphera kulupsa.

-Akamati munthu wataika ndiye kuti wachita

zinthu zomwe sumafuna kuchita kapena

walephera kuchita zomwe amafuna.

Kuswa mtedza chokhala n’kwabwino.

-Kuti ntchito igwirike bwino pamafunika

kuifatsira.

Miyambi ya Patsokwe

215

Kutapa nzeru m’thumba la Likongwe.

-Mawuwa amanena za munthu amene

amayamba kaye wafunsa ena asanachite

zinthu. Kuchita zimenezi kumathandiza

munthu kuchita zinthu mwanzeru.

Kutaya udzu womwetamweta.

-Mawuwa amatanthauza kutaya mwayi

wopezapeza.

Kutchena ndi kupirira.

-Kuti atsikana kapena azimayi atchene, kaya

ndi m’mutu, amafunika kupirira ululu.

Mwachitsanzo, ena amapsa ndi livuloni koma

samasiya.

Kutemetsa nkhwangwa pamwala.

-Kutaya mwayi pogwiritsa ntchito chinthu

mosayenera. Mawuwa angatanthauzenso

kukanitsitsa.

Miyambi ya Patsokwe

216

Kukana kwam’tuwagalu.

-Mawuwa amatanthauza kukanitsitsa.

Kutengera zinthu pamgong’o.

-Kutenga zinthu udyo kapena kumva zinthu

molakwika. Si bwino kumazezeduka kapena

kumajijirika kwambiri.

Kuthamanga sikufika.

-Kuchita zinthu mofulumira kwambiri

kumabweretsa mavuto kapena kuwonongetsa

zinthu.

Kuthawa mtswatswa wako womwe.

-Kunamizira kukana chinthu chomwe

wachita ndiwe wemwe.

Kuthawa ndewu si mantha, koma

kusamala mano.

-Kupewa zinthu zobweretsa mavuto ndi nzeru

kusiyana ndi kuzichita n’kupeza mavuto.

Miyambi ya Patsokwe

217

Kuthyola ndiwo n’kuwerama.

-Munthu akafuna kupeza zinthu amafunika

kugwira ntchito molimbika.

Kutola fulu ndi kulawira.

-Ngati munthu ukufuna kugwira ntchito

bwino ndi bwino kulawira.

Kutola khobwe n’kum’mawa.

-Munthu akafuna kuchita chinthu

amafunika kuchichita mwansanga.

Kutola khobwe ndi m’mawa.

-Tisamazengereze tikafuna kuchita kanthu.

Tisamachedwe pochita zinthu ngati omwe

akukolola khobwe, akachedwa khobwe yense

amathera pansi n’kuthetheka. Tikafuna

kugwira ntchito ndi bwino kulawira kapena

kuchita moyambirira n’kufunika.

Kutola nkhwangwa ndi mpini womwe.

-Mawuwa amanenedwa pamene munthu

Miyambi ya Patsokwe

218

wachita mwayi waukulu kwambiri umene

samayembekezera.

Kutola si kuba.

-Kutola kanthu si kuba, koma ukatenga

pakhomo pa munthu osapempha.

Kutsutsa Galu n’kukumba.

-Ngati munthu akukana kuti sanalakwe

pamafunika kukhala mboni yoti imutsutse.

Si bwino kutsimikizira chinthu usadapeze

umboni wokwanira.

Kutsutsa ngomwa n’kuivulira.

-Potsutsa munthu umafunika kukhala ndi

umboni weniweni.

Kutukwana samangira mtanda.

-Munthu uyenera kumachita manyazi

ukapanga chinthu cholakwika.

Miyambi ya Patsokwe

219

Kuuma kwa mutu kumachititsa kuti

pakamwa patsegule m’mimba.

-Anthu opanda nzeru ndi amene

amalongolola kwambiri.

Kuutsa mapiri pachigwa.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

wachititsa kuti anthu ayambane, kaya ndi

apachibale kapena ena adera.

Kuvala khoza ndi kuwolowa dzanja.

-Khoza ndi chibangiri. Kuti munthu avale

chibangiri amafunika kufewetsa dzanja lake.

Kuti munthu azikondedwa kapena

kupatsidwa zinthu amafunika kukhala

wopatsa. Komanso munthu wopatsa sachita

kudikira kuti ena amupemphe kuti

awathandize.

Kuwerengera madzi a mphutsi.

-Mayi wina amawiritsa madzi kuti aphere

mphutsi, koma mlendo ankaganiza kuti ndi

Miyambi ya Patsokwe

220

madzi a nsima. Mawuwa amatanthauza

kuwerengera zinthu zosakhala zenizeni.

Kuwerengera mbewa ndi michira yomwe.

-Kuwerengera ndi zinthu zoti palibe zomwe.

Kuweta Galu ndi kum’ponyera chakudya.

-Mwambiwu umatanthauza kuti kuti munthu

akhale ndi ana kapena anthu ena, amafunika

kuwadyetsa komanso kuwasamalira.

Kuwongola mtengo mpoyamba.

-Kuti munthu akhale ndi makhalidwe abwino

ayenera kuphunzitsidwa kuyambira ali

wam’ng’ono.

Kuyandikana si kuyanjana.

-Kudziwana si kukhala pamodzi ayi, koma

kuyenderana.

Kuyasamula n’kupempha, mwana wa

mfulu adziwa yekha.

-Kuyasamula n’kupempha mosafuna

Miyambi ya Patsokwe

221

kuonetsera. Choncho, munthu wachifundo

amadziwa yekha chochita.

Kuyenda awiri si mantha.

-Anthu mukakhala pagulu mumathandizana

komanso mumalimbitsana mtima.

Kuyenda koma pamodzi.

-Anthu mukakhala pagulu mumathandizana

komanso mumalimbitsana mtima.

Kuyenda m’mawa n’kudya nawo.

-Munthu akafuna kugwira ntchito yake

bwino amafunika kulawira.

Kuyenda n’kupiringizika.

-Paulendo sungadziwe pomwe ukafikire.

Kuyenda n’kuvina.

-Munthu ukakhala kwanu, si bwino

kumachitira mwano alendo, chifukwa tsiku

lina ukayenda udzawapeza ndipo

adzakuchitira zoipanso. Munthu sudziwa

Miyambi ya Patsokwe

222

kuti mawa ukapezeka kuti. N’zotheka kufika

kumene sumaganizira kuti ungafikeko.

Kuyenda ndi kuseri kwa phazi.

-Mawu onena kuti chinthuchi

sindichikhulupirira kuti chingachitike, koma

chikadzachitika ndidzakhala ndi chimwemwe

kwambiri.

Kuyenda usiku si kuona fisi.

-Kuyenda usiku ndi kuyenda ndi mdima

waukulu, kunja kuli zii ndi zoopsa

zosiyanasiyana. Koma si kuti nthawi zonse

amene amayenda usiku amakumana ndi

afisi.

Kuyenda utsi uli tsitu.

-Kuyenda ngati munthu wosazindikira.

Kuyera ndi madzi a nyemba.

-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe

pomwe si zokongola kwenikweni.

Miyambi ya Patsokwe

223

Kuyimba nthungululu pamaliro.

-Ngati munthu sukulongosola mbali yako

pamlandu, anthu sangadziwe kuti ndiwe

wosalakwa. Umakhala ngati ukuimba

nthungululu pamaliro zonse si zimene

umafunika kuchita. Ngati anthu akukuimba

mlandu, umafunika kulira nkhawa zako

zonse.

Kuzima chinutu uzimba ukalipo.

-Chinutu ndi moto womwe alenje amayatsa

pofuna kuvumbulutsa nyama. Nthawi zina

ndi bwino kumazimitsa motowo chifukwa

mawa mudzafunanso kusaka. Tiyenera

kumasamala ndi zinthu zomwe timagwiritsa

ntchito. Komanso, kulemekeza amene

amatisamala ndi chinthu chofunika

kwambiri.

Kuzingwa kwa Kalulu kukapsa.

-Anthu ambiri amakhala osangalala ngakhale

Miyambi ya Patsokwe

224

ndi zochepa zomwe ali nazo. Koma zimene

amadalira monga makolo akamwalira,

amakhala m’mavuto aakulu, osowa nawo

pothawira.

Kwa amake a mwana ndiko kuli madyera.

-Mwana kapena munthu aliyense

amasangalala kwa amayi ake chifukwa mayi

sanganyoze mwana wake.

Kwa ena n’chitsiru, amake ati mwana.

-Makolo amakondabe ana awo ngakhale

atakhala ndi mavuto ena.

Kwa eni kudyetsa nthanga dzungu

ukulifuna.

-Munthu ukakhala kwa eni umakhala

wopanda ufulu wochika kapena kuyankhula

chilichonse chimene ukufuna. Tiyenera

kukhala odzichepetsa tikakhala kwa eni.

Miyambi ya Patsokwe

225

Kwa eni kuika moyo, kuipira kudwala.

-Ukakhala kwa eni umapulumuka zoipa

zochokera kwa abale, koma ukadwala

umakumbukira kwanu.

Kwa eni kulibe “mkuwe,” ukakuwa

wadzikuwira nkhondo.

-Munthu ukakhala kwa eni sumalamulira,

ukachita zimenezi amatha kukuthamangitsa.

Kwa eni kulibe mkuwo, mutu wa nkhuku

n’chiwalo.

-Ukakhala kwa eni umachita zomwe kwanu

sukanachita monga kudya mutu wa nkhuku

pomwe kwanu umadya ziwalo zofewa.

Kwa eni kusunsitsa msuzi ndiwo

ukuzifuna.

-Munthu ukakhala kwa eni umalephera

kuchita zomwe ukadachita uli kwanu.

Miyambi ya Patsokwe

226

Kwa eni uyenda umayeteka.

-Kuchilendo sukhala ndi ufulu wochita

kapena kuyankhula chilichonse chimene

ukufuna.

Kwa eni, kapitolosi umaika m’kamwa.

-Munthu ukakhala kwa eni umakhala

opanda ufulu wochika kapena kuyankhula

chilichonse chimene ukufuna. Tiyenera

kukhala odzichepetsa tikhala kwa eni.

Kapitolosi ndi ndevu za pamlomo.

Kwafa galu kulibe mbiri.

-Munthu wosadziwika akalakwa, choipa

chake sichidziwika kwambiri. Munthu

wodziwika akalakwa, mbiri imapita patali.

Kwagwa chauta.

-Mawuwa amanenedwa kukachitika mliri

womwe wapulula anthu ambiri kapena

kukachitika maliro.

Miyambi ya Patsokwe

227

Kwagwera mtengo wanthambi sikusowa.

-Anthu otchuka akalakwa mbiri imafala

kwambiri, koma osatchuka nkhani yake

sidziwika kwenikweni.

Kwakuchera uname.

-Pali anthu ena omwe kukangocha ntchito

imakhala kunena miseche. Ukanena zabodza

suchedwa kugwidwa.

Kwakula kometa, waperewera kundwe

(pawudala).

-Pogwira ntchito pamafunika anthu

okwanira. Mawuwa amanenedwa ikakhala

kuti ntchito ndi yambiri koma anthu ndi

ochepa.

Kwalusa n’kulinga wina atajiwa.

-Timachenjera kwambiri pavuto ngati wina

zamuonekera.

Miyambi ya Patsokwe

228

Kwanu n’kwanu, m’nthengo mudalaka

njoka.

-Osamanyoza kwanu chifukwa zinthu

zikakuvuta umabwerera kwanu.

Kwanu sikutalika.

-Kwanu kungatalike bwanji, umachita

zotheka kuti ukafikeko.

Kwapsa kwamera, koma kwatsala thengo.

-Zinthu zikachitika sizitheratu,

mwachitsanzo mlandu ukhoza kutha koma

anthu n’kumasungiranabe chakukhosi.

Kwatsala tchire moto umapita komweko.

-Chaona mnzako lero mawa chidzaona iwe.

Kweza Mbawala m’mwamba.

-Osamadziika dala m’mavuto pokhala dala

pamalo oipa kapena kuchita zosayenera.

Miyambi ya Patsokwe

229

L

Ladza dzinja, ana anole mano.

-Mavuto akakupanikiza kumakumbukira

kuti amatha ndipo chisangalalo chimabwera.

Lakoma thendo, nyama ilowa m’mano.

-Nyama ndi yokoma kwambiri koma kuipa

kwake imalowa m’mano. Munthu akakhala

ndi moyo wosalira zambiri savutika.

Lambulire, nawe ndidzakulambulira.

-Zinthu zimayenda mukamathandizana.

Laponda diwa lamphawi.

-Nthawi zina munthu amapeza mwayi womwe

samayembekezera.

Lekani! manong’onong’o adadzutsa njovu.

-Zinthu zazing’ono zimatha kuyambitsa

zazikulu. Mwachitsanzo, phokoso laling’ono

Miyambi ya Patsokwe

230

lingachititse kuti njovu idzuke n’kupha

anthu.

Lende n’kukankhana.

-Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi

bwino kumuchitira zabwino.

Katungwe n’kukankhana.

-Zimakhala bwino kumathandizana.

Lero lomwe lidadetsa Nthengu.

-Nthawi zina ndi bwino kudikira pochita

zinthu chifukwa tikachita mofulumira nthawi

zina zinthuzo sizichitika bwino. Kuchita

zinthu modekha kumathandiza kuti zinthu

zisasokonekere. Mwachitsanzo, nthengu

inkafuna kuti aimalize kuipenta tsiku

lomwelo. Chifukwa chosafuna kubweranso

mawa, anaipaka penti wakuda.

Lero muchira ndi madzi okha.

-Mkuluwikowu umatanthauza kuti pakhomo

Miyambi ya Patsokwe

231

palibe chakudya.

Lero zakumana mbombo zokhazokha.

-Anthu a makhalidwe ofanana akakumana

pamakhala mavuto, palibe angapusitse

mnzake.

Likawomba wotheratu.

-Mwayi ukapezeka, kapenanso ukakhala ndi

nthawi, mpofunika kuchitiratu zomwe

ukufuna kuchita, chifukwa mwina tsiku

lotsatira kudzakhala mitambo. Si bwino

kumachita zinthu mochedwa mwayi

ukapezeka. Ndi bwino kumachitiratu zinthu

mwayi ukadalipo.

Linda madzi apite, kenako uziti “ndadala.”

-Osamapupuluma kunena kuti zinthu zili

bwino, chifukwa pamapeto pake ukhoza

kupusa utakumana ndi mavuto. Si bwino

kudzitama vuto lisanathe.

Miyambi ya Patsokwe

232

Linda mphepo iwombe kuti uone

maliseche a Nkhuku.

-Pakagwa mavuto m’pamene umadziwa

khalidwe lenileni la mnzako.

Lirime ndi nkhondo.

-Mawu akhoza kuyambitsa nkhondo. Ndi

bwino kumaganiza kaye tisanayankhule

kuopera kubweretsa mavuto titayankhula

zopanda nzeru.

Liuma lidakumbitsa Mbewa zapachulu.

-Nthawi zina makani amachititsa kuti

uvutike kwambiri. Mwachitsanzo, kuti

munthu ukumbe mbewa zapachulu

umafunika kukhala ndi mphamvu. Ngati

munthu ukufuna kuchita chinthu monga

kukumba mbewa zapachulu, uyenera

kuchita khama. Kusamva kungachititse kuti

munthu akumbebe mbewazi n’kukhaula.

Miyambi ya Patsokwe

233

Liwiro la mumchenga n’kuyambira

limodzi.

-Ngati ukufuna kuti zinthu zikuyendere

bwino, ndi bwino kuyambira limodzi ndi

anzako.

Liwiro lilibe manyazi, chikakula patuka.

-Sitingathe kulimbana ndi Njovu ikakalipa.

Tiyenera kungothawa basi. Si bwino

kumayesetsa kuchita zinthu zomwe

tikudziwa bwino kuti sizingatheke.

Lonjezo linadulitsa mutu wa Yohane.

-Uyenera kukwaniritsa zimene walonjeza.

Lungalunga mpobadwa, chilema chidza ku

usana.

-Munthu ukhoza kulumala utakula kale.

Munthu akhoza kubadwa ali bwinobwino

n’kukhala ndi chilema atakula kale chifukwa

cha matenda kapena ngozi.

Ungatanthauzenso kuti munthu ukhoza

Miyambi ya Patsokwe

234

kuyamba bwino koma pamapeto pake

n’kusokoneza zinthu.

Lungalunga mpobadwa, chilema chimadza

utakula.

-Munthu ukhoza kulumala utakula kale.

Ungatanthauzenso kuti munthu ukhoza

kuyamba bwino koma pamapeto pake

n’kusokoneza zinthu.

Miyambi ya Patsokwe

235

M

M’bakadya adalinda kwawukwawu.

-Kuzengereza kapena kukomedwa pochita

zinthu kumabweretsa mavuto.

M’bakadyam’bakadya adachoka fumbi lili

koboo.

-Kuumirira zinthu ndi koipa.

Osamakomedwa kuchita zinthu zomwe

tikudziwa kuti zikhoza kutibweretsera

mavuto.

M’chenicheni, mpeni wa Chiwoko.

-Mpeni wa a Chiwoko ndi mpeni wakuthwa

konsekonse. Mwambiwu umanenedwa ngati

munthu waweruza mopanda chilungamo

mlandu wa m’bale wake. Munthu akaweruza

mlandu wa m’bale wakeyo mokondera amati

ndi mpeni wa Chiwoko.

Miyambi ya Patsokwe

236

M’chiuno mwa mwana simufa Nkhuku.

-Mwana ngakhale achite zabwino zotani

sayamikiridwa chifukwa anthu ena amati

mwana sangachite zinthu zopambana.

Mwachitsanzo, mwana akhoza kuvina bwino

kwambiri, koma anthu sangamufupe

Nkhuku. Nthawi zambiri anthu amene

amalimbikira ntchito sadyerera, amadyerera

ndi mabwana awo.

M’dzaonanji adaona Mbawala yake tsiku

lamvula.

-Munthu wonyozeka amadzapeza mwayi

womwe sitinauyembekezere chifukwa choti

wachita khama.

M’dziko la akhungu, wadiso limodzi

amakhala mfumu.

-Anthu olongosokako ndi amene

amalamulira.

Miyambi ya Patsokwe

237

M’kamwam’kamwa mudatha lichero la

mapira osaviika.

-Tisamangofulumira kulonjeza kuti tidzachita

chinachake, chifukwa tikadzalephera

tidzachita manyazi.

M’madzi munanyenga Chule.

-Mawuwa amanena za munthu amene

amadzitukumula chifukwa cha maonekedwe

kapena kudzisamalira kwake, kumangofuna

kukhala wosiyana ndi anzake kumene

wapita.

M’mera m’poyamba.

-Ndi bwino kumachita zinthu moyambirira.

Ngati ukufuna kuti ana ako akule bwino, ndi

bwino kuyamba kuwalangiza kuyambira ali

aang’ono. Kuti tidzakolole zambiri,

timafunika kudzala moyambirira. Kuchita

zinthu moyambirira n’kofunika kwambiri.

Miyambi ya Patsokwe

238

M’mimba ndi m’chipala.

-Ngakhale ana obereka mayi m’modzi amatha

kukhala osiyana m’maonekedwe, makhalidwe

komanso zochita zawo. Pa chipala ndi

pamene amasulira zinthu zosiyanasiyana

monga makasu, mipeni, zikwakwa ndi zina.

M’mphechepeche mwa njovu sapitamo

kawiri.

-Ngati munthu wapulumuka pa vuto

mwamwayi, si bwino kubwereza kuchitanso

zomwezo.

M’mwemo anakhazikitsa tsindwi pakhudu

(pambali).

-Munthu waulesi amawononga zinthu

ngakhale zake zomwe.

M’nyumba mukasowa ufa, sataya mkute.

-Tisamawononge zinthu zathu ngakhale

titakhala pabwino, chifukwa tikhoza

kudzazifuna mawa.

Miyambi ya Patsokwe

239

M’nyumba yamwini saotcheramo mbewa.

-Si bwino kumachita chilichonse chomwe

timachita kwathu tikapita kuchilendo

chifukwa mwina eni akewo sasangalala nazo.

M’thengo saikizamo bowa.

-Munthu ukakhala ndi chinthu ndi bwino

kuchisamala chifukwa ukapusa anzako

akhoza kukutolera.

M’thumba lamwini sapisamo dzanja.

-Osamayamba zinthu podalira ndalama za

m’thumba la munthu wina.

M’thunzi umodzi suthera nkhani.

-Ndi bwino kukhala odekha m’malo

mopupuluma kuti zinthu zina zithe

mwachangu.

M’tsuko sulowa m’chiko, koma chikho

ndicho chimalowa mumtsuko.

-Munthu waudindo ndi amene amapatsidwa

Miyambi ya Patsokwe

240

ulemu, koma iyeyo sachita zimenezo kwa ena

omwe ndi otsika.

M’yang’ana dzuwa adasochera.

-Ngati tikukayika kapena sitikudziwa

zoyenera kuchita ndi bwino kufunsa kuti

tichite zinthu moyenera.

Mabatani akunsana amakumanga ndi

anzako.

-Timafunika kuthandizidwa ndi anthu ena.

Mabingu a mvula anathawitsa mkamwini

kumudzi mvula isanagwe.

-Osamapupuluma kusiya kuchita zinthu

chifukwa cha zinthu zomwe sitikutsimikizira

ngati zingachitikedi.

Machokero a pabwalo.

-Munthu akatsanzika kuti akubwera

kukatenga chinachake ndiyeno osabweranso,

anzake amanena kuti, “anangonama kuti

Miyambi ya Patsokwe

241

akukatenga chinthu, anali machokero a

pabwalo.”

Madoli (matodwe) adafera mchenga

woyera.

-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe

zili zosathandiza kwenikweni.

Madoli anafera mchenga woyera.

-Pali zinthu zina zomwe zimaoneka zabwino

zomwe pambuyo pake zikhoza kutiika

m’mavuto.

Madzi adzadza, mlamba usangalale.

-Munthu ukapeza zinthu zabwino umafunika

kusangalala.

Madzi akataika sawoleka.

-Zinthu zikataika kapena zikasokonekera,

zimakhala kuti zasokonekera basi.

Madzi amachuluka ndi a m’njira.

-Zinthu zazikulu zimayamba

Miyambi ya Patsokwe

242

pang’onopang’ono, monga mtsinje

umadzadza ndi madzi a m’ngalande.

Madzi amakoma akakhala m’chinkho,

koma akakhala mumtsinje amapha.

-Pali zinthu zina zoopsa zikakhala malo ena

kapena zikakhala zambiri.

Madzi apamwala amatunga ndi amene

walawira.

-Ukafuna kuchita chinachake umafunika

kuchita zinthu mofulumira. Ulesi

umamanitsa zambiri.

Madzi apamwala watunga walawira.

-Ukafuna kuchita chinachake umafunika

kuchita zinthu mofulumira. Ulesi

umamanitsa zambiri.

Madzi n’kulubza, mchenga upita pansi.

-Mawu onenedwa ndi anthu awiri odziwana

kuti amuchenjerere munthu wina.

Miyambi ya Patsokwe

243

Madzi odikha ndi amene amalowa pansi.

-Munthu waphee ndi amene amakhala ndi

maganizo akuya kapena oopsa.

Madzi oyera umasambira kumutu, akuda

kumapazi.

-Alendo mumawapatsa zabwino, zinazo

zimakhala zanu.

Madzi saiwala khwawa.

-N’kovuta munthu kuleka chizolowezi chake.

Si bwino kuiwala makolo kapena zinthu zina

zofunika.

Madzi saiwala mkolokolo.

-Si bwino kuiwala makolo kapena zinthu zina

zofunika. Angatanthauzenso kuti zimakhala

zovuta kuiwala zimene unazolowera.

Mafukufuku sayenda, imayenda ndi

nyama.

-Ngati wafunsira mkazi amayembekezera kuti

Miyambi ya Patsokwe

244

uzimuyendera kuti adziwe kuti

umamukondadi. Munthu akabwereka

ngongole umamupitira kwawo chifukwa

kawirikwawiri sangabwere kudzakupatsa

ndalama yako.

Mafuta amagwera pa anzake.

-Ulemerero umabwera pamene pali ulemerero

kale. Mwayi umakupeza uli pabwino kale.

Magulugulu a mvula anathawitsa

mkamwini kumudzi mvula isanagwe.

-Si bwino kumataya mtima msanga

tikakumana ndi mavuto kapena tikamva

zinazake zokhumudwitsa. Tisamapupulume

kuchita zinthu tisanamvetse bwino nkhani.

Magwiragwira amapha manja.

-Kugwiragwira kumabweretsa mavuto.

Maimvaimva adathawitsa zolo paukwati.

-Mamveramvera amabweretsa zowawa. Ndi

Miyambi ya Patsokwe

245

wino kuchita zinthu zimene ukuona kuti

zikuthandiza m’malo momvera anthu ena.

Maimvaimva amapha makutu.

-Si bwino kumangokhulupirira zonena za ena

tisanafufuze bwinobwino.

Makale sapangana adalira m’thumba.

-Pamakhala chinthu choululitsa zobisika

kapena zachinsinsi.

Makale sapangana.

-Mawuwa amanenedwa pamene anthu awiri

apita kumlandu asanapangane kapena

kugwirizana chokanena.

Makani sawombola munthu.

-Kumva zako zokha kukhoza kuika munthu

pamoto. Munthu amayenera kumamva

malangizo a ena. Mwayi umakupeza uli

pabwino kale.

Miyambi ya Patsokwe

246

Makasu akalira ndiye kuti alipo awiri.

-Tiyenera kumathandizana ngati tikufuna

kuti tichite zakupsa.

Mako ndi mako angachepe mwendo.

-Osamanyoza makolo ngakhale atakhala kuti

ndi osaoneka bwino. Chikondi cha pachibale

sichitha.

Mako ndi mako usawaone kuchepa

mwendo.

-Osamanyoza makolo ngakhale atakhala kuti

ndi osaoneka bwino. Chikondi cha pachibale

sichitha. Tizipereka ulemu kwa makolo

ngakhale ali onyozeka.

Makolo amasamalira ana mano awo

akamamera, ana amasamalira makolo

mano awo akayamba kuguluka.

-Ndi bwino kumasamalira makolo chifukwa

nawonso anavutika kutisamalira tili ana.

Miyambi ya Patsokwe

247

Makolo atsoka amati, “ndinadya chiyani

ine kuti ndibereke chitsilu ngati

chimenechi?”

-Pali ana ena omwe ngakhale tiwalele bwino,

amatha kuyamba zawo n’kusokonekera.

Makondamakonda, Buluzi anakonda

khonde.

-Zokonda zimasiyanasiyana, choncho

mnzathu akamakonda zinazake, tisamuseke

chifukwa zokonda zathunso zikhoza kukhala

zoseketsa kwa anthu ena.

Makutu achitirana nsanje.

-Sizingatheke kumamvetsera munthu ndi

khutu limodzi, linalo n’kumamvetsera wina.

Umafunika kumvetsera m’modzi kaye.

Kuchita zinthu ziwiri sikuthandiza.

Makutu sakhuta ndi kumva, maso sakhuta

n’kuona.

-Sitingakwanitse kupeze zonse zimene

Miyambi ya Patsokwe

248

timaona kapena kumva. Ndi bwino

kumakhala okhutira.

Malawalawa anapha milomo.

-Tiyenera kuchenjera ndi zinthu zomwe

timakonda chifukwa pamapeto pake

chikhoza kutiika m’mavuto.

Maliro m’mbale.

-Mawuwa amatanthauza ndiwo za nyama.

Maliro n’kulirana.

-Zovuta zikachitika kapena mavuto akabwera

timayenera kuthandizana.

Malonda amakoma ndi kugulana.

-Zinthu zimayenda bwino anthu

akamathandizana.

Malonda ali m’maso.

-Munthu umafunika uyambe kaye waona

malonda usanagule.

Miyambi ya Patsokwe

249

Malonda amakoma ndi n’kuikira (banyira).

-Wamalonda akamapereka banyira, anthu

ogula amamukonda.

Malonda ndi m’maso, pakamwa

pamangotenderera.

-Munthu ukamafuna kugula kanthu

umafunika uchionetsetse m’malo

mongotengeka ndi zimene otsatsa malondawo

akunena.

Malunje sadya Sakhwi.

-Tisaope tikafuna chinthu chifukwa cha

kuwopsedwa ndi maonekedwe a chinthucho.

Si bwino kuopa kunena vuto lathu kuti

anthu atithandize.

Mamveramvera amapasula banja.

-Osamangotengeka ndi zonena za anthu.

Mamveramvera anachotsa zolo paukwati.

-Kumangomvera zonena za anthu kukhoza

Miyambi ya Patsokwe

250

kutitayitsa mwayi. Komanso potumiza anthu

kuti akatiyimire, tizitumiza okhulupirika kuti

nkhani isasokonekere.

Manda a mkonzi sakhala akuya.

-Nthawi zina ngakhale munthu ukhale

wabwino chotani pamudzi anthu sayamika.

Munthu wina wokumba manda ankathandiza

anthu pakachitika maliro. Koma atamwalira

anthu anangokumba moti athane nazo ndipo

anangolekera m’maondo.

Manda sakana maliro.

-Manda alibe tsankho, amalandira olemera

ndi osauka omwe.

Mankhwala a utsi n’kuthawa.

-Munthu ukafuna kupewa zinazake kapena

ngati zinazake sizikukusangalatsa ndi bwino

kungochokapo.

Miyambi ya Patsokwe

251

Mankhwala amalimba ndi chizimba.

-Mawuwa amatanthauza kuti mlandu

umazengedwa bwino pakakhala mboni

kapena umboni wooneka bwino.

Mano a Ng’ona umawaona bwino uli

m’kamwa mwa Ng’onayo.

-Ndi mano ochepa omwe amaonekera

pakamwa pa ng’ona. Kungakhale kupanda

nzeru kusuzumira kuti uone mano onse a

ng’onayo chifukwa ikhoza kukuika m’kamwa.

Si nzeru kumachitabe zinthu zomwe

zingatiike m’mavito.

Mano kunamiza.

-Mawuwa amanena za munthu yemwe

amakusekerera koma mumtima akukufunira

zoipa.

Mano saona umphawi.

-Ngakhale munthu akhale wosauka,

amafunikabe kudya. Zoti zithu zikuvuta

Miyambi ya Patsokwe

252

kupeza, mano alibe nazo ntchito.

Manong’onong’o amapha ubwenzi.

-Miseche ikhoza kulekanitsa mabwenzi

apamtima.

Mantha ali n’kuseka, ukali uli ndi maliro.

-Pamene munthu wachita mantha amathawa

kuti adzipulumutse. Koma akalimba mtima

kuthawira panja amakadyedwa ndi chilomo.

Mantha anadyetsa n’nombwe.

-Chifukwa cha kuopa zirombo anthu ena

amaopa kukasaka nyama ndipo

amangodyera zopanda pake ngati masamba a

n’nombwe. Munthu ukamaopa kugwira

ntchito yomwe ingakuthandize umphawi

umakukwatira.

Manunkhanunkha amapha mphuno.

-Mawuwa amanenedwa pofuna kukhazika

mtima anthu pansi, kuti asamangozunguzika

Miyambi ya Patsokwe

253

ndi zilizonse.

Manyazi adapha Lambe.

-Lambe ndi mbewa yomwe sinkafuna

kutuluka kunja chifukwa cha manyazi moti

inafa ndi njala. Tisamachite manyazi kuchita

zinthu zofunika.

Manyazi anapha kamba.

-Ukamasowa chinachake umafunika kulimba

mtima. Kuchita mantha kapena manyazi

kungachitise kuti tizingovutika ngati mmene

kamba amachitira kumangobweza mutu

wake m’chikamba chifukwa cha manyazi.

Manyazi ndi mantha, anakwatitsa mkazi

wadiso limodzi.

-Mnyamata wina anakwatira mkazi wa diso

limodzi chifukwa chochita manyazi

kumuyang’anitsitsa. Munthu usanafunsire

kapena kuchita chinachake chofunika

kwambiri, umafunika kufunsa ena komanso

Miyambi ya Patsokwe

254

kuonetsetsa kuti wakhutira nacho.

Manyi akale sanunkha.

-Zinthu zakale nthawi zina zimakhala zoti

zinkagwira ntchito panthawiyo. Tiyenera

kumatsatira zatsopano.

Mapanga awiri avumbwitsa.

-Kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi

kumachititsa kuti zonse ziwonongeke.

Sungachite zinthu ziwiri nthawi imodzi.

Mwambiwu umanena za munthu amene

anapita m’phanga lina n’kukaona kuti

kukudontha kenako n’kuganiza zopita kwina.

Atafika kumeneko anaona kuti bolanso

kujaku. Ananyamukanso ulendo wa koyamba

kunja, ndipo ali m’njira ananyowa.

Mapenyapenya amapha maso.

-Tisamangotengeka ndi zilizonse zimene

tikuona chifukwa tikhoza kuona zosaona.

Kuyang’anayang’ana zinthu kumabweretsa

Miyambi ya Patsokwe

255

mavuto.

Mapesi kumunda alinda moto.

-Anthu olimba mtima amafunika

kuwasamalira bwino kuti zikativuta

atithandize.

Mapundi amadya n’chika.

-Munthu wamphulupulu amalangika

chifukwa cha zochita zake. N’chika ndi

Swiswiri ndipo anthu a mphulupulu amadya

Swiswiri chifukwa chosamva.

Mapundi amaphwanya mpini.

-Olima mwamphamvu kwambiri amatha

kuthyola mpini. Chimodzimodzi munthu

wovuta kapena wandewu amakumana ndi

mavuto chifukwa cha zochita zakezo.

Masamba auma.

-Mwambiwu umanenedwa pamene munthu

wina waphwanya pangano.

Miyambi ya Patsokwe

256

Masewera anabala mwana.

-Nthawi zina zinthu zangati zongocheza

zimatha kubweretsa mavuto aakulu. Ndiye

ukaona kuti zayamba kusokonekera, ndi

bwino kungochoka.

Masewera sakhala paulimbo.

-Osamachita chibwana ndi zinthu zomwe

zikhoza kutiika m’mavuto.

Masiku adalinda tsiku kufula.

-Masiku akachuluka umakumana ndi

mavuto ena. Umangofunika kulimbana nawo

basi ndipo zimakuyendera.

Masiku adameta Nkhanga mpala.

-Nkhanga inayembekezera kwa nthawi yaitali

kuti pangano loti ikametetse likwaniritsidwe.

Ndi bwino kumasunga pangano lanthu.

Masiku adatsutsa buthu.

-Munthu akalakwa koma osafuna

Miyambi ya Patsokwe

257

kuvomereza, nthawi imafika ndipo

zimaululika.

Masiku ali pakamchira kanyama.

-Munthu usamataye mtima kuti zimene

ukufuna zidzachitika kalekale chifukwa

masiku sachedwa kutha.

Masiku amaoletsa njovu.

-Nthawi ikamapita, ngakhale zinthu

zamphamvu komanso zazikulu kwambiri

zimatha kutha.

Masiku amatha n’kugona.

-Tikamayembekezera chinthu timafunika

kuugwira mtima chifukwa masiku sachedwa

kutha.

Masiku amathera kuchitseko.

-Masiku sachedwa kupita. Ukamakumana

ndi mavuto ndi bwino kudekha chifukwa

masiku amavutowo akatha zinthu zikhoza

Miyambi ya Patsokwe

258

kukuyendera.

Masiku anadya atakumana.

-Ngakhale munthu atachita zoipa mwanseri,

tsiku lina zimazadziwika ndipo amachita

manyazi.

Masiku ndi ambiri, ubweya wa nyama

kuchepa.

-Tisamataye mtima nsanga, zabwino zili

m’tsogolo.

Masiku sakoma onse.

-Nthawi zina timakumana ndi mavuto ndipo

pena timakumana ndi zabwino.

Kukumbukira mfundo imeneyi

kungatithandize kuti tisamade nkhawa

kwambiri zikativuta.

Maso a nyama ngofiira, sachedwa

kutembenuka.

-Zinthu zimatha kusintha nthawi iliyonse,

Miyambi ya Patsokwe

259

choncho tikakhala pabwino tizikumbukira

kuti zinthu zimatha kusintha nthawi iliyonse.

Maso a usiku anagona ndi wakhate.

-Pali zinthu zina zomwe sitingazidziwe,

mwachitsanzo chifukwa cha m’dima, munthu

wina anagona ndi mzimayi wakhate.

Osamasankha kuchita zinthu usanazimvetse

bwinobwino.

Maso achule saopsa ovula nyanda.

-Tisamaope kuuza ena mavuto amene

tikukumana nawo kuti atithandize. Ngati

tikudziwa zoonadi pankhani inayake si bwino

kuchita mantha kunenepo.

Maso akhuta, m’mimba muli njala.

-Zokhumba zimakhala zambiri koma zomwe

umapeza zimakhala zochepa.

Maso akutali, nyani anadzipha ndi mpeni.

-Tsiku lina nyani anaona mlenje akuika

Miyambi ya Patsokwe

260

mpeni mthumba. Ndiye nayenso atatola

mpeni ndipo ankafunanso kuchita

chimodzimodzi koma m’malo mwake

anadzibaya pamimba n’kufa. Phunziro lake

ndi loti tiziyamba taonetsetsa bwinobwino

tisanatengere zochita za ena.

Maso ali ndi dumbo (njiru).

-Maonekedwe okha sangatiuze zambiri za

chinthu. Sitingadziwe khalidwe la munthu

pongomuona koma zimadalira kucheza naye

n’kumudziwa bwinobwino.

Maso alibe mpanda.

-Maso akhoza kuona chilichonse, kaya ndi

chabwino kapena choipa. Mawuwa

amanenedwa ngati wina akunena kuti waona

zinazake zoipa, ndiye potsutsa winayo amati

maso alibe mpanda.

Miyambi ya Patsokwe

261

Maso alibe kuti uku n’kwa apongozi.

-Maso amangoona chilichonse, ndipo nthawi

zina amaona zinthu mwangozi.

Mwachitsanzo, akhoza kupezeka kuti

mwangozi aonera apongozi.

Maso amaipitsa, kamwa limakonza.

-Choipa m’maonekedwe nthawi zina

chimakhala chokoma ukachidya. Kuyang’ana

mbali imodzi monga kukongola kumapusitsa

koma mnzeru komanso zoyankhula.

Maso apatali amawongola mtengo.

-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe

pomwe si zokongola kwenikweni.

Maso apatali, phiri limakhala losalala,

ukaliyandikira si zigwembe zake.

-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe

pomwe si zokongola kwenikweni.

Miyambi ya Patsokwe

262

Maso apatali mkango ukunga nyani.

-Chinthu chikakhala patali sichidziwika

bwino. Tiyenera kuchiyandikira kuti tichione

bwinobwino.

Maso ndi madiwa.

-Nthawi zambiri timatengeka ndi zinthu zoipa

kapena zabwino chifukwa choti taziona.

Mwachitsanzo, ena amachita chiwerewere

chifukwa choti aonera zolaula.

Maso ndi msampha.

-Nthawi zambiri timatengeka ndi zinthu zoipa

kapena zabwino chifukwa choti taziona.

Mwachitsanzo, ena amachita chiwerewere

chifukwa choti aonera zolaula.

Maso ngati kapachike.

-Umbombo si khalidwe labwino. Mawu

okuluwika otanthauza kuti akasunge

chakudyacho mpaka alendo atapita.

Miyambi ya Patsokwe

263

Maso saadya.

-Kuona chinthu sindiye kuti uchitenga

kapena uchiwononga. Mawuwa amanenedwa

munthu akamanena kuti akungofuna kuona

sikuti atenga chinthucho.

Maso sakhuta.

-Maso sakhutitsidwa ndi zimene umaona.

Tisalole kuti atipusitse.

Maso sakhutsa n’kupenya.

-Kumangoyang’ana zinazake sikungathandize

kuti chitheke koma kugwira ntchito. Mawuwa

anganenedwenso kwa munthu amene

sakhutira ndi zimene ali nazo. Maso

amangofunabe kuti aone zina zatsopano.

Maso samangira mpanda.

-Maso akhoza kuona chilichonse, kaya ndi

chabwino kapena choipa. Mawuwa

amanenedwa ngati wina akunena kuti waona

zinazake zoipa, ndiye potsutsa winayo amati

Miyambi ya Patsokwe

264

maso alibe mpanda.

Matako saleka kuperesana.

-Pamene pali anthu sipalephera kukangana

kapena kusemphana chichewa.

Matako sangatsogole ngakhale

atafunitsitsa bwanji.

-Matako amakhala kumbuyo basi, akhoza

kufuna kutsogola koma kwawo n’kumbuyo.

Si bwino kumayesa kuchita zinthu zomwe

sizingatheke.

Matama a Kambuzi.

-Makani opanda ntchito kapena ongofuna

pofera.

Matenda amabwera pagalimoto koma

amachoka wapansi.

-Matenda amabwera kamodzin’kamodzi koma

amachedwa kuti achoke.

Miyambi ya Patsokwe

265

Matenda bisani, maliro tidzamva.

-Munthu sungathe kubisa zimene zikuchitika

pamoyo wako chifukwa tsiku lina

zidzamveka. Ndi bwino kuuza ena mavuto

athu kuti atithandize. Osamabisa zinthu

zimene simungakwanitse kuzibisa.

Matukutuku a pida.

-Mawu amenewa amanenedwa kwa anthu

omwe ndi opanda mphamvu koma

n’kumachita makani kuti akhoza kulimbana

ndi adzitho.

Matumbo a Nkhuku amafinyidwa paokha.

-Osamadzitama pagulu chifukwa tsiku lina

zoipa zako zimadzaululika n’kuipitsa mbiri

yako yonse.

Matupa akumana.

-Anthu amakani okhaokha akakumana

sakuna kugonjerana pokhapokha wina

awalanditse.

Miyambi ya Patsokwe

266

Maungu amafuwa pali moto.

-Amenewa ndi mawu amene anthu amanena

mwana wa makolo abwino akakhala

wamakhalidwe oipa.

Maungu kubalira kumphuno.

-Mawawa amanenedwa munthu

akamadandaula kuti zabwino zabwera

mochedwa.

Mavu anapangana kuning’a pamimba.

-Ndi bwino kumachita zinthu mogwirizana.

Ngakhale kuti pangano limavuta kusunga

nthawi zina, komabe tiziyesetsa kusunga

zomwe tagwirizana popewa kukhumudwitsa

ena.

Mavuto saona nkhope.

-Aliyense kaya ndi wabwino, wokongola kaya

wotani, amakumana ndi mavuto.

Miyambi ya Patsokwe

267

Mavuto sasowa.

-Kulikonse kumapezeka mavuto, palibe

angawathawe.

Mavuto si maliro okha.

-Pali zinthu zina zomwe zimasowetsa

mtendere kwambiri ngati imfa, monga

kusamvera kwa ana komanso zina.

Mawa ndi lero lomwe.

-Mwambiwu anthu amaunena popempha

ngati kunena kuti ndi bwino

mungondibwereka chifukwa mawa ndi lero

lomwe, si kalekale.

Mawere awirirana.

-Mawuwa amanenedwa ngati anthu

apachibale sakugwirizana. Mawere kapena

kuti mabere amafunika kumakhala limodzi

pamtima, koma ngati atakula kwambiri

amayamba kupanikizana.

Miyambi ya Patsokwe

268

Mawonekedwe amapusitsa.

-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe

pomwe si zokongola kwenikweni.

Mawu a akulu amakoma akagonera.

-Mawu amene munthu wamkulu wanena

amadzaoneka kuti anali othandiza pakapita

nthawi. Ndi bwino kumawatsatira.

Mawu a chitsiru amakoma akagonera.

-Mawu onenedwa ndi munthu wooneka ngati

wopusa amadzakhala othandiza m’tsogolo. Si

bwino kumanyoza malangizo a anthu ooneka

monyozeka chifukwa nthawi zina amakhala

othandiza.

Mawu a munthu m’modzi ndi chisa cha

njuchi.

-Ndi bwino kufunsa ena ukamva zinazake

m’malo mofunsa m’modzi chifukwa nthawi

zina amangooneka okoma koma liri bodza.

Miyambi ya Patsokwe

269

Mawu a akulu amakoma akagonera.

-Mawu a akulu amakumbukiridwa pakapita

nthawi ndiponso pamene zomwe amanena

zachitikadi.

Mawu abwino saiwalika.

-Mawu oona samalephereka, amachitikadi.

Komanso mawu abwino, omwe munthu

wanena amakumbukiridwa kwa nthawi

yaitali.

Mawu akuseri.

-Mawu achinsinsi. Anthu amanena mawu

amenewa m’malo monena kuti mawu

achinsinsi kapena mawu ena omwe anthu

amanena kuseri, mwina kujeda munthu.

Mawu amakoma kuti naye mdzakazi

azikondwa.

-Mawu okoma amasangalatsa aliyense.

Tiyenera kukhala osamala ndi zomwe

timanena kuti tisakhumudwitse ena.

Miyambi ya Patsokwe

270

Mawu mpoyamba, otsiriza m’mang’ombe.

-Ndi bwino munthu kusamala mawu oyamba

omwe ukufuna kuyankhula chifukwa ndi

amene anthu omvetsera amawerengera kuti

ndi zomwe wanena.

Mawu ndi mphepo, sungawatchere

msampha.

-Tifune tisafune mawu ayenera kupita

kulikonse.

Mawu ndi ng’oma.

-Tizichenjera ndi zimene timanena chifukwa

tikayankhula sabwerakonso.

Mawu ndi oyamba, otsiriza ndi

mang’ombe.

-Pa nkhani, mawu oyamba ndiye amakhala

nkhani yeniyeni, obwera pambuyo pake

amangokhala mang’ombe.

Miyambi ya Patsokwe

271

Mawu ngotsogoza (ndi oyamba).

-Munthu akalephera kunena zoona pamene

wafunsidwa ndiye kuti ndi wolakwa. Tiyenera

kumayamba kaye taganiza bwino

tisanayankhule.

Mawu okoma anatulutsa Ng’azi kumphako.

-Anthu ena akafuna kuchitira ena zoipa

kapena akamafuna kuwabera amayankhula

zosyasyalika, zokokomeza kuti apusitse

munthuyo. Tiyenera kuchenjera ndi anthu

amenewa.

Mawu okoma ndi kamba, oipa ndi ndulu.

-Mawu abwino amabweretsa mtendere, oipa

amayambitsa ndewu, mikangano komanso

nkhondo.

Mawu okweza ndawamva, am’munsi ndi

nkhondo.

-Mawu abwino amawakweza, oipa

amawang’ung’udza kuti ena asamve.

Miyambi ya Patsokwe

272

Mawu osiyiza adaombola Kalulu.

-Nthawi zina anthu akatifunsa kuti tifotokoze

nkhani tiyenera kukamba nkhani

modzigwira, osangonena chilichonse

pokhapokha ngati pakufunika kutero.

Mawu oswera mpanje (ng’oma) adautsa

Fisi.

-Pakakhala mlandu ndi bwino kungonena

zolakwazo, koma ukayamba kufotokoza

zidani zimene zinalipo kale, umatosa zambiri.

Mawu oyamba anaphetsa Kalulu.

-Munthu ukafuna kuti umve zambiri

umafunika kukhala woleza mtima,

osamangotengeka ndi zinthu zomwe

sunazimvetse.

Mawu salawa, amalawa ndi chakudya.

-Osamayankhula moyerekeza ngati

ukuwalawa kaye.

Miyambi ya Patsokwe

273

Mayankhayankha a pabwalo anatalikitsa

Sakhwi mlomo.

-Poyankhula tizisamala, osamangochulukitsa

mawu osafunika.

Mayendayenda amapha mapazi.

-Kuyendayenda kapena kuthamangathamana

kumabweretsa mavuto mwinanso imfa.

Anthu amatha kumwalira chifukwa mapazi

awo anawatengera malo olakwika.

Mayendayenda amapha miyendo.

-Kuyendayenda kapena

kuthamangathamanga kumabweretsa

mavuto nthawi zina.

Mbalame ikakhala pauta silasika.

-Zimakhala zovuta kuweruza mlandu wa

m’bale wako.

Mbalame ikakula siikhala paphira.

-Munthu wamkulu ayenera kukhala ndi

Miyambi ya Patsokwe

274

khalidwe, monga munthu wamkulu osati

ngati mwana.

Mbalame ikatera pauta silasika.

-Kumakhala kovuta kuti uweruze mlandu wa

m’bale wako makamaka akapezeka kuti iyeyo

ndi amene ali wolakwa.

Mbalame yagwa pa uta.

-Zinthu zavuta, zimakhala kuti zavuta basi.

Mbalame yakwawo ndi yakwawo, siiwala

kwawo.

-Palibe angaiwale kwawo ngakhale kutakhala

kutali bwanji.

Mbalame yamchira imamveka ikalira.

-Munthu waluso amadziwika ndi zimene

amachita.

Mbalame zamthenga zofanana zimamwera

chigoba chimodzi.

-Anthu ochita zofanana amayendera limodzi.

Miyambi ya Patsokwe

275

Mbalame zofanana nthenga zimayendera

limodzi.

-Anthu ochita zofanana amayendera limodzi.

Mbalame zomwera chigoma chimodzi

zimadziwana mthenga.

-Anthu a khalidwe lofanana amadziwana

komanso kuchitira zinthu limodzi.

Mbaliwali idabutsa chimoto.

-Zinthu zazing’ono zikhoza kuyambitsa

mavuto aakulu ngati mmene kamoto

kakang’ono kamayambitsira chomoto

chachikulu n’kuotcha nkhalango yonse.

Mbawala siimwa madzi Galu ali kumbuyo.

-Munthu sangachite bwino chinthu, anthu

ena akamamusowetsa mtendere.

Mbawala yamantha idapota nyanga.

-Mantha amapulumutsa, umapewa mavuto

omwe anakakubweretsera imfa.

Miyambi ya Patsokwe

276

Mbeta silola tsiku limodzi.

-Sungafunsire mbeta n’kukulola koyamba.

Tiyenera kukhalabe opirira ngati tikufuna

kupeza zabwino.

Mbewa yamanyazi inafera kuuna.

-Mbewa ina sinafune kutuluka kuuna

kuthawa utsi chifukwa cha manyazi ndipo

inafera komweko. Tisamachite manyazi ndi

anthu ena pakakhala zofunikira kuchita.

Mbewa zikachuluka siziika masa.

-Pa ntchito pakachuluka anthu, ntchitoyo

siyenda.

Mbewa zikachuluka sizitsekera.

-Anthu akachuluka ntchito siyenda bwino.

Aliyense amangosiyira mnzake.

Mbewa zikatha amanona ndi aswiswiri.

-Zinthu zabwino zikatha, zotsikirapo ndi

zimene zimakhala zofunika.

Miyambi ya Patsokwe

277

Mbiri ndi ng’oma.

-Mbiri imafalikira mwansanga kwambiri ngati

ng’oma.

Mbiri ya mnzako saimira pachulu.

-Osamayalutsa mnzako ponena zimene

amalakwitsa kwa aliyense.

Mbiya ikasweka siibwereranso, ndikafa

ndafa ndatha.

-Chinthu chikaonongeka chimavuta

kuchibwezereretsa, monga munthu akafa

wafa basi.

Mbiya ikasweka siiwumbikanso.

-Zinthu zina zikachitika, zachitika zatha.

Sizingabwererenso ngati kale.

Mbombo ndi mwala, mtengo umataya

mayani.

-Mwala sutaya kanthu. Koma mitengo

imataya masamba. Mwambiwu umanena za

Miyambi ya Patsokwe

278

munthu womana, yemwe safuna kugawira

ena zinthu. Munthu wotero amangokhala

ngati mwala.

Mbumba n’kudyetsa.

-Munthu ukakhala ndi ana kapena achibale

umafunika kumawasamalira.

Mbumba ndi anthu onse.

-Tiyenera kumasamalira achibale onse

mosasankha.

Mbuto ya Kalulu idakula ndi tadzaoneni.

-Mbuto kapena kuti malo okhala Kalulu

amakhala aang’ono. Anthu atabwera kuti

adzawaone, inakula chifukwa

chopondaponda. Zinthu zazing’ono zimakula

zikamanenedwanenedwa chifukwa anthu

amawonjezerapo bodza.

Mbuzi ikacheuka yasiya mwana.

-Tiyenera kumachita zinthu tikakakhala ndi

Miyambi ya Patsokwe

279

zifukwa zomveka zochitira zinthuzo monga

kujomba kuntchito, kusiya ntchito komanso

zina.

Mbuzi ikalawa zamchere sisiya.

-Mbuzi ikalawa zinthu zokoma sisiya,

imavuta koopsa. Chimodzimodzi ndi munthu

amene wayamba khalidwe linalake,

zimamuvuta kuti asiye. Amakhala ngati

walawa zamchere.

Mbuzi ndi mkota.

-Akuluakulu ndi ofunika pamudzi chifukwa

amakhala aona zambiri pa moyo wawo. Ana

amatengera zimene makolo awo amachita.

Mbuzi ya gudu imafikira kumunsi.

-Khalidwe loipa limachititsa kuti munthu

alangidwe. Tizichita zinthu mosamala kuti

tisapalamule.

Miyambi ya Patsokwe

280

Mchenga woyera unathetsa madondwe.

-Pali zinthu zina zomwe zimaoneka zabwino,

koma pambuyo pake zimabweretsa mavuto

aakulu.

Mchepera wa Kalulu, mtima ndi phiri.

-Nthawi zina anthu onyozeka kapena ovutika

amakhumba zikuluzikulu.

Mdima umasaka.

-Pamene walakwira makolo masana, umatha

kuthawa. Koma kukada umapitanso kwa

makolo ako n’kukalangidwa. Cholakwa

sichithawika, nthawi imafika ndipo munthu

amalandira chilango cha zimene wachita.

Mdima wa dzinja udakwatitsa mkazi

wonyansa.

-Zinthu zina zikamachitika zimaoneka ngati

tsoka, koma nthawi zina zimabweretsa

mwayi. Mwachitsanzo, mkazi wonyansa

adakwatiwa chifukwa cha mdima wa dzinja.

Miyambi ya Patsokwe

281

Mdima wamadzulo umathyola mwendo.

-Tisamayende ndi anthu oipa chifukwa

akhoza kutipaka mavuto.

Mesewera sachedwa kubala ndewu.

-Ukaona kuti macheza kapena masewera

akulowera kwinakwake koipa, ndi bwino

kungochokapo chifukwa nthawi zina

masewera abwinobwino kapena macheza

amatha kusintha n’kukhala ndewu ya mtima

bii.

Meta mpala opanda madzi.

-Mawuwa amatanthauza kuchenjeretsa

munthu kotheratu.

Mfiti idzafanso.

-Munthu ngakhale woipa bwanji amafabe.

Mfiti Kuliritsa.

-Munthu amene amalira kwambiri pamaliro

ndi amene nthawi zina amakhala kuti wapha

Miyambi ya Patsokwe

282

munthuyo.

Mfiti yaikazi kulimba moyo.

-Anthu amene amakhulupirira za ufiti amati

mfiti yaikazi ndi imene siimva chisoni popha

munthu.

Mfiti yaikazi kuuma mtima.

-Anthu amene amakhulupirira za ufiti amati

mfiti yaikazi ndi imene siimva chisoni popha

munthu.

Mfiti zimadziwana.

-Anthu okonda zofanana kaya zabwino

kapena zoipa amadziwana.

Mfulumira adameza nsima yamoto.

-Tisamafulumire kuchita kapena kunena

kanthu chifukwa chotengeka. Chifukwa tsiku

lina tikhoza kudzanena kapena kuchita

chinthu chomwe chingadzatibweretsere

mavuto.

Miyambi ya Patsokwe

283

Mfulumira anadya gaga.

-Kuchita zinthu mofulumira kwambiri

kumapangitsa kuti munthu apeze mavuto

kapena awononge zabwino zonse.

Mfulumira sachedwa kugwa m’mbuna.

-Kufulumira kapena kupupuluma

kumagwetsera munthu m’mavuto.

Mfumu n’kudzala.

-Amfumu pamudzi kapena pantchito

amakhala ngati kudzala chifukwa nkhani

zonse zimakathera kwa iwo.

Mfumu ndi mbatata, ukaongola wathyola.

-Nthawi zambiri anthu omwe ndi otchuka

kapena audindo waukulu amavuta

kuwalangiza. Ukalimbana nawo umakumana

ndi mavuto ndi iweyo.

Mfumu ndi nkhuti.

-Munthu wamkulu kapena mfumu imadziwa

Miyambi ya Patsokwe

284

zinthu zambiri zomwe sangaziulule

wambawamba.

Mfumu sidyera kuwiri.

-Mfumu poweruza nkhani siyenera

kukondera. Komanso si bwino kudikira kuti

ena atichitire zabwino chifukwa choti

amatidziwa, chifukwa akadzachoka tidzasowa

kulowera.

Mfumu sikoma kuwiri.

-Mfumu poweruza nkhani siyenera

kukondera. Komanso si bwino kudikira kuti

ena atichitire zabwino chifukwa choti

amatidziwa, chifukwa akadzachoka tidzasowa

kulowera.

Mfumu yandewu simanga mudzi.

-Atsogoleri olongolola kapena okonda ndewu

amapweteketsa anthu awo. Anthu akaona

kuti mtsogoleri wawo ndi woipa amasamuka

pamudzi ndipo mudzi umapasuka.

Miyambi ya Patsokwe

285

Mfuti yolasa woombera.

-Nthawi zina zinthu zako zomwe, monga

agalu ndi zina ndi zimene zimakupweteka.

Mimba imodzi siibala nkhoswe.

-Anthu apachibale ayenera kumakondana,

chifukwa pamawa pamadzabwera zinthu

zomwe ungadzafune kuti abale ako

akuthandize. Kuchulukana n’kofunika.

Mimba ndi mtengakako, phewa ndi

mtengakaeni.

-Munthu ukakhala ndi chuma umafunika

kumachidya, apo ayi amadzachichecheta ndi

ena.

Mimba ndi yanji?

-Mayi akakhala ndi pathupi sitimadziwa kuti

mwana amene adzabadwe adzakhala wotani.

Si bwino kumawerengera zinthu zimene

sizinachitike.

Miyambi ya Patsokwe

286

Mimba njosadzitamira.

-Si bwino kumadzitama chifukwa cha zinthu

zomwe sizinachitike. Mwachitsanzo, mayi

akakhala ndi pakati, sayenera kudzitama

mpaka atabereka.

Mimba simapha namwino.

-Namwino amangothandiza munthu kuti

abereke. Ngakhale zitavuta bwanji, sangafe

chifukwa cha mimba ya munthu wina.

Amangofunika kuthandiza munthuyo basi.

Chimodzimodzi pamlandu, ngati tafunsidwa,

tiyenera kusachita mantha polongosola

zimene tikudziwa chifukwa mimba si yathu.

Minga ikabaya, zula.

-Ukakumana ndi mavuto ndi bwino kupeza

njira yothetsera mavutowo.

Minga ya pansana amakuzula ndi mnzako.

-Pali zinthu zina zomwe sitingakwanitse

tokha. Timafunika kuthandizidwa ndi ena.

Miyambi ya Patsokwe

287

Miphika yaphulana.

-Nthawi zambiri anthu okondana amadziwa

zimene mnzawo akusowa. Kuthandizana

n’kofunika.

Misala si chamba chokha.

-Pali zinthu zambiri zimene zingachititse kuti

munthu akhale mwanjira inayake.

Mwachitsanzo, munthu akhoza kudwala

misala chifukwa cha matenda osati kusuta

chamba.

Miseche ilinda mwini.

-Anthu akamanena za ena amafunika

kusamala chifukwa akhoza kuwapezerera

n’kumva zonse.

Mitengo yoyandikana imaperesana.

-Anthu akakhala pamodzi salephera

kuyambana.

Miyambi ya Patsokwe

288

Mivi sumaponya yonse.

-Poyankhula osamaneneratu zonse chifukwa

kusanenako kukhoza kudzakupulumutsa

m’tsogolo.

Mjedo umalinda mwini.

-Anthu akamanena za ena amafunika

kusamala chifukwa akhoza kuwapezerera

n’kumva zonse.

Mkamwini asamakule mwendo.

-Mkamwini ayenera kukhala wofatsa

pamudzi m’malo momavuta kapena

kulamulira ena.

Mkamwini mnzako mpachulu, mtengeze

uta.

-Ndi bwino kumathandizana mnzathu

zikamugwera, chifukwa mwina mawa

zidzagwera ife. Ndiye ndi bwino

kumathandizana.

Miyambi ya Patsokwe

289

Mkamwini ndi Mlamba, sachedwa

kuterereka.

-Akamwini komanso anthu ena ofunika

pantchito tiyenera kuwasamala chifukwa

tikawachitira nkhanza amachoka n’kutisiya

tikuvutika.

Mkamwini sadya gaga, likadza dzinja

mpatse.

-Ngakhale munthu wodyada akavutika,

muthandize mosayang’ana za kunyada

kwakeko.

Mkamwini sawiringula.

-Ngakhale mkamwini aziona zovuta pakhomo

sayankhula. Choncho, tiyenera kuonetsetsa

kuti tikuwachitira zabwino.

Chimodzimodzinso pantchito.

Mkamwini wankhuli adathira thendo la

inswa pansanamira.

-Tiziyamba taonetsetsa tisananyanyale

Miyambi ya Patsokwe

290

kuchita zinthu, chifukwa nthawi zina

tikanyanyala timataya zabwino.

Mkamwini waumbombo anakabisa mtolo

wa mapira kumadzi.

-Tikakhala ndi zinthu ndi bwino

kumagawirako ena chifukwa tikapanda

kutero zimawonongeka.

Mkanda wako ndi umene uli pakhosi.

-Timafunika kumakhutira ndi zomwe tili

nazo.

Mkango ukazingwa umadya udzu.

-Ukakhala pamavuto susankha, kunyada

umakusiya kaye apo, n’kuyesetsa kuchita

chilichonse kuti uthandizike.

Mkazi m’modzi diso limodzi, akazi awiri

maso awiri.

-Munthu ukakhala pamitala sukhala

pamavuto kwambiri ngati mkazi m’modzi

Miyambi ya Patsokwe

291

wamwalira. Mwambiwu umatanthauza kuti

ukakhala ndi podalira pawiri suvutika

kwenikweni pamodzi pakavuta.

Mkazi mmodzi ndi diso lopsinya.

-Si bwino kudalira chinthu chimodzi,

chifukwa zikavuta umasowa pogwira.

Mkazi ndi chitenje, chimathera pakhomo.

-Mkazi amayenera kukhala pakhomo

n’kumasamalirapo bwino.

Mkazi si m’bale wako.

-Nthawi zambiri ukakwatira umakonda

kwambiri mkazi wako. Ena amafika

pomanyoza achibale. Koma banja likatha

limawawasa kwambiri moti anthu ake

amafika polakalaka wina atamwalira kuti

asadzamuonenso. Chikondi chimatha banja

likatha.

Miyambi ya Patsokwe

292

Mkazi wa mfumu akati mlomo tololo,

wataya mudzi.

-Ngati mkazi wa mfumu ndi wolongolola,

zinthu zimasokonekera m’mudzi. Koma

akakhala wofatsa zinthu zimayenda bwino.

Mkazi wa mfumu asamati khutu petupetu.

-Mkazi wa mfumu asamakhale wamabodza

chifukwa akhoza kunamiza mwamuna wake

n’kupasula mudzi. Mkazi wa mtsogoleri

ayenera kukhala wodziletsa.

Mkazi wophika msima yosazizira.

-Mawuwa amanenedwa potamanda mkazi

amene amalandira bwino alendo powaphikira

chakudya chabwino. Mwamuna wakenso

amalandiridwa bwino akapita kwa anzake,

m’mawu ena nsima imene anaphika ija

imakhala ngati ikutenthabe.

Miyambi ya Patsokwe

293

Mkhalamba msana, usiku ndi

kamnyamata.

-Maonekedwe amapusitsa. Anthu ena

amaoneka abwino pamaso, koma kuseri ali

zilombo.

Mkoma akadadza.

-Pali anthu ena omwe amaonetsa

makhalidwe abwino akakhala kuchilendo,

koma akakhazikika amayamba kuonetsa

mawanga awo enieni.

Mkuntho umodzi supha njoka.

-Pofuna kuchita zinthu pamafunika khama,

osati kungochita kamodzi kokha.

Mwachitsanzo, ngati ukufuna kulangiza

munthu kuti asiye khalidwe loipa,

umayenera kuchita khama, apo ayi njoka

imene ili mwa iye singafe.

Mkwita umodzi sulira m’mwendo.

-Mkwita ndi chibangiri cha m’mwendo.

Miyambi ya Patsokwe

294

Chikakhala chokha sichimalira. Zinthu

zimayenda bwino kwambiri pakakhala anthu

ambiri. Mudzi umatchuka chifukwa cha

zochita za anthu onse.

Mlamumwako ndi Likongwe, akalowa

mphanga koma kumutsekera ndi

masamba.

-Ukamuthandiza mnzako amene ali

pamavuto ndiye kuti wamutsekera ndi

masamba. Koma ukakana kumuthandiza

ndiye kuti wamutsekera ndi mwala. Ena

akatilakwira tiziwakhululukira.

Mlandu sagula ndi chipanda cha mowa.

-Si bwino kuweruza mlandu mokondera

chifukwa choti wina watipatsa ziphuphu.

Mlandu sugwera pamtengo.

-Kulikonse anthu amalakwirana ndipo palibe

amene salakwa. Choncho zikachitika ndi

bwino tizikhululukirana.

Miyambi ya Patsokwe

295

Mlandu suwola.

-Ngakhale munthu atathawira kutali, mlandu

wake amadzaupeza patapita zaka zambiri.

Munthu akapalamula amakumana ndi

zotsatira za zimene wachita kaya afune

asafune.

Mlandu uli m’kamwa.

-Kuyankhula mosasamala kukhoza

kutibweretsera mavuto. Mpofunika

kumayamba taganiza kaye tisanayankhule.

Tisakhale a zikachitika mumvera kwa ife.

Mlatho wathyoka, tsopano tiwoloka

bwanji?

-Mawuwa amatanthauza kuti gwero la

chithandizo chathu laphwera, ndiye tikhala

moyo bwanji?

Mleleni bwino aiwale kwawo.

-Pakhomo pakakhala akamwini kapena

alendo timafunika kuwasamalira bwino kuti

Miyambi ya Patsokwe

296

asamadandaule n’kukumbukira kwawo.

Mleme anangowola, sanaike maliro.

-Mleme umakhala ngati zinthu ziwiri, khoswe

komanso mbalame. Mleme utadwala unapita

kwa mbalame ndipo zinakana kumulandira.

Kenako unapita kwa makoswe ndipo

nawonso anamukana. Mlemewo utafa palibe

anaika maliro ake moti anangowolera

pamtunda. Munthu wopanda anzake enieni

amasowa omuthandiza.

Mlendo ndi amene amadza ndi kalumo

kakuthwa.

-Mpofunika kumamva maganizo a alendo

chifukwa mfundo zawo zikhoza kukhala

zothandiza kwambiri. Mlendo akhoza

kuthandiza pa vuto limene eni mudzi ali nalo.

Mlendo ndi mame, sachedwa kulakatika.

-Tisamachite nkhanza ndi alendo chifukwa

sakhalitsa. Komanso umbombo

Miyambi ya Patsokwe

297

umaonongetsa zambiri. Nkhani yake imanena

kuti, kalekale panali mayi wina dzina lake

Nasiketi. Nasiketi anali kudziwika kwambiri

chifukwa cha umbombo. Tsiku lina anavuula

mphale, ndipo atasinja ufa anaganiza kuti

ndiwo zimene adyere nsima tsikulo zikhale

nyama. Anasinjadi ufa wosalala bwino

ndiponso anapezadi nyama yonona bwino

imene anakagula pamudzi woyandikana ndi

mudzi wawo. Pa nthawiyi Nasiketi anali

asanataye matsukwa a mphale ija. Akumaliza

kuphika nsima anamva panja munthu wina

akuodira. Poonetsetsa anaona kuti ndi

mlendo amene sanali kumuyembekezera. Apa

nzeru zinamuthera Nasiketi. Ananyamula

nsima ndi kuika pamphika wa nyama uja

kenako n’kuika mphika wa nyama ndi nsima

ija pakamwa pa mtsuko umene munali

matsukwa uja. Tsoka ndi ilo nyama ndi

nsima ija zinagwera m’matsukwa muja.

Miyambi ya Patsokwe

298

Atatuluka panja kuti akumane ndi mlendo

uja, mlendoyo anamuuza kuti, “Pepani ndi

wosakhalitsa, ndimafuna mundigawireko

madzi akumwa.” Mlendoyo atamwa madziwo

ananyamuka n’kumapita.

Mlendo ndi mame, sakhalitsa.

-Tisamadane ndi alendo kapena

kumawachitira umbombo, chifukwa

sachedwa kubwerera kwawo.

Mlendo ndi Nkhuku yoyera.

-Mlendo amafunika kusamalidwa bwino.

Mlendo ndi nkhungu, sachedwa kupita.

-Tizilandira bwino alendo chifukwa sachedwa

kupita.

Mlendo ndiye amapha njoka.

-Mlendo ndi amene amathandiza pamavuto

ena kapena kupereka mfundo yothandiza

kwambiri.

Miyambi ya Patsokwe

299

Mlendo sathyola mphasa.

-Alendo sawononga zinthu zambiri, choncho

tisamachite mantha kulandira alendo.

Sangamalize mphasa yathu pongogonera

usiku umodzi wokha.

Mlenje wa misampha amafa ndi msampha.

-Munthu amene amachita zoipa zinazake

monga kuba, amadzafa ndi khalidwe

lomwelo.

Mlirira kwawo andanka ndi madzi.

-Kuthamanga sikufika. Tisamathamangire

kuchita zimene tikufuna chifukwa mapeto

ake tikhoza kukumana ndi mavuto.

Mlomo wakumwamba ndi wakunsi, pho!

-Mwambiwu umanenedwa pamene munthu

wapandikizidwa ndi mafunso ndiye akusowa

choyankha.

Miyambi ya Patsokwe

300

Mluzu wa agalu ndi umodzi.

-Munthu wanzeru sadikira kuti amve

uthenga wakewake. Pa zochitika zina monga

maliro kapena msonkhano timafunika

kuchita zinthu mofulumira komanso

mogwirizana.

Mmene ndalimira ndi msana wanga

sindingalephere kudyapo.

-Munthu amayenera kusangalala ndi ntchito

imene wagwira komanso zimene wazivutikira

kuti azipeze.

Mnyanga sulemera mwini.

-Ana kapena abale ako ngakhale atakhala

ovuta kapena olumala timafunika tisatope

nawo chifukwa amadalira ifeyo basi.

Mnzako akakuchenjeretsa pogona, iwe

umuchenjerere podzuka.

-Ngati mnzako ali ndi luso linalake lomwe iwe

ulibe, uyenera kulimbikira zimene umachita

Miyambi ya Patsokwe

301

wino kuposa iyeyo.

Mnzako akakutema mphini kumbuyo,

iwenso umuteme kumbuyo.

-Mnzathu akatithandiza, ndi bwino

kudzamuthandizanso akadzavutika m’malo

mobweza chipongwe.

Mnzako akakuti konzu, nawe umam’ti

konzu.

-Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi

bwino kumuchitira zabwino.

Mnzako akapsa ndevu m’zimire.

-Tizithandiza anzathu akakhala pamavuto

chifukwa tsiku lina tidzawafuna.

Mnzako akapsa ndevu mzimitse, mawa

adzazimitsa zako.

-Mnzako akakhala pamavuto muthandize

chifukwa mawa akhoza kudzakuthandiza

iweyo.

Miyambi ya Patsokwe

302

Mnzako ali pomwe (mnzako akakhala

pafupi).

-Mwambiwu umanena za munthu amene

amaoneka ngati mnzako akakhala pafupi,

koma akangokhala kumbali amayamba

kukunena miseche.

Mnzako si amene umadya naye n’kukhuta,

koma amene amati zikavuta amabwera

n’kudzakuthandiza.

-Mnzako weniweni amaonekera pamavuto.

Monga mphuno, maso amatakataka.

-Tisamachite zinthu modzionetsera.

Osamasonyeza anthu kuti ifeyo ndiye abwino

kwambiri kuposa ena.

Moto umapita kwatsala tchire.

-Zikagwera ena, dziwa kuti watsala ndi iwe.

Ndi bwino kumathandizana kuti nawenso

zikakuvuta adzakugwire mkono.

Miyambi ya Patsokwe

303

Moto wapathupi sakuuza ndi mnzako.

-Vuto limene ukukumana nalo umalidziwa

wekha, suchita kudikira kuti ena akuuze.

Moto wopanda masekera umavuta kuyaka.

-N’kovuta kuweruza mlandu popanda mboni.

Mowa m’chimera.

-Pochita zinthu pamafunika luso logwiritsa

ntchito zinthu zofunika kuti zinthu ziyende

bwino.

Mowa n’kumwera pamodzi.

-Kuchitira zinthu limodzi n’kumene

kungachititse kuti anthu asangalale

kwambiri.

Mowa n’kumwerana.

-Kuti chibale chilimbe pamafunika

kuyenderana komanso kuthandizana.

Moyo kunyenga.

-Munthu ukakhala ndi thanzi labwino

Miyambi ya Patsokwe

304

umakhumba utachita zambirimbiri komanso

umatha kunyoza abale ako kuiwala kuti

tsiku lina udzadwala.

Moyo ndi mpamba, usamalireni.

-Kuti munthu achite chilichonse amafunika

kukhala ndi moyo.

Moyo saika pachiswe.

-Tiyenera kupewa kuchita zinthu zomwe

zingaike moyo wathu pangozi.

Moyo samanga ndi njerwa.

-Mwambi wosonyeza kuti umafunika kudya

kuti ukhale ndi thanzi.

Moyo uli ngati anyezi, timausenda

tikulira.

-Moyo ndi wovuta kwambiri. Masiku ambiri

amatha munthu akuvutika.

Miyambi ya Patsokwe

305

Moyo uli ngati moto, umafunika

kusonkhezera.

-Kuti zikuyendere umafunika kumasamalira

moyo wako.

Moyo wanga ndi kambiya, ndisunga

ndekha.

-Palibe munthu angakusamalire moyo wako

koposa mwini wakewe.

Moyo wanga ndi mbiya, ndisunga ndekha.

-Munthu aliyense amasamalira moyo wake,

choncho zikakuvuta suyenera kuloza

munthu wina chala chifukwa udindo

wosankha zochita pamoyo wako ulinso

m’manja mwako.

Moyo wathombozi wouma kumodzi.

-Thombozi ndi mtengo womwe umauma

mbali imodzi n’kukhala moyo mbali imodzi

koma suferatu. Mawuwa amatanthauza kuti

ngakhale tili moyo, koma tikukumana ndi

Miyambi ya Patsokwe

306

mavuto ambiri.

Mpandamachokero, mkamwini anachokera

mamina.

-Kumakhala ndi chifukwa chenicheni

pochoka pamalo monga kuchikamwini

kapena pantchito. Osamagwiritsa ntchito

zifukwa zosamveka.

Mpandamachokero, anakodzera moto wa

ana.

-Kumakhala ndi chifukwa chenicheni

pochoka pamalo monga kuchikamwini

kapena pantchito. Osamagwiritsa ntchito

zifukwa zosamveka.

Mpani wa mbewa utsatira mwini.

-Munthu aliyense amalimbikira kuchita

zinthu zake. Amaonetsetsa kuti zachitika

bwino kwambiri koposa mmene akanachitira

za ena. Ungatanthauzenso kuti choipa

chimatsata mwini. Ukapalamula, ngakhale

Miyambi ya Patsokwe

307

utathawa kapena patapita nthawi yaitali

bwanji, tchimo wachitalo limakulondola,

ndipo kenako limakuluma.

Mpatse fupa mwana atonthole.

-Nthawi zina ndi bwino kumalolera kuti ana

achite zofuna zawo. Ndi bwino kumaloleza

maganizo kapena zimene anthu ena akufuna

kuti aphunzirepo kathu.

Mpatseni tione chakhalitsa galu pakhomo.

-Pamudzi pakakhala mapokoso kapena

mavuto ena, timafunika kuonetsetsa kuti

tidziwe chimene chayambitsa vutolo.

Mpeni ulibe bwenzi.

-Munthu akakhala woipa sakhala ndi bwenzi

ndipo anthu amamuopa kuti tsiku lina

angadzawachitire zachipongwe. Mpeni

umatha kupha ngakhale mwini wa mpeniwo.

Miyambi ya Patsokwe

308

Mpeni wakuthwa konsekonse.

-Munthu wokonda kukometsa kuwiri,

mthirakuwiri. Munthu wotereyu amati

akapita uku, amakatapa nkhani kumeneko

n’kupita kukazikhuthura kwina.

Amachitanso chimodzimodzi ndi zimene

wamva kumeneko.

Mphamba ikasowa Nkhukhu imatola udzu.

-Ukakhala pamavuto susankha, kunyada

umakusiya kaye apo, n’kuyesetsa kuchita

chilichonse kuti uthandizike.

Mphamvu za Ng’ona zili kumchira.

-Anthu audindo amakhala ndi mphamvu

chifukwa cha anthu omwe akuwalamulira.

Choncho, ayenera kumalemekeza anthuwo.

Mphamvu zimaphetsa.

-Kudzitukumula kumabweretsa mavuto.

Ukakhala ndi mphamvu kumalemekeza ena

chifukwa tsiku lina ungadzakumane ndi wina

Miyambi ya Patsokwe

309

wamphamvu kuposa iweyo n’kukumenya.

Mphawi dziko alidyera ku uchi.

-Ngakhale munthu wosauka, anthu ena

amamuitana kuphwando ndipo amadya nawo

zabwino. Kuthandizana n’kofunika.

Mphawi nayenso ndi mzimu,

musamunyoze.

-Munthu aliyense ayenera kulemekezedwa

ngakhale wosauka.

Mphechepeche mwa Njovu sapitamo

kawiri.

-Ngati tapulumuka pa zoopsa, monga kwa

Ng’ona padziwe, si chanzeru kubwereranso

chifukwa mapeto ake tikhoza kugwidwa

n’kulephera kudzipulumutsa.

Mphemvu m’dyera kum’thiko.

-Mawuwa amanena za munthu wosauka

yemwe amapeza zinthu movutikira monga

Miyambi ya Patsokwe

310

chakudya ndi zina.

Mphenzi siimenya mtengo kawiri.

-Pali zinthu zina zomwe zimachitika kamodzi

kokha pamoyo wa munthu. Choncho ndi

bwino kumagwiritsa ntchito mwayi umene

tapeza.

Mphepo yakumpoto indachititsa

mkamwini kuba m’munda mwa apongozi.

-Umphawi kapena mavuto ena chisamakhale

chifukwa chochitira zoipa monga kuba,

kutukwana ndi zina.

Mphini yobwereza ndi imene imawala.

-Malangizo obwereza ndi amene amamveka

bwino.

Mphongo ya Chiwala sichepa.

-Si bwino kunyoza amuna kapena akazi a

ena chifukwa ndi amuna kapena akazi awo

basi.

Miyambi ya Patsokwe

311

Mphongo zidana.

-Nthawi zambiri amuna sachitira amuna

anzawo zabwino. Koma akakhala mkazi

amatha kumuchira zabwino kwambiri.

Mphungu sataya nthenga.

-Mawuwa amanena za munthu woumira.

Mphungu ndi mbalame imene imauluka

m’mwamba kwambiri, koma ikagwetsa

nthenga, imawakha mthengayo isanafike

pansi.

Mphuno imodzi silowa zala ziwiri.

-Si bwino kuchita zinthu ziwiri nthawi imodzi

chifukwa nthawi zina umatha kulephera

kukwaniritsa zonsezo.

Mphuno salota, adawombera mfiti

m’manja.

-Munthu woipa kapena wabwino alibe fungo.

Nthawi zina amene timawaona ngati abwino

ndi amene amadzatipha. Ukhoza kuchitira

Miyambi ya Patsokwe

312

zabwino munthu amene angadzakunyoze

patsogolo.

Mphwanga ndiye wamkulu msinkhu,

ngakhale kuti ndinatsogola ndine.

-Kukhala ndi mnzeru si kubadwa kale

kapena kutalika.

Mphwanga, mukakula bwino ngati mwana

wa Mlamba.

-Ndi bwino kumakhala wochenjera ndiponso

kumakhala bwino ndi akuluakulu.

Zikakuvuta anthu omwewa ndi amene

amakuthandiza.

Mphwayi ndi tsoka, ulesi ndi minyama.

-Munthu wamphwayi sangapeze zimene

akufuna. Tizichita khama pazinthu.

Mphwayi ndi tsoka.

-Munthu wamphwayi kapena waulesi

satukuka ndipo amakumana ndi mavuto

Miyambi ya Patsokwe

313

adzaoneni.

Mphwayi zilibe mtolo.

-Ulesi umabweretsa umphawi. Tiyenera

kumagwira ntchito kuti tipeze zimene

tikufuna.

Mpingu saloza ndi chala.

-Mpingu ndi munthu amene amakhala ndi

ulamuliro wovomereza zinthu zofunika. Ngati

utamuloza ndi chala ndi mwano. Mwambiwu

umatanthazua kuti si bwino kumanyoza

anthu omwe angatithandize.

Mpotepote m’poyamba, potsiriza

n’chingwe.

-Zinthu zimaoneka zonyozeka poyamba koma

zikakula zimatha kupanga zazikulu.

Mwachitsanzo, kuba zinthu zing’onozing’ono

kukhoza kudzatibweretsera mavuto aakulu.

Miyambi ya Patsokwe

314

Mpsalazingo wamukho wapamwala.

-Mawuwa amanena za munthu amene

amakhala wochenjera kwambiri pozemba

ntchito kapena mlandu chifukwa chodziwa

kuyankhula.

Mseche udaombola mbiya.

-Aliyense ndi wofunika pambali inayake.

Ngakhale ena azioneka onyozeka tiyenera

kumawalemekeza chifukwa akhoza

kudzatithandiza.

Mseka pamwamba, m’kati mwa mtima

muli zina.

-Kuonetsa chisangalalo pamaso koma

mumtima muli chiwembu.

Msika ndi wekha.

-Kuti zikuyendere umafunika kuchita khama.

Msipu suyenda, imayenda ndi nyama.

-Ngati munthu akusowa chinthu ayenera

Miyambi ya Patsokwe

315

kupita kukachifunafuna chifukwa

sichingamupeze pamene wakhalapo.

Msipu wamera m’khola.

-Kuchita mwayi kuti zimene umafuna

zachitika mmene umafunira. Kupeza mwayi

waukulu.

Msipu wobiriwira udapha mbuzi.

-Mbuzi itapeza msipu wobiriwira

inkangodyabe mpaka inaphulika mimba.

Tisamakomedwe ndi zinthu ngakhale

zitakhala zokoma bwanji chifukwa pamapeto

pake tikhoza kupeza mavuto.

Msirikali wa atate (imfa) ndiye amachotsa

chimwemwe.

-Imfa ikamachitika kawirikawiri pakhomo

anthu sakhala osangalala.

Msonjosonjo andautsa amene ali chete.

-Msonjosonjo ndi kulozana zala. Nthawi

Miyambi ya Patsokwe

316

zambiri anthu akamaloza anzawo chala

amapangitsa kuti amene anali chete akwiye.

Ungatanthauzenso kuti nthawi zina anthu

apachibale akamadana zimapangitsa kuti

anthu adera alowererepo.

Msonkhasonkha unang’amba thumba.

-Munthu akamangotolera pang’onopang’ono

osasiya, zimachuluka kwambiri ndipo kenako

zmawonongeka. Nthawi zina ndi bwino

kuchita zinthu mosathamanga komanso ndi

bwino kulimbikira kuti zomwe ukufuna

zitheke.

Msuma sudyera pomwepo.

-Msuma ndi chakudya kapena zinthu zomwe

tapatsidwa popemphetsa panthawi ya njala.

Ndi bwino kukumbukira banja lako chifukwa

nawonso akufuna kudya. Tiziganizira

anzathu ovutika.

Miyambi ya Patsokwe

317

Mtakataka kunsengwa, kumunda kumlaka.

-Pali anthu ena omwe amajijirika pakakhala

zakudya, kunsengwa basi (kale anthu

ankapakulira chakudya munsegwa, mbale

zisanabwere). Koma akauzidwa kuti akalime

amakana.

Mtanga umakoma ndi kusomekera.

-Pochita zinthu pamafunika kuchita khama

kuti zimene tikufuna zitheke kaya ndi

kusukulu kapena pantchito.

Mtaya makoko saiwala, amaiwala ndi

m’dya nyemba.

-Munthu ukakhala pamavuto suiwala wina

akakuchitira zoipa, koma wochita zoipazo

amaiwala.

Mtedza woola umalavulitsa zonse.

-Kulakwa kwa munthu m’modzi kumaipitsa

mbiri ya banja lonse kapenanso dziko.

Miyambi ya Patsokwe

318

Mtengo suphuka masamba usanagwetse

akale.

-Kusintha kwenikweni kumabwera ngati

munthu wasiya zimene amachita poyamba.

Mtengo umagwera kumene waweramira.

-Nthawi zambiri ana amachita zimene

amaona makolo awo akuchita.

Ungatanthauzenso kuti munthu akakhala

wakhalidwe loipa amadzafa ndi khalidwe

lakelo. N’kovuta munthu kuleka chizolowezi

chake.

Mtengo usamakome pokwera pokha.

-Si bwino kumakonda anthu tikamafuna

chinachake kuchokera kwa iwo basi, ngati

mmene munthu amakwerera mumtengo kuti

akangothyola mango basi.

Mtengo wopanda tsinde mudauonapo?

-Ngati tikufuna kuona khalidwe la ana ndi

bwino tiyang’ane makolo awo. Kuti umvetse

Miyambi ya Patsokwe

319

zochita za munthu wina ndi bwino kufufuza

mbiri yake.

Mthamangira kuotha anasiya moto

ukuyaka.

-Munthu wothamangira kuchita zinthu ndi

amene amayambirira kukumana ndi mavuto.

Ndiye anzake amabwera n’kudzapeza

zabwino, apo ayi amaphunzirira pa tsoka

lakelo.

Mthanga kunena adapisa Likongwe wa

apongozi.

-Mwambiwu umanena za mkamwini wina

yemwe anafulumira kapena kuti kuthanga

kunena kuti amene atathawitse Likongwe

asamuka pamudzi. Ndiye zinachitika kuti

iyeyo ndi amene anathawitsa Likongweyo

ndipo zinamuvuta. Tisamalonjeze msanga za

chinthu chomwe sitikudziwa kuti chitha

bwanji.

Miyambi ya Patsokwe

320

Mtima suvala nsanza.

-Munthu akhoza kukhala wosauka, koma

mumtima mwake n’kukhala wolemera

kwambiri pa zimene amakhumba. Palibe

amalota ali wosauka.

Mtima uli ngwizi, kadziwe ka mu Likuni.

-Mwambiwu umanenedwa pofuna

kutanthauza kuti wakwiya kwambiri, uli ndi

nkwiyo wosaneneka.

Mtima ulikuperewera, chanka patali.

-Ngati mtima sukhumbira chinachake ndiye

kuti n’zosatheka kuchipeza.

Mtima wabwino ngwaumulungu.

-Munthu wamtima wabwino amachitanso

zabwino.

Mtima wake waika pa mfuti.

-Kuchita mwano kapena kukula mtima

chifukwa choti uli ndi podalira.

Miyambi ya Patsokwe

321

Mtima walasa phaso.

-Mwambiwu umanena za munthu yemwe

wakumbukira kwawo. Ungatanthauzenso

kuti ndapeza chokhumba cha mtima wanga.

Mtima wamnzako ndi m’thumba, sudziwa

chomwe chilimo.

-Zomwe wina akuganiza n’zovuta kuzidziwa.

Mtima wamnzako ndi tsidya lina.

-Za mumtima wa munthu wina sungazidziwe.

Mtolo waukulu suchiza njala.

-Ndibwino kumayamikira zimene tili nazo

ngakhale zochepa.

Mtsinje umalimba ndi miyala.

-Kudya n’kumene kumathandiza munthu

kuti akhale wamphamvu.

Mtsinje wa Tinkanena udathera mu Siizi.

-Mawu a akulu amakumbukiridwa pakapita

nthawi ndiponso pamene zomwe amanena

Miyambi ya Patsokwe

322

zachitikadi. Munthu akakhala wosamva

akamalangizidwa zotsatira zake amakumana

ndi mavuto.

Mtsinje wopanda miyala susunga madzi.

-Miyala ndi imene imathandiza kuti madzi

azisungika mumtsinje. Chimodzimodzinso

m’mudzi, mfumu imafuna anthu oithandiza

pa zinthu zambiri.

Mtsuko sulowa m’chikho, koma chikho

ndicho cholowa mumtsuko.

-Munthu waudindo ndi amene amalandira

ulemu kuchokera kwa otsika, koma iyeyo

sapereka ulemu kwa anthuwo.

Mtunkhatunkha udayatsa lipande.

-Munthu ukamakhuthulakhuthula mphale,

ina imataika. Nafenso tiyenera kukhala

anthu okhazikika m’malo momati apa tagwira

apa tagwira, tikhoza kugwira posagwira

kapena kuwononga zinthu. Lipande ndi

Miyambi ya Patsokwe

323

mphale.

Mudzi umalimba ndi anyamata.

-Dziko lililonse liyenera kusamalira ndi

kunyadira achinyamata chifukwa ndi amene

adzakhale atsogoleri amawa.

Mukanakhala mbewu, tikadangokazinga.

-Mawuwa amanenedwa akamafotokoza za

anthu ovuta kapena ana ovuta. Anthu ena

akakwiya amanena mawuwa potanthauza

kuti anthuwo ndi amphulupulu omwe

sangawasunge pakhomo.

Mukhoza kusinja chitsiru mumtondo,

koma uchitsiru wakewo sungamuchoke.

-N’zovuta kuthandiza munthu wopusa.

Mulereni ayiwale kwawo.

-Mwana wamasiye kapena wa ena amafunika

kumulera bwino kuti aiwale kwawo kapena

mavuto amene akukumana nawo.

Miyambi ya Patsokwe

324

Mulimbalimba goli lili m’khosi.

-Munthu ukagwidwa ndi mlandu, ngakhale

udziteteze bwanji zimakhala zopanda phindu

chifukwa umboni wonse umakutsutsa.

Mulungu amapatsa wolimbika.

-Tiyenera kumadzithandiza tokha ngati

tikufuna kuti Mulungu atithandize.

Mulungu amapatsa wopirira.

-Tiyenera kumadzithandiza tokha ngati

tikufuna kuti Mulungu atithandize.

Mumphasa yongoima mumabisala zoluma

zambiri.

-Munthu amene wangokhala chete, timuope.

Mumphuno imodzi simulowa zala ziwiri.

-Umafunika kuchita chinthu chimodzi kaye.

Ukaphatikiza zingapo umatha kuwononga

zonse.

Miyambi ya Patsokwe

325

Mungatero, mwaperekeza mwana wolima.

-Mwambiwu umanenedwa anthu

akamadandaula kuti munthu yemwe

amamudalira pamudzi kapena pakhomo

wachoka.

Munthu akamafuna kufa, amayamba ndi

makutu kutsekeka.

-Kusamvera kumapezetsa munthu mavuto

aakulu monga imfa.

Munthu akatsala pang’ono kufa,

amayamba ndi makutu kufa.

-Kusamvera kumapezetsa munthu mavuto

aakulu monga imfa.

Munthu azilimba ngati mthiko, chipande

chilira madzi.

-Tisamangodalira chithandizo chochokera

kwa anthu ena ngati chipande, tizilimba

ngati mthiko n’kumadzithandiza tokha.

Miyambi ya Patsokwe

326

Munthu ndi Galu, Galu ndi munthu.

-Nthawi zina Galu amachita zabwino kuposa

munthu kapenanso zabwino zomwe

zimafanana ndi zochita za anthu ena. Anthu

ena kuwachitira zabwino sayamika, pomwe

Galu amakugwedezera mchira posonyeza

kuyamikira.

Mkazi wabwino amaphika nsima

yosazizira.

-Mkazi akamalandira bwino alendo,

zimachititsa kuti mwamuna wake akadzipita

koyenda anthu adzamuphikire nsima.

Zikatere nsima anaphika mkazi wake ija

imakhala ngati sinazizire.

Munthu sakula pa kamwini, amakula pa

kake.

-Munthu aliyense sakhala ndi ulamuliro pa

chinthu chamwini koma chake. Tiyenera

kugwira ntchito kuti tipeze zathu.

Miyambi ya Patsokwe

327

Munthu salakwira mtengo.

-Kulikonse anthu amalakwirana ndipo palibe

amene salakwa. Choncho, zikachitika ndi

bwino tizikhululukirana.

Munthu samenyana ndi maliro.

-Tisamalimbane ndi munthu yemwe ali

wofooka kwambiri.

Munthu sangadziteme mphini kumbuyo.

-Timafunika anthu ena kuti atithandize pa

zinthu zina.

Munthu satola kanthu ndi chala chimodzi.

-Kugwirizana komanso kuthandizana

n’kofunika kwambiri.

Munthu wadyera adanka ndi mvula ya

mawawa.

-Munthu wokonda kuchita chiwerewere

amafa nsanga potenga matenda.

Miyambi ya Patsokwe

328

Munthu wamagwiragwira samera tsitsi

loyera.

-Munthu wamakhalidwe oipa sakalamba.

Munthu waphuma adapsa paphewa.

-Kupupuluma kumawononga zinthu. Ndi

bwino kumafatsa.

Munthu wolemera safa ndi chuma.

-Tiyenera kukhala ndi chuma kuti

chitithandize pamoyo wathu.

Munthu wongodutsa amene amalowerera

mkangano womwe si wake n’kukwiya

nawo, ali ngati munthu wogwira makutu a

galu.

-Osamalowerera nkhani imene sikutikhudza.

Munthu amene wagwira makutu a galu

amafunika kusamala chifukwa akangowasiya

makutuwo, galuyo amatha kumuluma.

Miyambi ya Patsokwe

329

Munthu wopanda maso samunamiza maso.

-Tisamalonjeze zinthu zomwe sitingakwanitse

kuchita, monga kuchititsa kuti wakhungu

aone.

Munthu wopata safa ndi chuma.

-Munthu akamwalira samatenga chuma

kumanda. Choncho ngakhale tilemere, si

bwino kumayerekedwa chifukwa ndalama

sizingatiike m’manda.

Munthu wosabala amasowa

chomutukwanira mwamuna.

-Mayi amene ali ndi mwana amatha

kum’tukwana mwana wake pamene

wayambana ndi mwamuna wake. Akakhala

wopanda mwana amasowa womutukwana.

Munthu wosauka sapha nyama ya nguwo.

-Munthu umayenera kufufuza zinthu

mogwirizana ndi mmene umapezera zinthu.

Osamafuna zinthu zomwe sungathe

Miyambi ya Patsokwe

330

kuzipeza.

Munthu wotolatola samera ndevu zoyera.

-Munthu wamakhalidwe oipa sakalamba.

Musade Vumbwe, akudya nkhukhu ndi

Kalulu.

-Nthawi zambiri pamudzi pakachitika zoipa

amaganiza kuti mdani wawo ndi amene

wawachitira zimenezo. Koma nthawi zina

anthu omwe amaoneka ngati Akalulu ndi

amene amakhala atachita zoipazo.

Musamati ndi masweswe lili dazi.

-Si bwino kumanyozera zinthu anthu ena

akamanena.

Musamati ndikuthawa mlomo, mlomo uli

kulikonse.

-Kuthawa mlomo ndi kuthawa kulongolola.

Mavuto ali ponseponse ndipo sitingawathawe.

Amene akufuna kuwathawa kuli bwino

Miyambi ya Patsokwe

331

angomwalira.

Musamaumirire mtunda wopanda madzi.

-Osamakanirira pa zinthu zomwe zilibe

phindu chifukwa zingangotitayira nthawi.

Musamayese ndi masweswe, ndi dazi.

-Mawuwa amenenedwa munthu

akamatsimikizira kuti zimene akunena ndi

zoona zenizeni.

Musandiike chibanzi pakamwa.

-Musandiletse kunena zomwe ndikufuna

kunena.

Musandiike dzungu pakamwa.

-Musandiletse kunena zomwe ndikufuna

kunena.

Musandipatse masamba chifukwa pali

kapado.

-Mwambiwu umanena za kukhutira ndi

zabwino zimene munthu ali nazo. Ku Africa

Miyambi ya Patsokwe

332

kuno pamene munthu wadyera nyama ndiye

kuti paterela. Choncho, amafuna kuiwalako

kudya masamba akakhala kuti wapeza

nyama.

Musandiyangire nkhata pakamwa.

-Musandiletse kunena zomwe ndikufuna

kunena.

Musandiyese chulu cha ndiwo chokwera

ndi nthekwe m’chiuno.

-Si bwino kuyesa munthu wina ngati wopusa

kuti azingokuthandiza nthawi zonse.

Tiziyamikira zimene ena amatichitira.

Musawongole mbewa yopondaponda.

-Ukadziwa kuti walakwa ndi bwino

kungopepesa osachita makani.

Musayese ndi masweswe, limeneli ndi dazi.

-Si bwino kumanyozera zinthu anthu ena

akamanena.

Miyambi ya Patsokwe

333

Mutu ukakula sulewa nkhonya.

-Munthu ukakhala wamkulu mavuto onse

amafikira kwa iwe.

Mutu umodzi susenza denga.

-Palibe munthu amene angathe kuchita

zonse payekha. Choncho, ndi bwino

kumadalirana komanso kuthandizana.

Mutu wodwala Kasire adatema Kadzidzi.

-Zochita za ena zimatha kubweretsera ena

mavuto. Si bwino kulola kupusitsika ndi

maonekedwe.

Muvi kalase Nungu.

-Munthu ankafuna kulasa Nungu ndipo

Nungu inamulasa ndi minga yake. Nthawi

zina choipa chimene munthu akufuna

kuchitira mnzake chimatha

kumutembenukira.

Miyambi ya Patsokwe

334

Muvi woyang’anira suchedwa kugwera

m’maso.

-Mavuto owayang’anira amakula kwambiri,

monga matenda. Tisamadikire kuti zinthu

zifike poipa. Komanso, kuzengereza

kumagwetsera munthu m’mavuto.

Muvi woyang’anira suchedwa kulowa

m’maso.

-Mavuto owayang’anira amakula kwambiri,

monga matenda. Tisamadikire kuti zinthu

zifike poipa. Komanso, kuzengereza

kumagwetsera munthu m’mavuto.

Myang’ana dzuwa adasochera.

-Munthu amene safunsa nthawi zambiri

amakumana ndi mavuto ngati mmene

zimakhalira ndi munthu amene amayang’ana

kumene kuli dzuwa akamayenda ulendo.

Dzuwalo limasuntha ndiye amasokonekera

n’kusochera.

Miyambi ya Patsokwe

335

Mvula ikakuona litsiro sikata.

-Nthawi zina mavuto akakuyamba sakusiya.

Mvula ya mpoto kunyenga mkamwini.

-Si bwino kutengeka ndi zinthu zomwe

zimaoneka ngati si zoipa kwenikweni

chifukwa pamapeto pake zimachititsa kuti

tidziimbe mlandu kapena tikumane ndi

mavuto.

Mvula yamvumbi kunyenga ana.

-Si bwino kutengeka ndi zinthu zomwe

zimaoneka ngati si zoipa kwenikweni. Zinthu

ngati zimenezi zimachititsa kuti tidziimbe

mlandu kapena tikumane ndi mavuto ngati

mmene mwana amene wanyowa kapena

wadzidetsa ndi matope a mvumbi amachitira.

Mvumbi kwa ana, akulu nadya nthanga.

-Mawuwa amadzudzula khalidwe lodzikonda.

Mwachitsanzo, makolo kumadya kapena

kumapeza zabwino ana ali pamvumbi,

Miyambi ya Patsokwe

336

kapena akuvutika.

Mvuu zikatha, amakankha bwato ndi

kampango.

-Mavuto satherapo, akatha awa

amabweranso ena.

Mwa limodzi anaonera khumi kutha.

-Nthawi zina mukagwira wakuba m’modzi

amatha kuulula anzake ambiri.

Mwachaje satafuna.

-Munthu sangatafune m’kamwa mopanda

kanthu. Munthu wina akamadandaula ndiye

kuti pali vuto, tiyenera kumumvetsera.

Mwachaje satafuna.

-Ndi bwino kumakhutitsidwa ndi zimene uli

nazo ngakhale zili zochepa.

Mwakumbakumba mbewa mwalema,

m’sakadandaule ndiwo.

-Munthu uyenera kuvomereza zotsatira za

Miyambi ya Patsokwe

337

ntchito yako. Mwachitsanzo, mbewa

zikakukanika kukumba umasowa ndiwo

n’kuswera nayo njala.

Mwala umene amisili aukana umasanduka

wapangodya.

-Nthawi zina zinthu zimene tikuziona kuti

n’zosafunika zimakhala zothandiza kwambiri.

Mwala wogubuduzika sumera ndere.

-Kusakhazikika pamalo kapena pantchito

kumachititsa kuti tisapeze mwayi.

Mwala woyendayenda suyanga ndere.

-Kusakhazikika pamalo kapena pantchito

kumachititsa kuti tisapeze mwayi.

Mwalemera nyanga yanga simuidya.

-Munthu ukazolowera moyo wofewa mavuto

suwaganizira.

Mwamuna koma kumuyang’ana kumimba.

-Mayi amayenera kudziwa kuti kuti

Miyambi ya Patsokwe

338

mwamuna agwire ntchito bwino amafunika

kumupatsa chakudya.

Mwamuna mnzako mpachulu, umalinga

utakwerapo.

-Osamaderera mnzako usanaone mphamvu

zake, chifukwa nthawi zina wonyozeka

m’maso ndi amene amakutidzimula kapena

kukuposa pa chinachake.

Mwamuna mpamimba, nkhope siisintha.

-Mayi amayenera kudziwa kuti pakhomo kuti

mwamuna agwire ntchito bwino amafunika

kumupatsa chakudya.

Mwamuna ndi kabudula, amathera

moyenda.

-Mwamuna sakulira malo amodzi. Amafunika

kuyendayenda kuti akasake ndalama

zothandizira mkazi komanso abale ake.

Miyambi ya Patsokwe

339

Mwamuna ndine ndekha adam’pachika ndi

mkuzi.

-Osamadzikuza chifukwa ena akhoza

kutichititsa manyazi ife n’kunyowa.

Mwana akalilira fupa m’ninkhe.

-Nthawi zina ndi bwino kumalolera kuti ana

achite zofuna zawo. Ndi bwino kumaloleza

maganizo kapena zimene anthu ena akufuna

kuti aphunzirepo kathu.

Mwana akalilira nyanga ya nsatsi,

m’semere im’fotere yekha kumanja.

-Munthu akamafuna zinthu zopanda pake

ndi bwino kumusiya kuti awone yekha

zotsatira zake. Zimenezi zingamuthandize

kuti amvetse chifukwa chake

mumamukaniza ndipo sangadzabwerezenso.

Mwana amalira ndi mkodzo wake womwe.

-Anthu achibwana amachita zinthu zomwe

pambuyo pake amadzanong’oneza nazo

Miyambi ya Patsokwe

340

ondo n’kumafuna kuti ena awathandize.

Mwana amaopa kachirombo kakamuluma.

-Kuti munthu adziwe kuti chinthuchi

n’choopsa, amaphunzira akakumana ndi

mavuto.

Mwana m’nyanja alimbikira mpani wake.

-Munthu aliyense amalimbikira kuchita

zinthu zake. Amaonetsetsa kuti zachitika

bwino kwambiri koposa mmene akanachitira

za ena. Mawuwa amanenedwanso munthu

akamachita zinthu zokondera pa mlandu wa

m’bale wake.

Mwana ndi bango, akafa amaphuka wina.

-Mawuwa amanenedwa potonthoza makolo

omwe mwana wawo wamwalira kuti

asadandaule Mulungu adzawapatsa wina.

Mwana sakulira nakubala.

-Ngakhale mwana ataphunzira bwanji

Miyambi ya Patsokwe

341

kapena atakula chamtundu wanji, ayenera

kumalemekezabe makolo ake. Angachite

zimenezi ngakhale zitakhala kuti aliyense

amamulemekeza kwambiri kapena ndi

mtsogoleri wa dziko.

Mwana sasowa amake.

-Ana kapena ziweto zimadziwa makolo

komanso mbuye wawo. Munthu sulephera

kuzindikira chinthu chako.

Mwana ukam’zoloweza kukwera

pathandala, saleka.

-Mwana amachita zimene makolo ake

amuphunzitsa. Akamuphunzitsa zabwino,

mwanayo amakhalanso wabwino.

Mwana wa a Matumbo wamwalira,

adzanena ndi a M’masomwada.

-Mkuluwikowu umanena zoti munthu ali ndi

njala.

Miyambi ya Patsokwe

342

Mwana wa amfumu anaotha uta wake.

-Chifukwa chodalira udindo wa bambo ake,

mwana wa amfumu anaotcha uta wake

modzionetsera. Si bwino kunyada kapena

kudzionetsera chifukwa zimenezi zikhoza

kutayitsa munthu zinthu zambiri ngati

chuma.

Mwana wa “kaya” sachira.

-Munthu wina akamadwala si bwino kunena

zokhumudwitsa, koma kumulimbikitsa

ngakhale ukudziwiratu kuti sachira. Ena

akatifunsa zinazake tiyenera kunena

motsindika osati kumakayikira.

Mwana wa mfulu ndi mbatata, ukaongola

wathyola.

-Nthawi zambiri anthu omwe ndi otchuka

kapena audindo waukulu amavuta

kuwalangiza. Ukalimbana nawo umakumana

ndi mavuto ndi iweyo.

Miyambi ya Patsokwe

343

Mwana wa mnzako ndi wako yemwe,

ukachenjera manja udzadya naye.

-Tizikonda ana a anzathu monga ana anthu

chifukwa tsiku lina anawo mwinanso atakula

akhoza kudzatithandiza, tikhoza kudzadya

zawo.

Mwana wa mnzako ndiye ‘kasambe

m’manja,’ wako ndiye ‘tazingodya!’

-Tisamachitire nkhanza ana a anzathu.

Tiziwachitira mofanana ndi ana athu.

Mwana wa munthu wopatsa sagona ndi

njala.

-Munthu ukamakhala bwino ndi anthu,

ukamawathandiza ndi kuwachitira zabwino,

ngakhale umwalire ana ako samadzazunzika.

Amadzawathandiza pokumbukira khalidwe

lako labwino.

Mwana wa mwini ndi gaga, saundika.

-N’zovuta kuthandiza mwana wa mwini

Miyambi ya Patsokwe

344

kusintha khalidwe. Ukamupatsa chilango

amaona ngati nkhanza. Ena ngakhale

akadzakula amatha kudzakuthawa n’kupita

kwa abale awo.

Mwana wa mwini ndi tsabola wokomera

m’kamwa, akagwa m’maso ndi nkhondo.

-Ana a anthu ena akhoza kungooneka

abwino pamaso, koma nthawi zina akhoza

kuyambitsa chipwirikiti komanso kuwononga

zinthu zathu.

Mwana wa Ng’ombe amadya udzu,

anaonekera amake kudya udzu.

-Ana amatengera makolo awo pa zabwino

kapena zoipa.

Mwana wa Ng’ona ndi uyo ali pamchira, wa

pambuyo ngwa Ng’azi.

-Ngakhale ana amafanana ndi makolo awo,

ngati samamvera malangizo awo

amadzakumana ndi mavuto, amakhala ngati

Miyambi ya Patsokwe

345

ana a Ng’azi.

Mwana wa Ng’ona salephera kuyangalala.

-Nthawi zambiri ana amatengera luso la

makolo awo. Ng’ona imayendayenda m’madzi

chifukwa ndi zimene makolo awo amachita.

Mwana wa Nkhuku chenjera, Kabawi

watulukira.

-Mawuwa amakonda kunena ndi ogwira

ntchito akamachenjeza anzawo kuti abwana

kapena owayang’anira akubwera.

Mwana wa pang’oma salephera kuyangala.

-Nthawi zambiri mwana amatengera khalidwe

la makolo ake.

Mwana wa Ng’ona alibe makutu, kumva

kwake ndi kum’panda.

-Ngati mwana samvera makolo, nthawi zina

ndi bwino kumulanga mwina pomukwapula

kapena kumupatsa chilango china.

Miyambi ya Patsokwe

346

Mwana wa Ng’ona sakulira dziwe limodzi.

-Mwamuna sakulira malo amodzi. Amafunika

kuyendayenda kuti akasake ndalama

zothandizira mkazi komanso abale ake.

Mwana waulemu amakodza kwambiri.

-Munthu waulemu amapeza zinthu zambiri

pakati pa anzake. M’mawu ena amadya

zambiri zomwe zimachititsa kuti

azingokodzakodza.

Mwandimangitsa madzi m’masamba.

-N’zosatheka kumanga madzi m’masamba.

Choncho mawuwa amatanthauza kuti

mwandipusitsa.

Mwandimangitsa madzi m’mayani.

-N’zosatheka kumanga madzi m’masamba.

Choncho mawuwa amatanthauza kuti

mwandipusitsa.

Miyambi ya Patsokwe

347

Mwandiyesa kankhuku kachilendo.

-Mawu otanthauza kuti mukuyesa ndine

mlendo?

Mwandiyesa “kankhuku kadza ndi yani?”

-Mawu otanthauza kuti mukuyesa ndine

mlendo?

Mwaupaka matope, mpanje wakanika

kulira.

-Ng’oma ikakhala ndi matope siimveka

bwino. Tizionetsetsa kuti zonse zili bwino

tisanayambe kuchita zinthu.

Mwauza Kambuku kugwira pakhosi.

-Ngati Kambuku wagwira nyama pakhosi ndi

kuti yapita imeneyo. Chimodzimodzinso

kulekerera anthu kuchita khalidwe loipa

kumakhala ngati kulimbikitsa khalidwelo.

Mwavomera chamutu, mtima wakana.

-Mawu otanthauza kuti simunavomere ndi

Miyambi ya Patsokwe

348

mtima wonse.

Madzi akatayika sawoleka.

-Pali zinthu zina zomwe zikachitika,

sizingathekenso kuzibwezeretsa.

Mwayi kusiyana.

-Anthufe timapeza zinthu mosiyana.

Mwayi ndi mwayi.

-Ngati munthu wapeza mwayi wochita

zinazake ndi mwayi wake basi.

Mwayi sudziwika.

-Tizingochita zomwe tikuganiza kuti

zingatithandize.

Mwayi sufanana.

-Anthufe timapeza zinthu mosiyana.

Mwayi sulingana.

-Anthufe timapeza zinthu mosiyana.

Miyambi ya Patsokwe

349

Mwayi wa munthu mmodzi sangagonere

wina pabwalo.

-Mwayi umasiyana. Tisamachite zinthu

chifukwa choti anzathu atachita zomwezo

zinawayenera bwino.

Mwayi wamzama wofukula ndi manja.

-Mwayi waukulu kwambiri.

Mwana yemwe amasamba m’manja amadya

ndi akuluakulu.

-Munthu amene ali ndi khalidwe labwino

kapena wolimbikira ntchito amakondedwa

ndi ena ndipo zinthu zimamuyendera bwino.

Mwazi ukutuluka pampini.

-Mawu otanthauza kuti pakuchitika

zodabwitsa.

Mwendo wa amfumu kulemera.

-Anduna akampempha anthu kuti atumidwa

ndi amfumu kuti apemphe thandizo lawo

Miyambi ya Patsokwe

350

anthuwo n’kukana ndunazo zimamva

mwendo wa mfumu kulemera. M’mawu ena

zimaona kuti udindo wawowo ndi wolemera

kwambiri.

Mweranitu, ukadza kuno subwerera,

ndigubula.

-Mwayi kapena nthawi ikapezeka, ndi bwino

kuchitiratu chifukwa zamawa sizidziwika.

Mwezi satungira mkanda.

-Ntchito iliyonse ili ndi nthawi yake yoyenera

kugwiridwa. Kuchita chinthu pa nthawi

yolakwika sikuthandiza. Mwachitsanzo,

kufuna kulowetsa ulusi pabowo la singano

usiku pa kuwala kwa mwezi.

Mwezi sayanikira ufa.

-Pali zinthu zina zomwe zimachitika masana

okha kapena pa nthawi yake osati nthawi

iliyonse.

Miyambi ya Patsokwe

351

Mwezi uli kumwamba, mitengo ili pansi.

-Pali zinthu zina zomwe zili kutali zomwe

n’zobisika kwa anthu koma zina n’zodziwika

kwa aliyense ngati mitengo yomwe ili pansi

pano.

Mwini phala sada chala.

-Nthawi zambiri munthu saona kulakwa

kwake kapena kwa ana ake.

Mwiniwake wapha pa mbewu yake.

-Mawuma amanena za munthu yemwe

amapha anthu a pabanja pake kuti achitire

zizimba. Zimenezi ndi zina mwa zimene

anthu a ku Africa kuno amakhulupirira

zomwe zilibe umboni kuti zimathandizadi.

Myendera mwana salema.

-Munthu akakhala ndi mwana wake satopa

kumuyendera. Tikamachita chinthu

sitiyenera kutopa mpaka titachikwaniritsa.

Miyambi ya Patsokwe

352

N

N’takalamba n’kusiya dziko likali nsonga.

-Mawuwa amanenedwa munthu akamafuna

kunena kuti akufuna kuchoka zinthu

zikadali bwino, pamalo pasanaipe.

Nachonso chitsiru chili ndi mwini.

-Munthu ngakhale wopusa amakhala ndi

m’bale wake amene amamukonda.

Akaphedwa abale ake adzaoneka. Choncho si

bwino kunyoza ena chifukwa cha khalidwe

kapena maonekedwe awo.

Nalikukuti saluma, koma akaluma alibe

chivumulo.

-Pali anthu ena omwe amaoneka a phee,

koma tsiku lina ukadzawaputa umadzaona

kuti ali ndi ululu woopsa kuposa wa njoka.

Miyambi ya Patsokwe

353

Namkwichi akaona akazi ndiye

amakondwa.

-Namkwichi ndi mbalame yokonda akazi

kwambiri. Mwambiwu umanena za munthu

wokonda akazi.

Nankholowa ali m’manja n’kulinga

utalawa.

-Pali njira zosiyanasiyana zophikira

nankholowa (masamba a mbatata).

Tisamaweruze nsanga chinthu

tisakuchidziwa bwino.

Nankungwi chilanga anzake, mwake sazira.

-Pali anthu ena omwe amakonda kulangiza

anzawo pomwe iwowo sachita zimenezo,

kapena alibiretu khalidwe.

Nankununkha sadzimva.

-N’kovuta kuti munthu adziwe za momwe

anthu ena amamuonera makhalidwe ndi

maonekedwe ake, koma anthu enawo ndiwo

Miyambi ya Patsokwe

354

amamudziwa bwino.

Nanzeze apitira m’kuleza.

-Timanena mawu amenewa munthu

akawomboka pamavuto amene anawapeza

kuchokera kwa anthu amene sanamvetse

bwino nkhani yonse. Ngati Nanzeze yemwe

anapulumuka chifukwa choti anthu

sanamumvetse bwino.

Ndabwerera pakamwa pa Mkango.

-Mawuwa amenena za munthu amene

wapulumuka pamavuto aakulu.

Ndagunda, dziko lonse landimva.

-Mawuwa amanena za munthu amene

watchuka padziko lonse chifukwa cha ntchito

zake.

Ndakutama kukongola kwako, nzeru zako

sindizitama.

-Mawuwa amatanthauza kuti, ngakhale

Miyambi ya Patsokwe

355

munthuyo ali wokongola koma ndi

wamakhalidwe oipa.

Ndakwatiwa kumbuyo, kumaso kulira ena.

-Mawuwa amanena za munthu amene

wakwatiwa ndi munthu wolemera koma

mwamuna wake ndi gojo, sangathe

kumupatsa ana.

Ndakwatiwa n’kumbuyo komwe.

-Wakwatiwa ndi munthu wabwino, wachuma

komanso wakhalidwe labwino.

Ndalama zidaphetsa Yesu.

-Anthu ena amachita zolakwa zikuluzikulu

chifukwa chokonda ndalama.

Ndalama zikamayankhula, chilungamo

chimakhala chete.

-Nthawi zambiri anthu ena amatha kupereka

ziphuphu kuti mlandu wawo uyende bwino.

Zimenezi zimachititsa kuti osalakwa

Miyambi ya Patsokwe

356

amangidwe kapena chilungamo chisaoneke.

Ndalowa m’chala.

-Mawuwa amatanthauza kudwaladwala.

Anganenenso za munthu yemwe anali

wachuma koma anasauka, moti akusowa

pogwira.

Ndam’meta mpala wopanda madzi.

-Munthu amanena mawuwa potanthauza

kuti wamuchenjeretsa winawake kapena

wamukhaulitsa.

Ndangotsala madzi amodzi.

-Mawuwa amatanthauza kuti ndangotsala

pang’ono kufa.

Ndani amene angaike khala lamoto

pamalaya ake koma osapsa?

-Palibe munthu amene angachite choipa

osakumana ndi zotsatira zake.

Miyambi ya Patsokwe

357

Ndapakonda adasiya khonde.

-Kuzengereza pochita zinthu kumapezetsa

mavuto.

Ndaphwa mafuta, patsala thonje lokha.

-Mawuwa amatanthauza kuti munthu ali ndi

njala. Kuphwa mafuta akutanthauza kuti

wapuma koma akumva njala.

Ndawonera momwemu mwambi wa

gulugufe.

-Ndi bwino kumakhutitsidwa ndi zimene uli

nazo ngakhale zili zochepa.

Ndayala mayani, awuma.

-Ndadikira mokwanira moti ndatopa.

Ndewonetsetse adathetsa nkhosa.

-Kuzengereza kumagwetsera munthu

m’mavuto.

Ndewu siimanga mudzi.

-Mikangano komanso ndewu zimapasula

Miyambi ya Patsokwe

358

mudzi. M’malo mochita zimenezi ndi bwino

kukambirana mwamtendere.

Ndi bwino kunena maganizo ako udakali

ndi moyo, kusiyana n’kumadzawanena

ukutsirizika.

-Osamamangika kunena maganizo ako

chifukwa mwina angathandize.

Ndi mwamuna akadya.

-Munthu ayenera kuonetsa chamuna chake

pogwira ntchito osati pakudya pokha.

Ndi mwamuna pakudya pokha.

-Munthu ayenera kuonetsa chamuna chake

pogwira ntchito osati pakudya pokha.

Ndikanadziwa ndikanaphika therere.

-Mkazi wina ankayembekezera kuti

mwamuna wake abweretsa nyama kuchokera

ku uzimba. Koma anadandaula mwamuna

wake atabwerako chimanjamanja. Mawuwa

Miyambi ya Patsokwe

359

amanenedwa zinthu zimene umayembekezera

zikakhala kuti sizinachitike, ndiye

ukudandaula kuti bola ukanachita zinthu

zina.

Ndikhale nawo analanda malo.

-Si bwino kumangolola anthu osadziwika

bwino kuti mukhale nawo pamudzi kapena

kuwapatsa udindo chifukwa pamapeto pake

amakhala eni mudzi. Tizisamala ndi anthu

omwe sitikuwadziwa bwino.

Ndikudula tsitsi ndi mano.

-Mawuwa munthu amawanena akakhala kuti

wavutika kapena wasauka kwambiri.

Ndim’khulupirira adam’gonetsa m’nkhufi.

-Munthu amene umamudalira, nthawi zina

ndi amene amakukhumudwitsa kwambiri.

Ndimveke ndine adaphetsa fisi.

-Kususukira kutchuka kumabweretsa tsoka.

Miyambi ya Patsokwe

360

Ndinatha Ngombo ndi Akamundi, kuli

Achanga ndisanafike.

-Munthu amanena mawuwa podandaula kuti

akanadziwa kuti zabwino zili kutsogolo

akanadikira. Amakhala kuti anafulumira

kuchita zinazake n’kutaya mphamvu zake

pachabe.

Ndiwonetsetse adathetsa nkhosa.

-Kuzengereza pochita zinthu kumapezetsa

mavuto.

Ndodo imodzi siipha njoka.

-Mawuwa amanenedwa pofuna kulangiza ena

kuti afunika kumachita zinthu mobwereza

osati kamodzi kokha.

Ndodo ya ana ndi imene amaphera njoka.

-Osamanyoza maganizo a ana. Nthawi zina

mnzeru zawo ndi zimene zimathandiza

pamavuto, monga njoka ikalowa m’nyumba

umatha kutenga ndodo yomwe mwana

Miyambi ya Patsokwe

361

amaseweretsa n’kuphera njoka.

Nena chilungamo n’kuthawa.

-Nthawi zina munthu ukanena chilungamo

anthu amakuda. Koma kunena chilungamo

n’kofunika. Choncho, zimakhala bwino

kunena chilungamo koma umafunika

kusamala chifukwa ukhoza kukumana ndi

mavuto.

Nena poipa kuti pabwino patuluke.

-Munthu ukamafuna kudzudzula choipa

umanena ngati nthabwala kuti nkhaninkhani

ituluke n’kukonzedwa.

Ng’oma imalira ikaona inzake.

-Anthufe timafunikira anthu ena kuti zinthu

zitiyendere bwino. Mwachitsanzo, kuti

munthu usangalale ndi phwando umafunika

anzako.

Miyambi ya Patsokwe

362

Ng’oma silira yokha.

-Ng’oma ikamalira ndiye kuti wina

akuimenya. Chimodzimodzi munthu,

akamadandaula pakakhala kuti penapake

pali vuto.

Ng’oma yolira bwino sichedwa

kung’ambika.

-Munthu ukatchuka kwambiri usamadzitame

chifukwa kutchukako sikuchedwa kutha.

Zikamakuyendera bwino kwambiri dziwa kuti

zikhoza kukusokonekera.

Ng’ombe ya mnzako sumaiitana.

-Tisamale ndi zinthu za ena kuti nawonso

asamale zinthu zathu.

Ng’ombe yaukali imagwa m’mbuna.

-Munthu ukakhala waukali, anthu

samakuchenjeza ngati pena pali zoopsa

chifukwa amaopa kuti uwakalipira. Munthu

wofatsa ndi amene amathandizidwa ndi ena.

Miyambi ya Patsokwe

363

Ngakhale chitsiru nachonso chili ndi

amake.

-Aliyense anganyanse bwanji, angaipe bwanji,

amakhala ndi abale ake komanso anthu

amene amamukonda.

Ngakhale matako atafunitsitsa bwanji,

sangakhale kutsogolo.

-Pali zinthu zina zomwe sitingakwanitse

kuchita ngakhale titafunitsitsa bwanji.

Ngakhale nkhalango ikamapsa,

Birimankhwe sasintha mapondedwe.

-N’zovuta kusintha zimene unazolowera.

Ngakhale wapamtima, usamuuze mawu

onse akukhosi.

-Mnzako amene umamukhulupirira

amakhalanso ndi anzake moti chinsinsi

chimene wamuuza amakauzanso anzakewo

nkhaniyo n’kufala.

Miyambi ya Patsokwe

364

Ngaluwe idalira msampha utaning’a.

-Mawuwa amanena za kulephera kupirira

vuto litatsala pang’ono kutha.

Ngati mtengo wauwisi ukuyaka, ndiye

wouma ungatani?

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

wolimba kapena amene amachita bwino

zinazake walephera. Ngati zotere zitachitika

ndiye kuti ena omwe si olimba

amangogweratu. Zimene zavuta anthuanthu,

ofooka sangazithe.

Ngati n’zotheka kuwapha ndi uchi,

n’chifukwa chiyani ukufuna kuwapha ndi

chiphe?

-Kumagwiritsa ntchito njira imene ukuona

kuti ndi yabwino kwambiri.

Ngati umakonda bwenzi lako,

usamubwereke ndalama.

-Nthawi zambiri nkhani za ndalama

Miyambi ya Patsokwe

365

zimachititsa kuti anthu asiyane. Tizisamala

pa nkhani yobwereka ena ndalama. Ngati

munthu timagwirizana naye kwambiri,

tingachite bwino osamubwereka ndalama

chifukwa akhoza kungotikhumudwitsa.

Ngongole imakoma potenga, koma

pobweza imawawa.

-Ukamatenga ngongole zimasangalatsa koma

kuti ubweze pamakhala nkhani. Tiziganiza

kaye tisanatenge ngongole.

Nguluwe inalira nsampha utaning’a.

-Nguluwe itagwidwa pansampha analimbana

nawo mpaka kutsala pang’ono kuduka.

Koma m’malo molimbikira inatopa ndipo

inayamba kulira. Anthu atamva kulirako

anabwera n’kudzaipha. Osamataya mtima

msanga tikakhala pamavuto.

Nguluwe ya ana sinona.

-Nguluwe imene yabereka ana ambiri

Miyambi ya Patsokwe

366

imakhala yoonda. Chimodzimodzinso ndi

munthu yemwe ali ndi ana ambiri kapena

amene amamudalira ambiri. Chifukwa

ndalama zake zimachuluka kopita, satukuka.

Tizikhala ndi ana omwe tingakwanitse

kuwasamalira.

Nguwo yobwereka siilimba m’thupi.

-Nguwo ndi nsalu. Nsalu yobwereka

simachedwa kugwa chifukwa umakhala

sunaizolowere. Tisamadalire za ena, tizipeza

zathu.

Ngwazi nayonso imafa ndi mpeni umodzi.

-Ukakhala wamphamvu si bwino

kumadzitama chifukwa umagwa ndi kanthu

konyozeka.

Njala ikadza umaimangira kacheka.

-Kacheka ndi lamba kapena nsalu imene

anthu amamanga pamimba. Ukakhala

pamavuto monga njala uyenera kuumanga

Miyambi ya Patsokwe

367

mtima kuti usaganize zakuba. Ngakhale

zinthu zivute bwanji ndi bwino kupitirizabe

kuchita chilungamo.

Njala ikafika, ubale umatha.

-Anthu ambiri amakukonda ukakhala

pabwino, zinthu zikavuta amakuthawa.

Njala ili m’mano.

-Chakudya chingachepe, chimathandizabe

kuti usafe.

Njala ndi kamtengo, kanagwetsa Undi.

-Njala imagwira aliyense ngakhale mfumu.

Undi inali mfumu, ndipo nayonso inagwa ndi

kamtengo kameneka, njala.

Njala sailowetsa m’nkhokwe.

-Si bwino kuuza munthu yemwe akusowa

chinachake kuti atenge zimene akufuna

chifukwa akhoza kumaliza zonse. Munthu

amene kwawo kuli njala sungamuuze kuti

Miyambi ya Patsokwe

368

alowe munkhokwe, akhoza kukumalizirani

chonse.

Njala ya mnzako ndi yako yomwe.

-Anzathu akakhala pamavuto monga

matenda kapena imfa, tiyenera

kumawathandiza n’kumawamvera chisoni

ngati zachitikira ife.

Njala yapita pa mlimi.

-Nthawi zina pamakhala mavuto moti anthu

amene timawadalira amakhalanso kuti

sangatithandize. Zikatero timayenera kuchita

zimene tikuona kuti zingatithandize.

Njira salimbira, chikakula patuka.

-Pali zinthu zina zomwe sitingalimbane nazo,

zoterozo zimafuna kungozisiya.

Njira ya kwa amfumu siiwirira.

-Nkhani zonse zofunika kwambiri kaya ndi za

maliro, zimayenera kukanenedwa kwa

Miyambi ya Patsokwe

369

amfumu kuti akuthandizeni.

Njira zonse sizipita pamutu pako.

-Nthawi zina ndi bwino kulola kuti zinthu

zina zitipite.

Njiwa sasosolera pamsampha.

-Ukasosolera njira pamsampha, zinzake

zimadziwa, n’kuchenjera. Tisamaulule zinthu

zomwe tikudziwa kuti zikhoza kupereka

mphamvu kwa ena kuti atilange.

Njoka ndi njoka, singasinthe manga.

-Munthu woipa ndi woipa, sangasinthe

ngakhale mutamulangiza bwanji.

Njoka yopusa imalumira kumchira.

-Pali anthu ena ooneka opusa, anthuwa

sitimadziwa zimene akuganiza kusiyana ndi

ena omwe akungolongolola.

Njovu idagwa m’mbuna mwa Aonenji.

-Munthu aliyense ali ndi mwayi wake.

Miyambi ya Patsokwe

370

Choncho, si bwino kuganiza kuti anthu ena

ooneka onyozeka sangapeze mwayi.

Njovu inatuma nyerere.

-Mawu onena moseka omwe ena amagwiritsa

ntchito akamatuma mwana kapena munthu

wonyozeka.

Njuchi yako ndi iyo yaluma.

-Osamangotsata zinthu zomwe ulibe nazo

umboni. Kumatsata zinthu zenizeni.

Njuchi zikachuluka siziika.

-Anthu akachuluka pamalo kapena

pantchito, zinthu siziyenda. Aliyense

amangosiira mnzake.

Njuchi zikachuluka zilibe usinda.

-Anthu akachuluka pamalo kapena

pantchito, zinthu siziyenda. Aliyense

amangosiira mnzake.

Miyambi ya Patsokwe

371

Njuchi zingalume, koma ine phula

nditenga.

-Kuti upeze zabwino umafunika kulimba

mtima komanso kupirira mavuto. Kuti

munthu afule njuchi n’kutenga malesa,

njuchi zina zimamuluma koma iye sagonja

mpaka atatenga uchiwo.

Nkhali imafuna mafuwa.

-Aliyense amafuna wina woti amuthandize.

Nkhali yodikirira imachedwa kuwira.

-Chilichonse chili ndi nthawi yake, ndi bwino

kumadikira. M’malo mongokhala ndi bwino

kumachita zina kuti usaone kuchedwa.

Nkhanga ikakula, siikhala paphira.

-Munthu ukakula umayenera kusiya

chibwana.

Nkhanga yaikulu saweta.

-N’zovuta kusintha Nkhanga yaikulu kuti

Miyambi ya Patsokwe

372

ikhale yoweta. Munthu amene wakula ndi

zizolowezi zoipa amavuta kumusintha.

Nkhanga zinapangana kusanaspe.

-Ndi bwino kumaganizira zimene tingachite

mavuto atatigwera, kusiyana n’kumakhala

pansi kuti tidziwe chochita mavutowo

akatipanikiza.

Nkhani ndi kamchira, umafunika

uyang’ane kaye pali mutu wake.

-Kumafufuza chimene chachititsa vuto.

Nkhani ndi kamnyamata.

-Kucheza sikutha, nkhani zikayamba

zimabwerabe zina. Ndi bwino kumaona

polekezera kucheza kuti tizigwira ntchito.

Nkhani siidzala mtanga.

-Kucheza sikutha, nkhani zikayamba

zimabwerabe zina. Ndi bwino kumaona

polekezera kucheza kuti tizigwira ntchito.

Miyambi ya Patsokwe

373

Nkhani siikalamba.

-Kucheza sikutha, nkhani zikayamba

zimabwerabe zina. Ndi bwino kumaona

polekezera kucheza kuti tizigwira ntchito.

Nkhani yalowa m’chala.

-Anthu ena amapondereza nkhani chifukwa

choti wolakwayo ndi m’bale wawo kapena

wawapatsa chiphuphu. Zikatere timati

nkhaniyo yalowa m’chala.

Nkhokwe imalimba ndi mphanda.

-Munthu aliyense amafuna wina woti

azimuthandiza. Kudalirana n’kofunika.

Nkhondo kadzikumbire.

-Nthawi zina pofuna kupezetsa ena mavuto,

timapezeka kuti tawavala mavutowo

n’kukhaula nawo. Kutchera msampha kuti

wina akodwe, n’kupezeka wakodwa wekha.

Miyambi ya Patsokwe

374

Nkhondo ndi anansi

-Amakuchitira choipa nthawi zina ndi abale

ako kapena amene umakhala nawo pafupi.

Nkhonya ya “mudandiyambakale” idagwa

m’chikope.

-Mkwiyo ndi woopsa. Kusunga chidani

kumachititsa kuti munthu uchite zoopsa

kwambiri.

Nkhope ya muthu imanola khope inzake.

-Munthu amathandiza mnzake kuti azichita

bwino.

Nkhuku imalemekezeka ndi nthenga zake.

-Munthu amalemekezeka chifukwa cha

khalidwe komanso zochita zake.

Nkhuku yanjiru simaswa mazira.

-Nsanje simapindulitsa munthu. Umafunika

kulimbikira ntchito m’malo momangokhalira

kulimbana ndi anzako omwe zikuwayendera.

Miyambi ya Patsokwe

375

Nkhuku yoweta sagula pamsika.

-Mkazi wabwino samakapena koyenda.

Nkhululu yatcheru ndiyo imaimba lokoma

pachilimwe.

-Pa nthawi ya dzinja, Nkhululu imatolera

zakudya n’kukasiya kuuna ndipo

simadzavutika m’chilimwe. Tizichita zinthu

zomwe zidzatithandize m’tsogolo.

Nkhuni imodzi siipanga mtolo.

-Munthu payekha sangakhale ndi nzeru

zonse, umafunika kumva maganizo a ena.

Nkhuni imodzi siipsetsa mphika wa

nyemba.

-Munthu payekha sangakhale ndi nzeru

zonse, umafunika kumva maganizo a ena

komanso kulola kuti akuthandize.

Nkhunzi yamwini sang’ambira khola.

-Munthu sangakulitse khola lake chifukwa

Miyambi ya Patsokwe

376

cha tonde kapena ng’ombe yamwini.

Tizidalira zanthu osati za eni.

Nkhunzi yobwereka samangira khola.

-Si bwino kudalira chinthu chobwereka

chifukwa mwini wake akhoza kuchifuna

nthawi iliyonse.

Nkhutukumve.

-Mawuwa amatanthauza munthu wosamva,

amene amangochita zake.

Nkhuyu zodya mwana zidapota akulu.

-Nthawi zambiri ana akapalamula vuto lonse

limafikira kwa makolo ndipo makolowo ndi

amene amavutika nalo.

Nkhwangwa ikati chubwi m’madzi, dzanja

lako lipite pomwepo.

-Tisamazengereze kuchita zinthu. Mavuto

kapena zina zikachitika, ndi bwino

kuchitiratu chifukwa tikachita ulesi zikhoza

Miyambi ya Patsokwe

377

kutisokonekera.

Nkhwangwa imakhulupirira mpini.

-Anthu amayenera kukhulupirirana komanso

kuthandzana kuti zinthu ziyende.

Nkhwangwa siithwera pachipala.

-Munthu samaphunzira zonse kusukulu,

kuchinamwali kapena kwa makolo ake.

Amatha kuphunzira zina akamachita zinthu

ndi anthu ena.

Nkhwangwa yatema bondo.

-Nkhwangwa yako ikakutema sumaiwala.

M’bale wako akakulakwira ndi bwino

kumukhululukira m’malo momangosunga

chakukhosi.

Nkhwangwa yobwereka siichedwa

kuguluka.

-Munthu sachedwa kuchita ngozi ndi chinthu

chobwereka.

Miyambi ya Patsokwe

378

Nkhwangwa yobwereka sichedwa kusweka

mpini.

-Munthu sachedwa kuchita ngozi ndi chinthu

chobwereka.

Nkhwangwa yobwereka siichedwa

kuthyoka.

-Zinthu zobwereka sizikhalitsa, umafunika

kupeza zako.

Nkhwani saotchera.

-Mawuwa anganenedwe ngati wina wachita

zinthu zabwino kwambiri moti

sitingachitirenso mwina koma

kumuyamikira. Anganenedwenso ngati wina

akuyesa kuchita zosatheka.

Nsabwe yoyendayenda inakumana ndi

chala.

-Munthu woyendayenda salephera

kupalamula.

Miyambi ya Patsokwe

379

Nsalu ndi kukhosi.

-Aliyense ali ndi ufulu wosankha chimene

chamukomera kapena chimene akufuna

kuchita.

Nsalu ya “lekaleka.”

-Mawuwa amatanthauza mwana. Nthawi

zambiri ana amakonda kugwiragwira ndipo

mayi awo angamawaletse kuti aleke.

Akakhala wakhanda, mayi salola kuti

aliyense amunyamule poopa kumukhonyola.

Amauza munthuyo kuti aleke.

Nsalu yobwereka silimba m’chiuno.

-Zinthu zobwereka zimakhala zosadalirika,

choncho ndi bwino kumasamala chimene

wabwereka kuti ukachibweze chili bwino.

Nsalu yobwereka sithetsa usiwa.

-Kubwereka zinthu kwa ena si njira

yothetsera umphawi koma kugwira ntchito

kuti tipeze zimene tikufuna.

Miyambi ya Patsokwe

380

Nsangala za pamaliro ngati matenda

adakazonda.

-Kujijirika pa zinthu zoti wapeza zothaitha

kapena zochitidwa kale, pomwe poyamba

unalibe nazo chidwi.

Nsanjikizo udaphetsa Kunda.

-Kunda ndi mbewa. Kunda ankasunga zinthu

zambiri zomwe tizilombo tina timafuna kudya

nawo. Kunda anayamba kulimbana ndi

tizilomboto mpaka anaphedwa. Tizipewa

kuchita zinthu zomwe zingatibweretsere

mavuto. Dyera si labwino, limabweretsa

mavuto.

Nsanza zili ndi ntchito.

-Si bwino kumawononga zinthu zakale

monga chikhalidwe cha makolo chifukwa

chimakhalabe ndi ntchito.

Nsapato imodzi savala anthu awiri.

-Anthu angapo sangakhale pa udindo

Miyambi ya Patsokwe

381

umodzi.

Nsengwa siidya.

-Nsengwa, dengu kapena bwato

zimangosunga zinthu zimene mwaikamo,

sizimachepa kapena kuwonjezereka.

Tizikhutira ndi zimene tili nazo pamoyo

wathu.

Nsengwa ya muyeso amathyola ndi anansi.

-Nthawi zina anthu amene amakhala adani

athu chifukwa chowononga zinthu zathu

amakhala achibale kapena ena apafupi.

Nsengwa ya nsima savundikira ndi chikho.

-Timafunika kusamala zinthu zathu

pozisunga pabwino kuti zisawonongeke.

Nsengwa yobwereka samangira banja.

-Kuti munthu akwatire kapena achite

zinazake amafunika kukonzekera m’malo

momadalira zinthu za ena.

Miyambi ya Patsokwe

382

Nsikidzi zikalumaluma zimalowa

m’tsekera.

-Mawuwa amanena za anthu omwe amati

anzawo akawachitira zabwino

amangozimiririka osathokoza.

Nsikidzi zinachilira kwa alendo.

-M’nyumba anthu akhoza kukangana koma

kukabwera alendo anawaonetsa chikondi

komanso amaoneka ngati ogwirizana ndipo

nthawi zina mkanganowo umathera

pomwepo.

Nsima ya apongozi sasungira mlendo,

ngakhale yochokera kwa apongozi.

-Apongozi monga makolo, umayenera

kuwapatsa ulemu waukulu.

Nsomba ikawola imodzi, zonse zawola.

-Munthu m’modzi wosokoneza amaipitsa

mbiri ya anthu ambiri chifukwa cha khalidwe

lake loipa.

Miyambi ya Patsokwe

383

Nsomba ikaola imodzi, zaola zonse.

-Pamudzi munthu akakhala wamakhalidwe

oipa monga wakuba, anthu amangoti mudzi

wonse ndi wa anthu akuba ngakhale wakuba

ali m’modzi yekha. Kulakwa kwa munthu

wina kukhoza kukhudza anthu ena.

Nsomba ndi therere saphika mphika

umodzi.

-Nkhani kapena zinthu zosiyana si bwino

kuzikambira pamodzi. Chilichonse chiyenera

kuonedwa pachokha.

Nsungwi yantuwa sisiriridwa.

-Nsungwi yantuwa ndi yosakhwima. Palibe

munthu amene angaidule kuti akachitire

chinachake chifukwa imakhala yosalimba.

Munthu akakhala waulesi amuna kapena

akazi samufuna. Munthu azionetsa

chamuna.

Miyambi ya Patsokwe

384

Nsupa ndi nsupa, mulibe thonje.

-Munthu amadziwika ndi khalidwe lake.

N’zoona kuti tonse ndi anthu, koma

timasiyanabe zochita. Makhalidwe abwino

azionekera poyera.

Ntchembere yamapasa izigona chagada.

-Ukakhala pakati umaona mbali zonse ziwiri

n’kumapereka thandiza kumene

kukufunikira.

Ntchentche inati, “m’tsogolo moyo,

m’mbuyo moyo.”

-Si bwino kumachoka pamalo utaipitsapo

chifukwa tsiku lina udzafunanso

kubwererapo.

Ntchentche yadyera inapita ndi maliro

kumanda.

-Munthu wotengeka ndi zilizonse amataika

n’kukumana ndi mavuto.

Miyambi ya Patsokwe

385

Ntchentche yojijirika inaphinjidwa ndi

nchimba.

-Si bwino kukhala anthu ojijirika,

tingakumane ndi mavuto.

Ntchenzi idamva mawu oyamba.

-Munthu wina ananena kuti, “Nditchera

msampha mawa,” kenako anasintha

n’kunena kuti lero. Ntchenzi inangomva

mawu oyambawo ndipo inabwera

n’kugwidwa. Tizichenjera tikamanena zinthu

chifukwa anthu amagwira mawu anthu

oyamba.

Ntchenzi m’mbuyo.

-Mawuwa amanena za munthu wabodza.

Anthu amanena mawuwa pofuna kuchenjeza

anzawo kuti achenjere, wamabodza

akubwera.

Ntchito ndi mumtengo.

-Munthu ukakhala pantchito uyenera

Miyambi ya Patsokwe

386

kukhala mosamala ngati mmene umachitira

ukakwera mumtengo chifukwa nthawi

iliyonse ikhoza kutha, ukhoza kutsakamuka.

Ntchito siichepa.

-Ntchito ingakhale yonyozeka tiyenera

kuigwira mosamala komanso mwakhama.

Ntchito zimatsata msinkhu.

-Munthu wamkulu sayenera kumachita

zibwana.

Nthawi siidikira munthu.

-Kaya ukutani, nthawi simayembekezera kuti

uchite kaye zimenezo, imangopitabe.

Nthunzi sufuka pachabe.

-Nkhani simangomveka, pamakhala kuti

pachitika chinachake.

Nyalugwe m’chepsa chamnzake, iye

akapha chiwala achita kukoka.

-Pali anthu ena okonda kunyoza za anzawo

Miyambi ya Patsokwe

387

koma amakometsa zawo ngakhale zitakhala

zosalongosoka.

Nyalugwe mchepsa kanzake, mkuzakake

akapha chiwala achita chokoka.

-Pali anthu ena omwe safuna kuyamikira

zochita za anzawo, koma zawo ngakhale

kang’onong’ono amadzitamandira.

Nyama ya liuma inafa ndi ludzu.

-Nyama ina inkakakamira kuikidwa nyanga

zazitali. Chilala chitafika, madzi anayamba

kusowa moti nyama zina zinkamwa

kumphanga. Nyamayo inafa ndi ludzu

chifukwa cha nyanga zake zazikulu zina.

Kukula mtima, kusamva za ena kapena

mwano zimabweretsa mavuto.

Nyama yokoma idadza mano atantha

m’kamwa.

-Anthu ena akamabwekera nyama amanena

mawu amenewa.

Miyambi ya Patsokwe

388

Nyama yokoma idadza n’takalamba.

-Anthu ena akamabwekera nyama amanena

mawu amenewa.

Nyambo m’masiku, chimawerenga ndi

chitseko.

-Mawuwa amanenedwa wina akamachenjeza

mnzake kuti tidzaona m’tsogolo chifukwa

masiku sachedwa kutha.

Nyang’anyang’a amapulumutsa.

-Kuyenda kapena kuchita zinthu

mwachifatse kumapulumutsa munthu

m’zambiri.

Nyani samulekera munda.

-Si bwino kusiya kuchita chinthu chifukwa

cha munthu wina woononga kapena amene

akufuna kukusokoneza.

Nyau imakoma n’kuwala.

-Kuti mkazi kapena ana azioneka bwino

Miyambi ya Patsokwe

389

umafunika kuwaveka zovala zabwino.

Chinyau ndi chosaoneka bwino, koma

kuchipaka zina ndi zina kapena

kuchikongoletsa chimayamba kuoneka

bwino.

Nyenderera zidatha kakule.

-Munthu akamachita zinazake mobisa,

n’kupita kwa nthawi amalephera kuzisiya.

Nyimbo imodzi sachezera gule.

-Kusinthasintha zinthu kumathandiza.

Nyundo m’masulano.

-Nyundo ndi hamala. Nyundo imathandiza

kuti chigwandali chikhale mpeni. Ndi bwino

kumathandizana.

Nyumba imayamba ndi njerwa imodzi.

-Zinthu zikuluzikulu zimayamba ndi

zing’onozing’ono.

Miyambi ya Patsokwe

390

Nyumba ya chitsiru siipsa.

-Nthawi zina pooneka ngati wopusa,

umapewa mavuto ambiri.

Nyumba ya mwini saotchera mbewa.

-Munthu wina ankatenthetsa madzi oti

akawaze m’nyumba kuti aphe mphutsi.

Mlendo wake ankaganiza kuti akuphika

msima moti anaotcha mbewa zake.

Anadikirira koma nsima sinabwere.

Osamadalira zinthu za ena tikamachita

zinthu monga kukwatira tikuganiza kuti

makolo adzatithandiza.

Nyumba yabwino imakhala ndi moto.

-M’nyumba kuti mukhale mosangalatsa

muyenera kukhala zinthu zofunika monga

zakudya.

Nzeru ndi chuma.

-Munthu wanzeru ndi amene amatukuka

komanso kukhala moyo wabwino.

Miyambi ya Patsokwe

391

Nzeruzayekha adaviika nsima m’madzi.

-Ngati tikukayika kapena sitikudziwa

zoyenera kuchita ndi bwino kufunsa kuti

tichite zinthu moyenera.

Nzeruzayekha adaphika nyemba

zofumbwa.

-Kufunsa ena kumathandiza kuti tisapuse.

Nzeruzayekha anaviika nsima m’madzi.

-Kufunsa kumathandiza kuti tipewe kuchita

zinthu zopanda nzeru.

Nzimbe saidyera kutalika koma kuzuna.

-Maonekedwe amapusitsa. Tisamasankhe

zinthu chifukwa cha kukula kapena kuoneka

bwino koma kulimba.

Miyambi ya Patsokwe

392

O

Odwala agawa mphika.

-Mawuwa amanena za munthu amene

amakonda kupezeka pamene pali zabwino,

osati pamene pali mavuto.

Okazinga nthanga akazingira a mano kuti

akukute.

-Si bwino kuchitira nsanje ena

akamathandiza anzawo kuti atukuke. Anthu

amachitira zabwino anthu omwe akuoneka

kuti ali ndi tsogolo, m’mawu ena ali ndi mano

oti akhoza kukukuta.

Okoma apitana.

-Zabwino zimene timachitira ena zimachititsa

kuti ena azitichitira zabwino.

Okoma atani onga Fungwe.

-Anthu ena umatha kuwachitira zabwino

Miyambi ya Patsokwe

393

koma sayamika. Nyama ya Fungwe inali

yosowa kwambiri moti ena amati

akapatsidwa nyamayi amathokoza. Tiyenera

kumathokoza wina akatikankhira patsogolo.

Osachulutsa gaga m’diwa.

-Osachulutsa zonena zingasokoneze zinthu.

Munthu akaika gaga wambiri m’diwa, mbewa

imakhutsa isanafike padiwalo.

Osagula phazi la Njovu.

-Kungoona phazi la njovu sindiye kuti taona

njovu. Si bwino kumagula malonda omwe

sunawaone. Si bwino kumachita zinthu

mwaphuma komanso mosaganiza bwino.

Osamachepetsa kolemera.

-Osamaderera zinthu zomwe

zingakuthandize.

Osamafunsa chinyezi kubafa.

-Mawuwa amanena za munthu amene

Miyambi ya Patsokwe

394

akufunsa zinthu zoti akuzidziwa kale. Nanga

ndi ndani amene angakhale pansi

n’kumafunsa ngati kubafa kumakhala

chinyezi kapena ayi?

Osamafunsa za fungo m’chimbudzi.

-Mawuwa amanena za munthu amene

akufunsa zinthu zoti akuzidziwa kale. Ndani

angakhale pansi n’kumafunsa ngati

kuchimbudzi kumanukha kapena ayi?

Osamagenda kupolisi chamba chili

m’thumba.

-Kupalamula ukudziwa kuti uli ndi milandu

ina.

Osamagulitsana makasu othyoka.

-Tisamachitirane zinthu zopanda chilungamo

kapena kupusitsa anzathu.

Osamaluma dzanja limene limakuthandiza.

-Osamanyoza kapena kuchitira chipongwe

Miyambi ya Patsokwe

395

amene amakuthandiza.

Osamanyerera pambali pam’boo ukupaona.

-Osamachita zoipa, zabwino ukuzidziwa.

Mwachitsanzo, ena akakuuza malangizo

oyenera oti uchitire zinazake iwe n’kuchita

zosiyana ndi zimenezo, umakhala ngati

wanyerera pambali pam’boo ukupaona.

Osamasambira molimbana ndi madzi,

angakutenge.

-Si bwino kumachita zinthu zosiyana ndi

zimene ena akuchita chifukwa mapeto ake

umatha kukumana ndi mavuto. Munthu

amene akusambira n’kumalimbana ndi

madzi, amatopa ndipo madziwo amamutenga.

Osamasewera paulimbo.

-Pali zinthu zina zomwe zikhoza kuwononga

moyo wathu. Ndi bwino kupewa zinthu

zimenezo m’malo momachita masewera

n’kukumana ndi mavuto ngati mmene

Miyambi ya Patsokwe

396

mbalame imachitira ikakhala kuti imasewera

ndi ulimbo.

Osamatsinira mafulufute kuuna.

-Osamachita zinthu zomwe zingatsekereze

mwayi.

Osamayankhula za kuntchini kwadzadza.

-Osamayankhula zinthu zopanda nzeru

kapena zimene aliyense akuzidziwa kale.

Kapena kumanena zinthu zoti anthu

akudziwa kale. Nanga ndi ndani amene

sadziwa kuti kuntchini kumadzadza?

Osamayenda monyang’wa ngati supita

kuchimbudzi.

-Anthu tonse ndi ofanana. Tisamachite

matama chifukwa cha zinthu kapena udindo

umene tili nawo. Tonse ndi anthu ofanana.

Miyambi ya Patsokwe

397

Osamayerekedwa ngati supita

kuchimbudzi.

-Aliyense ndi munthu ndipo zimene

timafunika kuti tikhale ndi moyo n’zofanana.

Tisamawalire anzathu ngati tili ochita bwino

kapena ngati tili ndi luso lina, chifukwa tonse

ndi anthu basi.

Ngakhale nkhuku ataidula mutu,

singaganize choncho!

-Mawuwa ndi okokomeza osonyeza kuti

munthuyo sanaganize bwino mpang’ono

pomwe. Amayerekezera kuti ngakhale

Nkhuku itaduka mutu sigaganize choncho.

Osamwa mankhwala oyenera kupakidwa

pachilonda.

-Kusemphanitsa zinthu. Mawuwa

amachenjeza munthu amene akufuna

kuchita zinthu mopupuluma asanamvetse

bwinobwino zonse.

Miyambi ya Patsokwe

398

Osanditengera ku mtoso ngati maliro a

njoka.

-Mawuwa amatanthauza kutenga njoka

yakufa yomwe sukufuna utaikhudza ndi

kamtengo kotosera zomwe zimatanthauza

kunyoza. Tisamanyoze anzathu koma

tizilemekezana.

Osanditengera ku mtoso ngati nyama ya

galu.

-Mawuwa amatanthauza kutenga nyama

yagalu yomwe sukufuna utaikhudza ndi

kamtengo kotosera zomwe zimatanthauza

kunyoza. Tisamanyoze anzathu koma

tizilemekezana.

Osatsinira mafulufute kuuna.

-Munthu ukapeza mwayi winawake, uyenera

kupewa kuchita zinthu zomwe zingatsekereze

mwayiwo.

Miyambi ya Patsokwe

399

Osaotcha mlatho umene waolokera,

ungadzaufune ukamabwerera.

-Usamanyoza kapena kuwononga zinthu

zonse zatithandiza.

Oyanjana sagona nyumba imodzi.

-Mpofunika kumakondananso ndi anthu ena

m’malo mongokonda munthu m’modzi.

Oyenga mafuta satuwa.

-Anthu amene amachita zinazake amakhala

oyambirira kupindula ndi zinthuzo.

Miyambi ya Patsokwe

400

P

Pachedwa msulu pali nyerere.

-Kumene munthu amakonda kupita kapena

chimene akuchilimbikira ndiye kuti kuli

chabwino chimene akuona kuti apezako.

Pachoka mnzako pali malo.

-Wina akasiya kuchita zinazake, anzake

amapezerapo mpata wochita zinthuzo.

Pachulu ndapaleka, ana a mbuzi

angasewerepo.

-Pachulu ndi pamene anthu amakonda

kudzalapo ndiwo zamasamba chifukwa

zimabereka bwino. Mawuwa amanenedwa

munthu akasiya kuchita zinazake poopa kuti

zingowonongeka.

Pachulu palibe chiphe.

-Anthu ena otchuka amakhala okoma mtima,

Miyambi ya Patsokwe

401

koma pali ena osadziwika kwambiri omwe

amakhala oipa mtima.

Padiwa sasewera.

-Tisamachite zinthu zomwe zikhoza kutiika

m’mavuto.

Padutsa khasu sipanama.

-Kuchita khama pantchito kumabweretsa

phindu. Mwachitsanzo, munthu amene

wachita khama kulima sabwera

chimanjamanja.

Padyera mfulu, kapolo amadyera

pomwepo.

-Mnzako akakhala pabwino iwenso umadya

nawo zimene amapeza.

Padziwa ndi pansi mwana wa mfuko

akadwala.

-Munthu wina akakuchitira chipongwe

n’kuthawa, anthu amanena kuti,

Miyambi ya Patsokwe

402

“Ingomulekani, akadzapezeka tidzaona naye

chochita.”

Pafera kambuku pali matatalazi.

-Pamene pagonja wamphamvu kwambiri pali

mavuto.

Pafera munthu salephera kudzumapo.

-Munthu mavuto akamupanikiza amadzuma

ndipo ena amamva n’kumuthandiza.

Pafuka utsi pali moto.

-Mphekesera iliyonse imakhala ndi

nkhanikhani.

Pafupi ndi apo wafika.

-Osamadalira zinthu zomwe sunapeze. Ndi

bwino kumathokoza zimene uli nazo.

Pafupi padaolera njovu.

-Njovu itafa anthu ankati ili pafupi koma kuli

kutali moti mpaka njovuyo inaola anthu

asanapiteko. Ukamafuna kugwira ntchito,

Miyambi ya Patsokwe

403

ngakhale yaing’ono, umafunika kukonzekera

bwino kuti uimalize m’malo momangoiderera.

Pagona tonde padzinunkha.

-Munthu aliyense ayenera kuchita khama

pantchito kuti padzioneka kuti panali

munthu.

Pagule fumbi ndiwe mwini.

-Munthu aliyense amalimbikira kuchita

zinthu zake. Amaonetsetsa kuti zachitika

bwino kwambiri koposa mmene akanachitira

za ena.

Pagwa fisi paterera.

-Pamene munthu wamkulu walakwa ndiye

kuti panavuta.

Pakadafunda padajiwitsa galu.

-Tsiku lina galu anagona penapake pamene

pamkamveka bee, moti mpaka analephera

kukalowa m’nyumba ndipo anagona

Miyambi ya Patsokwe

404

pomwepo. Fisi atabwera anangomutola.

Kukakamira kuchita zoipa zomwe zimaoneka

ngati zosangalatsa kumabweretsa mavuto

oopsa. Osamakomedwa ndi zinthu.

Pakadapanda Njiri kufera m’dambo,

chizimba mukadayesanji?

-Dzino la Njiri ndi mankhwala a khunyu

komanso chizimba cha mankwala ena.

Osamapsera mtima munthu amene

watithandiza, ndi bwino tizimuthokoza.

Pakamwa ndi pa boma, ukasewera napo

pakumangitsa.

-Tiyenera kusamala ndi zomwe timanena

chifukwa zikhoza kutiika m’mavuto.

Pakamwa padzaulukira mbereswa.

-Mawuwa amanena za munthu wina amene

sanamvetse nkhani n’kumakauza ena. Anthu

akamamudzudzula amamuuza kuti

akamangoyankhulayankhula zomwe

Miyambi ya Patsokwe

405

sanazimvetse, pakamwa pake padzaulukira

mbereswa.

Pakamwa pakudya zamchere.

-Mawuwa amatanthauza kuti pakamwa

pamatha kutuluka zabwino ndi zoipa zomwe.

Munthu akhoza kulakwitsa ponena zinthu.

Pakamwa palibe m’dima.

-Munthu samaphonya pakamwa ngakhale

akamadyera mumdima, amakhala

anapazolowera kwambiri. Munthu

sangalephere kuchita zomwe anazolowera.

Pakamwa pamawombola.

-Anthu amene amadziwa kuyankhula amatha

kupulumuka pa mlandu chifukwa

chochenjera pakamwa.

Pakamwa pamodzi sipalawa ndiwo.

-Munthu m’modzi sanganene maganizo

oimira anthu onse. Timafunika kufufuza kwa

Miyambi ya Patsokwe

406

enanso kuti titsimikizire.

Pakamwa podya therere.

-Mawuwa amanena za munthu amene

amakonda kunena bodza. Pamakhala ngati

pakamwa pake mpoterera ndi therere.

Pakamwa saphonya.

-N’zovuta kulephera kuchita zimene

unazolowera. Ngakhale utakhala kuti ukudya

nsima mundima, sungaphonye pakamwa.

Pakamwa sipayamika, umayamika ndi

mtima.

-Tiyenera kumayamika anthu akatichitira

zabwino, osamangolandira ngati mmene

pamachitira pakamwa tikamadya.

Pakaphale phwiti sapheka.

-Mlandu wa m’bale wako umavuta kuweruza.

Pakati pa ine ndi inu pali kanthu.

-Mawuwa amanenedwa ngati mukuona kuti

Miyambi ya Patsokwe

407

pali kusamvana pakati pa inu ndi ena.

Pakhomo sitichoka ngati tikutuluka

m’chimbudzi.

-Ukamachoka pamalo umafunika kutsanzika

m’malo mongochoka ngati palibe amene

unawapeza.

Pakhota mchira wa nyani.

-Mawuwa amanenedwa potanthauza kuti

chenicheni sichikudziwika, pagona nkhani

sipakudziwika. Ngati padziwika amati,

“Tsopano tapeza pamene pakhota mchira wa

nyani.”

Pali chala pali munda.

-Kale anthu ankakonda kulozera anzawo

kumene kuli munda. Ndiye mawuwa

amatanthauza kuti pamene anthu

akulozerana ndiye kuti pali chinachake.

Mwachitsanzo, ena akamakuuza mavuto ako,

umayenera kudziwa kuti n’kutheka kuti

Miyambi ya Patsokwe

408

palidi vuto.

Palibe chinsinsi padziko lapansi.

-Ngakhale mutabisa chotani, zinthu

zimaululika.

Palibe munthu amasula mfuti nkhondo

itafika m’mudzi mwake.

-Munthu uyenera kumakhala wokonzeka

nthawi zonse kuti udziteteze ku mavuto.

Pamalima m’pamimba, khasu la Chidambo.

-Kuti munthu agwire ntchito amafunika

kudya mokwanira.

Palira mbirira pali khwawa.

-Pamene pakumveka madzi pamakhala kuti

pali mtsinje kapena khwawa. Mphekesera

zikamamveka ndiye kuti chinachake

chachitika.

Pama loyesera limathyola chala.

-Munthu akalakwa pamafunika kumupatsa

Miyambi ya Patsokwe

409

chilango chomuyenerera. Tikapereka

chilango chankhanza timakhala

tikulakwiranso munthuyo.

Pamene wapsa supitapo kawiri.

-Pamene munthu wakumana ndi mavuto

supitapo kawiri, pokhapokha ngati uli

woduka mutu.

Pamodzimodzi padawoletsa dzungu.

-Munthu amafunika kumayesanso zina.

Osamangochita chimodzimodzi chifukwa

pamapeto pake sangatukuke.

Pamsasa saipitsa.

-Ukakhala pamalo achilendo umafunika

kuonetsa khalidwe labwino. Komanso

ukachokapo si bwino kusiya utasokoneza

chifukwa umatha kukumana ndi mvula

n’kufunanso utabwerera kunsasa komwe

kuja.

Miyambi ya Patsokwe

410

Pamudzi pakakhala pa zitsilu, mkamwini

asamakulirepo mwendo.

-Si bwino kunyoza eni mudzi ngakhale

akuoneka opusa, chifukwa sudziwa zimene

amapangana.

Pamudzi pakakhala pa zitsiru mkamwini

asamakulirepo phazi.

-Ukakhala pamudzi wa eni usamadzionetse

kuti ndiwe wanzeru chifukwa sungadziwe

zomwe eni mudzi amapangana.

Pamudzi pamakoma ndi ana.

-Pakhomo popanda ana sipasangalatsa.

Pamudzi podziwadziwa, koma akusochera.

-Mawuwa amanena za munthu amene

akulephera kuchita chinthu chimene

akuchidziwa, ngati yemwe akusochera

m’mudzi womwe wakulira.

Miyambi ya Patsokwe

411

Pang’onopang’ono ndi mtolo.

-Zinthu zikuluzikulu zimayamba ndi zinthu

zing’onozing’ono. Mwambiwu

umatiphunzitsanso kuti kuchita zinthu

mwachifatse n’kothandiza kusiyana n’kuchita

zinthu mopupuluma.

Pankhondo sasekana.

-Chibwana sichimafunika pantchito pa

zinthu zofunika monga nkhondo.

Pantchito mpachikamwini, amakuchotsa

ndi usiku.

-Ndi bwino kumakonzeratu zimene ungachite

utachotsedwa ntchito chifukwa sudziwa kuti

ndi liti pamene udzachoke. Kumasamalira

ntchito pogwira ntchitoyo molimbika.

Pantchito n’kudyerana.

-Anthu omwe amagwira ntchito limodzi

amakonda kuchitira limodzi zinthu zina

monga kudyera limodzi mmemo. Tizigawana

Miyambi ya Patsokwe

412

zinthu zimene tapeza limodzi.

Papangano saika mwala.

-Kumakwaniritsa malonjezo ako m’malo

moikapo mwala.

Papita mkazi mnzako, nawenso pitapo.

-Nthawi zina ndi bwino kumachita zimene

ena akuchita monga pamaliro ndi malo ena.

Papita mnjere mpeni upita pomwepo.

-Mnjere ndi chakunja cha zipatso ngati

mandimu ndi malalanje. Munthu

ukamasenda ndi mpeni, mpeniwo

umangodutsa momwe chikhungucho

chathera. Munthu amalandira chilango

malinga ndi zimene wapalamula. Nthawi

zambiri munthuyo akakachita apilu,

zimapezeka kuti mpeni umadutsa momwe

woyamba uja unadutsa.

Miyambi ya Patsokwe

413

Papsa tong’ola sudziwa mtima wa moto.

-Ukamawotcha chimanga umafunika

kumangodyeratu chifukwa ukapusa

chimatha kupserera. Ndi bwino kumagwiritsa

ntchito mwayi ukapezeka chifukwa zamawa

sizidziwika.

Pasamba mfulu, kapolonso amasambira

pomwepo.

-Munthu ukakhala pantchito, chomwe bwana

wako wapeza monga phindu nawenso

umadyerera nawo. Komanso ukakhala ndi

anthu opeza bwino n’kumakhala nawo bwino

umadyerera nawo.

Pathindi Nkhwali, Mkango uli pomwepo.

-Nkhwali ikati itere powirira nthawi zina

pamakhalanso pali Mkango pomwepo.

Pamene pali zabwino pamakhalanso mavuto.

Ndi bwino kupirira mavutowo kuti upeze

zabwinozo.

Miyambi ya Patsokwe

414

Pati bii pali minga.

-Pamene pali ntchire nthawi zambiri

pamakhalanso minga. Pamene pali ntchito

pamakhalanso mavuto.

Patsala paja pagona chinziri.

-Nthawi zina ngakhale mlandu uweruzidwe,

anthu amasungiranabe chakukhosi, enanso

amadandaula kuti mlanduwo sunagamulidwe

bwino. Amakhala ngati akunena kuti “patsala

paja pagona chinziri.”

Patse salira tololo.

-Munthu wopemphetsa amafunika

kungolandira zimene wapatsidwazo. Mphatso

simadzadza dengu.

Patsogolo mpambuyo pomwe.

-Nthawi zina amene ali patsogolo amatha

kukhala pambuyo ngati anthuwo atauzidwa

kuti atembunuke. Chimodzimodzi ndi mwayi

umene ena ali nawo, mawa zikhoza

Miyambi ya Patsokwe

415

kutembenuka n’kupezeka kuti ndi wathu.

Paunjikana mtchembere pali bodza.

-Azimayi akakhala pagulu nthawi zambiri

amakonda kukamba mabodza.

Paunjinji samabuulirapo.

-Tisamayankhule pagulu zinthu zachinsinsi

monga nkhani za m’banja ndi zina chifukwa

zikhoza kungoyalutsa ife tomwe.

Paunjinji savulirapo.

-Nkhani zina zachinsinsi sitimaulula pagulu

poopa kupusa.

Paunyinji sabubulirapo.

-Anthu ena omwe safuna kuti anzawo

amveko zachinsinsi zawo amayesetsa kuti

akambirane zachinsinsizo enawo akachokapo

kapena amapita pamalo oduka mphepo.

Miyambi ya Patsokwe

416

Pavinidwa mfulu, kapolo amavinidwa

pomwepo.

-Munthu amadyerera akakhala kuti

amakhala bwino ndi anzake ochita bwino.

Pawiripawiri sipauzirika.

-Munthu sungapemerere utsi ku mauna awiri

a mbewa pa nthawi imodzi. Munthu m’modzi

sangachite zinthu ziwiri nthawi imodzi

zinthuzo n’kuyenda bwinobwino. Tizichita

chimodzi pa nthawi imodzi.

Payerepayere fisi anadya mkazi wake.

-Tsiku lina fisi anamva njala kwambiri ndipo

anadya mkazi wake. Anthu ena akasimidwa

amangochita zinthu bola apulumuke

m’mavuto awo. Anthu oterowo amachita

zinthu mwa payerepayere ngati zimene fisi

anachita podya mkazi wake njala itavuta.

Miyambi ya Patsokwe

417

Pendapenda si kugwa koma kuchalira

ulendo.

-Kulephera sikutanthauza kuti

sungakwanitse kuchita chinthu. Kuti

munthu achite bwino amafunika kukumana

kaye ndi mavuto.

Phika mowa kuti umve amene anapha

amako.

-Pamowa ndi pamene anthu amayankhula

zakukhosi kwawo ngakhale nkhani

zachinsinsi. Munthu woledzera ndi mwana

ndi amene amanenadi zoona akafunsidwa

zinthu. Kuti anthu akuuze zoona zenizeni

umafunika kuwanyengerera monga

kuwapatsa chinachake ndipo amasanza

nkhani yonse.

Phiri siliyendera munthu.

-Munthu amene akufuna chinachake ayenera

kupita kumene chinthucho chimapezeka.

Miyambi ya Patsokwe

418

Osamangodikira kuti chikupeza uli

pampando khale!

Phiri siliyendera nyani.

-Munthu amene akufuna chinachake ayenera

kupita kumene chinthucho chimapezeka.

Osamangodikira kuti chikupeza uli

pampando khale!

Phukusi la moyo sakusungira ndi mnzako.

-Munthu wamantha amakhala zaka zambiri

ndi moyo chifukwa manthawo

amamuthandiza kuti asamachite

mphulupulu zomwe zingachititse kuti afe

msanga.

Phuliphuli ndi penti, njinga ndi tcheni.

-Kumayang’ana mumtima m’malo

mopusitsika ndi maonekedwe akunja.

Maonekedwe amapusitsa.

Miyambi ya Patsokwe

419

Phwiti akakhuta salawira mtondo.

-Pali anthu ena ukawachitira zabwino

amangoti zii, osayamikira zimene

wawachitira. Amaoneka akakhala kuti

akufuna chinachake basi. Anthu

akakulandira bwino pamalo umafunika

kuwathokoza m’malo mongonyamuka ngati

ukutuluka m’chimbudzi. Phwiti akatha

kudya amangouyamba n’kumapita.

Piringupiringu ngwa njuchi, yoluma ndi

imodzi.

-Pokamba nkhani pafunika kunena zenizeni

m’malo momangozungulirazungulira.

Mwambiwu umanenedwanso pakakhala

anthu ambiri amene akuganiziridwa kuti

alakwa, koma pamapeto pake amapezeka

m’modzi.

Pita uko si kuyenda koma tiye kuno.

-Si bwino pamene muli paulendo umodzi

Miyambi ya Patsokwe

420

kupangana kuti dzera uko chifukwa pa

ulendo wotero pamavuta kukumana kwake.

Komanso pophunzitsa munthu zinazake, si

bwino kumangomuuza zochita iweyo

osachita.

Pofera salambula.

-Munthu sungadziwe kumene udzafere.

Choncho, kukhala bwino ndi ena n’kofunika,

ngakhale anthu akutali, kuti ukadzafera

kumeneko adzakuike m’manda.

Pokoma anatayira galu.

-Mawuwa amanena za munthu amene ndi

wosayenera kumupatsa zabwino.

Ukamupatsa nthuli yabwino amatayira agalu.

Pondupondu, njira idzera momwemo.

-Zomwe munthu umachitachita zimasanduka

chizolowezi. Ngati umachita zoipa

zimakulowerera, chimodzimodzi ukamachita

zabwino.

Miyambi ya Patsokwe

421

Popanda nkhuni moto sumayaka.

-Nkwiyo uli ngati moto, ukakhazikika

pamikangano komanso kumaputa anzako

moto umayaka. Anthu amatha kumenyana

chifukwa chosaugwira mtima.

Potepote mpoyamba, potsiriza ndi

chingwe.

-Zinthu zina zimayamba pang’onopang’ono

pomaliza n’kukhala zazikulu. Mwachitsanzo,

kuti vuto lichitika, pamakhala kuti pakhala

pakuchitika zambiri zomwe anthu

ankazinyalanyaza.

Psi! luma! n’kukhala ndi mbuyake.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wina

amakonda kudalira mphamvu za ena.

Pusepuse ulandira mpeni.

-Munthu sukhala wochenjera pa chilichonse,

tsiku lina anthu amakugwira

n’kukukhaulitsa.

Miyambi ya Patsokwe

422

Pusi adafa m’njakata.

-Tsiku lina pusi ankafuna kugwira zingwe

ziwiri nthawi imodzi moti anasokonezeka

n’kugwera pansi moti anathudzuka.

Sizimatheka kuchita zinthu ziwiri nthawi

imodzi. Nthawi zina umafunika kusankha

chimodzi.

Miyambi ya Patsokwe

423

S

Sadya galu adam’dula mlomo.

-Munthu wina ankanena kuti sadya galu.

Koma tsiku lina anthu anamupeza akutsuka

m’kamwa ndi galu yemweyo ndipo

anamudula mlomo. Tisamaneneretu kuti

chakuti sindingachite chifukwa tsiku lina

tingadzachite manyazi anthu atatipeza

tikuchita zomwezo.

Sadyeka adadyeka ndi ndi mafupa omwe.

-Si bwino kumadzitama ndi zimene tili nazo

chifukwa tingachite manyazi ena atatiposa.

Mwachitsanzo, munthu amene amadzitama

kuti amadziwa ndewu, anzake ena akhoza

kumuphwasamula.

Sadyeka adamudya ndi nyanga zomwe.

-Si bwino kumadzitama ndi zimene tili nazo

Miyambi ya Patsokwe

424

chifukwa tingachite manyazi ena atatiposa.

Mwachitsanzo, munthu amene amadzitama

kuti amadziwa ndewu, anzake ena akhoza

kumuphovomora.

Sadyeka anadyeka ndi mafupa omwe.

-Si bwino kumadzitama ndi zimene tili nazo

chifukwa tingachite manyazi ena atatiposa.

Mwachitsanzo, munthu amene amadzitama

kuti amadziwa ndewu, anzake ena akhoza

kumuphovomora.

Safunsa adadya phula.

-Munthu wina adadya phula m’malo mwa

uchi chifukwa chosafunsa. Kufunsira nzeru

kwa ena si kupusa, kumathandiza kuti

uchita zinthu moyenera.

Safunsa adafera m’chipululu.

-Ngati munthu sungafunse njira m’chipululu,

ukhoza kufera momwemo. Ndi bwino

kumafunsa ngati sitikudziwa chochita,

Miyambi ya Patsokwe

425

kusiyana n’kungochitabe, kenako

n’kukumana ndi mavuto.

Safunsa adamanga nyumba pamchenga.

-Munthu amene safuna kumva malangizo a

ena amachita zinthu zopanda nzeru monga

kumanga nyumba pamchenga.

Safunsa adanka ndi zoipa pabwalo.

-Munthu yemwe samafunsa ena amatha

kuchita kapena kunena zinthu zomwe

zikhoza kumuika m’mavuto.

Safunsa adapita kumanda.

-Kufunsa ena kumathandiza kuti

tisalakwitse.

Safunsa adataya mwana.

-Munthu wina ali paulendo anasungitsa

mwana wake kwa anthu ena. Iye sanaganize

zowafunsa kuti kwawo ndi kuti. Kenako

anthuwo ananyamuka n’kumapita ndi

Miyambi ya Patsokwe

426

mwana yemwe uja. Munthuyo anasowa

kolowera chifukwa sankadziwa kuti

angakawapeze kuti. Munthu amene safunsa

amatha kuwonongetsa zinthu zambiri.

Safunsa adatenga njira ya kumanda.

-Kufunsa ena kumathandiza kuti

tisalakwitse.

Safunsa adaviika nsima m’madzi.

-Mwana wina anapatsidwa mtolo wa luzi kuti

akauviike m’madzi. Iye sanafunse kuti

amuuziranji zimenezo, choncho anangoviika

n’kumabwerako. Atafika anthu anamufunsa

kuti, “Wadya nsima ija?” Iye anayankha kuti,

“Ayi.” Anamuuza kuti chifukwa cha

kuchuluka kwa anthu, anamuikira nsima

mu luzimo kuti akadyere kwina. Ndiye

chifuka choti sanafunse anakaiviika m’madzi.

Kufunsa zinthu si kupusa.

Miyambi ya Patsokwe

427

Safunsa anamangira nsima mumtolo.

-Kufunsa zinthu si kupusa. Munthu umatha

kuzindikira kapena kudziwa njira yochitira

chinthu ukafunsa.

Saweruzika adamera nyanga pamphumi.

-Nyama ina inauzidwa kuti kukagwa chilala

nyanga zimapangitsa kuti nyama izilephera

kumwa madzi. Koma iyo sinamvere ndipo

inameradi nyanga pachipumi. Chilala

chitabwera inafa ndi ludzu chifukwa imati

ikati imwe, nyanga zija zinkapezeka kuti

zagunda pansi. Kumvera kumathandiza kuti

tisakumane ndi mavuto oopsa.

Saweruzika anamanga nyumba pamwala.

-Munthu amene amadziyesa wodziwa zonse

amalephera kufunsa ena mapeto ake,

amalakwitsa anthu n’kumuseka. Ndi bwino

kumafunsa ena.

Miyambi ya Patsokwe

428

Sayenda adabala mwana adayenda.

-Usamachitire ena choyipa ngakhale iweyo

suyenda chifukwa nthawi ina amadzayenda

ndi mwana wako ndipo anthu unawanyozawo

amadzachitira choipa mwana wakoyo

pobwezera zimene iwe unawachitira.

Sayenda anabala mwana nayenda.

-Tisamanyoze anthu amene amaoneka

monyozeka chifukwa tsiku lina amadzachita

zinthu zomwe sitimayembekezera.

Sekerera cha nkhama, cha mano chiluma.

-Zinthu zikamakuyendera, nthawi zina ndi

bwino osasekerera (kusekerera cha nkhama)

chifukwa ena akakuona sasangalala.

Mwachitsanzo, kumangouza anthu kuti

wagula wailesi kungachititse kuti akubere.

Sekeserani, kumtondo kwanka ana,

Sakhwi watsala yense.

-Kusekesera ndi kusefa ufa. Munthu

Miyambi ya Patsokwe

429

amanena mwambiwu akamauza mkazi wake

kuti sanakhute, ndiye aphikenso chakudya

china.

Si mbewu yoisunga.

-Mawuwa amanenedwa akamafotokoza za

anthu ovuta kapena ana ovuta. Anthu ena

akakwiya amanena mawuwa potanthauza

kuti anthuwo ndi amphulupulu omwe

sangawasunge pakhomo.

Sikadza kokha kaopa kulaula.

-Kuti munthu atukuke kapena apeze

chimene akufuna amafunika kugwira ntchito

mwakhama.

Sikadza kokha, kaopa kulaula.

-Ngati munthu akusowa chinthu ayenera

kupita kukachifunafuna chifukwa

sichingamupeze pamene wakhalapo.

Miyambi ya Patsokwe

430

Sikuli komire kwa apongozi.

-Pachikamwini sipamafunika ulesi.

Umafunika kugwira ntchito mwakhama

m’malo modalira apongozi, chifukwa akatopa

nawe akhoza kukuthamangitsa.

Simbwesimbwe ananya chiwindi.

-Munthu wochita zinthu kuti ena

amutamande amadzakhaula tsiku lina.

Suku laliwisi silichedwa kukonyoka ndi

mphepo.

-Ana akakumana ndi mavuto samalimba.

Zimene akumana nazo zikhoza kusokoneza

tsogolo lawo lonse.

Sunga khosi, mkanda woyera udzavala.

-Munthu amafunika kupirira komanso

kudziletsa kuti adzapeze zabwino m’tsogolo.

Sunga khosi, mkanda uwoneka.

-Munthu amafunika kupirira komanso

Miyambi ya Patsokwe

431

kudziletsa kuti adzapeze zabwino m’tsogolo.

Suntche adati, “Pita pansi ukamve.”

-Osamamvera zilizonse zimene anthu

akunena. Kumatsimikizira kaye ngati zilidi

zoona.

Suzi suzi, alimba ndi mbalame zake.

-Munthu ukatchera msampha umasuzumira

kuti uone ngati wagwira kanthu. Ndi bwino

kumayang’ana kawirikawiri chinthu chomwe

tikuyembekezera.

Suzumire adaphetsa mkhalakale.

-Mbalame ina yomwe inkhakhala kuphanga

sinkasuzumira panja kuopa kuphedwa.

Tsiku lina inzake inabwera kudzakhala nayo

ndipo mbalameyi inalangiza inzakeyo kuti

isamasuzumire panja ikamva phokoso. Koma

mbalameyi sinamvere moti inasuzumira

ndipo anthu ataiona anaipha pamodzi ndi

inzake ija. Munthu wina akalakwa

Miyambi ya Patsokwe

432

n’kumafufuzidwa amapezeka kuti agwidwa

ndi ena amene anabisala n’kulangidwira

limodzi. Kuchenjeretsa kapena kusaugwira

mtima kumabweretsa mavuto ngakhale kwa

anthu ena aphee.

Miyambi ya Patsokwe

433

T

Taleka m’talawa adatha mphika.

-Munthu akazolowera kuchita chinthu

amafika polephera kuchisiya. Mwachitsanzo,

ukayamba kuchita zoipa umazolowera

n’kuyamba kuvutika kuti usiye.

Taleka ndiyese anakwatira mkazi wa

mfumu.

-Tisamataye mtima msanga ngati tikufuna

zinazake chifukwa nthawi zina zosatheka

zimatha kutheka.

Talemberana chimfine.

-Kulemberana chimfine ndi kupatsirana

chimfinecho. Anthu angapatsirane chimfine

ngati ali malo amodzi. Choncho, mawuwa

amanthauza kuti anthu akumana pamodzi

pachibale kapena anakumana kuti

Miyambi ya Patsokwe

434

akambirane zinazake.

Tambala adalipira fundudwa.

-Munthu ukamayenda ndi wina wokonda

zoipa tsiku lina umadzalipira chifukwa cha

zolakwa zake.

Tambala akavumbwa akunga nsoti.

-Tambala akanyowa nthenga zake

zimamatirira kuthupi lake moti amangooneka

ngati kankhuku kakang’ono. Chimodzimodzi

munthu wamkulu akachita zopusa anthu

amasiya kumulemekeza.

Tambala akavumbwa sayenda malonda.

-Tambala akanyowa nthenga zake

zimamatirira kuthupi lake moti amangooneka

ngati kankhuku kakang’ono. Utamugulitsa

sangayende malonda chifukwa amaoneka

ngati nkhuku yaing’ono. Chimodzimodzi

munthu wamkulu akachita zopusa anthu

amasiya kumulemekeza.

Miyambi ya Patsokwe

435

Tambala amakula kwawo, kwa eni

n’chipsolopsolo.

-Ngakhale kwanu utakhala wolemekezeka,

ukakhala kuchilendo umafatsa.

Tambala n’tabwali, amamasula tambwali

mnzake.

-Ukafuna kugwira mbala umafunika kutuma

mbala inzake.

Tambala salira kwa eni, amalira kwawo.

-Munthu sungakhale mfumu kwa eni, koma

kwanu.

Tangovutika, opanirira mphika ali chete.

-Nthawi zambiri anthu amene amagwira

ntchito yolemetsa komanso yokhetsa thukuta

sapeza ndalama zambiri, koma mabwana awo

omwe amangokhala muofesi.

Tapita m’njira adasiya tonse m’khola.

-Tikamadutsa pamudzi wa abale kapena

Miyambi ya Patsokwe

436

anthu owadziwa tiyenera kumakawaona kuti

ali bwanji, chifukwa tikhoza kuwadutsa iwo

ali m’mavuto kapena asakupeza bwino.

Tatuma chitsiru kuti chimange mtembo.

-Mawuwa amanenedwa anthu

akamadandaula kuti munthu amene

anamutuma kuti agwire ntchito inayake

wailephera kapena wachita zokhumudwitsa.

Tentha tizime adapsetsa anzake.

-Mawuwa amanena za munthu amene

ankauza anzake kuti ayatse moto ndipo

auzimitsa pamapeto pake n’kupezeka kuti

waotcha anzakewo. Anthu ena amaputira

anzawo mavuto chifukwa cha khalidwe lawo

loipa. Mwachitsanzo, bambo wokonda mowa

amachititsa kuti ana ake avutike.

Thendo limakoma, nyama kulowa m’mano.

-Masamba otendera amakoma. Komabe

nyama ndi yokoma kwambiri koma kulowa

Miyambi ya Patsokwe

437

m’mano. Ukafuna zokoma umafunika

kudziwa kuti zili ndi zowawa zake.

Thumba la Tambe amamasula ndi Tambe

yemweyo.

-Munthu akakhala kamberembere amene

amadziwa khalidwe lake ndi

kamberemberenso. Tambwali akamanga

thumba, amene angamasule ndi tambwali

mnzake.

Tidauluka tidapangana, mavu adaning’a

onse.

-Anthu amafunika kupangana kuti zinthu

ziyende monga pamilandu ndi zina.

Tikapha Mwiri m’mphako, koma kuloza

mwendo momwemo kuti tiphe wina.

-Tikapeza mwayi, tisasiyire pomwepo,

tipitirizebe mpaka titapeza wina.

Miyambi ya Patsokwe

438

Tikhale nawo adalanda malo.

-Pali anthu ena omwe amabwera pamudzi

kuti adzapemphe malo, koma kenako

amalanda malo kapena kuyamba kulamulira.

Timba anathyola mwendo dansi yothaitha.

-Munthu akamachita zinthu mopitirira

muyezo amakumana ndi mavuto. Ndi bwino

kumasamala ndi zinthu zikakhala kumapeto,

umatha kukumana ndi mavuto.

Timba sachepa ndi mazira ake.

-Tisamanyoze munthu chifukwa cha zimene

ali nazo. Munthu sachepa ndi zinthu zake.

Tinamva kale zanu.

-Palibe chinthu chatsopano chomwe

mungatiuze.

Tinthu m’nkhuni adalekera mwana wa

mkazi mnzake ku njoka.

-Tikamva zoti penapake pali zovuta tiyenera

Miyambi ya Patsokwe

439

kupitapo tokha m’malo mouza wina kuti

apite, chifukwa tingamuphetse. Zili ngati

kutumiza mwana kuti akaone chomwe chili

pamtolo n’kukamulumitsa njoka.

Tizisinja kamba, kuyenda kwa ulendo

sikudziwika.

-Kamba ndi chakudya cha paulendo. Ndi

bwino kumakonzekera zapatsogolo kuti

tisapeze mavuto monga kukonzeratu

chakudya cha paulendo chifukwa sitikudziwa

zimene zingatichitikire.

Tokoma sitichedwa kutha, ndaonera dowe.

-Zinthu zabwino sizichedwa kutha. Tisamaike

mtima wathu pa zinthu zosakhalitsa.

Tokoma sitikuti “leke.”

-Zabwino sizingauze munthu kuti asiye,

umafunika wekha kudziwa kuti pamene

ndafikapa ndakwana.

Miyambi ya Patsokwe

440

Tokoma sitioneka tsiku limodzi.

-Tizifatsa ndi kumaupeza mtima chifukwa

zabwino zimabwera pang’onopang’ono.

Tokoma tidadza n’takalamba.

-Zokoma zimabwera munthu utatha kale

kapena nthawi imene sumayembekezera.

Tonde akadula, sabwerera.

-Tonde akadula cholinga chake chimakhala

kupita komwe kuli matazi. Akawapeza

amangoumirira komweko. Chimene mtima

wako watsimikiza osaleka mpaka chitatheka.

Tsabola wakale sawawa.

-Mawuwa amatanthauza kuti malangizo a

anthu akale ndi osathandiza.

Tsachipenembe anaotcha nkhokwe.

-Munthu amene amadziwa bwino mmene

zinthu zimakhalira ndi kuyendera ndi amene

nthawi zina amabweretsa chipwirikiti.

Miyambi ya Patsokwe

441

Tsamba likagwa manyazi amagwira

mtengo.

-Mwana akalakwa manyazi amagwira makolo

ake. Makolo akhoza kupeza mavuto chifukwa

cha ana awo.

Tsata mphero.

-Mawuwa amanenedwa pochenjeza munthu

kuti angopitira kukapera ufa, osati kukanena

mabodza.

Tsatanetsatane ndi njira.

-Munthu poyankhula sangathe kunena

ndendende zonse zimene waona kapena

zimene wina wanena.

Tulo ndi nkhondo, tinagonetsa anamalira.

-Ena amaganiza kuti, kuti asonyeze kuti

amakonda kwambiri m’bale wawo amene

wamwalira, afunika kulira usiku onse. Koma

tulo tilibe masewera, timatha kugonetsa

munthu wotereyu.

Miyambi ya Patsokwe

442

Tsekera lili pachipadzo.

-Udzu wabwino umasadzulidwa ndi nsungwi.

Chimodzimodzinso mwana, kuti akule bwino

timayenera kuyambiratu kusadza

makhalidwe ake oipa adakali wamng’ono.

Tsiku limodzi silivunda nyama.

-Zinthu zina sizingatheke tsiku limodzi,

pamafunika nthawi.

Tsiku limodzi siliwoza mbewa.

-Nthawi zina ndi bwino kudikira pochita

zinthu chifukwa tikachita mofulumira nthawi

zina zinthuzo sizichitika bwino. Zinthu zina

sizingatheke tsiku limodzi, pamafunika

nthawi.

Tsiku lofera nyani mitengo yonse

imaterera.

-Anyani ena ankadalira mitengo kuti agalu

akamabwera angokwerapo. Koma tsiku lina

agalu akubwera anyaniwo anapeza kuti

Miyambi ya Patsokwe

443

mitengo yonse inali yoterera moti anagwidwa.

Tizikonzekera zinthu zomwe zikhoza

kutigwera.

Tsitsi likakula udzasowa wokumeta.

-Munthu wosamva amamva akakumana ndi

mavuto.

Tsoka chitambe.

-Chitambe chimakhwima nsanga kuposa

masamba ena. Zimenezi zimachititsa kuti

chikhale choyambirira kudyedwa. Mwana

woyamba ndi amene amakumana ndi zoopsa.

Tisamathamangire kuchita zinthu

tisanaganize bwino.

Tsoka la mnzako likupatse nzeru.

-Wina akalakwitsa chinachake, ndi bwino

kumaphunzirapo kanthu kuti tisabwerezenso

zomwezo. Moyo ndi waufupi kwambiri kuti

munthu aphunzire pa zolakwa zake zokha.

Miyambi ya Patsokwe

444

Tsoka la mnzako n’lakonso.

-Nthawi zina tsoka la ena limakhudzanso

anthu ena, monga oyandikana nawo

nyumba. Tizithandiza ena akakhala

m’mavuto.

Tsoka la msinde, chimanga chilinda moto.

-Misinde imacha mwamsanga moti anthu

amayamba kuidya chimanga chisanakhwime.

Anthu ena amazunza anzawo mosasamala

kanthu kuti ndi abale awo.

Tsoka la Nkhuku lopita kumanda nthenga

zokha.

-Limeneli ndi tsoka lalikulu kwambiri lomwe

munthu angakumane nalo. Nkhuku ikafa

maliro ake saikidwa m’manda. Kumanda

kumangopita nthenga zokha basi.

Tsoka likakuda Kamba amaoneka ngati

mwala.

-Kamba ngati sakusuntha amaoneka ngati

Miyambi ya Patsokwe

445

mwala. Nkhani zina zimakhala

zosamvetsetseka. Wina akhoza kudwala

mwakayakaya koma wina wolimba

n’kumwalira kusiya wodwalayo.

Tsoka likalimba amakuluma ndi galu wako

yemwe.

-Zinthu zikati zivute, nthawi zina anthu

amene umawadalira ndi amene amakutaya.

Tsoka likalimba umakuotcha ndi mkute.

-Zinthu zikati zivute, nthawi zina anthu

amene umawadalira ndi amene amakutaya.

Tsoka lilibe fungo.

-Tsoka limabwera mwadzidzidzi.

Tsoka limayambira kumwendo.

-Tsoka limayamba pang’onopang’ono. Anthu

ena a ku Africa kuno amakhulupirira kuti

munthu akamayenda ndiyeno n’kupuntha,

ndiye kuti kumene akupitako akapezako

Miyambi ya Patsokwe

446

matenda kapena maliro. Mawuwa

amagwiritsidwa ntchito ponena kuti uli ndi

tsoka lalikulu. Tsoka limayambira pa kanthu

kakang’ono komwe anthu sangakaganizire

kuti kangayambitse vuto lalikulu.

Tsoka msinde chimanga chilinda moto.

-Mawuwa amatanthauza kuchita tsoka

lalikulu.

Tsoka n’kusuzumira m’chizombwe.

-Munthu wachidwi kwambiri amatha

kukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo,

posuzumira pachulu amatha kulavuliridwa

ndi njoka.

Tsoka ndi mphwayi, ukafuna kanthu koma

kuyesa.

-Munthu wamphwayi sangapeze zimene

akufuna. Tizichita khama tikamachita

zinthu.

Miyambi ya Patsokwe

447

Tsoka sasimba, koma mwayi.

-Ukapulumuka tsoka, si bwino kukakamira

khalidwe lomwe lakubweretsera tsokalo

chifukwa mwina pambuyo pake ukhoza

kutaya moyo wako kapena osapulumukanso.

Tsoka silinunkha.

-Tsoka limabwera mwadzidzidzi.

Tsokonombwe adatha mtunda

n’kudumpha.

-Nthawi zina ndi bwino kuchita zinthu

mosathamanga komanso ndi bwino

kulimbikira kuti zomwe ukufuna zitheke.

Zinthu zikuluzikulu zimatheka pozichita

pang’onopang’ono komanso ngati titapirira.

Tulo n’timodzi, usiyana ndi mkonono.

-Tonse ndi anthu koma timasiyana khalidwe.

Tulo ndi imfa, susankha pogonera.

-Zinthu zina zimafika mosayembekezera

Miyambi ya Patsokwe

448

monga imfa.

Tulo ndi nkhondo, timagonetsa anamalira.

-Tizichita zinthu mwamphamvu komanso

molimba mtima ngati mmene tulo

timachitira.

Miyambi ya Patsokwe

449

U

Ubale waufulu uli pamalemba.

-Anthu amagwirizana akakhala patali, koma

akakhala pamodzi sachedwa kukhulana.

Ubwenzi wa “ponda apo mpondepo.”

-Chimenechi ndi chikondi chenicheni

chochitira zinthu limodzi.

Ubwenzi wa galu uli kumchira.

-Ubwenzi weniweni uyenera kumakhala ndi

ntchito zake, osati kumangonena pakamwa

pokha kuti awa ndi anzanga, zikawavuta

n’kuwathawa.

Ubwenzi wa madzi ndi nsomba.

-Ubwenzi weniweni umakhalapo ngati anthu

amakhalira limodzi osasiyana zivute zitani.

Miyambi ya Patsokwe

450

Ubwenzi wa Nkhwazi woyanjana polira.

-Polira pokha ndi pamene Nkhwazi

zimagwirizana. Koma ikagwira nsomba

imadya yokha. Mawu amenewa amanena za

munthu amene amakhala mnzako akavutika,

koma zikamamuyendera saoneka. Ubwenzi

weniweni umaoneka zinthu zikavuta.

Ubwenzi wa nsomba wosalekana ndi madzi.

-Ubwenzi wa nsomba ndi madzi ndi

weniweni. Pamene madzi aphwera nsomba

imafa. Mawuwa amatanthauza ubwenzi

weniweni woferana.

Ubwino wa dzuwa umaoneka likapita.

-Munthu wabwino amadziwika akapita.

Mwachitsanzo, ena amazindikira kuti mkazi

kapena mwamuna wawo anali wabwino banja

likatha. Nthawi zambiri amazindikira

zimenezi akakwatirana ndi chilombo.

Miyambi ya Patsokwe

451

Uchembere n’kudyerana.

-Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi

bwino kumuchitira zabwino.

Udakula bwanji wopanda tsinde?

-Tisamaiwale abale komanso anthu ena

omwe atithandiza kuti tifike pamene tili lero.

Udam’dyeranji pholokoto anzako akudya

kawerawera?

-Tizigwira ntchito molimbika kuti tipeze

zosowa zathu. Polima timawerama osati

kuimirira.

Udaotha chichiri cha ukonde.

-Chichiri chimathandiza kuti ukonde ukhale

wokungika. Mawuwa amagwiritsidwa ntchito

potanthauza munthu yemwe wapalamula

kapena kulakwira anthu omuthandiza.

Ufiti ndi mawu.

-Tisamayankhule zonyoza kapena kutukwana

Miyambi ya Patsokwe

452

chifukwa china chikachitika anthu amaloza

ife.

Ufulu umabweza ufulu.

-Ukachitira anzako zabwino nawonso

amakuchitira zabwino.

Ufulu wa ng’ombe wogwedeza mchira.

-Pali anthu ena omwe amati munthu

akawachitira zabwino sathokoza. Monga

mmene ng’ombe imachitira akaipatsa

chakudya, chinthu chimene imachita

ikamayamikira ndi kugwedeza mchira,

sibweza kalikonse.

Ufumu wanji wa Kadzidzi wokhala

pachitsa?

-Mfumu isamangokhala neng’a, koma izichita

zinthu zomwe zingathandize anthu ake.

Miyambi ya Patsokwe

453

Ufune kaya uleke, kulidetsa tsitsi ndi

ufulu.

-Chilichonse chili ndi nthawi.

Ufunthafuntha mphuku, mbiri nja khoswe.

-Munthu akakhala woipa kapena

wochenjeretsa amasowa mtendere, chifukwa

chilichonse choipa amangoti wachita ndiwe.

Uhule ndi mtima.

-Munthu sakhala hule chifukwa cha mmene

akuonekera koma mtima wake.

Ukabwereka miyendo ya munthu, umapita

kulikonse kumene iyeyo akufuna.

-Munthu amene ali ndi ngongole sakhala ndi

ufulu wochita zimene akufuna ndi ndalama

yake.

Ukachedwa umagula khutu.

-Mwambiwu umachenjeza munthu amene

amachita zinthu mochedwa kapena

Miyambi ya Patsokwe

454

mwachidodo. M’malo mogula nyama yabwino

amakapena kuti latsala ndi khutu.

Ukachenjera sunona.

-Nthawi zambiri amene amakonda

kuyankhulayankhula kapena ochenjeretsa

amakhala opanda nzeru. Chimodzimodzinso

okongola, amangokongola nkhope koma

n’kukhala opanda nzeru kapena opanda

khalidwe.

Ukachoka usamachitire dziko chipongwe,

umakumbukira pokabwera.

-Pochoka pamalo umayenera kuchoka

mwaulemu kuti mawa adzakulandirenso.

Ukachoka usamatseke potulukira ndi

mwala koma mayani.

-Osamachoka pankhomo utawonongapo

chifukwa tsiku lina udzabwerera.

Miyambi ya Patsokwe

455

Ukadya, umadziwa azungu ndi alendo.

-Ukalemera usamanyoze anzako chifukwa

ntchito ikatha, sudzakhalanso ndi azungu

koma abale ako. Komanso anzako omwe

unkawanyoza. Pang’ono mwambiwu

umalimbikitsa tsankho. Mukadzaugwiritsa

ntchito musadzadabwe apolisi

akadzakumangani.

Ukafuna kupha galu umapezeratu mtengo.

-Ndi bwino kupezeratu zinthu zonse zofunika

usanayambe kugwira ntchito.

Ukaipa dziwa nyimbo.

-Palibe munthu amene amadziwa zonse

kapena amene ali ndi zonse zofunikira.

Zikakuvuta zina umafunika kusakasaka

zimene umachita bwino n’kumachita

zimenezo.

Ukaipa nkhope, dziwa kuvina.

-Palibe munthu amene amadziwa zonse

Miyambi ya Patsokwe

456

kapena amene ali ndi zonse zofunikira.

Zikakuvuta zina umafunika kusakasaka

zimene umachita bwino n’kumachita

zimenezo.

Ukaipa nkhope, dziwa nyimbo.

-Palibe munthu amene amadziwa zonse

kapena amene ali ndi zonse zofunikira.

Zikakuvuta zina umafunika kusakasaka

zimene umachita bwino n’kumachita

zimenezo.

Ukakalamba usamabise lumo kuti ena

asametere.

-Tisamapondereze anzathu koma tiwapatse

mwayi wokhala ndi zomwe akufuna.

Ukakhala kwa eni umafunika kukhala

nkhosa.

-Munthu ukakhala kwa eni umayenera

kufatsa. Ukamachita matukutuku

amakuthamangitsa.

Miyambi ya Patsokwe

457

Ukakhala m’mwamba usamatukwane

pansi, ungadzasowe wokutola ukagwa.

-Osamanyoza anzathu tikakhala pabwino.

Ukakhala mwana, mphanje umayambira

pamchenga.

-Ukafuna kuphunzira kuchita zinazake,

umafunika kuyamba ndi chophweka.

Ukakhala pabwino, poipa pamakuitana.

-Mwayi suchedwa kutha. Nthawi zina

ukakhala pabwino pamakhala ziyeso zambiri

zingakukope kuti uchokepo pabwinopo.

Ukakhala wopanda chala, usamadane

n’kuloza.

-Tisamapondereze mwayi wa anzathu

chifukwa choti tilibe.

Ukakhala wopanda galu, umalimba ndi

mpiringidzo.

-Munthu amene alibe galu pakhomo

Miyambi ya Patsokwe

458

amafunika kukhoma chitseko chake. Kale

ankagwiritsa ntchito mtengo kapena kuti

mpiringidzo poteteza kuti chitseko chawo

chisatseguke chisawawa. Tizidalira zimene tili

nazo. Ngati tilibe galu, mtengo kapena mwala

zingathandize kupirikitsa akuba.

Ukakhala wopanda kanthu, dziko

umalidyera ku uchi.

-Ngakhale munthu wosowa, pa masiku a

phwando nayenso amadyako zabwino.

Ukakhala wopanda mano, usamaswe phale.

-Ifeyo zikatikanika, tisamatsekereze mwayi

wa anzathu.

Ukakhala wopanda mng’oma umadya

mavu.

-Munthu amapeza zinthu zogwirizana ndi

zomwe ali nazo. Munthu wopanda mng’oma

sangadye uchi.

Miyambi ya Patsokwe

459

Ukakhala wopanda tsitsi, usamabise lumo.

-Tisamapondereze anzathu koma tiwapatse

mwayi wokhala ndi zomwe akufuna.

Ukakhuta pachika, ana apano sakhuta.

-Ukakhala ndi zinthu kumasunga chifukwa

mawa ungadzazifune.

Ukakhuta umawotcha nkhokwe.

-Tisamapondereze ena powachotsera mwayi

wopeza zosowa zawo. Ukakhala pabwino

usamataye zinthu chifukwa njala ikhoza

kukupwetekanso.

Ukakhuta usamatsinkhire anzako ndiwo.

-Si bwino kupondereza ena ife tikakhala

pabwino.

Ukakhuta usamatukwane yemwe

wakupatsa chakudya.

-Munthu akakhuta amaganiza kuti njala

singamupwetekenso. Choncho amayamba

Miyambi ya Patsokwe

460

kunyoza komanso kuchitira mwano amene

amamuthandiza. Tisamachite khalidwe

limeneli.

Ukakoka dzungu, umakoka ndi ana ake

omwe.

-Munthu ukakwatira kapena kukwatiwa,

osasakonda munthu yekhayo komanso abale

ake.

Ukakoka khoka, umakokanso zonse

zomwe zilimo.

-Munthu ukakwatira kapena kukwatiwa

osasakonda munthu yekhayo komanso abale

ake.

Ukakongola kwatiwa, chifukwa kunyansa

kumachita kubwera.

-Mwayi ukapezeka tiziugwiritsa ntchito.

Ukakongola leka thyonyo.

-Ukakhala wokongola usamanyoze anzako

Miyambi ya Patsokwe

461

chifukwa za mawa sizidziwika, mwina ukhoza

kudzakhala ndi chilema m’tsogolo.

Ukakwera m’mwamba usamatukwane

pansi, ungasowe wokutola ukatsakamuka.

-Si bwino kumanyoza ena ukakhala pabwino

chifukwa zikadzakuvuta udzasowa

wokuthandiza.

Ukakwera m’mwamba usamatukwane

pansi.

-Ukakhala pabwino usamanyoze anzako

chifukwa zikadzakuvuta udzasowa

wokuthandiza. Mwachitsanzo,

ukamatukwana anthu omwe ali pansi

ukakwera mumtengo, ukatsakamuka

umasowa wokutola.

Ukakwera pamsana pa njovu, usamati

kulibe mame.

-Osamachita matama ukakhala pabwino

chifukwa za mawa sizidziwika. Ukakhala

Miyambi ya Patsokwe

462

pabwino usamanyoze anzako.

Ukalakwa usamafulumire kupita kuboma.

-Kumayamba watsikiza kuti ndiwe

wosalakwa ukamapita ndi nkhani kuboma

chifukwa ukhoza kungomangidwa nazo ulele.

Ukalemera cheuka, ona chakulemeretsa.

-Tisamaiwale anthu amene atithandiza kuti

tifike pano.

Ukalemera tsekako, ‘kulinji’ akudza

m’njira.

-Ukalemera usamadzitame chifukwa akuba

akhoza kukubera iwe n’kufota. Chakudza

sichiimba ng’oma.

Ukalemera umayankhulira m’chigulu.

-Tikalemera tisamaonetse zonse zomwe tili

nazo chifukwa ena akhoza kutibera. Chigulu

ndi chikho chomwera mowa. Kuyankhulira

m’chigulu kukusonyeza kuti suima pachulu

Miyambi ya Patsokwe

463

n’kumabwebwetuka za kulemera kwako.

Ukalemera usamavinire poyera, koma

m’nyumba.

-Tikalemera tisamaonetse zonse zomwe tili

nazo, chifukwa ena akhoza kutibera.

Ukalemera, abale sakondwera.

-Zinthu zikamakuyendera kapena ukakhala

pabwino, anthu sasangalala. Amafuna kuti

chinachake choipa chimuchitikire kuti

mufanane.

Ukalira mzinda usamapse mtima.

-Ngati mfumu ikufuna kukhala ndi mudzi

waukulu, iyenera kupewa kupsa mtima.

Mtsogoleri amafunika kukhala woleza mtima.

Ukamachoka umachoka bwino, suchoka

utakhadzula mnzako mlomo.

-Mlendo amayenera kuchoka bwino pamalo,

apo ayi anthu sangadzamulandirenso. Anthu

Miyambi ya Patsokwe

464

sangalandire munthu amene wachoka

pakhomo atakhadzula mlomo wa mnzake.

Ukamafuna dzino lalitali, uzikhala ndi

mlomo wovindikirira dzinolo.

-Ukamawaputa mavuto kumadziwa kuti

uthana nawo bwanji. Osamayamba kuchita

chinthu ulibe mapulani.

Ukanama sikuchedwa kucha.

-Ukanena zabodza suchedwa kugwidwa.

Chitsanzo: Ngati utanamiza wangongole kuti

abwere mawa, sikumachidwa kucha.

Ukaona chalero, usataye chakale.

-Ndi bwino kumasunga zinthu zakale,

osazitaya chifukwa choti tapeza zina.

Ukaona mtanda kukula ndiye umati,

“ndim’lere mwana wanuyu!”

-Anthu ena amakonda kapena kuchitira

zabwino anzawo akaona kuti apindulapo

Miyambi ya Patsokwe

465

kenakake. Mwachitsanzo, kuuza munthu

kuti amulelera mwana chonsecho akufuna

amunyengerere nsima yake.

Ukapalamula uzikhala wokonzeka.

-Munthu ukalakwa umayenera

kuyembekezera kuti ukumana ndi

zotsatirapo zake.

Ukapalana ubwenzi ndi mphezi, suopa

kung’anima.

-Munthu amene akufunitsitsa chinthu

ayenera kukhala wolimba mtima.

Ukapalana ubwenzi ndi Vumbwe umakhala

uli ndi Nkhuku.

-Tizikhala titakonzeka tisanayambe kuchita

chilichonse. Kuti anthu azikonda kubwera

pakhomo umafunika kumawadyetsa bwino.

Miyambi ya Patsokwe

466

Ukakhala wopanda chala usamadane

n’kuloza.

-Ngati sungathe kugwiritsa ntchito chinthu

usamadane ndi amene angathe.

Ukakhala wopanda mano usamaswe phale.

-Ngati sungathe kugwiritsa ntchito chinthu

usamadane ndi amene angathe.

Ukapeza ana a olemera akukazinga maso a

nkhono, kazinga nawo.

-Tizichita zimene anzathu akuchita.

Ukapeza anzako akukazinga maso,

nawenso kazinga ako.

-Munthu uzichita nawo zomwe eni mudzi

akuchita kapena wawapeza akuchita.

Ukapeza anzako akutong’ola maso, nawe

tong’ola ako.

-Tizichita zimene anzathu akuchita.

Miyambi ya Patsokwe

467

Ukapeza eni mudzi akukazinga maso,

nawenso kazinga ako.

-Tizichita zimene anzathu akuchita.

Ukapeza nyamu zikuuluka, ima pambali

uzitola imodziimodzi, upeza zadzaza

nsengwa. Koma ukaikapo dzanja, udzatola

imodzi yokha.

-Munthu ayenera kumachita zinthu mofatsa

kuti apeza zabwino. Dyera komanso changu

nthawi zina sizithandiza.

Ukapha mwiri umabweza mphanda.

-Munthu akalemera amakhala wokongola

ngati mwiri. Ndiye zikatero si bwino kuyamba

kunyada n’kumanyoza ena.

Ukapha tonde wonona, usamathe mawu.

-Tisamanyade kapena kudzitama tikakhala

ndi chinthu chinachake.

Miyambi ya Patsokwe

468

Ukapindula wotcha, akazi ndi alendo.

-Munthu asamaiwale kapena kunyoza abale

ake chifukwa cha mkazi, banja limatha koma

chibale sichitha.

Ukapita kuthengo usamakhudzane ndi

mtuvituvi, ungawonjezere kununkha.

-Osamaloza ena chala chifukwa cha zolakwa

zako. Anthu ena akalakwa amayamba kuloza

ena zala kuti ndiye alakwitsa kapena

achititsa kuti alakwe.

Ukaponya chakudya pamadzi,

udzachipeza.

-Ndi bwino kukhala woolowa manja chifukwa

tsiku lina anthu omwe ukuwathandizawo

angadzakugwire dzanja.

Ukasauka usadzimangilire.

-Munthu ukasauka usamadzichitire zoipa,

monga kudzikhweza kapena kumwa tameki,

chifukwa palibe chomwe ungapindulepo.

Miyambi ya Patsokwe

469

Ukasauka usamagwire nyanga.

-Ngati ndife osauka tizivomereza m’malo

moyamba kudalira nyanga, kuba kapena

kupha anthu.

Ukasauka usamaloze anzako chala.

-Ukasauka usamanamizire anzako kuti ndiye

akupangitsa.

Ukasawuka usamagwire nyanga.

-Si bwino kumachitira ena nsanje kapena

kumawafunira zoipa ukakhala kuti iweyo

ulibe kapena sungathe kuchita zinazake.

Nkhani yake imati, mkulu wina anakafunsira

ntchito kwa bwana wolemera kwambiri.

Kumene ankagwira ntchitoko anapezako

anzake amene anali atakhala kwa nthawi

yaitali ndi bwanayo. Anzakewo anali ndi

zinthu zambiri zimene anapata pa zaka

zimene anakhala akugwira ntchito. Chifukwa

chosirira kukhala ndi katundu ngati wa

Miyambi ya Patsokwe

470

anzakeyo ndiponso kukhala wolemera,

anaganiza zoti apeze mankhwala. Mumtima

anaganiza kuti mankhwalawo amuthandiza

kuti bwana wake azimukonda, kuti iye

akhupuke ndiponso kuti bwanayo achotse

ena mwa anzake ena amene sankagwirizana

nawo. Ngati zimenezi zikanatheka ndiye kuti

iye akanalandira udindo ndiponso

akanamuwonjera malipiro ake. Atapita kwa

sing’anga anapezadi mankhwala amene

ankafunawo. Sing’anga uja popereka

mankhwalawo anamuuzitsa kuti asakagone

kwa masiku atatu chifukwa ngati

angakagone ndiye kuti akatupa mimba.

Koma tulo ndi nkhondo timagoneka olira.

Tsiku loyamba analimbadi m’maso osagona.

Pamene kunkacha tsiku lachiwiri tulo tinali

titasonkhana, moti amati akati aimirire

sizimatheka. Atakhala pansi kuyambika kwa

matenda kunali komweko. Anzake amene

Miyambi ya Patsokwe

471

ankafuna kuwalodza aja atamufunsa

anafokotokoza kuti, “Pepani anzanga,

munthune ndimafuna kulemera. Ndiye

mankhwala amene ndinapeza, chizimba

chake china n’choti ndisagone masiku atatu,

koma ndalephera kuchikwaniritsa. Motero

thamangani mukamuuze sing’anga

wandipatsa mankhwalawa kuti atsukule

nyangayo n’cholinga choti ine ndikhale ndi

moyo.” Anzake aja atapita anakapeza kuti

sing’anga uja anali atamwalira cha dzana

lake moti anthu anali asanachoke pasiwa.

Anzake atabwerako anamufotokozera mmene

ayendera. Chifukwa chodziwa kuti kwake

kwatha anayamba kulira ndipo polirapo anali

kulira mochenjeza kuti, “Abale anga munthu

ukasauka si nzeru kugwira nyanga, taonani

zandichitikira inezi!” Pamenepo anzakewo

anavomerezadi kuti, “Ukasauka usamagwire

nyanga.” Nyanga zimene munthu uja

Miyambi ya Patsokwe

472

anakatenga ndi zimene zinam’phetsa.

Ukatambatamba uziyang’ana kum’mawa,

kunja kungakuchere.

-Tikamachita zoipa monga kuba, chiwerewere

tizizindikira kuti akadzangotigwira

tidzakumana ndi mavuto. Mwambiwu

umanena za kutamba chifukwa ena makolo

akalelo ankakhulupirira kuti afiti amatamba

usiku.

Ukatchula Mkango, kwera m’mwamba.

-Ukamanena za munthu wina ndiye kuti ali

pafupi. Mawuwa amanenedwa ndi ena ngati

njira yokupulumutsira kuti munthuyo

asakumve ukumunena. Anthu akamanena za

munthu wina, nthawi zambiri amakhala ali

pafupi.

Ukatukwana ng’ona, kumadzi usapiteko.

-Ngati tapalamula timasowa mtendere

mumtima podziwa kuti chilango

Miyambi ya Patsokwe

473

chikutidikira.

Ukayenda m’tchire (m’thengo) wayendera

zonse.

-Nthawi zina ukamayendera zina umathanso

kuchita mwayi wochitanso zina. Pamene

munthu akupita kwinakwake kukatenga

chinthu, kumeneko amatha kukapezanso

china chomwe sanachiganizire ndipo

ayeneranso kuchitenga.

Ukayenda m’fumbi usadane n’kutuwa.

-Sitingathe kulekanitsa zinthu zoyendera

limodzi monga fumbi ndi kutuwa.

Kumavomereza zinthu zina zikachitika.

Ukayenda ndi mwana wayenda wekha.

-Osamadalira kwambiri ana ukamachita

zinthu.

Miyambi ya Patsokwe

474

Ukayenda panjira usamagulule mano,

udzasowa chodyera nyama.

-Tisanayambe kuchita chinthu tiziona kaye

kuti tili ndi zonse zofunikira.

Ukayenda siya phazi, ukasiya mlomo

udzakutsata.

-Tikayenda tizisiya mbiri yabwino osati

kuchoka titasokoneza. Tisamanene mabodza.

Ukayendera nzengo usamati Asakhwi

afumbula.

-Ukapita kukadula mitengo usaiwalenso

chomwe wapitira n’kuyamba kuyang’ana

Asakhwi. Anthu amanena mwambiwu ngati

munthu amene watumidwa anayamba

kuchita zina zosiyana ndi zimene anamuuza.

Ukapita kwinakwake, usamayambe kuchita

zinthu zomwe sizinali cholinga chako.

Ukayipa nkhope, dziwa nyimbo.

-Ukazindikira kuti ndiwe wolephera pa

Miyambi ya Patsokwe

475

chinachake, phunzira kuchita chinthu china.

Ukaziputa limba.

-Osamayamba dala mavuto ngati ulibe

podalira.

Ukaziputa, limba nazo.

-Ukamapalamula kapena kuyamba mavuto

monga banja umayenera kukhala utakonzeka

kukumana ndi mavuto.

Uko kulire n’kumtsukwa.

-Mawuwa akutanthauza kuti kumene

kukulira ndi kosongoka kwa khasu. Pamene

pali nkhani yeniyeni ndi pamene

pamazunguza kwambiri.

Ukonde umayambira ku wakale.

-Poluka ukonde umangera ku wakale. Zinthu

zatsopano zimayambira ku zakale.

Ukonzi unapha msemang’oma.

-Chisoni nthawi zina chimapezetsa mavuto

Miyambi ya Patsokwe

476

kuchokera kwa anthu osayamika.

Uku kwawinda, tikudya mawa mande.

-Mawuwa amatanthauza kuti pali mapokoso

kapena chisokonezo ndiye anthu adya

bwinobwino mawa zimenezi zikatha.

Ukamachita phwando ndi bwino

kukonzekera chifukwa anthu amawerengera

kuti adzadya. Ena amachita kukhwefula

malamba awo kuti adzadye zambiri.

Ukufunsa za phula, njuchi ndi izi

ukuziona.

-Mawuwa amanena za munthu amene

akufunsa zinthu zoti akuzidziwa kale.

Ukukonda bwemba osakonda chulu!

-Usakonde bwemba koma chulu pamene

pamera bwembayo. Mawuwa amanena za

mwamuna yemwe amakonda mkazi wake

yekha koma osati apongozi ake.

Miyambi ya Patsokwe

477

Ukulu si msinkhu ayi.

-Kutalika kapena kubadwa kale si nzeru

koma kuchita kapena kuyankhula zakupsa.

Ukundisokosera n’kulinga utamva.

-Mfundo za mawu timazipeza tikamvetsera

kaye.

Ulemu n’kubadwa nawo.

-Tiyambiretu kuphunzitsa ana athu

makhalidwe abwino adakali aang’ono.

Ulemu n’kuthirana.

-Ukachitira wina ulemu nayenso amakupatsa

ulemu.

Ulemu ndi mpira, umabwerera.

-Mawuwa amayerekezera ulemu ndi mpira

womwe ukaulandira umafunika kupatsira

wina. Tizichitira ena ulemu, tikapanda

kuwapatsa ulemu nawonso satipatsira mpira.

Miyambi ya Patsokwe

478

Ulemu wa Buluzi m’nyumba ya mfumu.

-Anthu ena amalandira ulemu chifukwa cha

makolo komanso anthu amene akukhala

nawo, pomwe iwowo ndi onyozeka.

Ulemu wa Nkhukhu wopalasa pali anthu.

-Mwambiwu umanena za munthu wopanda

ulemu.

Ulendo n’kaphatikira, ukalinda wako

wachedwa.

-Mawuwa amatanthauza kuti ukamapita

kwinakwake umayenera kupita ndi anzako,

ukadikira ulendo wako umachedwa. Kuyenda

ndi anzako kumathandiza, ukakhala wekha

sungakwanitse kuchita zinthu zina.

Ulendo n’kudyera.

-Kuti munthu uyende ulendo makamaka

ngati ndi wapansi, umafunika kudyera.

Kudya kumatipatsa mphamvu zoti tigwire

ntchito.

Miyambi ya Patsokwe

479

Ulendo ndi uwu wachoka.

-Kuchita chinthu kumafuna kuchiyamba

osati kumangoyankhula.

Ulendo wa awa wakutha kamba.

-Kamba ndi chakudya cha paulendo.

Kuchedwetsa zinthu kumawonongetsa

zambiri kapena kubweretsa chipwirikiti. Ulesi

ndi mphwayi zimayambitsa umphawi.

Ulendo wa awa wakutha nkhokwe.

-Kuchedwetsa zinthu kumawonongetsa

zambiri kapena kubweretsa chipwirikiti. Ulesi

ndi mphwayi zimayambitsa umphawi.

Ulenje umasimba wako.

-Osamakonda kunena za ena, ukhoza

kupalamula. Nkhani yake imanena kuti,

kalekale panali munthu wina amene anapita

kuthengo kukapha nyama. Kumeneko

anapha nyama ziwiri. Pamene ankabwerera

kwawo n’kuti kunja kuli kachisisira ndipo

Miyambi ya Patsokwe

480

anamva phokoso likumveka m’mudzi

wakwawo. Atafika pamphambano,

mwadzidzidzi anangoona mkango watulukira.

Mlenjeyo anachita mantha kwambiri, koma

mkango uja unamuuza kuti, “Musachite

mantha achimwene. Panotu takumana

amuna okhaokha. Kaya inu mukuchokera

kuti ulendowu?” Poyankha munthu uja

anati: “Ine ndikuchokera m’malunjemu

ndimakasaka.” Ndiyeno mkango unati,

“Popeza tonse tikuchokera kosaka, aliyense

asaulule mnzake. Ulenje umasimba wako,

osati wamnzako.” Atangosiyana pamenepo,

mkango uja unalowa m’tchire ndipo

munthuyo anathamangira kwawo ali ndi

mantha. Kenako anayamba kuuza anthu kuti

wakumana ndi mkango utagwira nyama.

Mkango uja utamva zimenezi, unapita

kunyumba kwa amfumu n’kukagwira mwana

wawo n’kumupha. Kenako unakamuika

Miyambi ya Patsokwe

481

m’nyumba mwa mlenje uja. M’mudzimo

munayambika chipwirikiti chifukwa cha

kusowa kwa mwanayo ndipo mfumu

inalamula kuti anthu afufuze amene watenga

mwana wakeyo. Atafufuza anapeza mwanayo

atafa koma ali m’nyumba mwa mlenje uja

ndipo mfumu inalamula kuti nayenso

aphedwe.

Ulesi ndi matenda.

-Ukalekerera ulesi chimakhala chizolowezi

ndipo chimasanduka matenda.

Ulesi ulibe mtolo.

-Ulesi umabweretsa njala komanso mavuto

ena. Munthu waulesi sangakhale ndi kanthu

kolozeka.

Ulumbwana ulibe mainja awiri.

-Mawuwa amatanthauza kuti munthu

sangakhale mwana n’kupezeka kuti

wakhalapo mudzi wina n’kusamuka, kenako

Miyambi ya Patsokwe

482

n’kubwereranso kubwinja loyamba lija.

Mwambiwu umatanthauza kuti munthu

akamakula amafunika kusiya chibwana.

Munthu akakhala mwana nthawi zambiri

sachita zinthu mozindikira.

Umachokera pamodzi ndi mawu.

-Munthu akanena kanthu umayenera

kuchita zomwezo osati zina.

Umadikira kuti mafulufute atuluke.

-Si bwino kumachita phuma pochita zinthu

chifukwa zimenezo zingachititse kuti titaye

mwayi kapena titsekezereze zabwino.

Umaingitsa kachoka, walinga iwe nutola.

-Munthu amene wakumana ndi zambiri ndi

amene amayankhula zogwira mtima. Munthu

amene anali ndi khalidwe loipitsitsa ndi

amene amaphunzitsa bwino.

Miyambi ya Patsokwe

483

Umakongola ukusangalala, koma

umabweza ukulira.

-Ngongole imakoma ukamabwereka.

Tizisamala ndi nkhani yobwereka ndalama.

Umakumbukira mwana akapsa.

-Kawirikawiri sitichenjeza anzathu mpaka

atalowa m’mavuto.

Umalawa zogagada ndi nkhwangwa,

zocheka ndi mpeni suzilawa.

-Tisamalakelake kukhala ndi zinthu

zapamwamba kwambiri n’kumanyoza

zing’onozing’ono.

Umanena chatsitsa dzaye kuti Njovu

ithyoke mnyanga.

-Tizinena chayambitsa nkhani yeniyeni.

Anthu ena ankadabwa kuti n’chiyani

chathyola mnyanga wa Njovu. Atafufuza

bwinobwino anapeza kuti mumtengo wa

maye munali nyani. Nyaniyo ndi amene

Miyambi ya Patsokwe

484

anagwetsa dzaye kuti Njovu ithyoke

mnyanga.

Umanjata thumba tokoma tikuuluka.

-Ena amabisa zoipa, koma akamamanga

thumba lawo la zoipazo zina zimauluka

n’kudziwika kwa aliyense.

Umavomera ngati womva (wodwala) dzino.

-Mawuwa amatanthauza kuvomera

mokaikira, moti wina sangagwire chenicheni.

Munthu amafunika kunena motsimikiza osati

mokayikira.

Umayambira madzi akadali m’mapazi.

-Vuto likamayamba kumene limakhala

losavuta kuthana nalo monga matenda, njala

ndi zina.

Umayambirira madzi asanafike m’maondo.

-Vuto likamayamba kumene limakhala

losavuta kuthana nalo monga matenda, njala

Miyambi ya Patsokwe

485

ndi zina.

Umayambiza madzi ali m’maondo.

-Vuto likamayamba kumene limakhala

losavuta kuthana nalo monga matenda, njala

ndi zina.

Umazika mzimbi woyera kumene wachoka

ndi kumene upita.

-Kulikonse kumene wachoka ndi kumene

ukupita ndi bwino kusiya mbiri yabwino kuti

anthu adzakulandirenso mawa. Mzimbi

yoyera ndi nthenga yoyera, yomwe ikuimira

mbiri yabwino.

Umphawi n’kulumpha chiunda.

-Munthu ukachoka kwanu umasowa zambiri

zimene unkazipeza kwanu. Anthu amavutika

akakhala koyenda.

Unjiunji ajiwitsa.

-Kukondetsa zinthu kumabweretsa mavuto

Miyambi ya Patsokwe

486

makamaka zinthuzo zikakhala zoipa.

Unyinji ukoma, uipira kutha mchere.

-Kuchulukana n’kwabwino, kumangoipira

kuti zinthu sizichedwa kutha. Koma

pakakhala ntchito imayenda ndithu.

Usakhulupirire mazira a Koka.

-Mbalame ya Koka imafuna malo omwe

Khwangwala waikira kale mazira ake

n’kumuthamangitsa kuti aikirepo ake.

Choncho, munthu sangadziwe dzira lomwe

litulutse ana a Koka kapena a Khwangwala.

Mwambiwu umatanthauza kuti zam’tsongolo

sizidziwika.

Usakonde vembe, koma ukonde chulu.

-Ukakwatira umakhala wakwatira mudzi

wonse. Usamangokonda mkazi wako yekhayo

komanso makolo ake.

Miyambi ya Patsokwe

487

Usalimbitse goli pomanga bulu wako.

-Pofufuza zinazake timafunika anthu

kuwatenga pang’onopang’ono kuti asachite

mantha koma akhale omasuka.

Usamadikire kuti madzi afike m’nkhosi.

-Usamadikire kuti vuto liipe kwambiri ndiye

n’kumayamba kuchitapo kanthu.

Usamakokomeze chisanu ngati

chitolankhuni.

-Munthu akasauka asamangodandaula,

koma azigwira ntchito kuti umphawiwo

umuchoke.

Usamaloze chitsa usanachibzole.

-Osamachenjeza anzako kapena kuwauza

kuti asiye kuchita zoipa zinazake zomwe

iwenso umachita.

Usamanyoze thewera mkuzi uli nawo.

-Usamanyoze mkamwini wako pamene

Miyambi ya Patsokwe

488

mwana wako adakali nayebe.

Usamapake mnzako chipwidza.

-Mawuwa amanenedwa pouza munthu kuti

asamanamizire mnzake. Chipwidza ndi

ndowe kapena matudzi a chiweto.

Usamasule mtolo chifukwa muli liwiro la

tonse.

-Munthu usanapute mlandu ndi bwino

kumaganizira kuti zochita zakozo

zikhudzanso anthu onse a m’banja lako.

Usamaswere dzungu m’lichero.

-Kuswera dzungu m’lichero

kukungotanthauza kusaugwira mtima.

Ukamva nkhani yachilendo si bwino

kuyamba kufotokozera anthu chifukwa

ukhoza kupezeka ukufalitsa mabodza.

Miyambi ya Patsokwe

489

Usamatame ntchito zake mtima wake

usanaudziwe.

-Osamafulumira kuweruza munthu pa

ntchito zake usanamudziwe bwinobwino.

Usamathawe mkamwa, kumene

ukupitakonso ukalipeza.

-Padziko lapansili anthu ambiri ndi

am’kamwa moti palibe kumene ungalowere

osakapeza anthu otero.

Usamati ndathawa mlomo, kumene

ukupitako ukaupeza.

-Kuthawa mlomo ndi kuthawa kulongolola.

Mavuto ali ponseponse ndipo sitingawathawe.

Amene akufuna kuwathawa kuli bwino

angomwalira.

Usamati ndi chilonda, lidzakula.

-Mwana akalakwitsa ndi bwino kumulangiza

m’malo mongomulekerera. Kuti mwana akule

bwino tiyenera kuyamba kumulangiza ali

Miyambi ya Patsokwe

490

wamng’ono. Apo ayi chilonda chidzasanduka

bala lalikulu khalidwe lake litafika poipa.

Usanalavule mawu, yamba wawalawa kaye.

-Ndi bwino kumaonetsetsa kuti zimene

tikunena ndi zoona komanso zabwino, zomwe

sizingakhumudwitse ena.

Usanamwaze nthenga, kumayamba waona

kaye ngati ungazitolele.

-Kunena mabodza kuli ngati kumwaza

nthenga. Nthenga zimapita ndi mphepo.

Ndiye usananene bodza ndi bwino

kumaganiza kaye ngati kuti, “Kodi mwini

wake atandiuza kuti nditolele nthenga zomwe

ndamwazazo, ndikwanitsadi kudzitolera?”

Usanayambe kudzitama kutalika, ndi

bwino kumayamba waganizira kutalika

kwa zinthu zimene zakuzungulira.

-Mwambiwu umathanthauza kuti, kuti

munthu ukhale wodzichepetsa, umafunika

Miyambi ya Patsokwe

491

kumaganizira zimene anzako amachita

bwino. Ndipo ukachita zimenezi mpamene

umaona kuti anzakowonso ndi ofunika.

Usayimbe mbalule ukamachita bwino.

-Mbalule ndi ng’oma. Ukaona kuti

zikukuyendera si bwino kumadzionetsera.

Usiku ndi usiku ndithu, satungira mkanda.

-Zochitika za usiku ndi zoopsa. Usiku

kumakhala zilombo zoopsa choncho ndi

bwino kumachenjera poyenda usiku.

Mwambiwu ukutanthauza kuti sungaike

timikanda pa ulusi usiku, kuli mdima.

Choncho, chilichonse chili ndi nthawi yake

yomwe ungachichite.

Usiku ndi usiku, ndithu udathawitsa

Ligondo.

-Zochitika za usiku ndi zoopsa. Usiku

kumakhala zilombo zoopsa. Choncho ndi

bwino kumachenjera poyenda usiku.

Miyambi ya Patsokwe

492

Usinini sungakule suposa dzino.

-Dzino ndi lolimba kuposa usinini. Komanso

mano ndi amene amaonekera pamwamba pa

usininiwo. Si bwino kumadziona kuti ndife

apamwamwa kwambiri kuposa ena omwe

tawapeza kaya kuntchito kapena pamudzi.

Utsi sufuka popanda moto.

-Chilichonse chimakhala ndi chochititsa. Utsi

sungafuke pamene palibe moto.

Uyenda liti mwana wosayenda nsangawe,

utimalizira zam’nkhokwe.

-Kuchita zinthu mwachangu n’kofunika

kuopa kuti ntchito idzakupanikize nthawi

imodzi.

Uyo waona matumbuzi, nyama ndi yake.

-Chimene wapeza pogwira ntchito ndiye

chako. Si bwino kumachenjeretsa anthu ena.

Matumbuzi ndi mbalame zomwe zimakonda

kudya nyama zakufa, ndiye ngati waona

Miyambi ya Patsokwe

493

matumbuziwo, nyama imene akufuna

kudyayo ndi yako.

Uzikhoma chitseko chako kuti anthu

apafupi asakhale akuba.

-Zimene timachita zingachititse kuti anthu

ena akhale okhulupirika kapena ayi.

Mwachitsanzo, kumangosiya katundu wathu

paliponse kungachititse kuti anthu akopeke

n’kusanduka akuba.

Miyambi ya Patsokwe

494

V

Vuto la Phwiti, akakhuta salawira mtondo.

-Pali anthu ena ukawachitira zabwino

amangoti zii, osayamikira zimene

wawachitira. Amaoneka akakhala kuti

akufuna chinachake basi.

Miyambi ya Patsokwe

495

W

Waba nkhukhu ndamuona, sindimutchula

chifukwa choti ndili ndekha.

-Mawuwa amatanthauza kuti amene walakwa

ndikumudziwa, koma poti palibe amene

amagwirizana nane pamudzi pano,

sinditchula.

Wabisa mbuzi m’munda.

-Kumeneku ndi kusunga mavuto,

mwachitsanzo kusunga wakuba m’nyumba.

Wachaje ndi gaga wowawa, sasipika.

-Mawuwa amatanthauza kuti anthu adera

amakhala ngati gaga wowawa, yemwe nsima

yake sungadye yosipa. Anthu ena

amangofuna kuwathandiza basi koma

sangakuthandize zitakuvuta.

Miyambi ya Patsokwe

496

Wachake ndi wachake.

-Munthu amene ali ndi khalidwe loipa saleka.

Wachake sachileka.

-Munthu amene ali ndi khalidwe loipa saleka.

Wachedwa ndi makonkhwa.

-Makonkhwa ndi zinthu zopanda pake.

Mawuwa amanenedwa ngati munthu wina

wachedwa chifukwa cha zinthu zopanda

pake.

Wachenjera atalumwa.

-Munthu amachenjera atalumwa kapena kuti

atalumidwa ngati anthu ena, kaya alendo,

amuchitira chipongwe. Akazindikira

chipongwecho amati, “ndachenjera

nditalumwa,” zomwe zikutanthauza kuti

wachenjera zitaipa kale.

Wachenjeza ng’anga, chilonda chisanapole.

-Mawuwa amanena za sing’anga, kapena kuti

Miyambi ya Patsokwe

497

dokotala amene akukupatsa mankhwala oti

uchire bala lako, koma iweyo n’kumuchitira

chipongwe balalo lisanapole. Tisamanyoze

kapena kuchitira chipongwe anthu amene

akutithandiza.

Wachikumbakumba wasiya dzenje,

kumudzi usakati “ndiwo!”

-Mawuwa amanena za munthu yemwe wapita

kukafuna mbewa ndiye wakumba n’kutopa

n’kusiya una, ndiye kupita kunyumba

n’kumakadandaula kuti alibe ndiwo.

Mwambiwu umagwiritsidwa ntchito ngati

anthu akambirana zinazake ndiye akuuzana

kuti asakaulule zinthu zimene

amakambiranazo.

Wachita mwa mlatho.

-Kuchita chinthu chinachake kuti

upulumuke ngakhale kuti sumafuna

kuchichita.

Miyambi ya Patsokwe

498

Wachoka pa Chivuulandiwo wafika pa

Chimwamchere.

-Mawuwa amanena za munthu amene anali

woipa kale ndiye waipiratu.

Wada m’mimba, akanakhala maso

tikadatsukamo.

-Mwambi uwu umanenedwa zinthu zikavuta

kwambiri moti palibe chimene mungachite.

Wadabwa chule m’madzi muli mwake.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

wadabwa ndi zinazake chifukwa choti si

mmene zimayendera nthawi zonse.

Waduka lende, ana asewera pansi.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

wamwalira n’kusiya ana.

Wadula mchira.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wina

wapalamula kapena wachita chinachake

Miyambi ya Patsokwe

499

choipa. Mawu amenewa anachokera ku

zimene mchira wa buluzi umachita ukaduka.

Wadyera amakumba manda ake ndi mano.

-Dyera limaphetsa. Munthu akhoza kudwala

matenda osiyanasiyana chifukwa choti

amadya kwambiri.

Wadzoladzola matope, kumunda kulibe

ndime.

-Mawuwa amanena za munthu waulesi

amene amayerekezera kuti walima koma

asanalime, kungodzola matope kuti azioneka

ngati amalima.

Wafa atamva.

-Mawuwa amanenedwa zikakhala kuti

munthu wina wakumana ndi mavuto

chifukwa chosamva.

Wafa chona, khoswe akondwe.

-Mawuwa amanenedwa anthu

Miyambi ya Patsokwe

500

akamasangalala kuti munthu amene

amavuta pamudzi wachoka, kapena

wamwalira moti azikhalano mwamtendere.

Wafa mphaka makoswe asangalale.

-Mawuwa amanenedwa anthu

akamasangalala kuti munthu amene

amavuta pamudzi wachoka, kapena

wamwalira moti azikhalano mwamtendere.

Wafa ndi dama lake.

-Pa Chichewa mawu akuti dama

amatanthauza kunyada, angatanthauzenso

kuchita chiwerewere. Ndiye mawuwa

amatanthauza kuti munthu wafa chifukwa

cha kusamva kwake.

Wafulumira kumeza asanatafune, ndiye

cham’thimba pakhosi.

-Tisamafulumire kuchita zinthu. Kuchita

zinthu modekha n’kofunika.

Miyambi ya Patsokwe

501

Wafulumira kumeza kutafuna

kukadakoma.

-Tisamafulumire kuchita zinthu.

Wagenda katauluka.

-Kulephera kapena kunena mawu zinthu

zitapita.

Wakoka chingwe msampha uli pambuyo.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

wapalamula chifukwa chosamvetsetsa

kapena kusaonetsetsa bwino. Ngati munthu

wachita zimene mwambiwu umanena,

msamphawo umafwamphuka

n’kumuvwapula.

Wagwa m’mbuna yosavundikira.

-Mawuwa amatanthauza kuti munthuyo

walakwa dala. Mbuna ndi dzanje limene

anthu amatchera nyama n’kuima timaudzu

pamwamba kuti nyamayo isazindikire kuti

pali dzenje. Ndiye ngati munthu atagwa

Miyambi ya Patsokwe

502

m’mbuna yosavundikira, ndiye kuti amaona

kuti pali dzenje.

Wagwira pa Mbira, Nungu ali ndi ngololo.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wataya

chinachake kapena waluza ndalama moti zoti

aipezanso aiwale.

Waika phale watama mano.

-Munthu amene amakazinga chimanga ndiye

kuti ali ndi mano. Ndi bwino tizizindikira

zinthu zimene tingathe kuchita kapena ayi.

Waimba muluzi m’chimbudzi ndiye kuti

anakhuta.

-Munthu sungapite kuchimbudzi ulibe

cholinga. Munthu amene amati akakhala

pamavuto n’kumasangalala kapena

kumaimba muluzi ndiye kuti akudziwa zoti

mavuto akewo atha posachedwa kapena

akuimba mlandu munthu wina.

Miyambi ya Patsokwe

503

Waimba ng’oma yowambawamba.

-Mawuwa amanenedwa ngati wina wachita

zimene ena amayembekezera. Kapena ngati

wachita zinthu zimene enanso amafuna.

Anthuwo akamanena amati, “Waimba ng’oma

yowambawamba.”

Waimba yakale, ana aakazi abwerera.

-Mawuwa amanenedwa potanthauza kuti

munthuyo wachedwa. Mwachitsanzo,

munthu akhoza kumafuna kugula

chinachake n’kupita kwa wogulitsa

n’kukapeza zitatha. Wogulitsayo angamuuze

kuti, “waimba yakale, ana aakazi abwerera.”

Waisenzera pankhongo.

-Amenewa ndi mawu okokomeza onena kuti

nkhani sanaimvetse munthuyo.

Wakaduka alibe anansi.

-Munthu ukakhala wakaduka anthu

amakuthawa.

Miyambi ya Patsokwe

504

Wakalamba Wafuna.

-Masiku ano anthu ambiri akumachita

zinthu zomwe zingathandize kuti asaoneke

okalamba kwambiri, ndiye akamatchula

mwachining’a amangoti, “wakalamba

wafuna.”

Wakhala kuutsi dala.

-Munthu akamafuna kuchoka amachita

zinazake kuti achokepo. Mwambiwu

umaziyerekezera ndi kukhala dala kuutsi

kuti uziti wachoka chifukwa utsi

ukukupwetseketsa maso.

Wakhalira khute.

-Mawuwa amatanthauza kudikirira zinthu

zimene sitingazipeze.

Wakhate samunamiza nsapato.

-Tisamalonjeze zinthu zomwe sitingakwanitse

kuchita, monga kunamiza wakhate kuti

umugulira nsapato. Komanso si bwino

Miyambi ya Patsokwe

505

kulonjeza munthu mphatso yomwe sangathe

kuigwiritsa ntchito. Umenewu umakhala

mwano.

Wakhungu akakuuza kuti ndikugenda,

samala, waponda mwala!

-Munthu amene sumaganizira akakuuza

zinazake zachilendo, dziwa kuti palipo

pamene akudalira.

Wakhungu akati ndikugenda, ndiye kuti

waponda mwala.

-Munthu akamachita chinachake amakhala

ndi podalira.

Wakufa sadziwika.

-Mawuwa amanenedwa anthu

akamakangana n’kumanena kuti ndili ndi

mphamvu kwambiri ndine. Nkhani yake

imanena kuti, panali nkhanga ndi finye ndipo

tsiku lina zonse zikuyenda zinakumana.

Nkhanga inati: “Ndimakufuna iwe! Wafa lero!

Miyambi ya Patsokwe

506

Koma finye anangoti: “Wakufa sadziwika!”

Nkhanga inati, “Iwe ndi mwana wamwano

eti? Ine ndikuti wafa lero!” Mmeneno n’kuti

nkhanga itayamba kale kujompha finye, uku

finye akutulutsa utomoni woyera womwe

unali kukakamira pamlomo wa nkhangayo.

Nkhanga inayamba kulephera kupuma ndipo

inafa. Wogonja kapena wakufa sadziwika

mpaka zonse zitafika pamapeto pake.

Wakumba cha nje! mtengo wausiya.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

walephera kupeza zimene amafuna kapena

walephera kudziwa zoona zenizeni.

Wakutsina khutu ndi mnansi.

-Amene amakuchenjeza amakhala m’bale

wako komanso amasonyeza kuti

amakuganizira.

Miyambi ya Patsokwe

507

Wakwatira kwa mphezi, saopa kung’anima.

-Munthu amene akufunitsitsa chinthu

ayenera kukhala wolimba mtima. Chilichonse

chili ndi zovuta zake choncho si bwino

kungosiya kuchita zinthuzo chifukwa choti

ukukumana ndi mavuto. Ukamayamba

kuchita zinthu umayenera kuganizira mavuto

ake.

Wakwatira mende, waleka chitute.

-Mende samsunga chakudya anthu

akangokolola, pomwe chitute amasunga.

Ndiye munthu m’malo mokwara ndi mende

wosunga chakudya, wakwatira mlesi

weniweni chitute chifukwa cha kukongola.

Tikamachita zinthu tizionetsetsa kuti

tikusankha bwino. Si bwino kutengeka ndi

zinthu chifukwa cha maonekedwe. Ukhoza

kupezeka kuti wataya mwayi wopezapeza.

Miyambi ya Patsokwe

508

Walira mvula walira matope.

-Chilichonse chili ndi zovuta zake, choncho si

bwino kungosiya kuchita zinthuzo chifukwa

choti ukukumana ndi mavuto. Tiyenera

kumavomereza zotsatira za zomwe tasankha

monga kulowa m’banja.

Wamenya chikambakamba mtima uli

pansi.

-Mawuwa amatanthauza kuti munthu

walephera kuchita zimene umafunadi

kuchita.

Wamisala anaona nkhondo.

-Si bwino kunyoza munthu chifukwa santha

kuchita zinthu zina chifukwa ali ndi mbali

ina yomwe amachita bwino. Osamanyoza

zonena za ena ngakhale kuti ndi ana kapena

osaphunzira. Chifukwa nthawi zina zimene

anganene zimakhala zothandiza kwambiri.

Miyambi ya Patsokwe

509

Wam’kachisi amadya zam’kachisi.

-Munthu amapeza zimene akufunikira

pamene amagwira ntchito.

Wamkulu salakwa.

-Munthu wamkulu ngakhale alakwitse

sauzidwira pagulu pomwepo kuti walakwa,

koma kumukokera pambali.

Wampota bwanji khobwe ndili ku ula?

-Mkazi anapota khobwe kapena kuti

kumupanga chipere, pomwe mwamuna wake

ankakonda wochita kubwira. Zimenezi

zinakhumudwitsa mwamunayo moti

anakwiya. Chilichonse chimakhala ndi

dongosolo lake, choncho ndi bwino

kumafunsa tisanachite zinthu.

Wamtengatenga sagona.

-Munthu akafuna kuchita chinthu

amafunika kuchita khama m’malo mochita

ulesi. Ngati anthu amene amanyamula zinthu

Miyambi ya Patsokwe

510

samatopa kapena kugona.

Wamuonetsa chidameta mduliro nyani.

-Mawuwa amatanthauza kukhaulitsa

munthu wina.

Wamuonetsa chidameta nkhanga mpala

-Mawuwa amatanthauza kukhaulitsa

munthu wina.

Wamusiya ali njo! pabwalo.

-Mawuwa amanenedwa anthu akamaseka

munthu yemwe pabwalo lamilandu amasowa

chonena. Amayamba kumukuwiza

n’kumauza amene akuoneka kuti

tikuwayenderawo mawu amenewa.

Wamva m’mimba ndi amene amatsegula

chitseko.

-Munthu amene ali pamavuto ndi amene

amachitapo kanthu kuti mavutowo

amuchoke.

Miyambi ya Patsokwe

511

Wandalama sayimba nthungululu.

-Si bwino kumanyada ukakhala pabwino.

Wandibisira mpeni kumphasa.

-Mawuwa amanenedwa ngati munthu

akudandaula kuti wina wawachitira

chiwembu.

Wandigwiritsa fuwa lamoto.

-Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene

wapusitsidwa ndi winawake.

Wandiviika m’mbuna.

-Mawuwa amatanthauza kusungira munthu

chakukhosi kuti udzamubwezere nayenso

akadzalakwa.

Wanga ndi wamalonda.

-Munthu woumira safuna kungopereka

zinthu mwaulere.

Wangoopa njokaluzi.

-Kumeneku ndi kuopa chinthu chosayenera

Miyambi ya Patsokwe

512

kuopedwa.

Wani tambala ilibe chenje.

-Pabanja pamafunika kukhala mwamuna

mmodzi ndi mkazi mmodzi basi.

Wanjala safuna ndiwo.

-Munthu amene wayamba kuona kuti ndiwo

zake sizikukoma amakhala kuti wakhuta.

Wanjala saona zonsezo amangoti bola

akhute.

Wanjala salima, amalima ngwokhuta.

-Kuti munthu agwire ntchito amafunika

kudyera kaye.

Wanjiru sagonera, mvula yake ndi imodzi.

-Anthu oipa sakhalitsa.

Wanyanga aferanji?

-Mwambiwu umatanthauza kuti n’chifukwa

chiyani munthu wodalira mankhwala amafa?

Aliyense adzafabe afune asafune.

Miyambi ya Patsokwe

513

Waona kamwana tola, ukulu n’kuona kako.

-Munthu akayenda ndi mwana amayenera

kukhala wokonzekera. Si bwino

kumangodalira mwanayo pa chilichonse.

Waona mawanga a Nkhanga wataya

Nkhwali.

-Ukamamvera za anthu umatha kutaya

mwayi womwe uli nawo kale. Ukakhala ndi

chinthu si bwino kuchinyoza chifukwa waona

china chokongola kwambiri kuopera kuti

ungataye chabwino n’kulephera kupeza

chinacho.

Wapala moto kudambwe eni ake alipo.

-Mawuwa amatanthauza kuti wapalamula.

Kapena kuyankhula miseche za wina, mwini

wake akumva.

Waponya katapita.

-Kulephera kapena kunena mawu zinthu

zitapita.

Miyambi ya Patsokwe

514

Wapsa phwetekere kumunda kwa make

Chenjerani.

-Mawuwa amanenedwa pantchito kapena

malo ena pochenjezana kuti bwana kapena

woyang’anira akubwera. Mawuwa

amanenedwanso podziwitsa anthu kuti

kuyamba gule wamkulu.

Wasekerera fupa wayesa mnofu.

-Munthu asamangokhutira ndi zimene

akudziwa kapena zimene waphunzira.

Akhoza kudabwa atazindikira zinthu zinanso

zofunika kwambiri.

Wasosolera pamsampha.

-Kumeneku ndi kuchenjeretsa munthu.

Angatanthauzenso kuchita choipa ena ake

akuona.

Watcha ndikupenya, msampha wakewo

uwola.

-Pamene munthu wina ankatchera

Miyambi ya Patsokwe

515

msampha, nkhanga inaona ndipo

inachenjera. Mwambiwu umatanthauza kuti

munthu akhoza kumva zinazake

n’kuchenjera kuti asagwere m’mavuto.

Watchera kumwezi, Nkhanga zaona.

-Munthu wina ankatchera msampha mwezi

ukuwala ndiye nkhanga zinaona

n’kuchenjera. Mwambiwu umatanthauza kuti

munthu akhoza kumva zinazake

n’kuchenjera kuti asagwere m’mavuto.

Ukafuna kumugwira munthu si bwino

kuulula njira zako.

Watchera kumwezi.

-Munthu akamachita zachinyengo, nthawi

imafika yomwe anzake amamutulukira.

Watenga kafukanyeka.

-Kafukanyeka ndi matenda opatsirana.

Mawuna amanenedwa ponena za munthu

amene watenga matenda osachiritsika

Miyambi ya Patsokwe

516

chifukwa cha chiwerewere.

Watenga kamwana, wasiya amawo.

-Mawuwa amanedwa ngati munthu wina

wapusitsa mnzake. Munthu wopusitsidwayo

amanena kuti akuona ngati wachenjera

atatenga kamwana n’kusiya manthu.

Akadzabweranso adzaona.

Watenga ya kunkhuni kumchere amwera

madzi.

-Mawuwa amanena za munthu amene

akufulumira kuchita zinthu ngati mmene

amachitira munthu amene ali ndi ludzu

loopsa chifukwa choti akuchokera kotola

nkhuni. Munthu wotere amatha kumwa

madzi amchere chifukwa chopupuluma kuti

aphe ludzu lake.

Watha m’kamwa muuzimba zikalimo.

-Mwambiwu umanenedwa pamene mlandu

wagamulidwa koma anthu sakukhutira ndi

Miyambi ya Patsokwe

517

chigamulo. Nkhaniyo imakhala sinathe

atakumana ku uzimba wina akhoza kubaya

mnzake ali naye chifukwayo.

Wathundukwa, wadya yapaphewa.

-Mawuwa amanedwa poloza wina chala kuti

ndi mfiti ndipo wadziwika.

Watukwana nankungwi mawere atamera.

-Mawuwa amanena za munthu amene

wachitira mwano akuluakulu kuiwala zoti

awafuna. Mwachitsanzo, wachinyamata

kunyoza nankungwi wake atayamba kumera

mabere. Tiyenera kumalemekeza akuluakulu

chifukwa ndi amene angatithandize.

Watuluka m’mphuno n’kulowa m’kamwa.

-Mawuwa amanena za munthu amene

sanakwatire kutali, mwina wakwatira pafupi

ndi mudzi wake, kapena wakwatira msuweni

wake.

Miyambi ya Patsokwe

518

Wavina kumadzi.

-Mawuwa amanena mokokomeza za munthu

amene amatamba usiku. Kumadzi ndi

kumtsinje. Malinga ndi zikhalidwe za ku

Africa kuno, ena amakhulupirira za ufiti

ngakhale palibe umboni wokwanira woti

ulipodi.

Wawona Nkhanga maanga wataya Nkhwali.

-Si bwino kutengeka ndi zinthu chifukwa cha

maonekedwe. Ukhoza kupezeka kuti wataya

mwayi wopezapeza.

Wayanja mbatata, wataya mpeni.

-Mawuwa amatanthauza kusiya zinthu

zenizeni n’kumalimbana ndi zinthu

zosafunika.

Wayenda wapenga, wagona wafa.

-Ngati munthu wapita kuchilendo ayenera

kumakumbukira kuti tsiku lina adzabwerera

kwawo.

Miyambi ya Patsokwe

519

Wochenjera ndi munthu amene amati

akaona tsoka amabisala, koma chitsiru

chimangopitabe n’kukumana ndi mavuto.

-Mwambiwu ndi wochokera m’Baibulo koma

anthu ambiri amaugwiritsa ntchito

pochenjeza anthu ena omwe amachitabe

zinthu zomwe akudziwa kuti zikhoza kuwaika

m’mavuto.

Wodya nyemba amaiwala, koma wotaya

makoko saiwala.

-Zimene anthu ena amachita amaziiwala,

koma amene wachitiridwayo zimavuta kuti

aziiwale.

Wodya za kuchinamwali akudza ndi

tambala.

-Mawuwa amatanthauza kuti munthu amene

amakadya kuchinamwali ndi amene

amatenga tambala akamapita

kuchinamwaliko. Kukhala bwino ndi anthu

Miyambi ya Patsokwe

520

n’kothandiza.

Wodyera kuyenda adatha mtunda ndi

kukhuta.

-Munthu amene amangoyendayenda mwa

anzake n’kumapemphetsa samafa ndi njala.

Wofulumira kunena adathawitsa Likongwe

la apongozi.

-Nkhaniyi imanena za mkamwini wina yemwe

anafulumira kunena kuti amene atathawitse

Likongwe wa apongozi asamuka pamudzi.

Ndiye zinachitika kuti likongwe atabulika

anathawira mbali yake ndipo iyeyo

anambwita. Basitu, anasamuka pamudzi

chifukwa chopupuluma kuyankhula.

Tisamatsogoze mawu zinthu zisanachitike.

Wofunsa ndiye afunsa kutali.

-Kufunsa zinthu zisanasokonekere

n’kothandiza kusiyana ndi kumafunsa

zitavuta kale.

Miyambi ya Patsokwe

521

Wofunsa simung’ambira nguwo.

-Kufunsa si kulakwa, choncho wina

akatifunsa tisamamupsere mtima,

kumung’ambira nsalu yake. Koma

tizimuthandiza ndi vuto ali nalolo.

Woipa athawa yekha.

-Munthu amene wapalamula amathawa

popanda womuthamangitsa. Mwachitsanzo,

akangoona apolisi amaona ngati akufuna

iyeyo.

Wojeda salipira, alipira ndi woseka.

-Kuseka zinthu zopanda pake sikuthandiza.

Tisamauze ena nkhani zimene tangomva

chifukwa zina zimakhala zabodza.

Tingapalamule nazo.

Wokaona nyanja adakawona ndi mvuwu

zomwe.

-Nthawi zina ukamayendera zina umathanso

kuchita mwayi wochitanso zina.

Miyambi ya Patsokwe

522

Wokaona nyanja anakaona ndi mvuu

zomwe.

-Ukayendera zina umatha kukakumananso

ndi zina zomwe sumayembekezera.

Wokoma atani wonga fungwe.

-Mawuwa amanenedwa munthu

akamadandaulira anthu osayamika ngakhale

utawachitira zabwino.

Wokoma sagonera.

-Anthu abwino sakhala moyo nthawi yaitali.

Wokumba ndi amene amayenda ndi

mchopolo.

-Mchopolo ndi ndodo yokumbira. Munthu

sangakumbe popanda chokumbira. Tiyenera

kukonzekera bwino tisanayambe kuchita

chilichonse.

Wokwatira azidya mapira.

-Pabanja pamakhala mavuto ambiri omwe

Miyambi ya Patsokwe

523

amafunika kupirira. Ndiye mapira ndi mbewu

imene imapirira chilala. Choncho, kudya

mapira kukutanthauza kuti munthu amene

ali pabanja ayenera kukhala wopirira.

Wolanga mwambo sachita.

-Anthu ena amangodziwa kuuza anzawo

zochita koma iwowo osachita. Kuti malangizo

akhale ogwira mtima umafunika uyambe

kaye iweyo kuwatsatira.

Wolemera ndi amene amakhutira ndi

zomwe ali nazo.

-Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka

bwanji, koma osamakhutira, munthu

woteroyo sangakhale wolemera. Kulemera

kwenikweni n’kukhutira ndi zimene uli nazo.

Wolira samugwira pakamwa.

-Munthu amene akulira mumafunika

kumusiya kuti ayankhule zakukhosi kwake.

Miyambi ya Patsokwe

524

Wolirira kwawo adapita ndi madzi.

-Mawuwa amachenjeza munthu amene

akuchita makani anzake akamamulangiza.

Anthu ngati amenewa amakhala ngati

akudziwa zonse ndipo pamapeto pake

amakumana ndi mavuto oopsa.

Wolondera chitsime safa ndi ludzu.

-Munthu amadyera ntchito imene amagwira

monga wodikirira chitsime sangasowe madzi.

Woluka nsengwa (malichero) adyera

m’chipapa.

-Nthawi zina munthu wogwira ntchito zaluso

sakonda kutengako chimodzi chifukwa

choganiza kuti akatero akuwononga. Iye

amagwiritsa ntchito zipangizo zakutha

kapena zosweka.

Wongolozera kumtondo, kumunda kulibe

ndime.

-Mawuwa amanena kuti tisamakhale aulesi,

Miyambi ya Patsokwe

525

anthu omangokonda kudya osati kulima.

Wonukha samadzimva, amamumva ndi

anzake.

-N’zovuta munthu kudziwa kulakwa kwako

kapena makhalidwe ako oipa koma anzako.

Ndi bwino kumafunsako ena kuti atiuze

mavuto athu.

Wopempha salira tololo.

-Tizikhutitsidwa ndi zomwe tili nazo kapena

tapatsidwa. Mwachitsanzo, munthu

wopemphetsa samafuna kuti amupatse

zodzadza thumba.

Wopemphetsa sakulitsa chitete.

-Wopemphetsa amafunika kumakhutira ndi

zimene wapatsidwa.

Wophikira ena amafa ndi njala.

-Tiziyamba kuona zosowa zathu kaye

tisanayambe kuthandiza ena.

Miyambi ya Patsokwe

526

Wopunduka n’Chauta, mpembedzeni.

-Tiyenera kulemekeza anthu ngakhale

atakhala wolumala chifukwa nawonso ndi

ana a Mulungu.

Wopupuluma anadzikodzera chifukwa cha

mvula yongodutsa.

-Mawuwa anabwera chifukwa cha munthu

wina yemwe ankafuna kutaya madzi. Ndiye

poona kuti mvula ikubwera ndipo anyowabe,

anangodzikodzera koma mvulayo

inangolambalala umo, osamunyowetsa moti

anachita manyazi kwambiri.

Tisamapupulume pochita zinthu.

Wopusa amamanga nyumba, wochenjera

nagula.

-Ndi bwino kumaganiza kaye tisanachite

chinthu kuopa kuchita zinthu zopanda

mnzeru.

Miyambi ya Patsokwe

527

Wopusa anaomba ng’oma, wochenjera

navina.

-Nthawi zina anthu amene amaoneka opusa

ndi amene angatithandize. Tiziona ena

kukhala otiposa pa chinachake.

Wosamva adamva nkhwangwa ili m’mutu.

-Munthu wosamvera malangizo

amadzawamvera atakumana kale ndi

mavuto. Kumamva nkhwangwa itafika kale

m’mutu komwe ndi kumva mochedwa.

Wosamva za anzake n’chitsiru.

-Munthu amene samva za anzake amakhala

chitsiru, wopulukira komanso wosadziwa

kanthu chifukwa saphunzira chilichonse

kuchokera kwa ena.

Wosamvera za anzake adalira

ching’ang’adza.

-Munthu amene ndi wosamvera ena,

amadzilirira yekha akakumana ndi mavuto.

Miyambi ya Patsokwe

528

Wosauka ndiye wolemera.

-Wosauka ndiye amapeza tulo komanso

kusangalala ndi zomwe wapeza pomwe

wolemera sapeza tulo.

Wosoka mphasa amagonera pazidutswa.

-Nthawi zina munthu wogwira ntchito zaluso

sakonda kutengako chimodzi chifukwa

choganiza kuti akatero akuwononga. Iye

amagwiritsa ntchito zipangizo zakutha

kapena zosweka. Mwachitsanzo, woluka

mphasa akhoza kumagona pansi, akasoka

mphasa kumangogulitsa.

Wosoka mphasa amagona pamachika.

-Nthawi zambiri anthu amene amasoka

mphasa ndi amene amagonera mphasa

zakutha. Ndi bwino kumasungako zinthu

zina kuti tigwiritse ntchito.

Wosuma chakudya alibe mawu.

-Ngakhale tikusowa zinthu zina, tiyesetse

Miyambi ya Patsokwe

529

kumakhutitsidwa ndi zomwe tili nazo.

Wotchera ulimbo satsokomora.

-Pa mlandu timafunika kuyankhula

mosamala kuti tisaulule zina.

Wotengera Nguluwe kuutsa n’chayamba

kale.

-Anthu amene amavumbulutsa nguluwe

kutchire n’kuigwira amafunika kukhala oti

anayamba kale. Ukapeza ena akuchita zinthu

zachilendo si bwino kungoyamba kuchita

nawo, mwina iwowo amadziwa machitidwe

ake.

Wothabe upse mbala.

-Ukamayenda ndi anthu oipa, usamadabwe

ukagwera m’mavuto.

Wotsirira anzake amatsiriridwa.

-Ukachitira anzako zabwino nawonso

amakuchitira zabwino.

Miyambi ya Patsokwe

530

Wotuwa mpake mafuta.

-Tiyenera kuthandiza ena omwe akuvutika.

Wotuwa m’pemphe mafuta.

-Osauka nthawi zina amatha kukhala ndi

zinthu zimene olemera alibe, monga

masingano.

Wotuwa ndiye amafuna mafuta.

-Ndi munthu amene ali pamavuto amene

amayesetsa kuti apeze zimene akufuna.

Woumba mbiya alibe mkhate.

-Si bwino kumaumira kugwiritsa ntchito

zomwe tili nazo.

Woumba mbiya amaphikira m’phale.

-Nthawi zina munthu wogwira ntchito zaluso

sakonda kutengako chimodzi chifukwa

choganiza kuti akatero akuwononga. Iye

amagwiritsa ntchito zipangizo zakutha

kapena zosweka.

Miyambi ya Patsokwe

531

Woumba mbiya saphikira m’phale.

-Si bwino kumaumira kugwiritsa ntchito

zomwe tili nazo.

Woumiriza ndiye amapha nyama.

-Nthawi zina chinthu choumirizidwa ndi

chimene chimatheka komanso kuchitidwa

bwino kwambiri.

Wovala nyanda salumpha moto.

-Nyanda ndi kampango komwe azimayi

amavala m’chiuno. Nyanda sichedwa

kugwirira moto. Si bwino kumachita zinthu

zimene zingatiike m’mavuto monga kuchita

chiwerewere ndi zina.

Wovinidwa sapisa dzanja m’mphika wa

ndiwo.

-Tiyenera kusiya kuchita zachibwana

tikakula.

Miyambi ya Patsokwe

532

Woyenda ndi lupanga amafa ndi lupanga

lomwelo.

-Chinthu chimene umakonda n’chimene

chimakupha.

Woyenga mafuta satuwa.

-Munthu amapeza zimene akufunikira

pamene amagwira ntchito.

Woyerekedwa anagwa m’mpheto mwa

apongozi.

-Munthu ukamachita zinthu moyerekedwa,

nthawi zina umadzachita zinthu zosayenera

monga kugwera apongozi povina.

Miyambi ya Patsokwe

533

Y

Yagwa m’mbale ndi ndiwo.

-Tisamasankhe ndiwo tikamadya.

Yakondwa nkhwichi, Kalulu wakwiya.

-Anthu ena sakondwa mnzawo akatukuka.

Yangeyange adaphetsa kangaude.

-Tiyenera kumachita zinthu mwadongosolo

komanso mogwirizana kuti tisapeze mavuto.

Yaphwa nyanja ana atole nkhombe.

-Mauwa amanena za mavuto amene ana

amakumana nawo chifukwa choti makolo

awo amwalira.

Yaponda thope yamwa.

-Pakakhala chizindikiro chinachake ndiye

kuti chinthucho chachitikadi.

Miyambi ya Patsokwe

534

Yemwe umam’konda usamubwereke

ndalama.

-Munthu amene umamukonda akhoza

kukukhumudwitsa ngati utamubwereka

ndalama iyeyo osabweza. Posonyeza

kumukonda, popeza ambiri sabweza

ngongole, ndi bwino usamubwereke.

Yotema ndi nkhwangwa udzadya, ya mpeni

sudzadya.

-Munthu akatema nyama ndi nkhwangwa

anthu ena amamva ndipo amabwera kuti

adzadye nawo. Koma yodula ndi mpeni palibe

amadziwa. Tisamachite zinthu

modzionetsera.

Miyambi ya Patsokwe

535

Z

Za eni n’za eni, madzi amoto satentha

nyumba.

-Sitiyenera kumajijirikira zinthu za eni

chifukwa tikhoza kungopusapo.

Za kumzinda saulura.

-Ndi bwino kuti tizisunga chinsinsi cha

zimene tamva kapena kuona.

Zabwino zili m’tsogolo.

-Ngati munthu utayesetsa kuchita khama,

ukhoza kukhala ndi tsogolo labwino.

Zachoka ndundu tiyanike inswa.

-Mwambiwu ndi wofanana ndi wakuti,

“Achoke malizagudu, tiyanike inswa ziume.”

Umanenedwa posangalala kuti anthu amene

sumafuna kuti akhalepo ukamachita

zinazake achoka.

Miyambi ya Patsokwe

536

Zachoka ndundu tiyanikeko inswa.

-Anthu ena omwe safuna kuti anzawo

amveko zachinsinsi zawo amayesetsa kuti

akambirane zachinsinsizo ena aja

akachokapo kapena amapita pamalo oduka

mphepo.

Zadzera usetekera, mkombaphala anaduka

chala.

-Chala chamkombaphala chikhoza kuduka

chifukwa chochigwiritsa ntchito udyo.

Tizichita zinthu moyenera.

Zafera m’mazira.

-Zalephereka, sizinapite patali.

Zakuba sizilemeretsa.

-Munthu amene ali ndi zinthu zakuba

sazisamalira ngati mmene zikanakhalira

akanagwira ntchito.

Miyambi ya Patsokwe

537

Zakumva zimaondetsa.

-Osamangomvera zilizonse chifukwa zina

zimakhala zabodza ndipo zimangokupatsa

nkhawa.

Zakumva zimapweteketsa mutu.

-Osamangomvera zilizonse chifukwa zina

zimakhala zabodza ndipo zimangokupatsa

nkhawa.

Zakusimba saulula.

-Tizisunga chinsinsi, osamangoulula

chilichonse chimene tamva ngati kuti kamwa

lathu lili ndi chiboo.

Zala sizifanana, nawoso anthu amasiyina.

-Tiyenera kumachitira aliyense mofanana.

Ngakhale kuti zala ndi zotalika

mosiyanasiyana, zonse zimafuna

kusamaliridwa mofanana.

Miyambi ya Patsokwe

538

Zam’dengu zimapindula ukachita khama.

-Malonda amafunika khama komanso

kulimba mtima.

Zamwini sakulira mwendo.

-Si bwino kumachita matama chifukwa cha

zinthu za eni kapena kumanyoza ena

chifukwa cha chuma cha abale athu.

Zamwini savalira thewera.

-Tisamalowerere nkhani za anthu ena.

Zanga zili kuphiri, zifulumira kutsika.

-Tisamakongole tilibe podalira.

Zangazanga zidathyola bwampini msana.

-Munthu amene amangosonkhanitsa zinthu

zomwe sangazigwiritse ntchito ndi wopusa

chifukwa amangovutika.

Zaona atondo n’zolaula.

-Atondo ndi mbewa. Mbewazi zinakumana

ndi mavuto aakulu zitakodwa mumsampha.

Miyambi ya Patsokwe

539

Aliyense akhoza kukumana ndi mavuto.

Zathu, salowa m’khola.

-Munthu m’modzi sakhala ndi mphamvu pa

zinthu zagulu.

Zawombera mpeni.

-Zomwe ndimafuna zalephereka, ndalephera.

Zembeni kumowa, kumlandu andiitana.

-Anthu ena amaitana anzawo zikavuta,

zikamayenda amawataya.

Zengerezu adalinda kwawukwawu.

-Kuzengereza kumagwetsera munthu

m’mavuto. Kungatilepheretsenso kuchita

zinthu zofunika kwambiri.

Zidze pano n’za tonse.

-Pamudzi pakagwa mavuto timayenera

kuthandizana.

Miyambi ya Patsokwe

540

Zigwinjiri maliralira, zinalira mumsongolo

wa mbala.

-Munthu wina ataba zingwinjiri anagwidwa

zitalira m’thumba. Choipa sichingabisike

chimaululika.

Zika ukaona, Kamba anga mwala.

-Kamba ngati sakusuntha amaoneka ngati

mwala. Nkhani zina zimakhala

zosamvetsetseka. Wina akhoza kudwala

mwakayakaya, koma wina wolimba

n’kumwalira kusiya wodwalayo.

Zikachuluka sizidyeka.

-Ndi bwino kumachita chinthu chimodzi pa

nthawi imodzi.

Zikagwera pamphuno sizidyeka.

-Mawuwa amanena za munthu amene

akulephera kugamula mlandu chifukwa choti

ndi wa m’bale wake.

Miyambi ya Patsokwe

541

Zikatalika zala ngati nkhonje wakhobwe.

-Mawuwa amanena za munthu wakuba.

Zikungokhala pachilowelo.

-Mwambiwu umanena za anthu amene

akubwera kumadzapempha chifukwa choti

amva zoti anzawo anapatsidwa.

Mwachitsanzo, mwana akakhala m’chilowero

anthu amabwera kudzamuona kuti

adzamupatse mphatso.

Ziliko n’kulinga utatosako.

-Si bwino kutsimikizira chinthu usadapeze

umboni wokwanira. Umboni weniweni

umafunika kuchoka pa zimene waziona.

Zina kambu zina leku.

-Umafunika kusankha zoyenera kuyankhula

kapena ayi.

Zinapangana zinaulukira pamodzi.

-Tiyenera kumachita zinthu mogwirizana.

Miyambi ya Patsokwe

542

Zingale akaipa, aipa ndi nthenga zomwe.

-Munthu woipa mtima amaipa ndi mawu

komanso zochita zomwe. Zochita zakezo

zimakhudzanso abale ake.

Zingalume phula nditenga.

-Mawuwa amanenedwa kuti ngakhale

akumane ndi mavuto otani, sasiya mpaka

atapeza chimene akufuna.

Zingwinjiri sizipanganika, zimalira

m’thumba la mbala.

-Munthu wina ataba zingwinjiri anagwidwa

zitalira m’thumba. Choipa sichingabisike

chimaululika.

Zingwinjiri zimalira zikakhala ziwiri.

-Kuti zinthu ziyende timafunika

kuthandizana.

Zingwinjiri zimalira ziwiri, osati chimodzi.

-Anthu akakhala awiri amathandizana pa

Miyambi ya Patsokwe

543

zambiri. Munthu akakhala wodzikonda

zikamuvuta amasowa womuthandiza.

Zinthu zimayenda ndi zinzake.

-Anthu opeza mofanana amagwirizana.

Zipupa zili ndi makutu.

-Tizionetsetsa tisananena zachinsinsi

chifukwa makutu ali ponseponse.

Zizikanika zitayang’anana.

-Ndi bwino kumayesetsa kuchita khama

pochita zinthu. Zichite kukanika zokha.

Zizingokomera mbuzi kugunda galu, galu

akati alumeko akuti waboola nguwo.

-Munthu wokondedwa kapena wotchuka

akachitira ena zoipa, si kawirikawiri

kumudzudzula. Koma munthu wooneka

ngati wopanda ntchito akachitira anthu ngati

amenewa zoipa amalandira chilango

chokhwima.

Miyambi ya Patsokwe

544

Zokoma zili m’tsogolo.

-Munthu ukachita khama umadzakhala

pabwino.

Zolowere n’kudyere mwana.

-Mawuwa amanenedwa pochenjeza munthu

kuti akufuna akuchitire zoipa

pokunyengerera.

Zonse ndi moyo.

-Kuti munthu achite chilichonse amafunika

kukhala ndi moyo. Munthu ngati ali moyo

akhoza kuchita chilichonse chimene

akufuna.

Zonse ndi nthawi.

-Chilichonse chimachitika pa nthawi yake.

Zumba likoma ndi nsinjiro.

-Nkhani yongomva imapita iwonjerezeredwa

mpaka imasokoneza zinthu. Zumba ndi

masamba owawa. Amakonda ndi nsinjiro.

Miyambi ya Patsokwe

545

Ya m’mitengero

“Akuchita dala” adapita ndi madzi.

-Tisamalekerere anthu akuchita zoipa

kapenanso akusochera pongoganiza kuti

adziwa chochita popeza ndi aakulu msinkhu

kapena ophunzira kwambiri. Mpofunika

kuwachenjeza ndi kuwathandiza kuti

asagwere m’mavuto.

“Andilekere” adapha make.

-Kuti zinthu zitiyendere bwino, tizipempha

mnzeru kwa ena, apo ayi tikhoza kuchita

zinthu zomwe tinganong’oneze nazo bondo.

“Bongololo ndi ndiwo” uli ndi anzako

amene umadya nawo.

-Umboni umafunika ngati ukuchita zinthu

kuti udziwe ngati ukulondoladi.

Miyambi ya Patsokwe

546

“Chitachita” sachichitika.

-Kuumiriza kapena kuzunza anthu pogwira

ntchito sikuthandiza, chifukwa mapeto ake

ntchitoyo ndi imene imawonongeka.

“Chitani” adagulira nkhwangwa matowo.

-Pafunika kuganizira mofatsa tisanagule

chinthu chifukwa mwina tikhoza

kungowononga ndalama pachinthu chopanda

ntchito kwenikweni.

“Chitani” adakafera kunyanja.

-Munthu wolamula asodzi anafera kunyanja

chifukwa chosadziwa kupalasa bwato. Nthawi

zonse ankangouza ena kuti apalase. Pofuna

kuchita kanthu kena pafunika kufunsa ena

kuti atithandize kachitidwe kake, kenaka

n’kuganizira bwino ngati tingathe. Zinthu

zoumiriza sizichita bwino.

Miyambi ya Patsokwe

547

“Diso la Lumbe lili m’kamwa,” n’kulinga

utaliona.

-Sibwino kumanena zinthu zimene

sukuzidziwa bwinobwino.

“Gona n’kuphe” sali patali!

-Ena akatiuza kuti tidikire, tisamanyinyirike

chifukwa nthawi sichedwa kutha.

Chachikulu n’kudikira kuti winayo

akwaniritse lonjezo lake.

“Gona” ndi mwini nyumba (mudzi).

-Ukakhala mlendo sungachite kapena

kutenga kalikonse, pokhapokha eni

pakhomopo atakuuza.

“Gona” ndi mwini wake wa nyumba.

-Ulamuliro wa chinthu umayenera kuchoka

kwa mwini wake chinthucho.

Miyambi ya Patsokwe

548

“Ichi chakoma, ichi chakoma,” pusi

adagwa chagada.

-Osamangotengeka ndi chilichonse koma

kumaika mtima pachinthu chomwe ukufuna.

Ukamati uku wapita, uku wapita, mapeto ake

umalephera zonse.

“Ichi chakoma,” adagona m’khufi atafika

kwawo.

-Ukamakonda kwambiri zosangalatsa,

umayenera kudziwa kuti mavuto

akukusunzumira mochenjera.

“Ichi n’changa” chidapinditsa mchira wa

nyani.

-Nthawi zina chifukwa cha umbombo

timawonongetsa zinthu. Munthu angaganize

kuti, “Ndikatulutsa pano ndidya ndi

anzangawa,” akamati akaone amakapeza

zawonongeka.

Miyambi ya Patsokwe

549

“Ichi n’changa” chinaolera pansalu.

-Kuumira kumachititsa kuti zinthu

ziwonongeke.

“Ichi n’chiyani” n’kulinga muli awiri.

-Anthu akakhala awiri amatha kuchita

zinthu modalirana ndipo amatha

kuthandizana wina akapeza mavuto.

“Ichi n’chiyani” n’kulinga muli awiri.

-Munthu aliyense amafuna wina woti

azimuphunzitsa, kumusangalatsa komanso

kumulangiza. Pawekha sungachite kalikonse.

“Ili kutali mvula,” m’mera uona ng’amba.

-Mawuwa amagwiritsidwa ntchito pamlandu

ngati mboni yachedwa. Mboniyo ikachedwa,

mlandu umayambikabe. Akabwera,

adzapereka umboniwo panthawi yake.

Mwambiwu umalimbikitsa anthu kuti

azichita zinthu pa nthawi yake.

Miyambi ya Patsokwe

550

“Ili kutali mvula,” mpesa umera

m’ngamba.

-Zinthu zimachitika panthawi yake

mosatengera kuti wina kapena chinachake

palibe.

“Ine panalibe” adang’amba thumba.

-Kumvetsera ena akamakufotokozera zimene

zinachitika iwe kulibe n’kothandiza kuti

usanene kapena kuchita zinthu zomwe

sumayenera kuchita.

“Izo zokha ndiye ayi,” fisi adakana nsatsi.

-Si zonse zimene anthu amanenera munthu

zimakhala zoona. Ngakhale munthu atakhala

wamakhalidwe oipa, pamafunika umboni

weniweni tisanamunene kuti wachita

cholakwa.

“Kakadachepa,” n’kuona msandulizo.

-Tizipempha thandizo kuchoka kwa anzathu

zinthu zisanafike poipa.

Miyambi ya Patsokwe

551

“Kwapita apongozi,” n’kulinga utawaona.

-Umayankhula za chinthu chimene wachiona

kapena ukuchidziwa.

“Kwaya kwaya” ndi uchitsiru, wochifuna

apempha yekha.

-Osamakakamiza munthu kuchita zimene

sakufuna.

“Kwaya kwaya” wam’kamwa, mtima uli

pomwepo.

-Mawuwa amanena za munthu amene

amalonjeza kukupatsa chinthu asakufuna

kukupatsa kapena mtima wakenso uli

pomwepo.

“Kwazizira” alibe mpani.

-Munthu waulesi amakhalanso ndi njala.

Tiyenera kugwira ntchito kuti tipeze zimene

tikufuna.

Miyambi ya Patsokwe

552

“Mbewa zidyana,” amatero Aphiri

pofunsira Naphiri.

-Mawuwa amanenedwa ngati anthu a

pachibale akuchita zosayenera pophwanya

chikhalidwe chawo monga pankhani ya

kukwatira.

“Mchakwawo” adanka ndi madzi.

-Tisamalekerere anthu akuchita zoipa

kapenanso akusochera pongoganiza kuti

adziwa chochita popeza ndi aakulu msinkhu

kapena ophunzira kwambiri. Mpofunika

kuwachenjeza ndi kuwathandiza kuti

asagwere m’mavuto.

“Momwemo” walinga utamwamo.

-Kuti munthu udziwe zinthu, umayenera

kuzichita kaye.

“Mpokoma pano” ndiye kuti mwagona

awiri.

-Kuti munthu uyamikire kuti pamudzi

Miyambi ya Patsokwe

553

kapena pakhomo ndi pabwino, umayenera

kucheza ndi ena n’kumva za anthu a

pakhomopo.

“Mulungu akundiona” anadyedwa ndi

ng’ona.

-Mulungu amathandiza munthu yemwe

amadzithandiza yekha.

“Muonere ine” adadyedwa ndi ng’ona.

-Si bwino kumadzionetsera kuti timadziwa

zinazake, chifukwa tikhoza kupeza mavuto.

“Mwana wa a uje wasamba” n’kulinga

atakhuta.

-Ngati mwana wasamba m’manja atadya

ndiye kuti wasangalala ndipo wakhuta.

Tizipatsa ana zinthu zokwanira kuti

azisangalala.

Miyambi ya Patsokwe

554

“N’chomwecho” chidaletsa Nkhandwe

kubwera kumudzi.

-Nkhandwe imakonda moyo wakutchire.

Munthu azichita zinthu zimene

zimamukomera.

“N’dzalemera” adamka ndi nguwo ya insa.

-Osamazengereza kugwira ntchito chifukwa

ukakhala waulesi umangosaukirasaukirabe

mpaka kufika povala chikopa cha insa.

“N’konzen’konze” adanyula maliro a eni.

-Munthu usamajijirike pa zinthu za eni

chifukwa ukhoza kupeza mavuto ngati

utalakwitsa chinachake.

“N’konzen’konze” adasupula mtembo wa

eni.

-Si bwino kumachita phuma pa zinthu

chifukwa umatha kupalamula nazo.

Miyambi ya Patsokwe

555

“N’kulen’kule” adagwa padzala.

-Kuthamangira kudziwika kumagwetsera

munthu m’mavuto.

“N’kulendinen’kulendine” adagwa padzala.

-Munthu wodzikuza komanso wonyada,

anthu ena amamuchepetsa n’kumuchititsa

manyazi.

“N’tapen’tape” adataya lipande.

-Timafunika kuchita zinthu mwachifatse,

osapupuluma chifukwa ukapululuma

umawononga zinthu ngati munthu amene

akufuna kuchotsa lipande (mphale)

mumtondo n’kumachita mwachangu

kwambiri amataya mphale yambiri.

“Ndafulumira” adadya zosapsa.

-Tisamachite zinthu mofulumira kwambiri

chifukwa pamapeto pake zimakhala

zosalongosoka. Tisamafotokoze nkhani

yomwe sitinaimvetse bwino, chifukwa

Miyambi ya Patsokwe

556

tingafotokoze zosapsa.

“Ndafulumira” anasiya tonde m’khola.

-Changu nthawi zina chimawononga zinthu

monga munthu amene sanatsegulire ziweto

zake.

“Ndakhupuka” adagwetsa nyumba.

-Si bwino kumadzitama ndi zimene tili nazo

chifukwa sitidziwa za mawa.

“Ndakulapa” n’kulinga utayenda naye.

-Kuti munthu udziwa khaliwe la mnzako

umayenera kukhala naye pafupi osati

kungomuona.

“Ndakuona” adalasa galu.

-Munthu wina ali kosaka nyama anzake

anamufunsa ngati waiona nyama. Iye

anangovomera chifukwa ankaona kuti achita

manyazi ndipo anagenda n’kupha galu wake

yemwe. Ngati sukudziwa zinazake si bwino

Miyambi ya Patsokwe

557

kungovomerera manyazi. Ndi bwino

kupempha ena kuti atithandize.

“Ndakwatira” n’kulinga utagonera.

-Osamafulumira kunena kuti wapeza banja

labwino mpaka patatha nthawi ndithu,

chifukwa anthu ena amabisa khalidwe lawo

poyamba.

“Ndaonera momwemo,” mwambi wa

gulugufe.

-Tsiku lina gulugufe ankamwa timadzi ta

m’maluwa. Ena pomufunsa anati: “Kodi

ukhuta timadzi tomweto?” Gulugufeyo

anayankha kuti, “Ndaonera momwemo”

kutanthauza kuti ndavomera zonse zimene

mukunenazo. Mawuwa amatanthauza kuti

tizikhutitsidwa ndi zimene tili nazo ngakhale

ena atamakhamba kuti sangathe kukhala

moyo wachoncho.

Miyambi ya Patsokwe

558

“Ndapakonda” adasiya khonde.

-Ukakhala mlendo uyenera kudziwa nthawi

yochoka chifukwa ukakhalitsa eni ake

amatopa nawe ndipo amasiya kukusamalira

ngati mlendo.

“Ndichite bwino,” gondwa anafa.

-Munthu wochita zinthu modzitama,

amadzachita manyazi tsiku lina.

“Ndidyeretu” adasowa mbewu.

-Tisamatsiriziretu katundu kapena mbewu

zonse. Tizisunga zina kuti zidzatithandize

m’tsogolo.

“Ndifa, ndifa” adalaula moyo nthawi

yaitali.

-Tisamapange malonjezo opanda pake.

“Ndikanakhala ine” anathawitsa anyani a

mwini wake.

-Mawuwa amanena za munthu womva

Miyambi ya Patsokwe

559

zayekha, wopereka malangizo osathandiza

kapena wosowetsa anzake mtendere.

“Ndikanakhala ine” sapita kumilandu.

-Pali anthu ena omwe amati zinthu zikadutsa

amayamba kunena maganizo awo koma

pamene zimachitika anangoti du. Kuchita

zimenezi sikuthandiza.

“Ndikhale nawo” analanda malo.

-Alendo ena amakhala ndi cholinga cholanda

malo, moti mukapanda kusamala amapezeka

kuti ayamba kukulamulirani. Chitsanzo ndi

bonongwe. Amayamba ndi m’modzi koma

kenako amadzadza munda wonse.

“Ndikometsendikometse” ndiko kuipitsa.

-Osamachita zinthu chifukwa chongofuna

kuyamikiridwa, mapeto ake umalakwitsa

kapena kuwononga zinthu.

Miyambi ya Patsokwe

560

“Ndikonzendikonze” adanyula mtembo wa

eni.

-Si bwino kumachita phuma pa zinthu

chifukwa umatha kupalamula nazo.

“Ndikudziwa kale” adamanga nyumba

yopanda khomo.

-Munthu amene amadziyesa wodziwa zonse

amalephera kufunsa ena, mapeto ake

amalakwitsa anthu n’kumuseka. Ndi bwino

kumafunsa ena.

“Ndikupha mawa” sali patali.

-Ena akatiuza kuti tidikire, tisamanyinyirike

chifukwa nthawi sichedwa kutha.

Chachikulu n’kudikira kuti winayo

akwaniritse lonjezo lake.

“Ndili ndekha ndili ndekha” ndi amene

akutha anthu.

-Anthu omwe alibe ana ndi amene amachitira

ana a ena nkhanza. Ena omwe alibe katundu

Miyambi ya Patsokwe

561

amabera anthu ena.

“Ndimam’khulupirira” anam’goneka

pabwalo.

-Pochita zinthu si bwino kumadalira ena kuti

adzatithandiza. Munthu wina

ankayembekezera kuti mnzake akumudziwa

ndipo amupatsa malo ogona. Zitalephereka

anagona panja.

“Ndimo alili” n’kulinga utamuona.

-Kuti udziwe khaliwe la wina umayenera

kukhala naye, m’malo mongogamula kuti ndi

woipa.

“Ndipatendipate” anapata bala.

-Ukamapupuluma kuti upeze zinazake

umakumana ndi mavuto.

“Nyemba zowola udya chaka chino”

n’kulinga uli nazo.

-Munthu sadandaula akawaputa yekha

Miyambi ya Patsokwe

562

mavuto.

“Nyemereko” adataya nsima kudzenje.

-Pali anthu ena omwe amafuna zonse zikhale

zawo moti sasangalala ena akapeza zawo.

Munthu womana amatha kuwononga zinthu

n’cholinga choti asapatse ena. Mwachitsanzo,

pobisa kupezeka kuti zawonongeka.

“Pali chikomere” adasiya chikho pabwalo.

-Munthu akamaumirira kuchita zoipa

amadzasiya chikho pakhonde, amamwalira

n’kusiya zomwe ankakondazo.

“Pangapanga” sapangika.

-Kungonena kapena kukalipira anthu

sikutanthauza kuti ntchito ichitika. Pogwira

ntchito pamafunika kukambirana komanso

kuthandizana.

“Pano mpakwathu” adagona ndi njala.

-Osamadalira ena kuti atipatsa zimene

Miyambi ya Patsokwe

563

tikufuna chifukwa mwina sangatipatse ndiye

tingavutike.

“Pano mpathu” n’kulinga utakhuta.

-Kuti munthu usangalale kapena uzichita

zina momasuka umafunika kudya kaye

mokwanira. Koma kuti chakudyacho

chipezeke umafunika kugwira ntchito.

Munthu amamera mizu pamalo ngati pali

chakudya chokwanira.

“Pano ndi panga” adakazinga chimera.

-Osamadalira ena kuti atipatsa zimene

tikufuna chifukwa mwina sangatipatse ndiye

tingavutike.

“Patse” samatula chiluli, amatula chiluli

ndi “taona apa.”

-Munthu wopempha amatha kugwiritsa

ntchito zimene wapatsidwa mwanzeru pomwe

munthu wakuba amangogwiritsa ntchito

zimene wapezazo mosasamala.

Miyambi ya Patsokwe

564

“Patsepatse” n’kulanda, munthu

woolowamanja amadziwa yekha.

-Ngati munthu safuna kupereka

asanapemphedwe, amaonedwa kuti ndi

womana. Ena ukawapempha

amangoperekera manyazi. Mwambiwu

umatanthauza kuti munthu azipereka mwa

kufuna kwake osati kuchita kumukakamiza.

“Pepani” sapoletsa chilonda.

-Kupepesa ukalakwa kapena ukawononga

chinthu chamwini sikukonza zinthu, koma

kuchitapo kanthu monga kubweza zimene

zawonongekazo.

“Pepani” sathetsa mlandu.

-Kupepesa ukalakwa kapena ukawononga

chinthu chamwini sikukonza zinthu koma

kuchitapo kanthu monga kubweza zimene

zaonongekazo.

Miyambi ya Patsokwe

565

“Pita uko” si kuyenda, kuyenda ndi “tiye

kuno.”

-Ukamaphunzitsa ena ntchito kapena

zinazake, si bwino kumangowauza zochita.

Ndi bwino kuwawonetsa m’mene angachitire

zinthuzo.

“Pwafu” salima, amalima ndi “bwete.”

-Munthu amene ali ndi njala sangalime,

koma amene wadya. Kuti munthu agwire

bwino ntchito, adye kaye.

“Pwatapwata phulu,” sapsetsa ndiwo.

-Kuti ndiwo monga nyemba zipse,

pamafunika ziwire kwa nthawi yaitali.

Choncho, kuziphula sikungapangitse kuti

zipse. Pochita zinthu umafunika kuzichita

motsimikiza mpaka zitatha.

“Sokanisokani,” anatenga jekete lothina.

-Munthu wina anakasiya jekete lake kwa

atelala kuti alibweze. Ndiye ankakakamiza

Miyambi ya Patsokwe

566

telalayo kuti alisoke mwachangu. Pamapeto

pake telala anasoka mwaphuma n’kupezeka

kuti iyeyo ataliyesa linali lothina.

Kupupuluma si kwabwino. Ndi bwino ena

akamatichitira zinthu tiziwapatsa nthawi

yokwanira kuti aichite molongosoka.

“Tidzaona mawa,” adagoneka munda.

-Ndi bwino kuyambiratu kuchita zinthu

m’malo modikira mawa, chifukwa zamawa

sizidziwika.

“Tilawetilawe” anatha lichero la mapira

osaviika.

-Chizolowezi chimayamba pang’onopang’ono

n’kufika poipa.

“Timwenji ife,” dzungu n’gonera kumodzi.

-Munthu angayankhule mawu amenewa

podandaula kuti alibe anzake omwe

angamamuuze nkhani za pamudzi.

Miyambi ya Patsokwe

567

“Tiyenitiyeni” sachoka, achoka ndi

vundumu.

-Kungonena mawu okha sikupindula koma

kuchita.

“Tizimve,” mwana wakwathu ali komweko.

-Ngakhale akufuna kubisa tidzamvabe

chifukwa anthu amene ali kumeneko

ndimadziwana nawo.

“Ukaphaneni” suchedwa kulekanitsa

mabwenzi.

-Ngati anthu ogwirizana amamvera kwambiri

zonena za anthu, ubwenzi wawo

umasokonekera.

“Ukutisokosera” n’kulinga utamva.

-Tisamadalire zonse zomwe anthu akutiuza.

“Usakanene” ndiye adanena.

-Osamakhulupirira anthu chifukwa sasunga

chinsinsi. Ukauza munthu kuti asunge

Miyambi ya Patsokwe

568

pakamwa mpamene amaulula.

“Vinavina” savinika.

-Si bwino kumakakamiza ena kuchita zimene

sakufuna.

“Wandiona bwanji?” palibe mlandu wa

maso.

-Chilichonse chinapangidwa kuti chigwire

ntchito yake pa nthawi yakenso.

“Zidzalezidzale” adalinda chiswe.

-Poyembekezera kuti dengu lidzadze, chiswe

chinadya dengulo. Tizichita zinthu

mwachangu popewa zinthu zimene

zingatilepheretse.

“Zikubwerera” anafa ndi linthumbu.

-Ukamachitira anzako zoipa, zomwezo

zimadzakuchitikira iweyo.

“Zili konku,” kudya kwa Awiza.

-Mawuwa amanena kuti tizidya mofanana

Miyambi ya Patsokwe

569

ngakhale ndisachitepo kanthu.

“Zili kwa amchira,” gondwa ali m’mphako.

-Mawuwa amanenedwa pokhana

kukhudzidwa ndi zinthu kapena nkhani za

ena.

“Zili uko” adabwera chaje osatenga

nsomba.

-Tisamatengeke ndi zinthu zongomva koma

tizifunsa kuti tidziwe chochita. Ngati munthu

wina anaona nsomba osafunsa n’kupezeka

wabwera chimanjamanja.

“Zili uku” anathyoletsa mwendo.

-Munthu wina anathyoka mwendo

pothamangira zongomva chabe. Tidziyamba

tafunsa kuti tidziwe mmene zilili

osamangomvera zilizonse zomwe ena

akunena.

Miyambi ya Patsokwe

570

“Ziliko” n’kulinga utatosako.

-Ndi bwino kukhala ndi umboni weniweni pa

zimene tamva tisanayambe kuchita zinthu.

“Ziri bwino momwemu,” anakhalitsa

tsindwi pakhudu.

-Pakhudu ndi pambali. Munthu wina anzake

ankamuthandiza kuika denga pankhokwe

yake. Ndiye anangoyankha mopupuluma kuti

ziri bwino momwemu ndipo denga lidakhala

pambali. Anthu ena samaika mtima wawo

pantchito, choncho amachita zosalongosoka

ntchitoyo n’kuwonongeka. Ena akabwera

amachita kudzayambiranso poyambirira.

Miyambi ya Patsokwe

571

Bonwell Rodgers

Pali anthu ena omwe amachititsa chidwi ponyadira

chinenero chawo. Iwo amaluka komanso kukazingira

chinenero chawo ndi nsinjiro za chiyankhulo komanso

mawu apatali. Amaluka mawu okhetsa dovu,

okhathamira ndi nsinjiro komanso ochititsa makutu

kumva kuzuna kwa chiyankhulo. Koma n’zomvetsa

chisoni kuti masiku ano ambiri akukankhira kumbali

chinenero chathu cha Chichewa n’kumasonkhezera

zinenero za mayiko ena. Chimenenechi ndi

chizindikiro choti kupanda kusamala Chichewa

chikhoza kutsenjira.

Miyambi ya Patsokwe

572

Dedicated to my beloved

sister, Susan. Thank you little

sister. Only a few match your

competence. You are clever,

I love you.

Hooray! Your file is uploaded and ready to be published.

Saved successfully!

Ooh no, something went wrong!