You also want an ePaper? Increase the reach of your titles
YUMPU automatically turns print PDFs into web optimized ePapers that Google loves.
! Yesu ada pempherera mapempho yasanu ndi imodzi. Yatatu yanali kwa mwini

Mulungu (kuti dzina la Mulungu iyeretsedwe, kuti ufumu wake udze ndipo kuti kufuna

kwake kuchitidwe padziko lapansi) aya yatatu yotsala, yanali yo pempherera pa

zofuna za munthu (zofuna zathu za lelo, ukhulukilidwa monga tikhulukila ena,

chichingilizo ndi chitetezo). Taonani kuti mapemphero yopereka kwa Mulungu ndiyo

yomwe yamatenga mbali yaikulu. Kuyeletsa dzina la Mulungu ndiye choyamba.

Chachiwiri, kuti ufumo wa Mulungu udze- uthandizila Akristu kuti akhale ngati Ambuye

YESU ndi ku peleka uthenga kwa osowa. Chachitatu, ndichakuti chifunilo cha Mulungu

chichitidwe padziko lochimwa lapansi pano monga chomwecho kumwamba. Pambuyo

pache Yesu apempherera zofunikila za moyo ndiponso apempherera chikulukililo

monga ifenso tikulukilila adani athu. Chimenechi chitisonyeza ukulu wache wa

chigwirizano kapena chiyanjano. Ambuye atisonyeza kuti tifunitsitse chiyanjano ndi

Mulungu chosaduku kupyolela ku umoyo olapa, ndiponse kuti tikhalenso mchiyanjano

chosaduku ndi Abale pamene tikulukililani wina ndi mzache tikalakwilana. Potsiliza

Yesu anapemphrera chitetezo ndi chimasuko ku Adani athu onse ndi ku mayeso

yonse. .

NDEMANGA/MAFUNSO: Kodi tinga gwiritsa bwanji nchito ichi chitsanzo cha pemphero

" kuti ifenso tiphindulile mʼmalo moti tizi phemphera popanda tanthauzo?

! Chotsiliza ndiponso Chachikulu chimene tipeza ndichakuti Ambuye Yesu ama

pempheladi. Samango lankhula kapena umphunzitsa chabe. EYA AMAPEMPHERA,

NDIPONSO APEMPHELADI. Ndichapafupi kuti Azibusa kapena Azitsogoleli kuti

aphunzitse anthu khalidwe yapemphero koma iwowo satenga nthawi yopemphera.

Tisachite mwachinyengo ai. Tisalankhule chabe, komabe tichite. Ngati tifunitsitsa

usata Ambuye Yesu, pemphero ndiyo funika tsiku ndi tsiku.

NDEMANGA/MAFUNSO: Fotokozelani abale njila imene yakuthandizani kuti mukhale ndi

" umoyo ozipeleka ku umoyo wapemphelo.

! 46